Mutu 8
Mlengi Aika Okhala pa “Chombo cha m’Mlengalenga Dziko Lapansi”
1. (a) Kodi ndi motani m’mene dziko lapansi limasiyanira ndi mwezi, ndipo ndi zombo zopita kutali m’mlengalenga zopangidwa ndi anthu? (b) Kodi ndi motani m’mene anthu ambiri amasonyezera kuti samayamikira kweni-kweni dziko lathu lapansi? (Salmo 10:4)
POFIKA mapeto a “tsiku lachinai” la Mulungu la kulenga, nkhope ya dziko lapansi inapereka kaonekedwe kokongola. Inali ndi maonekedwe osiyana-siyana. Posachedwapa kwambiri m’zaka zino za zana la makumi awiri za nyengo yathu ino, wopita kutali m’mlengalenga analiona ali pa nkhope ya mwezi yopanda zamoyo’yo, ndipo ananena kuti:
“Pamene uyang’ana dziko lathu lapansi uli ku utali wa mamailo zikwi mazana awiri mphambu makumi anai, maka-maka m’chizimezime m’mene mwakanthidwa kwa nyengo yosadziwika, umaona kuti pulaneti lathu ndiro chinthu chokha m’chilengedwe chonse chimene chiri ndi maonekedwe m’kati mwake . . . timakhala pa pulaneti lokongola kwambiri lotero’olo . . . Chodabwitsa chachikulu ndicho chifukwa ninji m’dziko sitingayamikire chimene tiri nacho.”
Mwa zimene anakumana nazo wopita kutali m’mlengalenga amene’yo anafikira pa kudziwa m’mene kuliri kopanda pake kukhala m’malo opanikizika a chombo chopangidwa ndi anthu kumasiyanira ndi moyo wachibadwa umene munthu angasangalale nawo panopo pa “chombo cha m’mlengalenga Dziko Lapansi,” m’malo okhala amene Mulungu anam’linganizira. Komabe, si kokha kuti unyinji wa anthu umalephera kuyamikira zimene uli nazo, koma kwakukulu iwo amanyalanyaza Wolinganiza ndi Wopanga wapandera wa dziko lapansi’li. Anthu ambiri amasankha kukhala ngati munthu wopusa amene “wanena mu mtima mwake: ‘Kulibe Yehova.’”—Salmo 14:1, NW.
NSOMBA “ZAMOYO” NDI ZOLENGEDWA ZOULUKA
2. (a) Kodi ndi liti pamene Mulungu anayamba kuika anthu pa ‘chombo chathu cha m’mlengalenga? (b) Kodi n’chiani chimene chiri “moyo”? (Chibvumbulutso 16:3) (c) Kodi ndi miyoyo yotani imene inalengedwa pa “tsiku lachisanu”?
2 Osati m’zaka mamiliyoni ambiri zapita’zo, monga momwe anthu ena amanenera, koma m’nthawi zaposachedwa pompa, Mulungu anapitiriza mogwirizana ndi ndandana yake ya nthawi kuika anthu pa ‘chombo chathu cha m’mlengalenga.’ Iye analenga “miyoyo” yoyambirira. Liu’lo “moyo” (Chihebri, ne’phesh), monga momwe likuonekera muno m’cholembedwa cha Baibulo cha chilengedwe, limanena cholengedwa chopuma ndi cholingalira, kaya nsomba, mbalame, chiyama kapena munthu. Pa ‘tsiku la kulenga’ lachisanu limene’li, Mulungu adalenga “miyoyo” ya nsomba ndi mbalame.—Genesis 1:20-23.
3. (a) Kodi ndi motani m’mene munthu wakhalira wokhoza kugwiritsira ntchito njira zochitira zinthu zimene amazipeza mwa zolengedwa, koma kodi n’chiani chimene iye ayenera kubvomereza? (Yobu 12:7-10) (b) Kodi ndi motani m’mene nsomba ndi mbalame zakhalira dalitso kwa anthu?
3 Ha, ndi nzeru yaumulungu yochuluka chotani nanga imene ikuoneka m’kaumbidwe ka zinthu zamoyo zimene’zi! Ku mlingo wakuti-wakuti, munthu wakhala wokhoza kutsanzira njira zochitira zinthu zimene iye amazipeza m’zolengedwa zimene’zi, monga ngati kusambira kofulumira kwambiri kwa chirombo cha m’madzi chochedwa sikwidi (squid), ndi chodziwira kumene kuli zinthu cha mleme ndi mphamvu zina zoulukira za mbalame. Koma pali zinsinsi zambiri zodabwitsa m’kuumbidwa kwa ‘miyoyo” imene’yi zimene munthu wakhala wosakhoza kuzitulukira. Nsomba ndi mbalame zaonjezera kukongola ndi kukondweretsa ku malo okhala munthu a pa dziko lapansi, kuphatikiza pa kupereka zoonjezera zokoma ku mpambo wake wa zakudya pamene Mulungu analamulira kuti izo ‘zitumikire monga chakudya’cha munthu.—Genesis 9:2, 3.
ZAMOYO KAAMBA KA DZIKO LAPANSI
4. (a) Kodi n’chiani chimene Mulungu anapanga pa “tsiku lachisanu ndi chimodzi,” ndipo motani? (b) Kodi zinyama zatumikira munthu m’njira zotani? (Genesis 1:25)
4 Pamene ‘tsiku lakulenga’ lachisanu ndi chimodzi linayamba, Yehova anati:
“Dziko lapansi libale zamoyo monga mwa mitundu yao, ng’ombe, ndi zokwawa, ndi zinyama za dziko lapansi monga mwa mitundu yao.” (Genesis 1:24)
Mzimu wosaoneka wa Mulungu unagwira ntchito m’kupanga kusyiyana-siyana kodabwitsa kwa “mitundu” ya zinyama, zina zake zimene zinakwaniritsa chifuno chakanthawi, ndi zina zake zimene ziripobe, kaamba ka ubwino wa munthu, mpaka lero. Zina za zinyama zimene’zi ziri zoposa zifuyo chabe: Pali akavalo oti azikweredwa, agalu oti azibusa, njobvu zoyendera, ng’ombe zolimira, nkhosa zoti zizipereka ubweya, ndi zina zotero. “Miyoyo” ya zinyama yatumikira’di kaamba ka phindu ndi chimwemwe cha anthu.
5. Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kuthokoza Mulungu kaamba ka zinthu zimene’zi? (Salmo 8:4, 6-9)
5 Tingathokoze’di Yehova kaamba ka zinthu zimene’zi! Monga momwe wolemba masalmo akunenera kuti:
“Ndidzayimbira zachifundo za Yehova nthawi zonse: . . . kumwamba ndi kwanu, dziko lapansi lomwe ndi lanu; munakhazika dziko lokhalamo anthu ndi kudzala kwake.”—Salmo 89: 1, 11.
ULEMERERO WOTSIRIZIRA WA ZOLENGEDWA ZA PA DZIKO LAPANSI
6. (a) Kodi ndi wothandiza wotani amene Yehova anali naye pambali pake m’kulenga? (Yohane 1:1-4) (b) Kodi Mulungu ananenanji kwa wantchito mnzake amene’yu, ndipo chotero kodi ndi unansi wotani umene munthu akakhala nawo ku zinyama?
6 M’kati mwa ntchito yonse ya kulenga imene’yi, Yehova anali ndi wothandiza pambali pake-“mnisiri”—wokondedwa kopambana mwa ana ake onse aungelo m’miyamba yosaoneka. (Miyambo 8:30) Cha kumapeto kwa ‘tsiku la kulenga’ lachisanu ndi chimodzi Yehova anati kwa wantchito mnzake amene’yu:
“Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu: alamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’lengalenga, ndi pa ng’ombe, ndi pa dziko lonse lapansi, ndi pa zokwawa zonse zakuwawa pa dziko lonse lapansi.”—Genesis 1:26-28.
7. (a) Kodi Mulungu analenga munthu mwa njira yotani? (Yobu 33:4) (b) Kodi n’chiani chimene chimatsimikizira kuti munthu sakakhala atasinthika? (Salmo 100:3)
7 Kodi Mulungu ndi ‘wantchito’ mnzake’yo anapanga munthu mwa njira ina yocholowana-cholowana ya chisinthiko? Ai, inali yosabvuta kwambiri koposa imene’yo. Pakuti Baibulo limatiuza kuti:
“Yehova Mulungu anaumba munthu ndi dothi lapansi, nauzira mpweya wa moyo m’phuno mwake; munthu’yo nakhala wamoyo.” (Genesis 2:7)
Baibulo pano silikunena kanthu ponena za munthu akusinthika kuchokera ku zolengedwa zaubweya ndi zosalankhula. Ndithudi, iye sakanapeza kuyamikira kukongola ndi nyimbo, kukhoza kufufuza za m’mbuyo ndi za m’tsogolo, kutulukira zinthu, chikumbu mtima cha kulekanitsa pakati pa zabwino ndi zoipa, ndi mikhalidwe yodabwitsa ya kukoma mtima ndi chikondi, mwa kungochitika zokha kwa chisinthiko! Kokha Munthu wapamwamba kwambiri ndi wanzeru kwambiri –Mulungu-akatha kupereka mikhalidwe yotero’yo. Yehova Mulungu analenga mwamuna woyamba mu “chifanizo” cha Iye mwini, ndipo osati chifunizo cha zolengedwa za pa dziko lapansi ziri zonse zakale, monga ngati “mbalame ndi zolengedwa za miyendo inai ndi zinthu zokwawa.” (Aroma 1:23, NW) Pakati pa zinyama zosalankhula, zosaganiza ndi cholengedwa chaumunthu ndi choongoka, pali mpata umene palibe njira iri yonse ya chisinthiko ikayamba kuoloka.
8. (a) Kodi n’chiani chimene chimasonyeza kuti munthu woyambirira anali wokhoza kugwiritsira ntchito bwino chinenero? (b) Kodi n’chiani chimene chinali mkhalidwe wa zolengedwa zonse za Mulungu? (Deuteronomo 32:4)
8 Pamene Mulungu pambuyo pake anatenga nthiti kuchokera mwa mwamuna pamene anali mtulo, naipanga mkazi, Hava, ndi kum’pereka mkazi wokongola amene’yu kwa Adamu, mwamuna’yo sanali kokha ndi kubangula kwa zinyama m’kusonyeza chikondwerero chake. Pa nthawi yomweyo iye ananena nyimbo yoyambirira kuti:
“Uyu tsopano ndiye pfupa la mafupa anga,
Ndi mnofu wa mmnofu wanga;
Ndipo adzachedwa Mkazi,
Chifukwa anam’tenga mwa mwamuna.”
Chotero m’kulenga anthu monga “mwamuna ndi mkazi” Mulungu anatsiriza kulenga kwake za pa dziko lapansi.
“Ndipo anaziona Mulungu zonse zimene adazipanga, ndipo, taonani, zinali zabwino ndithu. Ndipo panali madzulo ndipo panali m’mawa, tsiku lachisanu ndi chimodzi.”—Genesis 1:31.
ZIFUKWA ZOTHOKOZERA MLENGI WATHU
9. Kodi ndi mbali zina zotani m’kupangidwa kwa munthu zimene ziyenera kutipangitsa kutamanda Mlengi wathu?
9 Cholengedwa chokongola kopambana mwa zolengedwa za pa dziko lapansi za Mulungu-munthu-chinali’di ‘chabwino kwambiri.’ Monga mbadwa za mwamuna ndi mkazi oyamba amene’wo, tiyenera kukhala othokoza nthawi zonse kaamba ka ukatswiri wodabwitsa wa Mulungu. Taganizirani chisangalalo chimene tingachipeze m’mphamvu zathu zisanu-kukoma kwa zakudya zokoma, kukhudza kwa manja achikondi, kaonededwe ka malo okondweretsa, phokoso la mbalame kapena la nyimbo zokondweretsa, kununkhira kwa maluwa ndi kwa zakudya! Ndipo kaamba ka kupima bwino, Mulungu watipatsa maso, makutu, mphuno ziwiri-ziwiri ali yense, kuphatikiza pa ziwalo zina zofunika kwambiri za thupi. Zala khumi zimagwirizana bwino lomwe china ndi chinzake kuchititsa ntchito kuchitidwa ndi mano makumi atatu mphambu awiri olinganizidwa mokongola matitheketsa kuluma ndi kutafuna zakudya zathu, ndi kusonyeza kumwetulira kwa awo okhala pafupi nafe. Kukhoza kwathu kusonyeza chikondwerero ndi phwete mwa kuseka (kanthu kena kamene zinyama sizingathe kuchita) ndiko ena a madalitso athu ambiri. Ha, ndi chikondwerero chotani nanga chimene tingachipeze m’moyo mwa mphamvu zoperekedwa ndi Mulungu za kuyenda, kuthamanga, kudumpha, kusambira! Moyamikira mbali zikwi zochuluka za thupi zimene Mlengi wathu anatipatsa, tiyenera kufuna kunena mofanana ndi m’mene Mfumu Davide ananenera kuti:
“Munandisanthula, Yehova, nimundidziwa. Ndikuyamikani chifukwa kuti chipangidwe change n’choopsya ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwiza; moyo wanga uchidziwa ichi bwino ndithu.”–Salmo 139:1, 14.
10. Kodi ndi motani m’mene njira ya anthu imasonyezera nzeru ya Yehova? (Mlaliki 11:5)
10 Yodabwitsa’di pakati pa mphatso za Mulungu kwa munthu ndiyo mphamvu ya kubala mtundu wake. Ngakhale kuli kwakuti dziko loipa lagwiritsira ntchito molakwa ziwalo zogonanira ndi kuzigwiritsira ntchito kaamba ka zifuno zoipa, si koipa pamene zigwiritsiridwa ntchito ndi anthu okwatirana mogwirizana ndi chifuno cha Mulungu ndi malamulo. Ha, ndi njira yodabwitsa chotani nanga m’mene kubalana kwa anthu kuliri! Mwa mkazi, selo la dzira- losatalika koposa nsonga ya singano- limapatsidwa mphamvu ndi selo la ubwamuna la ukulu wa 1/85,000 wa selo la dzira limene’lo. Mwa kugwirizana kwa tinthu tiwiri timene’to mumakula m’nthawi yokwanira munthu wathunthu, wokhala ndi mikhalidwe yochokera kwa makolo onse mogwirizana ndi “chitsanzo” (DNA) chokhala ndi mbali zambiri chopangidwa pa nthawi imene maselo’wo anagwirizana. Odziwa kumanga amakono nthawi zina amadzaza malo akulu ndi zitsanzo za nyumba imene irinkumangidwa, koma Mulungu anatha kuika “chitsanzo” chopangira munthu wathunthu–wocholowana-cholowana kwambiri koposa nyumba iri yonse-m’selo limene liri pafupi-fupi losaoneka. Ponena za “chitsanzo” cha munthu chimene’chi, M’fumu Davide akubvomereza kuti Yehova ali wokhoza kuona zinthu zonse, kuphatikizapo zazing’ono kwambiri:
“Munandiphimbabe m’mimba mwa mai wanga. Maso anu anaona ngakhale mluza wanga, ndipo m’bukhu mwanu ziwalo zake zonse zinalembedwa, ponena za masiku’wo pamene zinapangidwa ndipo kufikira pa nthawi imene’yo panalibe chimodzi pakati pao. Chotero, kwa ine maganizo anu ndi amtengo wapatali chotani nanga m’mene aliri. O, Mulungu, chionkhetso chao chachikulu chimalingana n’chiani!”—Salmo 139:13, 16, 17, NW.
11. Kodi tiyenera kuthokoza Mulungu kaamba ka kukhoza kotani kwa ubongo wa munthu?
11 Zoona, maganizo a Mulungu ndi a mtengo wapatali! Ndipo tingakhale othokoza kopambana kuti Mulungu watipatsa ubongo umene uli wokhoza kuganiza malingaliro ake. Ha, chimene’chi ndi chiwalo chodabwitsa chotani nanga! Ubongo wa munthu iye mwini akanati apange kompyuta yoyendera mphamvu ya magetsi kuti ichite ntchito yofanana’yo, ikanafunikira kukhala yaikulu mofanana ndi nyumba yochedwa Empire State Building mu mzinda wa New Yorka Zoonadi, Yehova amadziwa kutsinira malo! Ndipo, mogwirizana ndi kunena kwa katswiri wa sayansi ya zamoyo, kukhoza kwa ubongo wa munthu kumaposa kwambiri kuja kwa maubongo a zinyama. Ukuyerekezeredwa kukhala uli ndi kukhoza kochititsa mantha kwa kusunga chidziwitso nthawi mamiliyoni chikwi chimodzi koposa chimene munthu tsopano akusuunga m’kati mwa nthawi ya moyo wa zaka makumi asanu ndi awiri kufikira makumi asanu ndi atatu. Mogwirizana ndi chifuno Chake chakuti munthu akhale ndi moyo pa dziko lapansi kosatha, Mulungu anam’patsa ubongo umene ukapitirizabe kuphunzira zinthu zatsopano kwamuyaya! Ha, ndi kofunika chotani nanga m’mene kulire kupitirizabe kudzaza maganizo athu ndi malingaliro “abwino!”—Afilipi 4:8, NW.
CHIFUNO CHA MULUNGU M’KULENGA MUNTHU
12. (a) Kodi n’chiani chimene chinali chifuno cha Mulungu m’kulenga munthu? (b) Mosasamala kanthu za njira zoononga za anthu, kodi dziko lapansi’li lidzasanduka chiani, ndipo liti? (Yesaya 65:17, 18)
12 Mulungu anali ndi chifuno m’kulenga munthu, ndipo chiyenera kukhala chikhumbo chathu kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno chimene’cho. Pa nthawi imene Yehova analenga anthu awiri, anawadalitsa, nawauza kuti:
“Mubulane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi, muligonjetse: mulamulire pa nsomba za m’nyanja, ndi pa mbalame za m’mlengalenga, ndi pa zamoyo zonse zakukwawa pa dziko lapansi.” (Genesis 1:28)
Komabe, kodi tikuonanji lero lino, zaka zikwi zisanu ndi chimodzi pambuyo pake? M’madera ena, dziko lapansi lakhala lodzazidwa ndi anthu, koma kwakukulu-kulu iwo samabvomereza kudalira kwao pa Mlengi wao, Yehova Mulungu, kapena’nso kum’lambira. Ndipo m’malo mwa kugonjetsa dziko lapansi, kwakukulu-kulu iwo akuliipitsa ndi kulisakaza, limodzi ndi zinyama zake zochuluka. Komabe, tingakhale othokoza kuti Mulungu walengeza chitsimikiziro chake cha “kuononga awo oononga dziko lapansi” ndi kupangitsa dziko lonse lapansi kusandulizidwa kukhala paradaiso wake waulemerero wolingaliridwa’yo pofika mapeto a ‘tsiku lake lakupuma’ lalikulu’lo.- Chibvumbulutso 11:18, NW.
13. Kodi ndi kaamba ka chiyembekezo chaulemerero chotani chimene tiyenera kukhala othokoza? (Salmo 145:11, 15, 16)
13 Ndithudi pali ziyembekezo zodabwitsa kaamba ka m’tsogolo mwa “chombo cham’mlengalenga Dziko Lapansi”! Ndi kaamba ka munthu wokhalapo! Malinga ndi chifuno chachikulu cha Mulungu, ‘tsiku lake la kupuma’ lidzatha ndi kusandulizidwa kwa dziko lapansi kukhala paradaiso, lokhalidwa ndi mtundu wa anthu wolungama umene ukulamulira miyoyo ina yonse yolengedwa ya padziko lapansi. Tingathe kuthokoza Yehova kuti analenga munthu “m’chifanizo chake,” ndi kuti amatisamalira pa dziko lapansi modabwitsa kwambiri-tsopano, ndi kupitirizabe mpaka ku nthawi yopanda malekezero.—Genesis 1:27.
[Mawu a M’munsi]
a The World Book Encyclopedia, 1973, Vol. 2, p. 459.
[Chithunzi patsamba 66]
Dziko lapansi limaposa m’mbali iri yonse chombo chiri chonse chopangidwa ndi anthu
[Chithunzi patsamba 69]
Mpata waukulu ukulekanitsa zolengedwa zaumunthu za Mulungu ndi zinyama, ukumatsimikizira “chisinthiko” kukhala chonama