Mutu 7
Kulinganizira Anthu Malo Okhala Achimwemwe
1. Kodi Yehova wapatsa chiani munthu monga kwao, ndipo kodi ndi motani m’mene tiyenera kuchiwerengerera? (Ahebri 3:4)
NGATI munthu wina analinganiza ndi kukumangirani nyumba yosangalatsa m’malo okongola naipereka kwa inu monga mphatso yaulere, kodi simukam’thokoza kaamba ka iyo? Ndithudi mukam’thokoza! Pamenepo muyenera kukhala othokoza kweni-kweni kwa Wolinganiza ndi Womanga wamkulu wa pulaneti iri dziko lapansi. Pakuti Baibulo limatiuza kuti “Yehova, Wakulenga kumwamba ndi dziko lapansi,” wapereka dziko lapansi “kwa ana a anthu.” (Salmo 115:15, 16) Ha, ndi mphatso yachifundo chotani nanga! Ndipo pamene tikupenda m’mene Yehova Mulungu analinganizira dziko lapansi kuti likhalidwe ndi anthu, tiyenera’di kudabwa ndi nzeru ndi mphamvu imene Iye anasonyeza monga Mulungu Wolinganiza ndi Wodziwa Kumanga.
“PACHIYAMBI”
2. Kodi ndi zinthu zotani zimene zimachitira umboni ukulu wa chilengedwe cha Mulungu? (Salmo 8:3, 4)
2 Potembenukira ku mau oyambirira eni-eni a Baibulo, timawerenga kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:1) Mosakaikira zinali zaka mabiliyoni ambiri zapita’zo pamene Mulungu anachita kachitidwe kakakulu kwambiri ka kulenga kamene’ka, ndipo mosasamala kanthu za malingaliro oombana a asayansi ena onena za m’mene zimene’zi zinachitikira, kumwamba kwaulemerero ndi dziko lapansi lokongola zikupitirizabe kuchitira umboni kukongola kwa chilengedwe cha Mulungu.
3. Kodi ndi motani m’mene Mulungu anasonyezera nzeru m’kupatsa dziko lapansi madzi ochuluka? (Salmo 104:1, 5, 6)
3 Ha, ndi nzeru ndi kuoneratu kotani nanga kumene Yehova anasonyeza m’kusonkhanitsa pamodzi zinthu za chilengedwe chonse! Mwa chitsanzo, pali madzi—chinthu chochuluka kopambana pa dziko lapansi pano. Mosafanana ndi zinthu zina zamadzi, iwo ali ndi mphamvu yodabwitsa ya kupepuka m’kulemera pamene kutentha kwake kutsika kufikira pa kuundana, kotero kuti kenako madzi ozizira kwambiri amakwera ndipo amapanga muyalo wotetezera wa madzi oundana pamwamba pa nyanja ndi nyanja zazikulu. Ngati madzi oundana akanakhala olemera koposa madzi, dziko lapansi’li likanakhala litaikidwa kale “m’kuzizira kwambiri” m’mene palibe chamoyo chikanatha kukhala ndi moyo. Lero lino, madzi amatumikira monga chofewetsera, chothiririra nthaka, monga magwero a mphamvu ya magetsi-inde, ngakhale zigawo ziwiri mwa zitatu za thupi lathu zapangika ndi madzi. Sitikanakhala ndi moyo popanda madzi. Mlengi wanzeru’yo anaoneratu zonse’zi pamene iye anakuta dziko lapansi ndi “nyanja.”—Genesis 1:2.
4. Kodi ndi motani m’mene kukhazikitsidwa kwa dziko lapansi mogwirizana ndi dzuwa ndi mwezi kumasonyezera nzeru ya Mulungu? (Yobu 26:7, 14)
4 M’chilengedwe chochitidwa ndi Mulungu chimene’chi kugwirizana kwa dziko lapansi ndi thambo kuli’nso kokondweretsa kwambiri. Mulungu anapendamitsa pang’ono kuima kwa dziko lapansi pa kupendama kwa madigri 23 1⁄2 kupendamira ku njira yake yozungulirira, kotero kuti m’kati mwa ulendo wake wa chaka ndi chaka wozungulira dzuwa, theka liri lonse limalowetsedwa motsatana-tsatana mu ngululu, dzinja, mphakasa ndi nyengo yachisanu. Utali wa dziko lapansi kuchokera ku dzuwa uli wongoyenerera kuchirikiza moyo. Ngati likanakhala pafupi kwambiri, dziko lapansi likanakhala lotentha kwambiri kosati n’kukhalapo zamoyo; ngati likanakhala kutali kwambiri, potsirizira pake likanaundana. Mwezi unaikidwa kotero kuti kukoka kwake kwa mphamvu yokoka kumachititsa kukwera ndi kutsika kwapang’ono-pang’ono kwa pfunde kuti atsuke magombe a nyanja za dziko lapansi. Polingalira zimene’zi, ndithudi tiyenera kufuna “kutamanda Ya [Yehova] . . . chifukwa cha ntchito zake za mphamvu”!—Salmo 150:1, 2.
“MASIKU” A KULENGA
5, 6. Kodi ndi motani m’mene tingalingalirire utali wa ‘masiku a kulenga’? (Ahebri 4:3-5)
5 Kwa nyengo zosawerengeka, dziko lapansi linakutidwa ndi mdima ndipo linali lopanda zamoyo. Koma “mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu inali kumayenda-yenda pamwamba pa madzi.” (Genesis 1:1, 2, NW) Kodi n’chiani chimene chikatulukapo?
6 Panopo tikulowa “m’masiku” asanu ndi awiri a kulenga. Kodi “masiku” amene’wa anali a utali wotani? Atali kwambiri koposa maola makumi awiri mphamvu anai! Baibulo limatiuza kuti “tsiku limodzi kwa Yehova liri ngati zaka chikwi.” (2 Petro 3:8, NW) Koma liri lonse la “masiku” a kulenga amene’wa liyenera kukhala lalitali koposa pamenepo. Kodi tikudziwa motani? Genesis 2:2 amanena kuti, pambuyo pa “masiku” asanu ndi limodzi a kulenga, Mulungu “anapuma tsiku lachisanu ndi chiwiri ku ntchito yake yonse.” Baibulo limasonyeza kuti ‘tsiku la kupuma’ la Yehova likupitirizabe. Pakuti mtumwi Paulo akulemba kuti Akristu ayenera, mwa chikhulupiriro ndi kumvera, kuchita “zonse zimene angathe kuti alowe mu mpumulo umene’wo.” (Ahebri 4:9-11) Kuwerengera nthawi kwa Baibulo kumasoneyza kuti tsopano kuli pafupi ndi zaka zikwi zisanu ndi chimodzi chiyambire pamene Mulungu anayamba ‘kupuma’ ku ntchito zake za kulenga pa dziko lapansi. Patsogolo pathupa pali kulamulira kwa zaka chikwi kwa Kristu, pofikira mapeto ake chifuno cha Mulungu cha kudzaza dziko lapansi ndi banja la anthu lachimwemwe chidzakhala chitakwaniritsidwa. Pamenepo “tsiku la kupuma’ la Mulungu lidzatha. Kumene’kukudzasonyeza kuti ‘tsikula kupuma’ limene’li likakhala la utali wa zaka zikwi zisanu ndi ziwiri. (Genesis 1:28; Chibvumbulutso 20:4) N’koyenera kunena kuti liri lonse la “masiku” asanu ndi limodzi apita’wo a chilengedwe akakhala ndi nyengo za nthawi zofanana’zo, m’kati mwa iri yonse imene Yehova anachita siteji loonjezereka la kulinganiza dziko lapansi kuti lidzakhale kwao kwa munthu kwa m’tsogolo. Pamene ife tsopano tikuona m’mene Iye anachitira zimene’zi, tiyenera kuzindikira’di mphamvu ya mau a wamasalmo’yo, akuti: “Ha! ntchito zanu n’zazikulu, Yehova, zolingalira zanu n’zozama ndithu.”—Salmo 92:5.
“KUYERE”
7. Kodi ndi motani m’mene ‘kunayerera’? (Yesaya 45:7)
7 Zaka zikwi makumi ambiri zapita’zo Yehova anapitiriza kunena kuti: “Kuyere.” Kumene’ko kunasonyeza chiyambi cha “tsiku la kulenga.’ Pofika pa mapeto a “tsiku” lalitali limene’lo, Mulungu anakonzera njira kuunika kochokera ku dzuwa kuwalira “pamwamba pa nyanja” imene inakuta dziko lapansi. Chophimba chokhuthala cha mdima sichinalepheretse’nso kulekanitsika kwa pakati pa Usana ndi usiku mogwirizana ndi dziko lapansi lino. Chifukwa cha kuwala kwa “Usana” kumene’ku, munthu m’nthawi yokwanira akakhala wokhoza kugwira ntchito ndi kusangalala ndi zokongola za dziko lapansi lom’zinga, ndipo “Usiku” ukam’theketsa kubwezeretsa nyonga zake mwa tulo tokondweretsa.—Genesis 1:3-5.
“PAKHALE THAMBO”
8. Kodi ndi kudziwiratu kotani kumene Yehova anasonyeza m’kupanga “mlengalenga”?
8 Pa “tsiku lachiwiri” la kulenga, Mulungu anapangitsa kugwanikana kwa madzi amene’wa, kukhala madzi amene anakhala pa nkhope ya dziko lapansi ndi madzi amene anakhala olenjekeka ngati thambo lalikulu lokuta dziko lathu lapansi. Iye anacha mlengalenga’wo pakati pa kuunjikana kwakukulu kwa madzi kuwiri kumene’ku kukhala “Kumwamba.” Kunaphatikizamo mlengalenga mwathu mwa mpweyamu. Munomo Mulungu anapereka kuchuluka koyenera kwa mipweya, maka-maka naitrojeni ndi okosijeni, kuti achirikize zomera ndi zolengedwa zopuma zimene iye akazipanga pambuyo pake. Iye anapanga mlengalenga mwa mpweya m’menemu kukhala moyenerera kwambiri kaamba ka kukhala ndi moyo kosangalatsa, ndi kutumikira monga chinjirizo ku miyala ya kumwamba ndi mbaliwali zobvulaza. Ndithudi Mulungu ali Mlengi wanzeru ndi wachikondi!—Genesis 1:6-8.
DZIKO LAPANSI, NYANJA NDI ZOMERA ZILENGEDWA
9. Kodi Mulungu anali kulingalira chiani m’kulenga “Dziko lapansi” ndi “Nyanja”? (Yesaya 45:18)
9 Mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu, kapena mzimu inapitirizabe kuyenda-yenda pamwamba pa dziko lapansi. Tsopano, pa “tsiku la kulenga’ lachitatu, iye anapitiriza kutukula mtunda wouma ‘m’madzi a pansi pa thambo’wo.’ Moaskaikira panali kukhwinyata kwakukulu pamene mtunda unakankhiridwa pamwamba ndi nyanja zinasonkhanitsiridwa m’malo ao otsika. Panopo, kachiwiri’nso, nzeru ndi chikondi cha Mulungu ziri zoonekera bwino. Pamene nthawi inafika ya kulengedwa kwao, zinyama ndi munthu zikakhala zokhoza kupanga malo ao okhala pa mtunda pouma. Nyanja zikakhala ndi zamoyo za m’madzi zochuluka kwambiri, ndipo zigawo zazikulu kwambiri za nyanja za mchere zikakhala ndi chiyambukiro chochepetsa kupambanitsa, zikumaletsa’nso kupambanitsa kwakukulu kwa kutentha ndi kuzizira pa dziko lonse lapansi.—Genesis 1:9, 10.
10. (a) Kodi n’chiani chimene chinaonekera kwa nthawi yoyamba pa “tsiku lachitatu,” ndipo m’mipangidwe yotani? (b) Kodi ndi motani m’mene zimene’zi zikapindulitsira anthu? (Genesis 1:29, 30; Salmo 104:14)
10 Koma zochuluka zinayenera kuonekera pa “tsiku lachitatu” limene’li. Kwa nthawi yoyamba, zamoyo! Baibulo limapereka cholembedwa chakuti:
“Mulungu ndipo anati, Dziko lapansi limere mauzu, therere lobala mbeu, ndi mtengo wazipatso wakubala zipatso monga mwa mtundu wake, momwemo muli mbeu yake, pa dziko lapansi.” (Genesis 1:11)
Chotero Mulungu analenga zinthu zodabwitsa zokhala ndi maselo, zopangidwa kuti ziswane mogwirizana ndi “chitsanzo” choikidwa mu selo liri lonse. “Mitundu” ina inakhala mitengo yaikulu kwambiri, ikumapereka mthunzi ndi kumanga nthaka. “Mitundu” ina inali mitengo yaing’ono kwambiri ndi zitsamba, yobala zipatso, mitedza ndi zibalobalo, kuti zipereke, pamodzi ndi masamba, mitundu yosiyana-siyana ya zakudya. Mulungu analenga mitundu yosiyana-siyana ya maluwa okongola kukometsa ndi kukongoletsa dziko lapansi. “Mtundu” uli wonse wa chomera unatulutsa kokha “mtundu” wake, koma m’maonekedwe ndi mapangidwe osiyana-siyana okongola-monga momwe kuliri ndi mitundu yokongola ya maluwa a rozi.—Genesis 1:12, 13.
11. Kodi ndi motani m’mene Mulungu analinganizira kuti dziko lapansi litulutse zakudya? (Yeremiya 10:12)
11 Mulungu anapatsa mbali yobiriwira ya zomera chinthu chochedwa “klorofili.” Mwa njira ya chinthu chocholowana-cholowana chimene’chi, kuunika kochokera ku dzuwa kumapangitsa kaboni daiokosaidi wochokera mu mpweya ndi madzi ochokera m’nthaka kugwirizana pamodzi kupanga shuga wosiyana-siyana, kukumapanga wochuluka wokwanira matani mabiliyoni a amene’yu pa dziko lonse lapansi chaka chiri chonse, ndi pa nthawi imodzi-modzi’yo kutulutsa okosijeni kuti ayeretse mpweya. Zomera zimagwiritsira ntchito shuga amene’yu pokula, zikumam’sandutsa kukhala mitundu yosiyanaj-siyana ya zakudya zimene timadya. Motero nyonga imene imachirikiza mitundu yosiyana-siyana ya zinthu zamoyo pa dziko lapansi yonse imachokera m’njira yodabwitsa yolowetsamo kuwala kwa dzuwa, mpweya ndi madzi, ndipo chinsinsi cha njira imene’yi n’chosadziwikabe kwa munthu! Oona kwambiri ndiwo mau awa: ‘Ntchito zanu zichuluka’di, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.”—Salmo 104:24.
ZOUNIKIRA ZIONEKERA KUMWAMBA
12. (a) Kodi n’chifukwa ninji palibe kuombana pakati pa Genesis 1:1 ndi 1:16? (b) Kodi n’chiani chimene mwachionekere chianchitika pa “tsiku lachinai”? (Salmo 136:1, 7-9)
12 Pa “tsiku lachinai,” Mulungu “anapanga zounikira zazikulu ziwiri; chounikira chachikulu chakulamulira usana, chounikira chaching’ono chakulamulira usiku, ndi nyenyezi zomwe.” (Genesis 1:14-19) Komabe, kodi Mulungu sanali atalenga makamu akumwamba amene’wa kale-kale, “pachiyambi”? Inde, iye anali atalenga. Koma chonde onani kuti pali kusiyana pakati pa mneni’yo “analenga” (Chihebri, bara’) pa Genesis 1:1 ndi mneni’yo ‘anapanga’ (Chihebri, ‘asah) pa Genesis 1:16. chimene mwachionekere chinachitika pa “tsiku lachinai” ndicho chakuti kwa nthawi yoyamba kaonekedwe ka dzuwa, mwezi ndi nyenyezi kanakhala koonekera bwino kwambiri pa nkhope ya dziko lapansi, mwina mwake chifukwa cha kuyeretsedwa kwa mlengalenga mwa mpweya. Dzuwa lowala’lo tsopano linatumikira monga “chounikira” kuwalitsa usana, likumadzetsa kufunda kosangalatsa. Koma bwanji ponena za mwezi? Eya, ofufuza kutali m’mlengalenga anena kuti yoposa 50 peresenti ya pa mwezi yapangika ndi tizidutswa tonyezimira ngati galasi, toyenerana kwambiri ndi kusonyeza mbaliwali za dzuwa. Pamene tikusangalala ndi kuwala kwa mwezi tingathe kulingalira nzeru ndi chikondi cha Mulungu m’kupereka “chounikira chaching’ono” chimene’chi kuti chiziwala usiku!
13. (a) Kodi munthu akawerengera chiani ndi zounikira zimene’zi? (Mlaliki 3:1) (b) Kodi n’chifukwa ninji “madzulo” akuikidwa patsogolo pa “mamawa”? (Miyambo 4:18)
13 M’nthawi yokwanira, munthu akakhala wokhoza kuwerengera nthawi ndi zounikira zimene’zi. Komabe, chowerengerera nthawi chiri chonse chopangidwa ndi munthu nthawi zonse chikakhala chaching’ono ndi cholamuliridwa ndi makamu akumwamba amene Wosunga Nthawi Wamkulu’yo, Yehova Mulungu, anayambitsa kuyenda pa nthawi zake zeni-zeni zolinganizidwa, kaamba ka phindu la munthu. Pa “tsiku lakulenga’ lachinai limene’li, mofanana ndi pa “tsiku” liri lonse, ntchito ya Mulungu inayamba “madzulo,” pamene kuoneka kwachizime-zime kwa ntchito yake kunyamba kuonekera, ndi kupitirizabe mpaka “m’mawa,” pamene ntchito zake zonse zaulemerero zinakhala zoonekera bwino kwambiri.
14. Kodi n’chifukwa ninji tiri ndi chifukwa chothokozera kaamba ka zinthu zimene’zi zimene Mulungu anachita? (Chibvumbulutso 4:11)
14 Potsiriza ntchito zake zazikulu za “tsiku” lachitatu ndi lachinai lomwe, Mulungu anaona kuti kunali “kwabwino.” (Genesis 1:12, 18) Koma “masiku” awiri okondweretsa a ntchito ya kulenga ndi “tsiku la kupuma’ analipobe. Mlengi Wamkulu’yo anayenera kupitirizabe kupanga kukonzekera kwachikondi kwa malo okhala a munthu, akumayembekezera chimwemwe chake cham’tsogolo. Kaamba ka zimene’zi, ali yense wa ife ayenera kukhala wothokoza, monga momwe analiri Mfumu Davide, amene anati:
“Inu, Yehova, Mulungu wanga, zodabwiza zanu mudazichita n’zambiri, ndipo zolingirira zanu za pa ife; palibe wina wozifotokozera Inu; ndikazisimba ndi kuzichula, zindichulukira kuziwerenga.”—Salmo 40:5.
[Chithunzi patsamba 63]
Mlengi modabwitsa analinganiza zomera kuti zigwiritsire ntchito kuunika kwa dzuwa, mpweya ndi madzi kupanga chakudya