Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gh mutu 4 tsamba 29-38
  • Chitsogozo Chopindulitsa ku Chimwemwe Cheni-cheni

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chitsogozo Chopindulitsa ku Chimwemwe Cheni-cheni
  • Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • BUKHU LIMENE LIMATHETSA ZOBVUTA
  • ACHIMWEMWE M’NTHAWI ZA CHIYESO
  • CHIKONDI CHENI-CHENI CHA PA MNASI
  • CHITSOGOZO CHENI-CHENI M’NTHAWI ZOBVUTA
  • Zimene Yesu Anaphunzitsa Zimatithandiza Kukhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Atumiki Achimwemwe a Yehova
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Anthu Amene Amatumikira “Mulungu Wachimwemwe” Amakhala Osangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2018
  • Zimene Zimafunika Kuti Munthu Akhaledi Wachimwemwe
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
gh mutu 4 tsamba 29-38

Mutu 4

Chitsogozo Chopindulitsa ku Chimwemwe Cheni-cheni

1. (a) Kodi ndi mtundu wotani wa chitsogozo umene tiyenera kuyamikira lero lino? (b) Kodi n’chifukwa ninji Baibulo likuyamikiridwa monga chitsogozo?

PA USIKU wa mdima, timakhala okondwa kukhala ndi magetsi a mu mseu owala kwambiri kuunikira njira yathu. Amene’wa angatithandize’nso kuona kukhala osungika. Tsopano, m’nthawi ya mdima kopambana ya mbiri ya dziko, ndithudi timayamikira chitsogozo chothandiza kuunikira njira kaamba ka ife eni ndi mabanja athu. Ndipo ngati tingathe kukhala ndi chitsogozo chimene chimatitsogolera ku chimwemwe chabwino kwambiri cha m’tsogolo, ndithudi tikafuna kudziwa za chitsogozo chimene’cho! Munthu wina wanzeru analankhula kwa Yehova pa nthawi ina, kuti:

“Mau anu ndiwo nyali ya ku mapazi anga, ndi kuunika kwa panjira panga.” (Salmo 119:105)

“Mau” a Mulungu ali m’Baibulo. Kukukhulupiriridwa kuti mudzapeza Baibulo kukhala chitsogozo ndi chithandizo chabwino kwambiri ndi chopindulitsa kulinga ku kukhala ndi moyo wachimwemwe ndi watanthauzo.

BUKHU LIMENE LIMATHETSA ZOBVUTA

2. Kodi m’stogoleri Wachihindu ananenanji ponena za phindu lothandiza la Ulaliki wa pa Phiri?

2 Baibulo lingathe kukhala lopindulitsa kopambana ndi lothandiza kwa ife. Anthu ambiri olingalira abvomereza cheni-cheni chimene’chi. Monga chitsanzo, pali mau otsatirapo’wa mu Treasure of the Christian Faith yolembedwa ndi S.J. Corey ponena za kukambitsirana pakati pa m’tsogoleri Wachihindu Mahatma Gandhi ndi Bwanamkubwa wapapitapo wa Britain ku India, Lord Irwin:

“Lord Irwin anakacheza kwa Mahatma ku mphala yake yochedwa ashram. M’kati mwa kukambitsirana Lord Irwin anafunsa funso iri kwa wom’chereza’yo: ‘Mahatma, monga munthu kwa munthu mnzake, ndiuzeni chimene mukulingalira kukhala chothetsera zobvuta za dziko lanu ndi langa.’ Atatenga kabukhu pa choikapo nyali chokhala pafupi, Gandhi anakatsegula pa chaputala chachisanu cha Mateyu nayankha kuti, ‘Pamene dziko lanu ndi langa lidzagwirizana pamodzi pa ziphunzitso zoperekedwa ndi Kristu mu Ulaliki wake wa pa Phiri, tidzakhala titathetsa zobvuta osati kokha za maiko athu koma zija za dziko lonse.’ Amene’wo ochokera kwa Mhindu!”

3. Kodi ndi motani m’mene awo amene akulira maliro angakhalire achimwemwe? (Yesaya 61:1, 2)

3 Monga chitsanzo cha chiphunzitso chopindulitsa cha Baibulo, tiyeni tilingalire mbali ya Ulaliki wochuka umene’wo. Umayamba ndi kusonyeza magwero a chimwemwe cheni-cheni:

“Achimwemwe ali awo ozindikira zosowa zao zauzimu, popeza kuti ufumu wa kumwamba uli wao.

“Achimwemwe ali awo amene amalira maliro, popeza kuti adzatonthozedwa.” (Mateyu 5:3, 4, NW)

M’nthawi zobvuta zino, anthu ambiri amaona kufunika kwa chakudya cha maganizo, kuti chiwakhutiritse mwauzimu. Anthu ambiri akulira maliro, akumabvutika mtima ndi mikhalidwe yoipa m’dziko. Kodi inu muli mmodzi wa amene’wa? Ngati kuli choncho, mudzakhala achimwemwe ngati muyesa-yesa zolimba kupeza chifukwa cha nthawi zobvuta zimene’zi ndi chimene chiri chiyembekezo chimene’cho, kulira kwanu maliro kudzasanduka’di chitonthozo.

4. Kodi ndi mtundu wotani wa anthu umene ungasangalale ndi dalitso la Mulungu tsopano, ndi m’tsogolo? (Salmo 24:4, 5)

4 Ulaliki wa Yesu ukupitirizabe ndi mau awa:

“Achimwemwe ali odekha mtima, popeza kuti adzalandira dziko lapansi.”

“Achimwemwe ali awo akumva njala ndi kumva ludzu la chilungamo, popeza kuti adzakhutitsidwa.”

“Achimwemwe ali achifundo, popeza kuti adzasonyezedwa chifundo.

“Achimwemwe ali oyera mu mtima, popeza kuti adzaona Mulungu.

“Achimwemwe ali ochita mtendere, popeza kuti adzachedwa ‘ana a Mulungu.’” (Mateyu 5:5-9, NW)

M’dziko m’mene muli chiwawa chochuluka kwambiri, ha, ndi dalitso lotani nanga m’mene kuliri kuzingidwa ndi anthu odekha mtima! Ndipo pamene dziko lonse lapansi lidzazidwa ndi anthu otero’wo, monga momwe Baibulo limatitsimikizirira kuti lidzatero, anthu adzakhala’di achimwemwe. Kodi simukufuna kuona kusaona mtima, chisalungamo ndi kuipa konse lero lino zikuchotsedwa pa dziko lapansi? Ndithudi mukufuna! Mungakhale achimwemwe tsopano, m’kulondola chilungamo monga njira yanu ya moyo, ndipo chimwemwe chimene’cho chidzasefukira pamene mukupitirizabe kukhala ndi moyo kuona Mulungu akubwezeretsa chilungamo m’chilengedwe chonse. Ngakhale m’nyengo yobvuta ino, achifundo, oyera mu mtima ndi amtendere angakhale ndi moyo wokhutiritsa, limodzi ndi dalitso la Mulungu. Koma kumeneku ndi kulawiratu chabe chimwemwe chimene chidzakhala chochuluka pa dziko lonse lapansi.

ACHIMWEMWE M’NTHAWI ZA CHIYESO

5. Ngati munthu wina anatsutsa kuphunzira kwanu Baibulo, kodi mukachita nakonji? (2 Petro 3:3, 13)

5 Mwa kupenda “mbiri yabwino” mungathandizidwe kukhala ndi lingaliro losangalatsa, lotsimikizirika, limodzi ndi chiyembekezo cheni-cheni cha m’tsogolo. Koma anthu ena angatsutse kapena kukusekani chifukwa cha kuphunzira kwanu Baibulo. Kodi chimene’chi ndi chifukwa cholekera kuphunzira kwanu Baibulo? Ai, pakuti kumene’ku kukatanthauza kusiya chitsogozo chokha chomkera ku chimwemwe m’nthawi zobvuta zino. Yesu akupitirizabe kunena mu Ulaliki wake, kuti:

“Achimwemwe ali awo amene azunzidwa kaamba ka chifukwa cha chilungamo, popeza kuti ufumu wa kumwamba uli wao.

“Achimwemwe muli inu pamene anthu akutonzani ndi kukuzunzani ndi kukunenerani chinthu choipa cha mtundu uli wonse monama chifukwa cha ine. Kondwerani ndi kulumpha chifukwa cha chisangalalo, popeza kuti mphotho yanu iri yaikulu kumwamba; pakuti m’njira imene’yo iwo anazunza aneneri’wo musanakhale inu.” (Mateyu 5:10-12, NW)

Mudzakhala achimwemwe chifukwa cha kukhala mutakaniza otsutsa otero’wo, pakuti mudzapita patsogolo kulinga ku kukhala ndi moyo wachifuno, wopindulitsa, ndi kulinga ku mphotho yosatha yochokera kwa Mulungu.

6. Kodi ndi mtundu wotani wa phunziro la Baibulo umene ukuyamikiridwa? (Deuteronomo 11:18, 19)

6 Ndipo’nso, ambiri amene amayamba kuphunzira Baibulo amaona kuti ena a m’banja lao, kapena pakati pa mabwenzi ao, amakondwera kugwirizana nawo. Bwanji osapreeka lingaliro limene’lo kwa iwo inu mwininu? N’chinthu chabwino kwambiri pamene banja likhala ndi phande m’kukambitsirana Baibulo. Kumene’ku kungathandizire kwambiri kupanga banja lachimwemwe.

7. Fotokozani mwa fanizo m’mene phunziro la Baibulo lingathetsere ngakhale zobvuta zazikulu kwambiri za banja.

7 Nthawi zina, Baibulo lathandiza mabanja m’kuthetsa zobvuta zazikulu kwambiri, monga momwe lipoti lotsatirapo’li likusonyezera:

Mwamuna wina m’Philippines anali chidakwa ndi wochova juga, anasuta ndudu makumi anai pa tsiku ndipo pamero pake panyamba nthenda ya kansala. Ngakhale kuli kwakuti anali ndi ana asanu ndi anai, banja lake linali kumuona mwa kamodzi-kamodzi. Iye anaononga yochuluka ya nthawi yake ndi ndalama m’malo okhala ndi mbiri yoipa, ngakhale kuli kwakuti anali wochedwa Mkristu. Banja’lo linayamba kugawanika. Koma iye anagwidwa mtima ndi kudzichepetsa ndi ubwenzi wa Mboni za Yehova pamene izo zinafika. Choyamba ena a ana ake, ndipo kenako banja lonse, anayamba kuphunzira Baibulo. Mwamuna amene’yu. anayenera kupanga kuyesa-yesa kwamphamvu kuthetsa zizolowezi zake zoipa, koma tsopano iye ndi ziwalo zina zisanu ndi ziwiri za banja lake’lo zapereka miyoyo yao kwa Mulungu, pamene banja lonse’lo likupitirizabe maphunziro ake a Baibulo. Chifukwa cha kusiya kwake fodya, nthenda yake ya pamero yatha. Tsopano iye ndi mwamuna wa banja wodzipereka. Achibale ake anadabwa ndi kusinthika kwake, ndipo’nso ambiri a iwo anakhala okondweretsedwa ndi phunziro la Baibulo.

Ngati banja lanu liri ndi bvuto, silingakhale lalikulu kwambiri mofanana ndi la mwamuna amene’yu. Komabe, Baibulo lingathe’nso kukhala chisonkhezero chodabwitsa cha chigwirizano m’banja lanu.

CHIKONDI CHENI-CHENI CHA PA MNASI

8. Kodi ndi motani m’mene Baibulo limachenjezera za chikhumbo cholakwa? (1 Yohane 2:15-17)

8 Tiyeni tipende ziphunzitso zina za Ulaliki wa pa Phiri’wo, mu umene Yesu akufika pa zochititsa zeni-zeni za zobvuta zimene zikukantha anthu. Mwa chitsanzo, posonyeza m’mbuyo ku Malamulo Khumi, iye akutiuza kuti:

“Munamva kuti kunanenedwa, Usachite chigololo; koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wakuyang’ana mkazi kum’khumba, pamenepo watha kuchita naye chigololo mumtima mwake.” (Mateyu 5:27, 28)

Chotero ndicho chikhumbo choipa chimene tiyenera kuchichenjerera. Ngati tikulitsa chikhumbo chotero’cho m’mitima mwathu, chidzatitsogolera ku njira yolakwa. Pamenepa, n’kofunika kwambiri chotani nanga, kuti tikulitse zikhumbo zoyenera, tikumalola maganizo athu ndi mitima kukhala pa nkhani zabwino, ndi zolimbikitsa!

9. Kodi zobvuta za anthu zikathetsedwa mwa kutsatira chitsanzo chotani? (Luka 6:35)

9 M’nthawi ya Yesu, panali awo amene anaphunzitsa kuti “Uzikondana ndi mnansi wako, ndi kumuda mdani wako.” Koma Yesu akukulongosola mosiyana, kuti:

“Koma ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu; kotero kuti mukakhale ana a Atate wanu wa Kumwamba; chifukwa Iye amakwezera dzuwa lake pa oipa ndi pa abwino, namabvumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.” (Mateyu 5:43-45)

Ha, ndi kopanda dyera chotani nanga​—kufunira zabwino adani athu! Koma onani kuti kumene’ku kuli motsanzira Atate ndi Mlengi wathu wakumwamba, amene amagawira modzala manja onse amene akukhala pa dziko lapansi-ngakhale anthu oipa. Ngati anthu onse akanasonyeza kulingalira kwachikondi kotero’ko kwa ena, zobvuta za dziko lonse zikanathetsedwa’di!

10. Kodi n’chifukwa ninji sitiyenera kudera nkhawa ndi zosowa za tsiku ndi tsiku? (Luka 12:15)

10 Moonjezerapo, Ulaliki’wo ukuti:

“Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzabvala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chobvala? Yang’anirani mbalame za kumwamba, kuti sizimafesa ai, kapena sizimatema ai, kapena sizimatutira m’nkhokwe; ndipo Atate wanu wa Kumwamba azidyetsa . . . Tapenyetsani maluwa a kuthengo, makulidwe ao; sagwiritsa ntchito, kapena sapota: koma ndinena kwa inu, kuti angakhale [Mfumu] Solomo mu ulemerero wake wonse sanabvala monga limodzi la amene’wa. Koma ngati Mulungu abveka chotero maudzu a kuthengo, . . . nanga si inu kopambana ndithu . . .? Chifukwa chake musadere nkhawa, ndi kuti, Tidzadya chiani? kapena Tidzamwa chiani? kapena Tidzabvala chiani? Pakuti anthu akunja azifunitsa zonse zimene’zo; pakuti Atate wanu wa Kumwamba adziwa kuti musowa zonse zimene’zo.”

11. (a) Kodi “akunja” amalondola chiani, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani? (Mateyu 6:19-21) (b) Kodi n’chiani chimene chiri njira yomkera ku chimwemwe cheni-cheni? (Luka 11:28)

11 Panopo Yesu akunena za nkhawa yachibadwa imene tonsefe tiri nayo kaamba ka chakudya, zobvala ndi nyumba. Timafunikira zinthu zimene’zi kuti zitipangitse kukhala achimwemwe. Komabe, “akunja” a mtundu wa anthu wotizinga nthawi zonse akulondola, osati zosowa, koma zikhumbo za munthu. M’kugogomezera chikhumbo chadyera ndi kunyada m’zimene anthu ali nazo, dziko ladyera’li limathandizira kupanda chimwemwe kwa anthu. Chuma chakuthupi chingadzetse chisangalalo chakanthawi, koma njira yomkera ku chimwemwe cheni-cheni ndi chosatha ndiyo “kupitirizabe. . . kufuna-funa choyamba ufumu [wa Mulungu] ndi chilungamo chake.” (Mateyu 6:33, NW) Kodi chikondi chanu cha chilungamo chimakusonkhezerani kuchita zimene’zi? Chiyenera. Ulaliki wa pa Phiri umapereka chilimbikitso chabwino kwambiri ku cholinga chimene’chi.

CHITSOGOZO CHENI-CHENI M’NTHAWI ZOBVUTA

12. (a) Kodi ndi mikhalidwe yonenedweratu yotani imene tikuiona motizinga lero lino? (b) Koma kodi tingapeze kuti chitsogozo chabwino? (2 Petro 1:19)

12 N’kofunika kweni-kweni kufuna-funa chilungamo m’nthawi zino m’zimene tikukhalamo ndi moyo tsopano. Pamene tiunguza-unguza m’dziko motizungulira, timaona m’mene kulongosola kwa mtumwi Paulo kotsatirapo’ku kukugwirizanira bwino lomwe:

“Masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwo’nso udzipatule.” (2 Timoteo 3:1-5)

Paulo akunena kuti mikhalidwe imene’yi idzakhalapo mu “masiku otsiriza.” Ndipo lero lino, ndi koonekera bwino chotani nanga m’mene kuliri kuti chitaganya cha anthu cikuyang’anizana ndi tsiku la mlandu! Likuipira-ipirabe mofulumira kwambiri. Chotero kodi tingayang’ane kuti kweni-kweni kaamba ka chitsogozo? Paulo akuyankha mwa kusonyeza ku “malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso,” ndipo akuti’nso: “Lemba liri lonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa.” (2 Timoteo 3:15, 16) Mlengi wathu, Mulungu, analinganiza “Lemba liri lonse” nalisunga kaamba ka phindu ndi chilimbikitso chathu ‘m’masiku otsiriza’ ano.”

[Chithunzi patsamba 31]

Ulaliki wa pa Phiri wa Yesu ukkupereka ziphunzitso zokhoza ‘kuthetsa zobvuta za dziko lonse lapansi’

[Chithunzi patsamba 34]

Phunziro la Baibulo linathandiza kuthetsa zobvuta za banja la Afilipino iri; lingakuthandizeni’nso

[Chithunzi patsamba 36]

Chimwemwe chimadza pamene titsanzira Mulungu wachikondi, amene amachititsa dzuwa lake kuwalira pa anthu a mitundu yonse

[Chithunzi patsamba 38]

‘M’masiku otsiriza’ obvuta ano, timafunikira chitsogozo cha Baibulo kuti tipulumuke

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena