Mutu 6
Magwero a Mbiri Yabwino—“Mulungu”
1. Kodi ndi mitundu yosiyana-siyana yotani ya milungu imene anthu akulambira lero lino?
KODI n’chiani chimene chikutanthauzidwa mwakuti “Mulungu”? Anthu mamiliyoni mazana ochuluka amanena kukhala akukhulupirira Mulungu wa Baibulo, koma m’malo mwa kum’lambira iwo amalambira Utatu wachinsinsi. Mamiliyoni mazana ochuluka a Ahindu nawo’nso amalambira Utatu, Trimurti wa mitu itatu wa Brahma, Vishnu ndi Siva, pakati pa milungu yao yachimuna ndi yachikazi mamiliyoni 330. Anthu mamiliyoni mazana ochuluka amalambira mafano osiyana-siyana a Buddha, ndipo Shinto ali ndi kachisi wake wa milungu miyanda 800, kuphatikizapo mlungu wachikazi dzuwa Amaterasu Omikami. Ndiyeno pali anthu mamiliyoni mazana ochuluka amene amanena kuti ali osakhulupirira mulungu. Ena a amene’wa amanena kuti chipembedzo chiri “choputsitsa anthu,” komabe iwo eniwo amamangira tiakachisi ndi kulambira monga mafano atsogoleri ao akufa.
2. Kodi n’chiani chimene ali yense wa ife ayenera kufuna kudziwa ponena za Mulungu? (1 Akorinto 8:5, 6)
2 Zoonadi, pali milungu yambiri-mbiri yosokoneza m’zipembedzo, zimene ziri ngati ufumu waukulu kwambiri wokuta dziko lonse lapansi. Kukakhala kotipindulitsa kupenda mkhalidwe umene’wu ndi maganizo omasuka, ndi kuona ngati tingathe kutsimikizira chimene chiri choonadi ponena za Mulungu.
MILUNGU YA BANJA
3. (a) Kodi tiyenera kulemekeza makolo athu? Deuteronomo 5:16 (b) Kodi kulambira makolo moyenerera kukatitsogolera ku chiani? (Genesis 3:1-6)
3 Pali anthu ambiri amene amalambira makolo ao akufa, ndipo ena ali oona mtima kwambiri m’zimene’zi. Ndithudi, ali yense ayenera kulemekeza makolo ndi agogo amene ali oyenerera ulemu wotero’wo. Mtumwi Paulo anagwira mau lachisanu la Malamulo Khumi motere: “Lemekeza atate wako ndi amako . . . kuti kukhale bwino ndi iwe, ndi kuti ukhale wa nthawi yaikulu padziko.” (Aefeso 6:2, 3) Koma kodi zimene’zo zimatanthauza kuti tiyenera kuwalambira? Ngati tikanati tilambire makolo athu akufa, ndi kubwerera nako kulambira kumene’ku ku chiyambi cha mbiri, tikakhala tikulambira makolo oyambirira a anthu, Adamu ndi Hava, amene kusamvera kwao m’munda wa Edene kunachititsa mtundu wa anthu kuyamba mabvuto ao ndi kupanda chimwemwe! Ndithudi sitikafuna kulambira makolo amene’wo!
4. (a) Kodi malipoti ochokera Kum’mawa amasonyezanji ponena za kulemekeza ndi kulambira? (b) Kodi ndi motani m’mene Mulungu akulongosoledwera pa Mateyu 22:32, ndipo chifukwa ninji? (1 Atesalonika 4:13)
4 Phindu leni-leni la kupereka ulemu woyenera kwa anthu okalamba pamene ali moyo likulongosoledwa mwa fanizo ndi mau awa ochokera Kum’mawa:
M’banja Lachijapana mwana wamkazi, amene anamamatira kwambiri ku malamulo a Baibulo a khalidwe labwino, anasamalira mwachikondi makolo ake Achibuda mpaka imfa yao. Iye anawapatsa chitonthozo cheni-cheni. Ku mbali ina, mwana wamwamuna sanachite kanthu kali konse kuthandiza makolo ake pamene anali moyo, koma atafa anawagulira butsudan (guwa lansembe Lachibuda la banja) la $300 kotero kuti akathe kulambiridwa.
M’Korea, mnyamata wina analandira chiphunzitso cha Baibulo, koma pamene anabwerera ku mudzi kwao iye anatsutsidwa moipa kwambiri ndi makolo ake olambira makolo akufa ndi akulu. Komabe, pamene analongosola za kulemekeza makolo amoyo ndipo osati kulambira akufa, mkulu wina wa usinkhu wa zaka makumi asanu ndi atatu mphambu chimodzi wa m’mudzi’wo anabvomereza kuti: “Tiyenera kuyenda m’njira ya amoyo m’malo mwa njira ya akufa.”
N’zoona kuti m’Chikristu cha Dziko, kudza’nso m’maiko osakhala Achikristu, kulambira kochuluka kumazikidwa pa misa, kuyimba nyimbo ndi madzoma ena ochitira akufa. Komabe, Mulungu wa Baibulo akulongosoledwa kuti “sali Mulungu wa akufa koma wa amoyo.” (Mateyu 22:32) Ngakhale anthu akufa amakhala amoyo m’chikhumbukiro chake, ndipo m’nthawi yokwanira iye adzawabwezeretsa ku moyo pa dziko lapansi. Chotero iye samabvomereza madzoma amaliro oonongetsa ndalama zambiri ndi odzionetsera. Pamenepa, kodi ndani, amene, ali Mulungu wamoyo amene’yu?
“MULUNGU WACHIMWEMWE”
5. Kodi ndi iti imene iri ina ya mikhalidwe ya “Mulungu wachimwemwe”? (Salmo 146:5, 6)
5 Baibulo limam’longosola kukhala “Mulungu wachimwemwe,” amene ali Mwini “mbiri yabiwno yaulemerero” kwa anthu. (1 Timoteo 1:11, NW) Iye amakonda dziko la mtundu wa anthu, ndipo amatifuna kuti tikhale’nso achimwemwe. Monga Mlengi wa chilengedwe chonse, iye ali ndi mphamvu ya kutipangitsa kukhala achimwemwe, ndipo monga “Nkhalamba ya Kale Lomwe” amene akukhala ndi moyo kwaumuyaya wonse, iye ali ndi nzeru yopambana yofunika yodzetsera mikhalidwe yachimewmwe pa dziko lapansi lino. (Danieli 7:9) Monga ‘wokonda chiweruzo,’ iye adzaona kuti awo amene ali okhulupirika kwa iye ndi malamulo ake olungama a khalidwe labwino “adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:28, 29) Baibulo ponena za Mlengi ndi Mulungu amene’yu limati:
“Mapiri eni-eni’wo asanabadwe, kapena musanapitirize kulenga . . . dziko lapansi ndi mtunda wobala zipatso, ngakhale kuyambira ku nthawi yosayamba kufikira ku nthawi yosatha inu ndinu Mulungu.” “Tsopano kwa Mfumu yamuyaya, yosabvunda, yosaoneka, Mulungu yekha, kukhale ulemu ndi ulemerero ku nthawi za nthawi.”—Salmo 90:2; 1 Timoteo 1:17, NW.
6. Kodi n’chifukwa ninji kukhala kolakwa kuyerekezera Mulungu ndi mafano? (Yesaya 42:5, 8)
6 Mulungu wa Baibulo ndiye Mulungu wamoyo, Mulungu wokhala ndi malamulo a khalidwe labwino abwino kopambana, Mulungu amene adzakwaniritsa chifuno chake chachikulu cha kupangitsa anthu kukhala achimwemwe. Mmodzi wa olemba masalmo ponena za iye akuti:
“Mulungu wathu . . . ali m’mwamba; wachita chiri chonse chim’konda.’ (Salmo 115:3)
‘Chotero iye sangayerekezeredwe konse ndi mafano osakhoza kuchita kanthu opanda moyo! Ponena za awo amene amakhulupirira mafano otero’wo wamasalmo yemwe’yo akupitirizabe kunena kuti:
“Mafano ao ndiwo a siliva ndi golidi, ntchito za manja a anthu. Pakamwa ali napo, koma osalankhula; maso ali nao, koma osapenya; makutu ali nao, koma osamva; mphuno ali nazo, koma osanunkhiza; manja ali nao, koma osagwira; mapazi ali nao, koma osayenda; kapena sanena pammero pao. Adzafanana nao iwo akuwapanga; ndi onse akuwakhulupirira.” (Salmo 115:4-8)
M’malo mwa kulambira mafano opanda moyo, tiyenera kulambira Mulungu wamoyo.
7. Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kufuna-funa Mulungu? (Salmo 34:8)
7 Njira yomka ku chimwemwe cheni-cheni ndiyo yakuti ife mwaphamphu tifune-fune kudziwa Mulungu wachimwemwe amene’yu, pakuti, monga momwe mtumwi Paulo akulongosolera, “iye . . . amakhala wopereka mphotho wa awo om’funa-funa mwaphamphu.” (Ahebri 11:6, NW) Mulung amene’yu sali wobvuta kwambiri ku’peza, ndipo’nso sitiyenera kumuopa. Paulo mmodzi-modzi’yu, polankhula kwa Agriki olambira mafano, anam’longosola motere:
“Amuna inu a Atene, m’zinthu zonse ndiona kuti muli akupembedzetsa. Pakuti popita, ndi kuona zinthu zimene muzipembedza, ndipeza’nso guwa la nsembe lolembedwa potere, Kwa Mulungu Wosadziwika. Chimene muchipembedza osachidziwa, chimene’cho ndichilalikira kwa inu. Mulungu amene analenga dziko lapansi ndizonse ziri momwemo, Iyeyo, ndiye mwini kumwamba ndi dziko lapansi, sakhala m’nyumba zakachisi zomangidwa ndi manja; satumikidwa ndi manja a anthu, monga wosowa kanthu, popeza Iye mwini apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse; ndipo ndi mmodzi analenga mitundu yonse ya anthu, kuti akhale ponse pa nkhope ya dziko lapansi, atapangiratu nyengo zao, ndi malekezero a pokhala pao; kuti afune-fune Mulungu, kapena akam’fufuze ndi kum’peza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife; pakuti mwa Iye tikhala ndi moyo ndi kuyenda-yenda, ndi kupeza mkhalidwe wathu; monga ena’nso a akuyimba anu ati, Pakuti ife’nso tiri mbadwa zake.’
“Popeza tsono tiri mbadwa za Mulungu, sitiyenera kulingalira kuti umulungu uli wofana-fana ndi golidi, kapena siliva, kapena mwala, wolocha ndi luso ndi zolingalira za anthu.” (Machitidwe 17:22-29)
Ena a omvetsera a Paulo anaseka monyodola, koma ena anakhutiritsidwa maganizo nakhulupirira Mulungu wamoyo.
MULUNGU MLENGI
8. Kodi tingaphunzirenji ponena za Mulungu kuchokera m’ntchito zake za chilengedwe? (Salmo 19:1)
8 Pali anthu lero lino amene amakana kukhalako kwa Mulungu. Ena amanena kuti, “Mulungu wafa.” Koma kodi lingaliro lao liri lolondola? Ponena za anthu otero’wo, Paulo mu imodzi ya makalata ake akulongosola kuti:
“Chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake [za Mulungu] ndizo mphamvu yake yosatha ndi Umulungu wake; popeza zazindikirika ndi zinthu zolengedwa, kuti iwo adzakhale opanda mau akuwiringula.” (Aroma 1:20)
Chilengedwe chopanda malekezero’cho ndi zodabwitsa zake zonse zimene zirimo ziri’di chisonyezero cha “mphamvu yosatha” ya Mulungu.
9. Kodi n’chiani chimene asayansi ochuka abvomereza ponena za mkhalidwe wa munthu m’chilengedwe?
9 Ngakhale asayansi ochuka nthawi ina anabvomereza kuchepa kwao poyerekezera ndi mphamvu yaikulu kwambiri ndi nzeru zoonekera m’chilengedwe. Mwa chitsanzo, Albert Einstein nthawi ina anabvomereza kuti:
“Kuli kokwanira kwa ine . . . kuganizira mosamalitsa kapangidwe kodabwitsa ka chilengedwe, chimene tingachizindikire mwapang’ono, ndi kuyesa modzichepetsa kuzindikira ngakhale mbali yaing’ono kopambana ya nzeru yosonyezedwa m’chilengedwe.”
10. Kodi ndi motani m’mene Newton anakhurtiritsira maganizo bwenzi lina kuti Mulungu aliko?
10 Wotumba “lamulo la mphamvu yokoka,” Sir Isaac newton, anali wina amene anagwidwa mtima kwambiri ndi umboni wa mikhalidwe yosaoneka ya Mulungu imene iyenera kuonedwa m’chilengedwe Chake. Nkhani yotsatirapo’yi ikusonyeza m’mene Newton anabvomerezera chikhulupiriro chake mwa Mulungu Wamphamvuyonse:
Newton nthawi ina anauza makaniko waluso kum’pangira chitsanzo cha dzuwa pamodzi ndi mapulaneti onse olizungulira. Mipira yoimira mapulaneti inagwirizanitsidwa pamodzi kuti iyende motsimikizira m’njira mwao. Tsiku lina bwenzi lina losakhulupirira Mulungu linachezera Newton. Litaona chitsanzo’cho linachiyendetsa, ndipo linanena modabwa kuti, “Kodi ndani anachipanga?” newton anayankha kuti, “Palibe!” Wosakhulupirira Mulungu’yo anayankha kuti, “Uyenera kuganiza kuti ndine chitsiru! Ndithudi munthu wina anachipanga, ndipo iye ndi wochenjera.” Pamenepo Newton anati kwa bwenzi lake’lo, “Chinthu chimene’chi chiri kutsanziridwa kwakung’ono chabe kwa dzuwa pamodzi ndi mapulaneti onse olizungulira zazikulu kwambiri zimene malamulo ake mukuwadziwa, ndipo sindiri wokhoza kukukhutiritsa maganizo kuti chinthu choseweretsa wamba chimene’chi chiri chopanda wopanga ndi wolinganiza; komabe umadzinenera kukhala ukukhulupirira kuti chinthu cheni-cheni chachikulu chimene chitsanzo’cho chatengedwako chakhalako popanda wolinganiza kapena wopanga.”
Mnzake wa Newton anafika pa kubvomereza kuti Wolinganiza ndi Wolenga wamkulu wa zinthu zonse ndiye Mulungu. Ndithudi, ife’nso, pamene tikuyang’ana zodabwitsa za chilengedwe chotizinga, kumwamba ndi pa dziko lapansi, tiyenera kubvomereza kuti Mlengi wa nzeru zonse analenga zonse’zo. Ha, ndi othokoza chotani nanga m’mene tiyenera kukhalira kuti Mlengi wamphamvu amene’yu anaika munthu pa dziko lapansi pano ndi kuti iye ali wokondwera nafe kwambiri!
DZINA LAPADERA KWAMBIRI LA MULUNGU
11. (a) Kodi n’chifukwa ninji kuli kokha koyenera kuti Mulungu akhale ndi dzina? (b) Kodi dzina la Mulungu ndani? (Yesaya 12:2, 4) (c) Kodi likupezekakangti m’Baibulo? (d) Kodi ndi motani m’mene Mulungu anapangitsira dzina lake kudziwika m’njira yapadera m’masiku a Mose? (Eksodo 6:3, 7, 8)
11 Monga anthu aumunthu ife ali yense tiri ndi dzina. Monga Munthu wamkulu kopambana m’chilengedwe chonse, Mulungu naye’nso ali ndi dzina. Kodi dzina limene’lo ndani? Dzina lalikulula Mulungu limaonekera nthawi zokwanira 7,000 m’cholembedwa cha Baibulo. Mwa chitsanzo, Salmo 83:18, NW, limachula motere: “Inu, amene dzina lanu liri Yehova, inu nokha ndinu Wam’mwamba-mwamba pa dziko lonse lapansi.” Pamene Mulungu anagwiritsira ntchito Mose m’kulanditsa Israyeli kwa Farao wa Igupto wankhanza, Iye anapangitsa dzina Lake kudziwika m’njira yapadera kopambana. Farao monyoza anati, “Yehova ndani, kuti ndimvere mau ake ndi kulola Israyeli apite?” (Eksodo 5:2) Yehova anasonyeza bwino lomwe amene iye anali! Pambuyo pa kudzetsa miriri khumi yosakaza pa Igupto, Yehova Mulungu anatulutsa anthu ake, mozizwitsa akumagawanitsa madzi a Nyanja Yofiira kuwapatsa mpata woolokera. Ndipo mgwazi za gulu lankhondo la Farao zinaonongedwa m’madzi amodzi-modzi’wo pamene iwo anakumana’nso.
12. Kodi dzina la Mulungu likugwirizanitsidwa ndi chifuno chotani? (Eksodo 3:13-15)
12 Motero Yehova anasoyeza kuti dzina lake lapadera kwambiri’lo likugwirizanitsidwa ndi chifuno chake cha kulanditsa awo amene amam’konda ndi kumumvera, kanthu kena kamene ife tingakazindikire ndi chiyamiko pamene Yehova posachedwapa achitapo kanthu kudzetsa chionongeko pa dziko lamakono la anthu opanda umulungu. Monga momwe Mulungu mwini amalengezera nthawi zoposa makumi asanu ndi limodzi kupyolera mwa mneneri Ezekieli, kuti, “Adzadziwa kuti Ine ndine Yehova.”—Ezekieli 38:23.
13. (a) Kodi Yehova anauzanji Mose ponena za mikhalidwe Yake? (b) Kodi ndi uti umene uli mkhalidwe wapadera kopambana wa Mulungu? (Aroma 8:38, 39) (c) Kodi ndi motani m’mene tingapezere mayankho okhutiritsa a mafunso onena za moyo?
13 Komabe, ambiri a mtundu wa anthu lero lino akufika pa kudziwa Yehova m’njira imene idzakhala dalitso kwa iwo. Mulungu wamkulu amene’yu ali ndi mikhalidwe yodabwitsa, monga momwe’di iye analengezera kwa mnereri wake Mose kuti:
“Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osawerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa; koma wosamasula wopalamula.”
M’Baibulo monse timawerenga za kusonyeza kwa Yehova kukoma mtima kwake kwachikondi kochuluka kwa awo amene amam’tumikira mokhulupirika. “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Iye ali wachifundo m’njira yaikulu kwa anthu amene amatembenuka ku njira yoipa ya dziko ndi amene amafuna-funa chilungamo chake. Iye ali ndi choonadi chochuluka, ndipo chimene’chi amachisonyeza m’masamba a Baibulo. Pamene tikufuna-funa choonadi chake, tidzapeza mayankho okhutiritsa a mafunso ambiri amene tingakhale nao ponena za moyo.
[Chithunzi patsamba 48]
Anthu amalambira milungu yambiri. Koma kodi ndani amene ali Mulungu wamoyo?
[Chithunzi patsamba 49]
Kulambira makolo akufa kapena kulemekeza mwachikondi makolo amoyo-n’chiti chimene chiri chopindulitsa?
[Chithunzi patsamba 55]
Mulungu wamoyo yekha akanatha kulinganiza ndi kupanga dzuwa ndi mapulaneti olizungulira
[Chithunzi patsamba 56]
יהוה YEHOVA
Yehova akukweza dzina lake mwa kuononga oipa, pamene akupulumutsa atumiki ake okhulupirika