Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • ts mutu 19 tsamba 167-176
  • Mabiliyoni Amene Ali Akufa Tsopano Adzakhala’nso ndi Moyo Posachedwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mabiliyoni Amene Ali Akufa Tsopano Adzakhala’nso ndi Moyo Posachedwa
  • Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • MAZIKO A CHIKHULUPIRIRO
  • KUUKITSIDWIRA KU MOYO WAUZIMU
  • KUUKITSIDWIRA KU MOYO PA DZIKO LAPANSI
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’champhamvu
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Chiukiriro—Cha Yani, ndipo Kuti?
    Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Chiyembekezo cha Chiukiriro N’chotsimikizirika!
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Njira Yokhayo Yothetsera Imfa
    Nsanja ya Olonda—2006
Onani Zambiri
Kodi Moyo Uno Ndiwo Wokha Umene Ulipo?
ts mutu 19 tsamba 167-176

Mutu 19

Mabiliyoni Amene Ali Akufa Tsopano Adzakhala’nso ndi Moyo Posachedwa

BOMA Laufumu lokhala m’manja mwa Yesu Kristu ndi olamulira anzake 144,000 lidzapereka’di madalitso akulu pa opulumuka “chitsautso chachikulu.” Pa nthawi imene’yo ziyambukiro zoononga za kudzilowetsa kwa Adamu ndi ana ake osabadwa mu uchimo sizidzakumbukiridwa m’njira yakuti m’kumva ululu mwamaganizo ndi mwamalingaliro. Mau ouzirida a mneneri Yesaya akulonjeza kuti: “Zinthu zakale sizidzakumbukika, pena kulowa mumtima.”—Yesaya 65:17.

Kuti zimene’zo zikhala choncho, ululu ndi chisoni zochititsidwa ndi ziyambukiro zochititsa imfa za uchimo ziyenera kuchotsedwa kotheratu. Zimene’zi zikaphatikizapo kuukitsa mabiliyoni ochuluka a anthu amene tsopano ali akufa. Chifukwa ninji?

Eya, ngati mukanapulumuka “chitsautso chachikulu,” kodi mukanakhala achimwemwe kweni-kweni kudziwa kuti mabwenzi ndi achibale okondedwa amene anamwalira zaka zapita’zo anali chikhalirebe opanda moyo ndi madalitso ake? Kodi kumene’ku sikukachititsa ululu wa mtima ndi maganizo kwa inu? Kuti achotse kuthekera kuli konse kwa ululu wotero’wo, akufa ayenera kuukitsidwa. Kokha ngati iwo angaukitsidwe ndi kuthandizidwa kupeza ugwiro m’thupi ndi maganizo ziyambukiro zoononga za uchimo zizidzakhala zitafafanizidwa kotheratu.

Malemba Oyera amatitsimikizira kuti akufa onse adzakhala’nso ndi moyo. Iwo adzapatsidwa mwai wa kukhala ndi moyo woposa utali wa moyo waufupi umene unathera pa imfa yao. Yehova Mulungu wapatsa Mwana wake Yesu Kristu mphamvu ya kuwaukitsa. (Yohane 5:26-28) Kupatsidwa mphamvu ya kuukitsa akufa kwa Yesu kumagwirizana ndi cheni-cheni chakuti iye molosera akuchedwa m’Baibulo kukhala “Atate Wosatha.” (Yesaya 9:6) Mwa kuukitsa awo ogona mu imfa, Yesu akukhala Atate wao.—Yerekezerani ndi Salmo 45:16.

MAZIKO A CHIKHULUPIRIRO

Kwa munthu amene amabvomereza kukhalako kwa Mulungu, sipayenera kukhala bvuto m’kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu m’chiukiriro. Kodi si koyenera kwa Uyo amene poyambirira anayambitsa moyo waumunthu kuti ali’nso wanzeru mokwanira kubwezeretsa moyo kwa akufa, kulenge’nso anthu akufa? Yehova Mulungu iye mwini walonjeza kuti akufa adzakhala’nso ndi moyo. Iye wachita’nso ntchito zamphamvu zimene zimalimbikitsa chikhulupiriro cha munthu mu lonjezo limene’li.

Yehova Mulungu anapatsa mphamvu ena a atumiki ake okhulupirika kudzutsa’di akufa. Pa Zerefati, osati kutali kwambiri ndi ku gombe lakum’mawa kwa Nyaja ya Mediterranean, Eliya mneneri’yo anaukitsa mwana mmodzi yekha wamwamuna wa mkazi wamasiye. (1 Mafumu 17:21-23) Wolowa m’malo wake Elisa anaukitsa mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mkazi wina wochuka ndi waufulu pa Sunemu, m’mbali ya kumpoto kwa Israyeli. (2 Mafumu 4:8, 32-37) Yesu Kristu anaukitsa mwana wamkazi wa Yairo, mkulu wa sunagoge pafupi ndi Nyanja ya Galileya; mwana wamwamuna mmodzi yekha wa mkazi wamasiye wa ku Nayini, kumwela chakumadzulo kwa Nyanja ya Galileya; ndi bwenzi lake lapamtima Lazaro, amene anali wakufa kwa masiku anai ndipo anaikidwa osati kutali kwambiri ndi Yerusalemu. (Marko 5:22, 35, 41-43; Luka 7:11-17; Yohane 11:38-45) Pa Yopa, pagombe la Mediterranean, mtumwi Petro anaukitsa Dorika (Tabita) kwa akufa. (Machitidwe 9:36-42) Ndipo mtumwi Paulo, pa kuima kwake m’chigawo cha Roma cha Asiya, anaukitsa Utiko atapunthwa ndi kugwa kuchokera pa zenera la chipinda chosanja chachitatu nafa.—Machitidwe 20:7-12.

Chiukiriro chapadera kopambana chinali chija cha Yesu Kristu iye mwini. Chochitika cha mu mbiri chotsimikiziridwa bwino lomwe chimene’chi chikupereka umboni wamphamvu kopambana wa kukhalako ka chiukiriro. Chimene’cho ndicho chimene mtumwi Paulo anachisonyeza kwa awo amene anasonkhana pa Areopagi mu Atene, Grisi, kuti: “[Mulungu] anapangiratu tsiku limene adzaweruza dziko lokhalamo anthu m’chilungamo, ndi munthu amene anamuikiratu; napatsa anthu onse chitsimikizo, pamene anamuukitsa Iye kwa akufa.”—Machitidwe 17:31.

Chiukiriro cha Yesu chinali cheni-cheni chotsimikiziridwa mosasiya mpata uli wonse wa chikaikiro. Panali mboni zoposa ziwiri kapena zitatu zimene zikanatha kuchichitira umboni. Eya, pa nthawi ina Yesu Kristu woukitsidwa’yo anaonekera kwa ophunzira okwanira zikwi zisanu. Chiukiriro chake chinali chotsimikiziridwa bwino kwambiri kwakuti mtumwi Paulo anatha kunena kuti kukana chiukiriro kunatanthauza kukana chikhulupiriro chonse Chachikristu. Iye analemba kuti: “Ngati kulibe kuuka kwa akufa, Kristu’nso sanaukitsidwa; ndipo ngati Kristu sanaukitsidwa kulalikira kwathu kuli chabe, chikhulupiriro chanu’nso chiri chabe. Ndipo’nso, ife tipezedwa mboni zonama za Mulungu kuti anaukitsa Kristu; amene sanamuukitsa, ngati kuli tero kuti akufa saukitsidwa.”—1 Akorinto 15:13-15.

Akristu oyambirira, mofanana ndi mtumwi Paulo, anadziwa motsimikizirika kuti Yesu anaukitsidwa kwa akufa. Chikhulupiriro chao cha kupfupidwa ndi chiukiriro chinali champhamvu kwambiri kwakuti iwo anali ofunitsitsa kukumana ndi chizunzo, ngakhale imfa yeni-yeni’yo.

KUUKITSIDWIRA KU MOYO WAUZIMU

Chiukiriro cha Yesu Kristu chimasonyeza kuti kuukitsa akufa sikumatanthauza kudzutsa’nso thupi leni-leni’lo. Yesu anaukitsidwira, osati ku moyo waunthu, koma ku moyo wauzimu. Ponena za zimene’zi, mtumwi Petro analemba kuti: “Eya, ngakhale Kristu adafa kamodzi kwatha ponena za machimo, munthu wolungama kaamba ka osalungama, kuti akakutsogolereni kwa Mulungu, iye akumaphedwa m’thupi lanyama, koma akumakhalitsidwa ndi moyo mu mzimu.” (1 Petro 3:18, NW) Pa chiukiriro chake Yesu analandira thupi, osati la nyama ndi mwazi, koma loyenerera moyo wakumwamba. —1 Akorinto 15:40, 50.

Ndithudi, thupi lauzimu limene’lo, linali losaoneka ku maso aumunthu. Chifukwa cha chimene’cho, kuti ophunzira ake amuone pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu anayenera kubvala thupi lanyama. Kuyenera kudziwidwa kuti Yesu sanaikidwe m’manda ali ndi zobvala koma anakulungidwa mu nsalu zabafuta wabwino kwambiri. Pambuyo pa chiukiriro chake nsalu’zo zinatsala m’manda. Chotero, monga momwe’di Yesu anafunikirira kubvala zobvala, iye anabvala’nso thupi lanyama kuti adzipangitse kuoneka kwa ophunzira ake. (Luka 23:53; Yohane 19:40; 20:6, 7) Zodabwitsa? Ai, zimene’zi ndizo zimene’di angelo anachita nthawi imene’yi isanafike pamene anaonekera kwa anthu. Cheni-cheni chakuti Yesu anabvala thupi lanyama chimasonyeza chifukwa chake ophunzira ake nthawi zonse sanam’zindikire poyamba ndi chifukwa chake iye anatha kuonekera ndi kuzimiririka mwadzidzidzi.—Luka 24:15-31; Yohane 20:13-16, 20.

Olowa naye nyumba 144,000 okha amene akugwirizana ndi Yesu Kristu mu ulamuliro adzakhala ndi chiukiriro chonga chimene’chi. Polongosola kuukitsidwira ku moyo wauzimu kumene’ko, Baibulo limatiuza kuti:

“Chimene uchifesa wekha sichikhalitsidwa’nso chamoyo, ngati sichifa; ndipo chimene ufesa, sufesa thupi limene lidzakhala, koma mbeu yokha kapena ya tirigu kapena ya mtundu wina; koma Mulungu aipatsa thupi monga afuna; ndi kwa mbeu yonse thupi lake-lake. . . .

“Chomwecho’nso kudzakhala kuuka kwa akufa. Lifesedwa m’chibvundi, liukitsidwa m’chisabvundi; lifesedwa m’nyozo, liukitsidwa m’ulemerero; lifesedwa lachibadwidwe, liukitsidwa thupi lauzimu. Ngati pali thupi lachibadwidwe, pali’nso lauzimu. Kotero’nso kwalembedwa, Munthu woyamba, Adamu, anakhala mzimu wamoyo. Adamu wotsiriza’yo anakhala mzimu wakulenga moyo. Koma chauzimu sichiri choyamba, koma chachibadwidwe; pamenepo chauzimu. Munthu woyamba’yo ali wapansi, wanthaka. Munthu wachiwiri ali wakumwamba. Monga wanthaka’yo, atero’nso anthaka; ndi monga wakumwamba, atero’nso akumwamba. Ndipo monga tabvala fanizo la wanthaka’yo, tidzabvala’nso fanizo la wakumwamba’yo.”—1 Akorinto 15:36-49.

KUUKITSIDWIRA KU MOYO PA DZIKO LAPANSI

Koma bwanji ponena za awo amene, mosafanana ndi Yesu Kristu ndi olamulira anzake 144,000, adzaukitsidwira ku moyo wa pa dziko lapansi? Popeza kuti iwo ‘abwerera ku pfumbi,’ kodi Mulungu adzafunikira kusonkhanitsa’nso tizinthu tonse timene pa nthawi tinapanga matupi ao kotero kuti matupi ao ali ofanana m’mbali iri yonse ndi m’mene iwo analiri pa nthawi ya imfa?

AI, sizingakhale choncho konse. Kulekeranji kutero? Choyambirira, chifukwa chakuti chimene’chi chikatanthauza kuti iwo akaukitsidwa ali mu mkhalidwe wapafupi ndi imfa. Anthu oukitsidwa m’nthawi zakale sanaukitsidwe ali mu mkhalidwe wodwala wofanana’wo umene anali nao imfa yao isanachitike. Ngakhale kuli kwakuti anali opanda ungwiro pa nthawi ya kuukitsidwa kwao, iwo anali ndi thupi lokwanira ndi labwino-bwino kwambiri.

Ndipo’nso, sikukakhala kwanzeru kuumirira kuti tizinthu timodzi-modzito tisonkhanitsidwe kuti tipange thupi lao lobwezeretsedwa’lo. Pambuyo pa imfa, ndi kupyolera mwa njira ya kubvunda, thupi la munthu limasandutsidwa kukhala zakudya zina. Zimene’zi zingatsopedwe ndi zomera, ndipo anthu angadye zomera zimene’zi kapena zipatso zao. Motero tizinthu Topanga munthu wakufa’yo potsirizira pake tingafikire kukhala mwa anthu ena. Mwachionekere, pa nthawi ya chiukiriro tizinthu timodzi-modzito sitingathe kutoleredwa mwa munthu ali yense woukitsidwa kwa akufa.

Pamenepa, kodi chiukiriro, chimatanthauzanji kwa munthu? Chimatanthauza kuukitsidwa kwake monga munthu yemweyo. Ndipo kodi n’chiani chimene chimapangitsa munthu kukhala mu mkhalidwe umene iye ali? Kodi ndizo zinthu zosanganizidwa zopanga thupi lake? Ai, popeza kuti zidutswa zazing’ono-zing’ono zokhala m’thupi zimalowedwa m’malo nthawi ndi nthawi. Pamenepa, chimene kweni-kweni chimam’siyanitsa ndi anthu ena, ndicho kaonekedwe kake konse kakuthupi, mau ake, umunthu wake, zokumana nazo zake, kukula kwamaganizo ndi chikumbu mtima. Chotero pamene Yehova Mulungu, mwa njira ya Mwana wake Yesu Kristu, aukitsa munthu kwa akufa, iye mwachionekere adzapatsa munthu amene’yo thupi lokhala ndi mikhalidwe yofanana ndi yakale. Munthu woukitsidwa’yo adzakhala ndi chikumbu mtima chimodzi-modzi chimene iye amachipeza m’kati mwa nthawi ya moyo wake ndipo iye adzakhala ndi kuzindikira kokwanira kwa chikumbu mtima chimene’cho. Munthu’yo adzakhala wokhoza kudzidziwa, ndipo awo amene anam’dziwa adzakhala’nso okhoza kutero.

‘Koma ngati munthu alengedwa’nso motero,’ wina angatero, ‘kodi iye ali’di kweni-kweni munthu m’modzi-modzi’yo? Kodi sali chitsanzo chabe?’ Ai, cheni chochulidwa poyamba’cho chakuti ngakhale m’moyo matupi anthu akusintha nthawi zonse. Pafupi-fupi zaka zisanu ndi ziwiri zapita’zo zinthu zopanga matupi athu zinali zosiyana ndi zinthu zowapanga lero lino. Timasiyana’nso m’kaonekedwe m’kupita kwa zaka. Komabe, kodi sitimakhala ndi kulembeka kwa zala kofanana? Kodi sitiri anthu amodzi-modzi’wo? Ndithudi tiri anthu amodzi-modzi’wo.

Kwa awo amene chiukiriro chimaonekera pafupi-fupi kukhala chosakhulupirika ayenera kulingalira njira yodabwitsa yofanana’yo imene imachitika pa nthawi ya kukhaliridwa pakati kwa munthu. Kaselo kamene kamapangidwa mwa kugwirizana kwa ubwamuna ndi dzira m’kati mwake kamakhala ndi kuthekera kwa kukhala munthu wosiyana ndi munthu wina ali yense amene wakhala ndi moyo. M’kati mwa selo limene’li mumakhala zinthu zimene zimatsogoza kupangika kwa munthu’yo ndi kupangika kwa umunthu weni-weni umene iye akuulandira kuchokera kwa makolo ake. Ndiyeno, ndithudi, zokumana nazo za moyo wake pambuyo pake zimaonjezera umunthu umene’wo. Mofanana ndi chimene chimachitika pa nthawi ya kukhaliridwa pakati, pa nthawi ya chiukiriro kapena kulengedwa’nso munthu wakufa’yo adzabwezeredwa umunthu ndi mbiri ya moyo wake, selo liri lonse la thupi lake likumakhomerezedwa ndi mikhalidwe imene imam’panga kukhala wosiyana ndi anthu ena onse. Ndipo mtima wake, maganizo ndi thupi zidzakhala zitakhomerezedwa mikhalidwe yoonjezeredwa’yo, makhalidwe ndi maluso zimene iye anazikulitsa m’kati mwa nthawi ya moyo wake yapapitapo.

Ponena za Mlengi, wamasalmo wouziridwa anasonyeza kuti: “Ndisanabadwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’bukhu mwanu, masiku akuti ziumbidwe, pakalibe chimodzi cha izo.” (Salmo 139:16) Chifukwa cha chimene’cho, pamene miphatikizo ya zinthu zopereka khalidwe yapangika pa nthawi ya kukhaliridwa pakati, Yehova Mulungu amakhala wokhoza kuzindikira ndi kukhala ndi cholembedwa cha mikhalidwe yaikulu ya mwana’yo. Chotero kuli koyenera kotheratu kuti iye ali wokhoza kukhala ndi cholembedwa cholongosoka mwa chimene angalenge’nso nacho munthu amene wafa.

Tingathe kukhala ndi chidaliro m’chikumbu mtima changwiro cha Yehova. Eya, ngakhale anthu opanda ungwiro, mwa njira ya tepu yogwirira mau ndi zithunzi-thunzi, angathe kusunga ndi kupanga zinthuzi-thuzi za anthu zooneka ndi zolankhula. Lalikulu kopambana ndiro luso la Mulungu la kusunga zolembedwa zotero’zo, pakuti iye amaitana nyenyezi zonse zosawerengeka’zo ndi dzina!—Salmo 147:4.

Chifukwa cha chimene’cho, kungaonedwe kuti, chiukiriro kapena kulengedwa’nso n’kothekera chifukwa chakuti munthu wakufa’yo ali wamoyo m’chikumbu mtima cha Mulungu. Chifukwa cha chikumbu mtima chake changwiro cha mikhalidwe ya moyo ndi chifuno chake cha kuukitsa akufa, Yehova Mulungu anatha kuona anthu akufa okhulupirika onga ngati Abrahamu, Isake ndi Yakobo kukhala amoyo. Chimene’cho ndicho chimene Yesu Kristu anauza Asaduki osakhulupirira’wo, kuti: “Za kuti anthu akufa auka, anasonyeza ngakhale Mose, pa Chitsamba chija, pamene iye am’chulira Ambuye, Mulungu wa Abrahamu, ndi Mulungu wa Isake, ndi Mulungu wa Yakobo. Ndipo Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa Iye.”—Luka 20:37, 38.

Ndithudi pali maziko okwanira okhulupirira chiukiriro kapena kulengedwa’nso. Zoona, ena angakane lingaliro’lo. Koma kodi mukakhala bwino kwambiri kutseka maso ndi maganizo anu ku umboni ndi kukana kukhulupirira chiukiriro? Kodi kukapangitsa kukhala kosabvuta kwambiri kwa inu kutaya wachibale wokondedwa kapena bwenzi mu imfa? Kodi mukakhala wokonzekera bwino kwambiri kukumana ndi chiyembekezo chosakondweretsa cha imfa ya inu mwini?

Kudziwa kuti moyo uno sindiwo wokha umene ulipo kumachititsa munthu kukhala womasuka ku kuopa kuuchititsa kudulidwa mwamsanga mwa njira yachiwawa. Mantha amene’wa agwiritsiridwa ntchito ndi Satana Mdierekezi m’kusunga anthu mu ukapolo, akumawachititsa kupyolera mwa oimira ake a pa dziko lapansi kuchita zofuna zake. (Mateyu 10:28; Ahebri 2:14, 15) Moopa kuthekera kwa kuphedwa, ambiri alephera kutsatira chitsogozo cha chikumbu mtima chao ndipo achita mwamantha maupandu ochitira anthu, monga momwe kunachitidwira m’ndende zachibalo za Nazi Jeremani.

Komabe, munthu wokhala ndi chikhulupiriro champhamvu m’chiukiriro, amalimbikitsidwa m’chitsimikiziro chake cha kuchita chimene chiri choyenera ngakhale ngati kumene’ko kungatanthauze imfa kwa iye. Kwa iye moyo umene adzasangalala nawo pa kuukitsidwa kwa akufa uli wamtengo wapatali kwambiri koposa zaka zowerengeka za moyo tsopano. Iye samafuna kuika pa ngozi mwai wake wa kupeza moyo wosatha kaamba ka chimene, moyerekezera, sichingachedwe kutalikitsidwa kwa moyo wake. Iye ali ngati amuna a m’nthawi zakale amene bukhu la Baibulo la Ahebri limawasimba kuti: “[Iwo] anazunzidwa chifukwa chakuti sakanalola kumasulidwa mwa dipo lina [kukanidwa kwina kwa chimene chiri choyenera], m’malo mwakuti akapeze chiukiriro chabwino kwambiri.”—Ahebri 11:35, NW.

Ndithudi awo amene ali ndi chidaliro mu lonjezo a Mulungu la kuukitsa akufa ali bwino kwambiri koposa awo amene alibe chiyembekezo cha chiukiriro. Iwo angayembekezere m’tsogolo popanda mantha.

Umboni wa Baibulo umasonyeza kuti dongosolo iri lidzatha posachedwapa, m’kati mwa mbadwo uno, ndi kulowedwa m’malo ndi boma lolungama lokhala m’manja mwa Yesu Kristu ndi olamulira anzake. Ndicho chifukwa chake mabiliyoni amene ali akufa tsopano adzakhala’nso ndi moyo posachedwa ndi kuyamba kupindula ndi ulamuliro Waufumu. Ha, kudzakhala kosangalatsa kwambiri chotani nanga kwa opulumuka “chisautso” kulandira’nso akufa! Taganizirani chisangalalo cha kukhala okhoza kachiwiri’nso kukhala ndi utsamwali wolimbikitsa wa mabwenzi okondedwa ndi achibale apamtima, kumva mau ao ozolowereka ndi kuwaona ali ndi thanzi labwino.

Kodi chimene’chi chiyenera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa inu? Kodi sichiyenera kukusonkhezerani kuthokoza Mulungu kaamba ka chiyembekezo chabwino kwambiri cha chiukiriro? Kodi chiyamikiro chanu sichiyenera kukusonkhezerani kuchita zonse zimene mungathe kuphunzira za iye ndi kenako kum’tumikira mokhulupirika?

[Chithunzi patsamba 172]

Kodi si kothekera kwa uyo amene amapangitsa khanda kukula m’mimba mwa mai wake kuukitsa’nso akufa?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena