Mutu 10
Kodi Chingakhale Chinyengo Chochenjera?
M’KATI mwa zaka mazana ambiri anthu aona zochitika zodabwitsa kopamba. Miyala, matambula ndi zina zofanana nazo zikuyandama m’lengalenga monga ngati zikuyendetsedwa ndi manja osaoneka. Mau, kugogoda ndi mapokoso ena zamvedwa ngakhale kuli kwakuti panalibe magwero kepana chozichititsa choonekera. Anthu osaonekera bwino aonekera ndiyeno n’kuzimiririka mwamsanga. Nthawi zina zochitika zotero’zo zachitiridwa umboni bwino lomwe kwakuti palibe chikaikiro.
Anthu ambiri amalingalira zooneka za mtundu umene’wu kukhala umboni wakuti imfa simathetsa kukhalako kodziwa. Ena amakhulupirira kuti mizimu ya akufa ikuyesa-yesa mwa njira ina kuonedwa ndi amoyo ndi kulankhula nawo.
Koma munthu angafunse kuti: Ngati amene’wa ali’di okondedwa akufa amene akuyesa-yesa kulankhula ndi amoyo, kodi n’chifukwa ninji kuonekera kwao kumachititsa mantha okuona? Kodi, n’chiani kweni-kweni, chimene chiri kutseri kwa zinthu zotero’zo?
Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti imfa imathetsa kukhalako konse kozindikira. (Mlaliki 9:5) Chifukwa cha chimene’cho, payenera kukhala mphamvu zina zochititsa zinthu zimene kawiri-kawiri zimanenedwa kukhala zochititsidwa ndi mizimu ya akufa. Kodi mphamvu zimene’zo zingakhale chiani? Kodi izo zingakhale zanzeru? Ngati kuli choncho, kodi izo zingakhale ndi liwongo la kupitirizabe chinyengo chochenjera pa mtundu wa anthu?
Ndithudi ife sitikufuna kunyengedwa. Kunyengedwa kukatanthauza kutayikiridwa kwathu ndipo, mwina mwake, kutichititsa kulowa mu mkhalidwe wa upandu waukulu kwambiri. Ndicho chifukwa chake tiri ndi chifukwa chabwino chopendera umboni umene ulipo, tikumaulingalira, kuti titsimikizire kuti sitinagwere mu msampha wa chinyengo chochenjera. Tiyenera kukhala ofunitsitsa kubwerera m’mbuyo monga momwe kungathekere mu mbiri ya anthu m’kuyesa-yesa kupeza choonadi chonena za nkhani’yo.
Baibulo limatitheketsa kuchita zimene’zo. Iro limatibwezera m’mbuyo ku nthawi imene anthu awiri oyamba anakhalako. M’chaputala chachitatu cha Genesis Baibulo limasimba kukambitsirana kumene kungamveke kukhala kosakhulupiririka kwa ambiri lero lino. Komabe sindiko nthano. Kukambitsirana kumene’ku kumapereka njira yodziwira ponena zakuti kaya wonyenga wochenjera akugwira ntchito m’zochita za anthu?
CHIYAMBI CHA CHINYENGO
Tsiku lina, pamene sanali limodzi ndi mwamuna wake, mkazi woyamba, Hava, anamva mau. Muli monse anali mau a njoka. Ponena za kukambitsirana’ko, Baibulo limalongosola kuti:
“Ndipo njoka inali yakuchenjera yoposa zamoyo zonse za m’thengo zimene anazipanga Yehova Mulungu. Ndipo inati kwa mkazi’yo, Ea! Kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu? Mkazi’yo ndipo anati kwa njoka, Zipatso za mitengo ya m’mundamu tidye. Koma zipatso za mtengo umene uli m’kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umene’wo, musakhudze umene’wo, mungadzafe. Njoka’yo ndipo inati kwa mkazi’yo, Kufa simudzafai; chifukwa adziwa Mulungu kuti tsiku limene mukadya umene’wo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziwa zabwino ndi zoipa. Ndipo pamene anaona mkazi’yo kuti mtengo unali wabwino kudya, ndi kuti unali wokoma m’maso, mtengo wolalakika.”—Genesis 3:1-6.
Uthenga woperekedwa ndi njoka’wo unali bodza. Bodza limene’lo linali loyamba kulembedwa. Chotero magwero ake ayenera kukhala woyambitsa kapena atate wa mabodza. Popeza kuti bodza’lo linatsogolera ku zotulukapo zochititsa imfa, wabodza’yo anali’nso wambanda. Mwachionekere wabodza amene’yu sanali njoka yeni-yeni, cholengedwa chimene sichinapatsidwe mphamvu ya kulankhula. Koma payenera kukhala panali wina kutseri kwa njoka’yo, munthu wina amene, mwa chimene chingachedwe kulankhulira kutseri kwa kanthu kena, anapangitsa kuonekera kuti njoka’yo inali kulankhula. Zimene’zo siziyenera kuonekera kukhala zodabwitsa kwambiri kwa ife m’zaka zino za zana la makumi awiri pamene chotulutsira mau m’chokuzira mau cha rediyo kapena wailesi yakanema chingachititsidwe kunjenjemera m’njira yakuti chitulutse mau a munthu. Koma kodi ndani amene anali wolankhula kutseri kwa chinjoka’cho?
WONYENGA WOSAONEKA
Iye akudziwikitsidwa ndi Yesu Kristu, amene iye mwini anachokera kumwamba ndipo anadziwa zinene zinachitika m’malo osaoneka. (Yohane 3:13; 8:58) Pamene atsogoleri ena achipembedzo anali kufuna-funa kumupha, Yesu anati kwa iwo: “Inu muli ochokera mwa atate wanu Mdierekezi, ndipo zolakalaka zake za atate wanu mufuna kuchita. Iyeyu anali wambanda kuyambira pachiyambi, ndipo sanaima m’choonadi, pakuti mwa iye mulibe choonadi. Pamene alankhula bodza, alankhula za mwini wake; pakuti ali wabodza, ndi atate wake wa bodza.—Yohane 8:44.
Pokhala wabodza ndi wambanda, Mdierekezi mwachionekere ali munthu amene ali ndi nzeru. Chimene’chi chikuchititsa funso lakuti, Kodi iye anakhalako motani?
Baibulo limabvumbula kuti ngakhale dziko lapansi lisanakhaleko, anthu osaoneka auzimu, anali kusangalala ndi moyo. Yobu 38:7 amanena za anthu auzimu amene’wa, “ana a Mulungu,” kukhala ‘akupfuula mwachimwemwe’ pamene dziko lapansi linalengedwa. Monga “ana a Mulungu,” iwo analandira moyo wao kwa iye.—Salmo 90:2.
Chifukwa cha chimene’cho, uyo amene ananyenga Hava mwa njira ya chinjoka ayenera kukhala anali mmodzi wa ana amuna auzimu mene’wa, modzi wa zolengedwa zanzeru za Mulungu. Potsutsa chenjezo la Mulungu lonena za mtengo wa kudziwitsa zabwino ndi zoipa, amene’yu ananeneza Mlengi wake, akumapangitsa Mulungu kuonekera kukhala wabodza. Motero iye moyenerera akuchedwa “Mdierekezi” pakuti liu limene’lo latengedwa m’liu Lachigriki di·aʹbo·los, lotanthauza “woneneza monama, wonamizira, wosinjirira.” Mwa njira yake ya kachitidwe cholengedwa chimene’chi chinadzipanga kukhala chotsutsa Mulungu ndipo mwanjir imene’yo chinadzipanga kukhala Satana (Chihebri, sa·tanʹ; Chigriki, sa·ta·nasʹ), limene limatanthauza “wotsutsa.”
Yehova Mulungu sangaimbidwe mlandu wa chimene cholengedwa chimene’chi chinachita. “Ntchito yake ndi yangwiro,” limatero Baibulo ponena za Mulungu, “pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo, Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Iye analenga ana ake anzeru, mizimu ndi anthu, okhala ndi kukhoza kuchita chimene angafune. Iye sanawaumirize kum’tumikira koma iye anawafuna kuti atero mofunitsitsa, kuchokera m’chikondi. Iye anawapatsa kukhoza kukulitsa kum’konda koonjezereka-onjezereka monga Mulungu ndi Atate wao.
Komabe, cholengedwa chauzimu chimene chinadzipanga kukhala chotsutsa ndi choneneza Mulungu, sichinasankhe kuchititsa kukonda kwake Mlengi wake kukhala kwangwiro. Icho chinalola zikhumbo zadyera kukula mu mtima mwake. (Yerekezerani ndi 1 Timoteo 3:6.) Zimene’zi zikusonyezedwa m’khalidwe la “mfumu ya Turo” pa imene nyimbo ya maliro inaperekedwa mu ulosi wa Ezekieli. M’nyimbo ya maliro’yo, kukunenedwa kwa mfumu ya Turo imene inasanduka yosakhulupirika ku ufumu wa Israyeli kuti:
“Wakomera muyeso ndi chizindikiro, wodzala ndi nzeru wokongola wangwiro, Unali m’Edene, munda wa Mulungu . . . Unali kerubi wodzozedwa wakuphimba, ndipo ndinakuika unali pa phiri lopatulika la Mulungu, unayenda-yenda pakati pa miyala yamoto. Unali wangwiro m’njira zako chilengedwere iwe, mpaka chinapezeka mwa iwe chosalungama. . . Unadzikuza mtima chifukwa cha kukongola kwako, waipsya nzero zako; chifukwa cha kuwala kwako ndakugwetsa pansi.”—Ezekieli 28:12-17.
Mwana wamwamuna wauzimu wopanduka wa Mulungu, mofanana ndi “mfumu ya Turo,” analingalira modzikweza kwambiri. Kunyada kunam’chititsa kufuna kulamulira mtundu wa anthu, ndipo anafuna kupeza zolinga zake kupyolera mwa chinyengo. Kufikira lero lino unyinji wa mtundu wa anthu uli chikhalirebe mikhole ya chinyengo chimene’chi. Mwa kukana kuchita chifuno cha Mulungu monga momwe chalongosoledwera m’Mau ake, Baibulo, iwo kweni-kweni amaimira kumodzi ndi Satana. Mwa kutero, iwo amabvomereza bodza lofanana’lo limene Hava anabvomereza, ndiko kuti, lakuti kusankha kuchita mosemphana ndi chifuniro cha Mulungu kungadzetse phindu leni-leni.
Popeza kuti Mau a Mulungu amatsutsa kulankhula ndi akufa, awo amene amayesa kulankhula ndi akufa amadziika ku mbali ya Satana. Pamene kuli kwakuti iwo angaganize kuti iwo akulankhula ndi akufa, iwo akhala mikhole ya chinyengo. Monga momwe’di Satana anapangitsira kwa Hava kuonekera kuti njoka inali kulankhula, momwemo’nso iye mosabvuta angapangitse kuonekera kuti akufa akulankhula kupyolera mwa olankhula ndi mizimu. Kodi zimene’zi zikutanthauza kuti Satana ndiye wochititsa mwachindunji zochitika zonse zachilendo zimene kawiri-kawiri zimanedwa kukhala zochititsidwa ndi mizimu ya akufa? Kapena, kodi ena’nso akulowetsedwamo?
ONYENGA ENA OSAONEKA
Baibulo limabvumbula kuti Satana sindiye cholengedwa chokha chauzimu chopanduka. Chibvumbulutso 12:3, 4, 9 chimasonyeza kuti pali zina. M’ndime imene’yi ya Lemba la Satana Mdierekezi mophiphiritsira akusonyezedwa kukhala “chinjoka chofiira” chokhala ndi “mchira” umene “uguza limodzi la magawo atatu a nyenyezi zam’mwamba.” Inde, Satana anali wokhoza kugwiritsira ntchito chisonkhezero chake, mofanana ndi mchira, kuchititsa “nyenyezi” zina, ana auzimu a Mulungu, kugwirizana naye m’njira yopanduka. (Yerekezerani ndi Yobu 38:7, pamene ana amuna a Mulungu auzimu akuchedwa “nyenyezi za m’mawa.”) Zimene’zi zinachitika chigumula cha pa dziko lonse la pansi cha m’nthawi ya Nowa chisanachitike. Angelo ambiri, mosemphana ndi chifuno cha Mulungu, “anasiya pokhala pao-pao” kumwamba, nabvala matupi aumunthu, nakhala ndi akazi monga amuna ndi kubala ana atali-tali ochedwa Anefili. Ponena za zimene’zi, tikuuzidwa kuti:
“Ndipo panali pamene anthu anayamba kuchuluka padziko, ndi ana akazi anawabadwira iwo, kuti ana amuna a Mulungu anayang’ana ana akazi a anthu, kuti iwo anali okongola; ndipo anadzitengera okha akazi onse amene anawasanka . . . Pa dziko lapansi panali anthu akulu-kulu [Anefili] masiku omwewo ndipo’nso pambuyo pake ana amuna a Mulungu atalowa kwa ana akazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amene’wo ndiwo anthu amphamvu akale-kale, anthu omveka.”—Genesis 6:1-4.
M’kati mwa Chigumula ana amuna a Mulungu amene’wa anataya akazi ao ndi ana ao atali’wo. Iwo eniwo anaumirizika kubvula matupi. Ponena za chimene chinawachitikira pambuyo pake, Baibulo limasimba kuti: “Mulungu sanalekerera angelo adachimwa’wo, koma anawaponya kundende nawaika ku maenje a mdima, asungike akaweruzudwe.” (2 Petro 2:4) Ndipo pa Yuda 6 iro limanena’nso kuti: “Angelo’nso amene sanasunga chikhalidwe chao choyamba, komatu anasiya pokhala pao-pao, adawasunga m’ndende zosatha pansi pa mdima, kufikira chiweruziro cha tsiku lalikulu.”
Popeza kuti malongosoledwe amene’wa akunena zolengedwa zauzimu, kuli koonekera bwino kuti ‘maenje a mdima waukulu’ ndi ‘ndende zosatha’ siziri zeni-zeni. Mau amene’wa amangopereka kwa ife chithunzi-thunzi cha kuletsedwa, nkhalidwe wotsitsidwa wosiyanitsidwa ndi kuunika konse kwaumulungu.
Palibe maziko Amalemba onenera kuti angelo osamvera amene’wa ali m’malo ofanana ndi Malo a mdima anthanthi a Iliad ya Homer, ndiko kuti, m’ndende ya pansi kwambiri m’mene mzimu wa Cronus ndi wina wa Titan inanenedwa kukhala itabindikiritsidwamo. Mtumwi Petro sanakhulupirire iri yonse ya milungu yanthanthi yotero’yo. Chotero palibe chifukwa chaonenera kuti kugwiritsira ntchito kwake mau Achigriki’wo ‘kuponya m’Malo amdima [Tartarus]’ kunasonyeza’di kukhalako kwa malo anthanthi ochulidwa ndi Homer zaka mazana asanu ndi anai kale’lo. Kunena zoona, m’mau Achigriki ‘kuponya m’Malo amdima’ ndiwo liu limodzi lokha, mneni, tar·ta·roʹo. Amagwiritsiridwa’nso ntchito kutanthauza kutsitsidwira ku mkhalidwe wotsikitsitsa.
Kuti tilongosole mwa fanizo, mau Achinyanja’wo ‘kutsitsa pa malo ali ndi dzina’lo “malo.” Komabe kugwiritsira nchito kwathu mau’wo sikumatanthauza kuti malo eni-eni m’malo ena a pa dziko lapansi akulowetsedwamo m’kachitidwe ka kutsitsidwa’ko. Chimodzi-modzi’nso liu Lachigriki lotembenuzidwa kukhala “kuponya m’Malo amdima [Tartarus]’ silidfunikira kuonedwa kukhala likusonyeza kukhalako kwa malo eni-eni, koma kukhala likusonyeza mkhalidwe.
Pa 1 Petro 3:19, 20 zolengedwa zauzimu zotsitsidwa pa malo’zo zikuchedwa kukhala “mizimu inali m’ndende, imene inakhala yosamvera kale, pamene kuleza mtima kwa Mulungu kunalindira, m’masiku a Nowa, pokhala m’kukonzeka chingalawa.” Motero Baibulo limalongosola momvekera bwino kuti pambuyo pa Chigumula “angelo adachimwa’wo” analowa mu mkhalidwe wa kuletsedwa kuchita kanthu. Palibe chisonyezero cha Baibulo chakuti iwo anali okhoza kubvala thupi ndi kuchita ntchito zoonekera pa dziko lapansi pambuyo pa Chigumula. Chotero moyenerera kuyenera kukhala kwakuti chiletso m’chimene analowa chinapangitsa kukhala kosatheka kwa iwo kubvala thupi kawiri’nso.
CHENJERANI NDI CHISONKHEZERO CHA ZIWANDA
Komabe, kuyenera kuzindikiridwa kuti, angelo osamvera’wo, amene tsopano anadzachedwa ziwanda, anali ndi chikhumbo champhamvu cha kugwirizana kwambiri ndi anthu. Iwo anali ofunitsitsa kusiya malo ao akumwamba chifukwa cha chisangalala cha kukhala ndi akazi monga amuna. Umboni Wamalemba umasonyeza kuti, ngakhale kuli kwakuti aletsedwa kugwirizana kwakuthupi kotero’ko tsopano, iwo sanasinthe zikhumbo zao. Iwo amafuna-funa njira iri yonse yotsegulira iwo kulankhula ndi anthu ndipo ngakhale kuwalamulira. Yesu Kristu anachula zimene’zi, akumagwiritsira ntchito mau ophiphiritsira m’kunena kuti:
“Koma mzimu wonyansa, utatuluka mwa munthu, umapitirira malo opanda madzi kufuna-funa mpumulo, osaupeza. Pomwepo unena, Ndidzabwerera kunyumba kwanga, konkuja ndinatulukako; ndipo pakufikako uipeza yopanda wokhalamo, yosesedwa ndi yokonzedwa. Pomwepo upita, nutenga pamodzi ndi uwu mizimu yina inzake isanu ndi iwiri yoipa yoposa mwinu yekhayo, ndipo ilowa, nikhalamo. Ndipo matsirizidwe ake a munthu uyu akhala oipa oposa mayambidwe ake.”—Mateyu 12:43-45.
Chifukwa cha chimene’cho kuli kofunika kwambiri kukhala maso kuopera kuti munthu angadzilowetse m’chisonkhezero cha ziwanda. Iye angakhale wosatsimikizira kwambiri ponena za iye mwini ndi mtsogolo mwake. Iye motaya mtima angafune chitsimikiziro chakuti zinthu zidzamuyendera bwino. Kapena iye angapeze chikondwerero china m’zooneka zina zodabwitsa ndi zochititsa mantha za machita-chita amatsenga. Iye angamve za munthu wina amene motsimikizirika anganeneretu za m’tsogolo molondola. Kapena iye angamve za njira zosiyana-siyana za kuombeza zogwiritsiridwa ntchito—matabwa oombezera ESP (kudziwa zinthu molota), magonedwe a masamba a tii m’makapu, maonekedwe a kuyandama kwa mafuta pa madzi, anam’londola, maphenda, malo ndi mayendedwe a nyenyezi ndi mapulaneti (kupenda nyenyezi), kuuwa kwa agalu, kuuluka kwa mbalame, kuyenda kwa njoka, kuyang’ana mpira wa galasi ndi zofanana nazo. Mkhalidwe wake ungaonekere kukhala wopanda chiyembekezo kapena chikondwerero chake chingakhale chachikulu kwambiri kwakuti iye angasankhe kukafuna wopenduza kapena wolankhula ndi mizimu kapena kutembenukira ku mpangidwe wina wa kuombedza. Iye angakhale wofunitsitsa kuyesa kanthu kali konse kamodzi kokha.
Kodi zimene’zo n’zanzeru? Ndithudi ai. Chidwi chake, chingatsogolere ku kulowa kwake mu ulamuliro wa ziwanda. Njira imene’yo m’malo mwa kudzetsa mpumulo kwa iye ndi chitonthozo, mkhalidwe wake ungangoipira-ipira. Zododometsa za mizimu zinga’msowetse tulo ndi kudzaza ngakhale maola a usana ndi mantha. Iye angayambe kumva mau odabwitsa, onena kuti iye adziphe kapena aphe wina wake.
Chifukwa cha chime’cho kodi si kwanzeru kupewa kuthekera kotero’ko ndi kulewa mipangidwe yonse ya kuombeza? Yehova Mulungu samaona nkhani imene’yi mopepuka. Kuti atetezere Aisrayeli kuti asanyengedwe ndi kubvulazidwa ndi mizimu yoipa, iye anapangitsa kachitidwe ka kuombedza kukhala chimo lokhala ndi chilango cha imfa, akumanena m’Chilamulo kuti: “Munthu wamwamuna kapena wamkazi wakubwebweta, kapena wanyanga, azimupha ndithu.”—Levitiko 20:27.
Lingaliro la Mulungu ponena za olankhula ndi mizimu, onse oneneratu za m’tsogolo ndi openduza silinasinthe. Lamulo la Mulungu likutsutsabe onse olankhula ndi mizimu.—Chibvumbulutso 21:8.
Chifukwa cha chimene’cho yesetsani kukaniza kunyengedwa ndi zolengedwa zoipa zauzimu. Ngati mutamva mau achilendo, mwina mwake osonyeza kuti ndiwo aja a bwenzi kapena wachibale wakufa, musamvetsere mpang’ono pomwe. Itanirani pa dzina la Mulungu woona, Yehova kuti akuthandizeni kulimbana ndi kulowa m’chisonkhezero cha ziwanda. Monga momwe Mwana wa Mulungu mwini analangizirira, pempherani kuti: ‘Ndipulumutseni kwa woipa’yo.’ (Mateyu 6:13) Ponena za zinthu zogwirizanitsidwa ndi kuombedza, tsanzirani chitsanzo cha awo amene analandira kulambira koona mu Efeso wakale. “Ambiri a iwo akuchita zamatsega [kumene’ko] anasonkhanitsa mabukhu ao, nawatentha pamaso pa onse.” Zamtengo wapatali monga momwe zinthu zimene’zi zinaliri, iwo sanakaikire kuziononga.—Machitidwe 19:19.
Polingalira chitsanzo chimene’chi, kodi mukaganiza kuti kukakhala koyenera kugwirizana mwadala ndi awo amene amadziwika kukhala akuchita kulankhula ndi mizimu ndi kulandira mphatso zochokera kwa iwo? Kodi izo sizingakhale zipangizo mwa zimene mungalowere m’chisonkhezero cha ziwanda?
Kuzindikira kwathu kuti mizimu yoipa kawiri-kawiri ndiyo imene imachititsa anthu kuona kapena kumva zooneka zodabwitsa ndi zochititsa mantha—mau, kugogoda ndi anthu osaonekera bwino zimene palibe zochititsa zoonekera bwino—ndiko chinthu chachikulu m’kutitetezera kunyengedwa. Chidziwitso chimene’chi chidzatimasula ku kuopa akufa ndi m’kuwachitira madzoma opanda pake. Chidzathandiza kutetezera kugwidwa kwathu ndi mizimu yoipa.
Koma ngati titi titetezeredwe ku mbali iri yonse ya chinyengo chimene Satana ndi ziwanda zake achichita mogwirizana ndi akufa, tiyenera kukhulupirira ndi kuchita mogwirizana ndi Baibulo lathunthu. Chimene’chi chiri chifukwa chakuti iro lonse liri Mau ouziridwa a Mulungu.