Mutu 12
Kodi N’chifukwa Ninji Mulungu Walola Kupanda Chimwemwe?
1. Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kukondweretsedwa ndi kudziwa chifukwa cha Mulungu chololera kuipa? (Salmo 94:2, 3)
MBIRI iri ndi cholembedwa chochititsa mantha chonena za nkhanza ya munthu kwa munthu mnzake. Masamba ake adetsedwa ndi mwazi wa nkhondo zachipembedzo, kupha aunyinji ndi zizunzo. Kuonongedwa koopsya kwa anthu osachimwa kwatsagana ndi nkhondo ziwiri za dziko zimene Chikristu cha Dziko chinaziyambitsa ndi nkhondo zimene zatsatirapo mu Korea, Indochina ndi malo ena. Chiwawa, chipanduko ndi upandu zikupitirizabe kubuka m’maiko ambiri. Kodi n’chifukwa ninji Mulungu amalola mikhalidwe yoopsya imene’yi? Kodi n’chifukwa ninji iye sanachotse kupanda chimwemwe kale-kale? Mulungu mwini amalongosola chifukwa chake, m’Bukhu lake la “mbiri yabwino.”
2. (a) Kodi Mulungu angathe kuchotsa kuipa, ndipo kodi iye amafuna kutero? (Yoweli 1:15) (b) Kodi ndi motani m’mene Mulungu wasonyezera nzeru m’nkhani imene’yi?
2 Mulungu amene akatha kulenga chilengedwe chopanda malekezero’cho ndithudi ali ndi mphamvu ya kuchotsa kupanda chimwemwe konse. Monga ‘Mulungu wa chikondi,’ iye amasamalira’di anthu. Komabe, iye ali’nso Mulungu wa “nzeru yeni-yeni.” (1 Yohane 4:16; Miyambo 2:6, 7) Nzeru yake ikusonyezedwa m’kutenga kwake nthawi kuthetsa nkhani yofunika m’chilengedwe chonse. Ngakhale kuli kwakuti zimene’zi zatanthauza kulola kwake kupanda chimwemwe kwa kanthawi, komabe chotulukapo cholowetsamo zochuluka chidzatsimikiziritsa chimwemwe chosatha kwa zolengedwa zonse za nzeru m’chilengedwe chonse.
3. (a) Fotokozani mwa fanizo chifukwa chake nthawi ikufunika kuti nkhani’yo ithesedwe? (b) Kodi n’chifukwa ninji nthawi yofunika’yo iri yaifupi poyerekezera? (Habakuku 2:3)
3 Zimene’zi zingayerekezeredwe ndi mlandu wa wakupha anthu wochuka. Kungatenge nthawi kukambitsirana nkhani’yo, kupenda maumboni onse ndi kufika pa chiweruzo cholungama ndi chotsirizira. Pamenepo wambanda’yo angaphedwe, ndipo ena onse amene miyoyo yao ingakhale itakhala pa upandu chifukwa cha iye angathe kukhala achimwemwe kuti upandu’wo wachotsedwa. Mofananamo, nthawi-zaka zokwanira zikwi zisanu ndi chimodzi-yakhala yofunika kuthetsa nkhani yodzutsidwa ndi wakupha anthu, mdani wamkulu wa Mulungu, koma kodi nthawi imene’yi ndi yaifupi motani poyerekezera ndi chimwemwe chamuyaya chimene chiri patsogolo! Pakuti m’maso mwa Mulungu “zaka chikwi zikhala ngati dzulo, litapita.”—Salmo 90:4.
NKHANI
4. (a) Kodi n’chiani chimene chiri nkhani yaikulu? (Salmo 83:18) (b) Kodi ndi motani m’mene ulamuliro wa Mulungu unatokosedwera?
4 Kodi n’chiani chimene chiri nkhani yaikulu imene iyenera kuthetsedwa? Imalowetsamo ulamuliro wa Yehova pa zolengedwa zake. Pa nthawi ya chipanduko mu Edene, Satana anatokosa ulamuliro wa Mulungu. Osati kuti iye anali ndi mphamvu ya kuchotsa Mulungu monga Mfumu. Ai, koma iye anafunsa funso lakuti, Kodi ulamuliro wa Mulungu pa zolengedwa zake uli woyenera ndi wochititsa zabwino kopambana kwa iwo? Kodi ulamuliro umene’wo uli wolungama, ndipo kodi umafunikira chichirikizo chao? Mwa chinjoka, Satana anati kwa Hava mu Edene: “Ea! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” Pambuyo pa kutokosa ulamuliro wa Yehova mwa kusonyeza kuti Iye anali atanama, Satana anasonkhezera Hava, ndipo mwa mkazi’yo Adamu, kudzitulutsa mu ulamuliro wa Mulungu, kuti aime paokha ndi kudzisankhira chimene chiri “chabwino” ndi chimene chiri “choipa.” (Genesis 3:1-5) Chotero kunali kuyenera, chilungamo ndi kuyenera kwa ulamuliro wa Mulungu kumene kunatokosedwa.
5. (a) Kodi n’chifukwa ninji Mulungu walola kuipa? (Aroma 9:17) (b) Kodi ndi motani m’mene chiweruzo cha Mulungu chidzatumikirira kwa umuyaya wonse?
5 Mulungu anapatsa chiweruzo cha imfa opanduka oipa’wo. Koma iye anawalola kukhalabe ndi moyo kwa kanthawi, ndipo iye analola Adamu ndi Hava kubala ana opanda ungwiro. Ndithudi, iye walola kuipa kupitirizabe, mu ulamuliro wa Satana, kufikira lero lino. Ndipo kodi chifukwa ninji? Kuti atsimikizire kotheratu kuti ulamuliro wake uli wolungama kotheratu ndi kuti palibe zolengedwa zimene zingathe kusangalala ndi chimwemwe chosatha mosadalira ulamuliro wake ndi malamulo olungama. Motero iye akutsutsa Satana kukhala “wambanda,” wabodza, woneneza ndi wonyenga, ndipo akum’chotsa limodzi ndi osamvera lamulo ena. Pamenepo chiweruzo cha Mulungu chidzakhala ngati chochitika choyamba ndi kutumikira monga muyeso kwamuyaya ngati cholengedwa chiri chonse chitokosa’nso ulamuliro wa Yehova.—Yohane 8:44.
6. (a) Kodi n’chiani chimene chasonyezedwa ponena za ulamuliro wa anthu? (b) Kodi ndi chithunzi-thunzi chotani chimene ulamuliro wa anthu ukusonyeza lero lino? (Mlaliki 8:9)
6 Kodi chiweruzo chimene’chi m’khothi la m’chilengedwe chonse chinayenda bwanji? Munthu wasonyeza bwino lomwe kuti iye ali wosakhoza kulamulira bwino lomwe kunja kwa ulamuliro wa Mulungu. Kwakhala ndendende monga momwe mneneri Yeremiya akulongosolera kuti:
“Inu Yehova, ndidziwa kuti njira ya munthu siri mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Yeremiya 10:23)
Palibe nthawi ina iri yonse imene chimene’chi chakhala choonekera bwino kwambiri koposa lero lino, pamene dziko lagawidwa kukhala zigawo za Demokratiki, za Chikomyunisti ndi “Maiko Osakhala a Mbali Ziwiri’zo.” M’kati, zigawo zimene’zi ziri zogawanitsidwa ndi kusagwirizana kwina’nso. Mu ulamuliro wa anthu, chinyengo ndi mau onama zingapezedwe kuli konse. Pamene kuli kwakuti chigawo chimodzi mwa zinai za anthu zikusaukira chakudya, olamulira amaonongera ndalama zochuluka pa kugula zida zankhondo, m’zochitika zambiri ndi zida za nyuklea zokhoza kufafaniza mtundu wonse wa anthu. Olamulira ochuluka ali okhala m’bvuto la chuma kapena lina lalikulu kwambiri, ndipo kawiri-kawiri amalandidwa ulamuliro mwadzidzidzi. Zigwirizano ziri zonse zopangidwa ndi atsogoleri a ndale za dziko zimayenerana ndi kulongosola kwa Salmo 127:1:
“Akapanda kumanga nyumba Yehova, akuimanga agwiritsa ntchito chabe.”
7. (a) Kodi n’chifukwa ninji ulamuliro wa Mulungu uli wapamwamba ku ulamuliro wa anthu? (Salmo 45:6) Kodi n’chiani chimene Mulungu tsopano adzachita nawo ulamuliro wa anthu, ndipo chifukwa ninji? (Nahumu 1:9)
7 Pali zifukwa zazikulu chifukwa chake ulamuliro wa Yehova uli wapamwamba kopambana poyerekezera ndi ulamuliro wa anthu. Ulamuliro wa Mulungu wazikidwa pa chikondi, chimene chiri “chomangira changwiro cha chigwirizano.” (Akolose 3:14, NW) Ulamuliro wa anthu kawiri-kawiri umaipa mpaka kukhala wadyera ndi waumbombo. Ulamuliro wa Mulungu uli ndi mphamvu ya kugwirizanitsa “pamodzi zinthu zonse.” (Aefeso 1:10, NW) Ulamuliro wa anthu umakulitsa kugwanika, udani ndi nkhondo. Ulamuliro wa Mulungu ukuchitidwa “mwa njira ya chiweruzo cholungama ndi . . . chilungamo.” (Yesaya 9:7, NW) Ulamuliro wa anthu kawiri-kawiri umakhala wotsendereza osauka ndi wa tsankho wokonda olemera. Watsimikizira poyesedwa kukhala wolephera momvetsa chisoni, ndipo tsopano Mulungu watsala pang’ono kuuchotsa m’malo mwakuti achite mokwanira ulamuliro wake wolungama pa dziko lonse lapansi kachi-wiri’nso.
UMPHUMPHU WA MUNTHU
8. Kodi ndi chitokoso chotani chimene Satana anadzutsa ponena za Yobu?
8 Komabe, nkhani yofanana’yo inadzutsidwa’nso m’munda wa Edene. Ndiyo iyi: Popeza kuti anthu oyamba anapanduka, kodi Mulungu angathe kuika munthu ali yense pa dziko lapansi amene adzakhalabe wokhulupirika kwa iye poyesedwa? Bukhu la Baibulo la Yobu limaosnyeza kuti pali nkhani yotero’yo. Machaputala ake awiri oyambirira amalongosola chimene chinachitika m’mabwalo a kumwamba zaka zokwanira 3,500 kapena kuposa zapita’zo. Kumene’ko, pamene ana amuna a Mulungu anasonkhana pamaso pa Yehova, Satana naye’nso anaonekera, ndipo Yehova analankhula kuti:
“Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? pakuti palibe wina wonga iye m’dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zopa. Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kodi Yobu aopa Mulungu pachabe? Kodi simunam’chinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pom’zinga ponse? ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoweta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kum’khudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”—Yobu 1:8-11.
9. Kodi ndi mbiri yotani imene Yobu anapanga, ndipo kodi ndi motani m’mene iye anafupidwira? (Yobu 42:12-16; Yakobo 5:11)
9 Yehova analola chiyeso chimene’chi. Yobu anatayikiridwa zifuyo zake, ndi ana ake mu imfa, koma sanatukwane Mulungu, kapena kum’pandukira. Pambuyo pake, pamene Satana anam’kantha ndi nthenda yonyansa, mkazi wake motaya mtima potsirizira pake anati: “Chitira Mulungu mwano, ufe.” Koma iye anasungabe zolimba umphumphu wake kwa Mulungu. Otonthoza atatu, onyenga pamenepo anaonjezera kubvutika kwake, koma Yobu analengeza kuti:
“Mpaka kufa ine sinditaya ungwiro wanga.” (Yobu 2:9, 10; 27:5)
Pambuyo pake, Yobu anafupidwa kwambiri chifukwa cha kusunga kwake umphumphu.
10. Kodi ndi mbiri yotani imene osunga umphumphu ena anapanga? (Ahebri 12:1)
10 Cholembedwa cha Baibulo, kuphatikizapo Ahebri chaputala 11, chimasonyeza kuti anthu ena ambiri asankha mopanda dyera kuchirikiza ulamuliro wa Yehova, mosasamala kanthu za mtundu uli wonse wa chiukiro chauchiwanda chimene Satana angapange pa umphumphu wao. Mzera wautali wa osunga umphumphu ukupitirizabe mpaka lero.
11. (a) Kodi ndi zitsanzo za osunga umphumphu zotani zimene ziripo lero lino ? (Miyambo 27:11) (b) Kodi ndi motani m’mene Mulungu adzadziwikitsira ulamuliro wake, ndipo kwa utali wotani? (Ezekieli 36:23)
11 Monga chitanzo, m’kati mwa ulamuliro wa Hitler m’Jeremani, mboni Zachikristu za Yehova zinakana kuchitira suluti mbendera ya Nazi ndi kulandira wolamulira wotsendereza ufulu’yo kukhala mpulumutsi wao. Mazana ambiri anatsimikizira umphumphu wao mwa kukhetsedwa kwa mwazi wao. Mmodzi wa amene’wa, pa usiku wa kuphedwa kwake, anatumiza uthenga wotsatirapo, wu, umene uli chitsanzo, kwa mkazi wake wokondedwa:
“Pamene kalata iyi ifika kwa iwe moyo wanga udzakhala utatsirizidwa. Tikudziwa kuti ululu wachotsedwa ku imfa ndipo chipambano chapezedwa pa manda . . . Nthawi idzafika apemene dzina la Mulungu Wamphamvuyonse lidzadziwikitsidwa ndipo anthu adzaliona. Pamene iwo amafunsa lero lino chifukwa chake iye sanachite zimene’zi kufikira tsopano, pamenepo ife timadziwa kuti chiri chifukwa chakuti mwa njira imene’yo mphamvu Yake idzasonyezedwa mwamphamvu kwambiri . . . Tsopano ndafika pa mapeto, ndipo ndikupemphera kuti nawe’nso upirire . . . chotero ndikuyang’ana kachiwiri’nso m’maso ako oyera ndi onyezimira, ndi kuchotsa chisoni chotsirizira mu mtima wako; ndipo, mosasamala kanthu za ululu, tukula mutu wako ndi kusangalala, osati ndi imfa, koma ndi moyo umene Mulungu adzapatsa awo amene amam’konda.”
Posachedwapa, Yehova adzadziwikitsa ulamuliro wake, ndi awo onse amene auchirikiza, mosonyeza mphamvu yotsutsana ndi adani ake imene idzakweza dzina lake “m’dziko lonse lapansi.”—Eksodo 9:16.
WOSUNGA UMPHUMPHU WAPADERA
12. Kodi ndani amene anali woyenera kopambana kutsimikizira mbali ya Yehova ya nkhani’yo, ndipo kodi anakhala munthu motani? (Yohane 1:14)
12 Komabe, nkhani ya umphumphu imene’yi imalowetsamo osati anthu tokhafe. Ngakhale mngelo wa kumwamba anapanduka nasanduka Satana, ndipo ‘ana amuna a Mulungu’ ena pambuyo pake anagwirizana naye m’chipanduko. (Genesis 6:4, 5) Motero nkhani’yo iri ya m’chilengedwe chonse. Palibe wina ali yense amene angatsimikizire bwino kwambiri ubwino wa mbali ya Yehova ya nkhani’yo koposa munthu wapamwamba kopambana m’chilengedwe chonse wachiwiri kwa Yehova—“mmisiri” amene anam’thandiza m’kulenga! Mwana wakumwamba amene’yu mokondwa anabvomereza kusamutsira kwa Mulungu moyo wake m’mimba ya namwali Wachiisrayeli, Mariya, kotero kuti anabadwa monga munthu pa dziko lapansi pano pamene Satana anadzutsa nkhani’yo.
13. Kodi ndi motani m’mene Yesu anayankhira chitokoso cha Satana? (1 Petro 2:21-23)
13 Atakhala wachikulire, Mwana wa Mulungu Yesu anabatizidwa mosonyeza kudzionetsera kwake kudzachita ntchito yapadera imene Mulungu anam’patsa. Satana posapita nthawi anayamba kutokosa! Iye ananena kuti akapatsa Yesu ulamuliro, umene Satana pa nthawi’yo anali nao, pa maufumu onse a anthu pa dziko lapansi, malinga ngati angachite kachitidwe ka kulambira Satana ndipo motero kuswa umphumphu kwa Yehova. Yesu anayankha Satana kuti:
“Choka Satana, pakuti kwalembedwa, Ambuye Mulungu wako udzam’gwadira, ndipo Iye yekha udzam’lambira.”—Mateyu 4:10.
14. Kodi n’chifukwa ninji Yesu akanena kuti Satana analibe ‘ulamuliro pa iye’?
14 Atalephera kupatutsa Yesu pa kutsatira lamulo lolungama la Yehova, Satana kenako anaika chitsenderezo chachikulu kwambiri pa iye kupyolera mwa atsogoleri achipembedzo a m’nthawi yake. Iwo anam’zunza mwankhanza ndipo potsirizira pake anachititsa kuti aphedwere pa mtengo wozunzirapo, koma iwo analephera kum’pambutsa pa njira ya umphumphu wangwiro ndi kumvera ulamuliro wa Mulungu. Pa tsiku la imfa yake, Yesu ponena za Satana anatha kunena kuti: “Palibe ulamuliro pa ine.” (Yohane 14:30, NW) Pa tsiku lachitatu pambuyo pake, Yehova anafupa Mwana Wake wokhulupirika’yo mwa kumuukitsa mu mzimu ndipo pambuyo pake kum’kwezera ku “dzanja lamanja” la iye mwini la chiyanjo kumwamba.—Machitidwe 2:32, 33.
15. Kodi ndi motani m’mene Yesu analimbikitsira ophunzira ake, ndipo kodi iwo atsimikizira kukhala chiani? (Afilipi 2:5, 8, 9)
15 Kwa ophunzira ake okhulupirika wosunga umphumphu amene’yu analengeza kuti:
“M’dziko inu mukukhala ndi sautso, koma limbani mtima! ndagonjetsa dziko.” (Yohane 16:33, NW)
Atumwi a Yesu ndi Akristu ambiri a pambuyo pao nawo’nso atsimikizira kukhala osunga umphumphu, kufikira imfa.
OLAMULIRA OYESEDWA NDI OKHULUPIRIKA
16. Kodi n’chifukwa ninji anthu angakhale ndi chidaliro mwa olamulira atsopano a dziko lapansi? (Yesaya 32:1)
16 Chifuno china chofunika chachitidwa mwa kulola kwa Mulungu ophunzira a Yesu kupirira ziyeso ndi zizunzo. Monga momwe’di Yesu iye mwini “anaphunzira kumvera ndi izi adamva kuwawa nazo,” chotero anamenewa’nso, aphunzitsidwa ndi kuumbidwa mwa kubvutika kukulitsa mikhalidwe yamtengo wapatali ya kukhulupirika ku ulamuliro wa Mulungu. Baibulo limasonyeza kuti Mulungu akusankha “kagulu ka nkhosa” ka ophunzira a Yesu amene’wa, “zikwi zana mphambu makumi anai kudza anai” kukhala ndi phande mu “chiukiriro choyamba” chauzimu, ndi kulamulira pamodzi ndi Kristu mu ufumu wake wa zaka chikwi pa anthu. Ha, ulamuliro wa Ufumu wakumwamba umene’wo udzakhala wosiyana chotani nanga ndi ulamuliro wa anthu woipa, ndi wosasunga malamulo a makhalidwe abwino wa lero lino! Ndipo’nso, olamulira ooneka a m’tsogolo a dziko lonse lapansi akaphatikizamo amuna onga ngati Yobu ndi unyinji wa ena osunga umphumphu, ponse pawiri a m’nthawi zakale ndi a m’zaka zino za zana la makumi awiri kumene ife tsopano tikukhala! Ha, ndi chidaliro chotani nanga chimene anthu adzakhala nacho m’boma limene’lo!—Ahebri 5:8; Luka 12:32; Chibvumbulutso 14:1-5; 20:6.
17. Kodi ndi chifukwa ninji kuleza mtima kwa Mulungu kwakhala kopindulitsa kwa ife? (2 Petro 3:9, 15)
17 Tiyenera kukhala okondwa kuti Yehova wakhala “woleza mtima” m’kulekerera kuononga oipa, pakuti kwapatsa ambiri mwai wa kuimira ku mbali ya Yehova ya nkhani yaikulu’yo. (Aroma 2:4, NW) Nanu’nso mukhaletu odalitsidwa m’kuchirikiza ulamuliro wake!
18. (a) Kodi ndi motani m’mene Mulungu adzaperekera chiweruzo? (Yeremiya 25:31) (b) Kodi dziko lapansi pa nthawi imene’yo lidzakhala malo a mtundu wotani? (Yesaya 11:9)
18 Nkhani yokhala kwa nthawi yaitali’yo yolowetsamo ulamuliro wa Mulungu ndi umphumphu wa munthu yatsala pang’ono kuthetsedwa kotheratu, ndi mokwanira m’chiyanjo cha Yehova. Posachedwapa, Yehova adzapereka ‘chiweruzo chake cha m’khothi’ m’kuchotsa pa dziko lapansi Satana ndi ena onse amene amatsutsa ulamuliro wa Mulungu. Pa nthawi imene’yo dziko lapansi lidzakhala malo okongola kwambiri kumene “zonse zakupuma zidzalemekeza Ya,” Yehova. (Salmo 150:6, NW) Koma kuti apitirizebe kulemekeza Mulungu, munthu adzafunikira kupitirizabe kukhala ndi moyo. Kodi zimene’zi zingatheke motani? Mutu wotsatirapo’wo udzafotokoza.
[Chithunzi patsamba 107]
Mlandu wa pa khothi umatenga nthawi. Chimodzimodzi’nso, nkhani yaikulu ya ulamuliro iyenera kupendedwa mokwanira
[Chithunzi patsamba 110]
Yobu, atayesedwa mobvutika, anasunga umphumphu
[Chithunzi patsamba 113]
Yesu Kristu, wosunga umphumphu wamkulu kopambana onse
[Chithunzi patsamba 115]
Ufumu wa zaka chikwi wa Kristu udzakweza ulamuliro wolungama wa Yehova ndi kudalitsa anthu onse