Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 14 tsamba 117-124
  • Chimene ‘Chizunzo m’Nyanja ya Moto’ Chimatanthauza

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chimene ‘Chizunzo m’Nyanja ya Moto’ Chimatanthauza
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • CHIZUNZO CHOPHIPHIRITSIRA
  • CHIZUNZO CHAMUYAYA SICHIMAGWIRIZANA NDI UMUNTHU WA MULUNGU
  • Kodi Nyanja ya Moto N’chiyani? Kodi ndi Yofanana ndi Gehena?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Helo—Chizunzo Chosatha Kapena Manda a Onse?
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kodi Helo Ndimalo a Chizunzo?
    Galamukani!—1986
  • Kodi Helo Ndimalo Amtundu Wotani?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 14 tsamba 117-124

Mutu 14

Chimene ‘Chizunzo m’Nyanja ya Moto’ Chimatanthauza

KODI mukadachita motani ngati, tsopano pakuti mukudziwa zimene Baibulo limanena ponena za mkhalidwe wa kusadziwa kanthu wa akufa, mukanapeza lemba la Baibulo likuchula malo a chizunzo? Kodi mukanalingalira kuti limene’li likupereka chifukwa chabwino chonyalanyazira malemba ena onse ndi kukhalabe ndi lingaliro lakuti payenerabe kukhala kuthekera kwa kukhalako kodziwa kopitirizabe pambuyo pa imfa? Kapena, kodi mukanapanga kupenda kosamalitsa kwa mau a pambuyo ndi patsogolo pa lemba’lo kuti mutsimikizire chimene lemba’lo lingatanthauze kweni-kweni ndi m’mene likugwirizanira ndi mbali ina yonse ya Baibulo?

Chifukwa cholingalirira zimene’zi n’chakuti bukhu la Baibulo la Chibvumbulutso limanena’di, za “chizunzo” mu “nyanja ya moto.” Chibvumbulutso 20:10 chimalongosola kuti: “Mdyerekezi wakuwasokeretsa anaponyedwa m’nyanja ya moto ndi sulfure, kumene’ko kuli’nso chirombo’cho ndi mneneri wonyenga’yo; ndipo adzazunzidwa usana ndi usiku ku nthawi za nthawi.”—Onaninso Chibvumbulutso 19:20.

Kodi ndi motani m’mene awo oponyedwa “m’nyanja ya moto” amazunzidwira? Chakuti sitiyenera kufulumira m’kulingalira mau amene’wa monga momwe aliri chiri choonekera bwino kuchokera mu mkhalidwe weni-weni wa bukhu la Chibvumbulutso. Mau oyambirira a bukhu’lo amati: “Chibvumbulutso cha Yesu Kristu, chimene Mulungu anam’bvumbulutsira achionetsere akapolo ake, ndicho cha izi ziyenera kuchitika posachedwa: ndipo potuma mwa mngelo wake anazindikiritsa izi kwa kapolo wake Yohane.”—Chibvumbulutso 1:1.

Monga momwe kwalongosoledwa pamene’po chibvumbulutso chimene’chi chunaperekedwa ‘m’zizindikiro.’ Bwanji, nanga, ponena za “nyanja ya moto” ndi “chizunzo” m’menemo? Kodi izo ziri zeni-zeni kapena kodi izo ziri’nso “zizindikiro” kapena ziphiphiritso?

Chidziwitso choonjezereka chonena za chimene chikuponyedwa m’nyanja ya moto, kuphatikiza pa Mdierekezi, “chirombo” ndi “mneneri wonyenga,” chimamveketsa bwino lomwe nkhani’yo. Onani mau a Chibvumbulutso 20:14, 15: “Imfa ndi Hade zinaponyedwa m’nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto. Ndipo ngati munthu sanapezedwa wolembedwa m’buku la moyo, anaponyedwa m’nyanja yamoto.”

Tsopano, kodi n’kotheka kwa imfa ndi Hade kuponyedwa m’nyanja yeni-yeni ya moto? Mwachionekere ai, pakuti izo siziri zinthu, zinyama kapena anthu. Imfa iri mkhalidwe. Kodi ndi motani m’mene ingaponyedwere m’nyanja yeni-yeni ya moto? Ponena za Hade, ali manda onse a mtundu wa anthu. Kodi ndi nyanja ya mtundu wanji imene ikam’sunga?

Ndiyeno’nso, Chibvumbulutso 20:14, 15 sichimanena kuti nyanja’yo iri yeni-yeni. M’malo mwake, timawerenga kuti “nyanja yamoto” yeni-yeni’yo iri chizindikiro kapena phiphiritso la “imfa yachiwiri.” Tanthauzo lofanana’lo likuchulidwa pa Chibvumbulutso 21:8 kuti: “Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse amabodza, cholandira cha chidzakhala m’nyanja yotentha ndi moto ndi sulfure; ndiyo imfa yachiwiri.”

Popeza kuti nyanja ya moto iri phiphiritso la imfa yachiwiri, kuponyedwamo kwa imfa ndi Hade kuli njira yophiphiritsira chabe yonenera kuti zimene’zi zidzachotsedwa kosatha. Imene’yi imagwirizana ndi mau a Baibulo akuti ‘mdani wotsiriza, imfa, ayenera kufafanizidwa.” (1 Akorinto 15:26) Ndipo, popeza kuti Hade, manda onse a mtundu wa anthu, akukhuthulidwa ndipo “sipadzakhala’nso imfa, “zimene’zo zikutanthauza kuti Hade akuleka kugwira ntchito, akuleka kukhalako.—Chivumbulutso 20:13; 21:4.

CHIZUNZO CHOPHIPHIRITSIRA

Pamenepaa, kodi n’chiani, chimene chiri “chizunzo” cholandiridwa ndi anthu oipa ndi ena amene akuponyedwa “m’nyanja yamoto”? Popanda kukhalako kozindikira, iwo sakanabvutika ndi chizunzo cheni-cheni, kodi iwo akanatero? Ndipo mulibe chiri chonse m’Malemba chosonyeza kuti iwo adzakhala ndi kukhalako kozindikira kuli konse. Chotero kodi n’chifukwa ninji Baibulo limachula chizunzo chosatha “m’nyanja yamoto”?

Popeza kuti “nyanja yamoto” iri yophiphiritsira, chizunzo chogwirizanitsidwa nayo chiyenera’nso kukhala chophiphiritsira kapena chokuluwika. Chimene’chi chingazindikiridwe bwino kwambiri mothandizidwa ndi chimene Baibulo limanena ponena za zinthu zimene zikuponyedwa “m’nyanja yamoto.” Chimene tiyenera kuzindikira n’chakuti “imfa yachiwiri” ndiyo imene ikuphiphiritsidwa ndi “nyanja yamoto.” Imfa ya Adamu, ndiko kuti, imfa imene mtundu wonse wa anthu wobadwa unailandira kwa Adamu ndi Hava iwo atachimwa, sikuyerekezeredwa ndi chinthu chochititsa mantha chotero’cho, ngakhale kuli kwakuti infa ndiyo ‘mphotho yake ya uchimo.”—Aroma 6:23.

Yesu anayerekezera ndi tulo mkhalidwe wa imfa wa awo amene amafa chifukwa cha uchimo wobadwa nao. Mwa chitsanzo, ponena za “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo; koma ndimuka kukamuukitsa iye tulo take.” (Yohane 11:11) Pambuyo pake, ngakhale Yesu anagona tulo ta imfa kwa masiku atatu. “Tsopano Kristu waukitsidwa kwa akufa, chipatso choundukula cha iwo akugona [mu imfa].” (1 Akorinto 15:20) Imfa iri ngati tulo, popeza kuti imathera m’kuuka.

Komabe, awo amene ayenera kukumana ndi “imfa yachiwiri” alibe chitonthozo cha chiyembekezo cha chiukiriro. Yao’yo siri tulo. Iwo samauka ku chionongeko mu imfa yachiwiri. Popeza kuti mkhalidwe wopanda chiyembekezo umene’wu umawamanga, iwo ‘akuzunzidwa kosatha’ m’lingaliro la kukanizidwa kosatha kukhala ndi kukhalako kuli konse kozindikira kapena ntchito. Chakuti kuletsedwa kwao mu “imfa yachiwiri” kukuyerekezeredwa ndi chizunzo mwa kubindikiritsidwa m’ndende kukusonyezedwa ndi Yesu m’fanizo lake la kapolo wosayamikira ndi wopanda chifundo. Ponena za kachitidwe kamene mbuye wake anam’chitira, Yesu anati: “Ndipo mokwiya mbuye’yo anam’pereka kwa ozunza kufikira iye atabwezera ngongole yake yonse.” (Mateyu 18:34, Jerusalem Bible), New World Translation imasonyeza amene ali ozunza amene’wa mwa kumati: “Atatero atapsya mtima, mbuye wake, anam’pereka kwa osunga ndende [mau am’tsinde: ozunza], mpaka iye atabwezera zonse zimene anakongola.”

Cheni-cheni’cho chakuti “nyanja yamoto” iri phiphiritso la ‘imfa yachiwiri” chimachotsa lingaliro la kukhala kwake malo a chizunzo chozindikira. Palibe pali ponse pamene Baibulo limasonyeza’di kuti akufa angakhale ndi chizunzo chozindikira, koma akufa ataya kuzindikira konse. Ponena za akufa’wo okhala m’manda onse a mtundu wa anthu, Baibulo limati: “Apo oipa aleka kumabvuta; ndi apo ofoka mphamvu akhala m’kupumula. Awo a m’kaidi apumula pamodzi, osamva mau a wofulumiza wao. Ang’ono ndi akulu ali komwe; ndi kapolo amasuka kwa mbuyake.”—Yobu 3:17-19.

Monga momwe’di imfa imene anthu onse akupitirizabe kubvutika nayo imathetsera kuzindikira ndi kulingalira konse, chimodzi-mozi’nso “imfa yachiwiri.” Komabe, palibe chikhululukiro cha machimo kapena kuombola kumene kuli kothekera kwa awo olangidwa ndi “imfa yachiwiri.” Mkhalidwe wa chitonzo umene’wo ndiwo gawo lao kosatha. Kukumbukiridwa kwao kuli ngati kwabvunda.—Yesaya 66:24; Miyambo 10:7.

Komabe ngakhale anthu oipa’wo asanaponyedwe m’chionongeko chotheratu, “imfa yachiwiri,” iwo amazunzika. Kumene’ku kukuchulidwa mophiphiritsira pa Chibvumbulutso 14:9-11 kuti: “Ngati wina alambira chirombo’cho, ndi fano lake, iye’nso adzamwako ku vinyo wa mkwiyo wa Mulungu, wokonzeka wosasanganiza m’chikho cha mkwiyo wake; ndipo adzazunzika ndi moto ndi sulfure pamaso pa angelo oyera mtima ndi pamaso pa Mwanawankhosa; ndipo utsi wa kuzunza kwao ukwera ku nthawi za nthawi; ndipo sapuma usana ndi usiku iwo akulambira chirombo’cho ndi fano lake, ndi iye ali yense akalandira lemba la dzina lake.” Kodi olambira “chirombo’cho” ndi “fano” lake akuzunzidwa ndi chiani? Mau a Chibvumbulutso amene akusatirapo mwamsanga pambuyo pake amapereka mfungulo: “Pano pali chipiriro cha oyera mtima, kwa iwo akusunga malamulo a Mulungu, ndi chikhulupiriro cha Yesu.”—Chibvumbulutso 14:12.

Sikukanafunikira chipiriro kwa oyera mtima’wo ngati olambira “chirombo’cho” ndi fanizo” lake akanatsekeredwa ku malo eni-eni a chizunzo. Olambira onyenga amene’wo pamenepo akanalandidwa mphamvu yonse ya kuchititsa chibvulazo kwa atumiki okhulupirika a Mulungu. Koma malinga m’machitidwe audani ndi ankhanza otsutsa “oyera mtima.”

Cheni-cheni chakuti “oyera mtima” akulowetsedwa m’nkhani’yo chikusonyeza kuti iwo ali zipangizo zodzetesera chizunzo pa oipa. Kodi zimene’zi zingakhale choncho motani? Eya, iwo amalengeza uthenga umene umasonyeza chionongeko chosatha choyembekezera olambira “chirombo’cho” ndi fano” lake. Uthenga umene’wu umazunza olambira onyenga amene’wa, osawapumitsa usana kapena usiku. Ndicho chifukwa chake iwo amayesa chiri chonse chimene angathe kuchita kutontholetsa atumiki a Mulungu. Chizunzo chotulukapo‘cho chimafunikira chipiriro kwa “oyera mtima.” Potsirizira pake, pamene olambira “chirombo’cho” ndi “fano” lake aonongedwa monga ngati ndi “moto ndi sulfure,” umboni wa chionongeko chotheratu chimene’cho, ngati utsi, udzabwera kumwamba kosatha.

Kutheratu kwa chionongeko chimene’cho kungathe kuyerekezeredwa ndi chimene chinagwera mizinda ya Sodumu ndi Gomora. . Wophunzira Yuda analemba kuti: “Sodomu ndi Gomora, ndi mizinda yakuizungulira  . . iikidwa chitsanzo, pakuchitidwa chirango cha moto wosatha.” (Yuda 7) Moto umene unaononga mizinda imene’yo unali utazima kale Yuda asanalembe kalata yake. Koma umboni wachikhalire ndi “wosatha” wa kuononga kwa moto umene’wo unalipobe, pakuti mizinda imene’yo inapitirizabe kukhala palibe.

CHIZUNZO CHAMUYAYA SICHIMAGWIRIZANA NDI UMUNTHU WA MULUNGU

Chakuti chionongeko chotheratu, osati chizunzo chozindikira kwamuyaya, ndicho chirango choperekedwa kwa awo opitirizabe m’chipanduko chimagwirizana’nso ndi Mulungu amabvumbula ponena za iye mwini m’Mau ake Baibulo. Yehova Mulungu ali ndi malingaliro achifundo kwa zolengedwa zake zazinyama.

Talingalirani kwa kanthawi lamulo la Mulungu lonena za nkhunzi yogwira ntchito: “Musamapunamiza ng’ombe popuntha tirigu.” (Deuteronomo 25:4) Lamulo limeneli linasonyeza nkhawa yachifundo ya Mulungu ndi chisamaliro kwa zinyama zopanda nzeru. Nkhunzi’yo sinayenera kuzunzidwa mwa kuletsedwa moumiriza kukhutiritsa chikhumbo chake cha kudya tirigu amene inali kupuntha.

Yaikulu kopambana ndiyo nkhawa ndi chikondi cha Mulungu kwa anthu koposa kwa zinyama zopanda nzeru’zo. Monga momwe Yesu Kristu anakumbutsira ophunzira ake kuti: “Kodi mpheta zisanu sizigulidwa timakobiri tiwiri? Ndipo palibe imodzi ya izo iiwalika pamaso pa Mulungu; komatu ngakhale matsitsi onse a pamutu panu awerengedwa. Musaopa, muposa mtengo wake wa mpheta zambiri.”—Luka 12:6, 7.

Pamenepa, kodi sikukakhala kosagwirizana kotheratu, kwa ali yense kunena kuti Mulungu wokhala ndi malingaliro achifundo otero’wo akazunza kweni-kweni anthu ena kwamuyaya? Kodi ndani wa ife amene akafuna kuona munthu wina akubvutika ndi chuzunzo choopsya ngakhale kwa ora limodzi? Kodi si zoona kuti anthu ankhanza okha akakondwera kuona ena akubvtika? Kodi lingaliro lathu la m’kati la chikondi ndi chilungamo silimabvutika pamene timamva kuti atate wina anazunza mwana wake mpaka pafupi imfa chifukwa cha kachitidwe kena ka kusamvera? Mosasamala kanthu za m’mene mwana’yo angakhalire anali woipa, timaona kukhala kosatheka kukhala ndi malingaliro ali onse achifundo kwa atate wotero’yo.

Komabe, kuchita kwa Mulungu kwachifundo ndi opanda ungwiro, kumakondweretsa’di lingaliro lathu la makhalidwe. Kumakondweretsa mitima yathu ndi kutichititsa kuyandikira pafupi kwambiri kwa Mlengi wathu. Tangoganizirani: Ngakhale pamene anthu akuyenerera chirango, Mulungu samakondwera kuchipereka. Monga momwe mneneri Yeremiya ananenera ponena za chiweruzo cha Mulungu chimene chinagwera Yerusalemu wosakhulupirira kuti: “Angakhale aliritsa, koma adzachitira chisoni monga mwa kuchuluka kwa zifundo zake. Pakuti samasautsa dala, ngakhale kumvetsa ana a anthu chisoni.”—Maliro 3:32, 33.

Ngati siziri mu mtima mwake kusautsa kapena kumvetsa chisoni anthu amene akuyenerera chirango, kodi ndi motani m’mene Yehova Mulungu kwamuyaya akayang’anira, mokondwera pa kubvutika kwa anthu oipa? Ndipo’nso, kodi kukatumikira chifuno chotani? Malinga ndi kunena kwa chiphunzitso chopanda malemba cha atsogoleri achipembedzo cha “helo wamoto” ngakhale ngati obvutika ndi chizunzo’wo anafuna kusintha iwo, saknatha kutero, kapena’nso kuongolera mkhalidwe wao. Komabe, Mau a Mulungu, amasonyeza mosalakwika kuti chionongeko chotheratu, osati chizunzo, ndicho chirango cha onse amene amapitirizabe m’kuipa.

Pozindikira kuti Yehova ali Mulungu wachikondi ndi wolungama, tingakhale otsimikizira kuti chifuno chake kaamba ka awo amene akufuna kum’tumikira chiri chabwino kwambiri’di. Pamenepo, ndi chiyembekezo chaphamphu tiyeni tipende Malemba kuti tiphunzire za makonzedwe achikondi amene iye wapanga kumasula mtundu wa anthu ku ukapolo wa kudwala ndi imfa.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena