Mutu 14
Kulambira Mulungu Wamoyo
1. (a) Kodi Mulungu amabvomereza kulambira kwa mtundu wotani? (b) Kodi n’chifukwa ninji sikuli kosungika kutsatira kagulu kali konse kachipembedzo? (Mateyu 15:14) (c) Kodi kulambira koona kudzakutsogolerani ku njira yotani? (Afilipi 4:8)
KULAMBIRA koona n’kolimbikitsa. Kumasonyeza kukonda Mulungu ndi mnansi, ndipo kumapewa kuipa kwa dziko. Mng’ono wa Yesu wa atate wina Yakobo akukulongosola motere:
“Mapembedzedwe oyera ndi osadetsa pamaso pa Mulungu ndi Atate ndiwo: kucheza ndi ana amasiye ndi akazi amasiye m’chisautso chao, ndi kudzisungira mwini wosachitidwa mawanga ndi dziko lapansi.” (Yakobo1:27)
Siri nkhani ya kutsatira kwanu kagulu kachipembedzo kali konse, monga ngati kutenga kanjira kali konse ka tinjira tambiri tokwera pa phiri. Tinjira totero’to tingakhale toopsya ndipo tingakusocheretseni, pakuti tsopano pali timagulu tambiri tachipembedzo toombana, tokhala ndi atsogoleri amene ali olakwa kapena amene ali ndi zolinga zadyera. Mosemphana ndi zimene’zo, kulambira koona kudzakutsogozani mogwirizana ndi “nzeru yochokera kumwamba,” imene “iyamba kukhala yoyera, nikhala’nso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.”—Yakobo 3:17.
2. (a) Kodi n’chifukwa ninji ena a makolo athu anasintha chipembedzo chao? (b) Chotero kodi n’chiani chimene chiri chanzeru kwa ife kuchita lero lino? (1 Atesalonika 5:20, 21)
2 Anthu ena amalungamitsa kukhala kwao achipembedzo china, mwa kunena kuti, ‘Ife ndi makolo athu talambira mwa njira imene’yi kwa mibadwo-mibadwo.’ Koma mbiri imasonyeza kuti ambiri a makolo amene’wo anali ofunitsitsa kusintha, ngati analingalira kukhala kopindulitsa. Mwa chitsanzo, m’Japan ali yense anatsatira kulambira kwa Shinto kufikira m’zaka za zana lachisanu ndi chinai. Pamenepo anthu ambiri anakopedwera ku Chibuda ndipo analandira chipembedzo chimene’cho. Lero lino Ajapana ambiri adzakuuzani kuti iwo ndi Abuda. Chimene’cho chiri chifukwa chakuti makolo ao sanakhale ndi mkhalidwe wakuti, ‘Chipembedzo cha makolo anga chiri chabwino kwambiri kwa ine.’ Iwo anali ofunitsitsa kumvetsera munthu wina’nso. Tsopano, anthu ambiri akumvetsera Baibulo.
3. Kodi ndi lingaliro lolakwa lotani imene Yesu analiongolera ponena za kulambira? (Yesaya 46:5-7)
3 Kodi Baibulo limayamikira mtundu wotani wa kulambira? Pamene Yesu anali pa dziko lapansi pano, anthu ambiri analingalira kuti dzoma ndi mwambo zinali zofunika m’kulambira. Ena analambira m’phiri lakuti-lakuti, ndipo ena pa kachisi m’Yerusalemu. Ponena za iwo Yesu anati:
“Ikudza nthawi, imene simudzalambira Atate kapena m’phiri iri, kapena m’Yerusalemu. Inu mulambira chimene simuchidziwa; . . . ikudza nthawi, ndipo tsopano iripo, imene olambira oona adzalambira Atate mumzimu ndi m’choonadi; pakuti Atate afuna otere akhale olambira ake. Mulungu ndiye mzimu; ndipo om’lambira Iye ayenera kum’lambira mu mzimu ndi m’choonadi.”—Yohane 4:21-24.
4. Kodi n’chiani chimene chikutanthauzidwa ndi kulambira Mulungu “mu mzimu ndi m’choonadi”? (Luka 10:27)
4 Kodi Yesu anatanthauzanji ndi zimene’zi? Iye anatanthauza kuti kulambira kwamwambo pa tiakachisi kapena chalichi, mwa madzoma odzionetsera, sindiko kumene Mulungu amafuna. Yehova Mulungu ndiye “Mzimu.” (2 Akorinto 3:18) Ndiko kulambira kwathu kokhala ndi mzimu, kosonyezedwa kuchokera m’mitima yoyamikira, kumene kuli kanthu kwa iye kuli konse. Monga momwe’di Mulungu amatikondera, ndi kukusonyeza ndi makonzedwe onse abwino kwambiri amene iye watipangira, chotero tingathe kum’lambira “mu mzimu” mwa kusonyeza chikondi chathu kwa iye, kudza’nso kwa anansi athu. Tingathe kum’lambira ‘ndi choonadi’ mwa kuphunzira kuchokera m’Baibulo chimene chiri chifuno chake ponena za ife, ndiyeno n’kumachita chifuniro cha Mulungu chimene’cho. Kulambira kwathu ‘ndi choonadi’ kumafunikira’nso kuti tikane mwamphamvu zinyengo zonse zachipembedzo.
“TULUKANI M’MENEMO, ANTHU ANGA”
5. (a) Kodi ndi mtundu wotani wa kulambira umene Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kuupewa? (Yeremiya 10:3-5) (b) Kodi ndi motani m’mene Chibvumbulutso chimalongosolera ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga, ndipo chifukwa ninji? (Yakobo 4:4)
5 Kuti kulambira kwathu kwauzimu kukhale kolandirika kwa Yehova, tiyenera kusiya kotheratu kulambira konse konyenga. Baibulo limasonyeza zimene’zi bwino lomwe m’ndime zingapo:
“Okondedwa anga, thawani kupembedza mafano.” “Simungathe kumwera chikho cha Ambuye, ndi chikho cha ziwanda.” “Tiana, dzisungireni nokha kupewa mafano.” (1 Akorinto 10:14, 21; 1 Yohane 5:21)
Ku zimene’zi, Chibvumbulutso chikuonjezerako lamulo lamphamvu lakuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga.” Kutuluka mwa yani? Mu “Babulo Wamkulu,” amai wa achigololo ndi zinthu zonyansa za dziko lapansi”-ufumu wa dziko wa chipembedzo chonyenga, Chikatolika, Chiprotestanti ndi zosakhala Zachikristu, zonse zimene zimakana choonadi cha Baibulo! Monga momwe taonera kale, chigololo chake chauzimu chiri ndi kupereka chitonthozo ndi chichirikizo cha olamulira ndi a ndale za dziko a dziko. Iye walinganiza’di zipani zake za ndale za dziko zolamulidwa ndi chpembedzo. Limodzi ndi ‘mwana wake wamkazi’ wa timagulu ta zipembedzo iye wapanga mbiri ya kuchirikiza olamulira otsendereza ndi olamulira ena a ndale za dziko m’nkhondo zao ndi malinganizidwe a chiwawa kapena chitsenderezo. Iye waonekera kukhala wokongola kunja, m’kunene kwake kukhala “akuyeretsa” ndale za dziko, m’kupatsa olamulira kaonekedwe ka chiyero ndi m’kudalitsa zida zao za nkhondo. Koma Kumwamba kukutiuza mofulumira kuti: ‘Patukani kwa iye!’ Pakuti maulamuliro a ndale za dziko—“okondana” nawo ake akale- atsala pang’ono kumuononga!—Chibvumbulutso 17:3-5, 16; 18:4, NW.
6. Kodi mungathe kuchula machita-chita ena ofala achipembedzo amene achokera ku Babulo wakale?
6 Chotero, tifunikira kudzilekanitsa ndi malinganizidwe, ziphunzitso ndi machita-chita onse a chipembedzo chonyenga. Kodi ndi anti amene ali ena a machitachita amene’wa? Kadinala Wachibritishi Newman akulongosola ena a iwo m’bukhu lake lakuti Essay on the Development of Christian Doctrine, lofalitsidwa mu 1878:
“Kugwiritsiridwa ntchito kwa akachisi, ndipo amene’wa operekedwa kwa oyera akuti-akuti, ndi okometseredwa pa nthawi zina ndi nthambi za mitengo, lubani, nyale, ndi makandulo; nsembe za chowinda pochira matenda; madzi oyera; malo othawirako apandu; masiku oyera ndi nyengo, kugwiritsiridwa ntchito kwa makalendala [achipembedzo], magulu a anthu oyenda nayimba, kudalitsa minda; zobvala za ansembe, kumeta mpala pamutu, . . . mafano a pambuyo pake, mwina mwake nyimbo yachimpembedzo.”
M’nkhani yake, kadinala’yo akunena za ‘kuyeretsa’ kwa Chalichi Chachikatolika machita-chita amene’wa mwa kuwalandira kuchokera ku zipembedzo zosakhala Zachikristu, ngakhale kuli kwakuti, m’mau ake, zimene’zi ziri “zipangizo ndi zoonjezera za kulambira ziwanda.”
7. (a) Kodi ndi mapwando otani a chipembedzo amene Mulungu samawabvomereza? (b) Kodi Krisimasi amakumbukiridwa pa deti la kubadwa kwa Yesu? (c) Malinga ndi kunena kwa Encyclopedia Americana, kodi miyambo ya Krisimasi inayambira kuti? (d) Kodi ndi lingaliro lotani limene olambira oona amatenga kulinga ku Krisimasi, ndipo chifukwa ninji? (2 Akorinto 6:17) (3) Kodi ndi chochitika chimodzi chotani chimene Kristu analamula otsatira ake kuchisunga? (Luka 22:19, 20)
7 Komabe, machita-chita otero’wo sali obvomerezedwa ndi Mulungu wa choonadi. Ndipo’nso iye samabvomereza mapwando ozikidwa pa chipembedzo Chachibabulo. Monga chitsanzo, pali phwando la chaka ndi chaka la Krisimasi limene limayerekezera kukhala likukumbukira kubadwa kwa Yesu, ngakhale kuli kwakuti liri ndi ziyambi zake zakale m’Babulo wakale. Baibulo limasonyeza kuti yesu anabadwa kweni-kweni pafupi-fupi pa October 1, 2 B.C.E. Koma phwando la Krisimasi, pa December 25, linangoyamba mu zaka za zana lachisanu C.E., pamene Chikristu cha Dziko chopanduka cinagwirizanitsa dzina’lo “Kristu” ndi zisangalalo zaphokoso za pa kutha kwa chaka za mitundu. Encyclopedia Americana, bukhu la 1959, Voliyamu 6, tsamba 622 imati:
“Miyambo yochuluka imene tsopano yagwirizanitsidwa ndi Krisimasi poyambirira sinali miyambo ya Krisimasi koma m’malo mwake inali miyambo ya Chikristu chisanakhale ndi yosakhala Yachikristu yotengedwa ndi chalichi Chachikristu. Saturnalia, mphwando Lachiroma lokumbukiridwa pakati pa December, anapereka chitsanzo cha miyambo yambiri ya kusangalala kwa pa Krisimasi. Mwa chitsanzo, kuchokera ku phwando limene’li kunatengedwa kudya zakudya zochuluka, kupatsa mphatso, ndi kuyatsa makandulo.”
M’mbali zina za dziko lapansi, Abuda osakhala Achikristu, Ayuda ndi ena amakumbukira “Krisimasi” ndi chikondwerero chachikulukwambiri mofanana ndi Akatolika ndi Aprotstanti. Kawiri-kawiri kumagwirizanitsidwa ndi malonda ndi umbombo. Sikuli Kwachikristu. Palibe pali ponse pamene Baibulo limachirikiza kuchita phwando la tsiku la kubadwa la Yesu kapena la wina ali yense, koma chimene Yesu analamula chinali chakuti otsatira ake chaka ndi chaka akumbukire imfa yake monga “chikumbukiro.” Chimene’chi chinali chifukwa chakuti imfa yake inali yofunika kaamba ka chipulumutso cha mtundu wa anthu.—1 Akorinto 11:23-26.
8. Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kwa ife kuti tipatuke ku chipembedzo chonyenga? (Yeremiya 51:6)
8 Mulungu wamoyo wa choonadi samabvomereza machita-chita a kulambira mafano ndi “ubwenzi” ndi ndale za dziko wa ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Ndithudi, zimene’zi zimaudziwikita kukhala “Babulo Wamkulu,” ponena za amene Chibvumbulutso 18:21 chimatiuza kuti:
“Ndipo mngelo wolimba ananyamula mwala, ngati mphero yaikulu, naiponya m’nyanja, nanena, Chotero Babulo, mudzi waukulu.”
Ngati titi tipewe ‘kukhala ndi phande limodzi naye m’machimo ake,’ ndipo m’chionongeko chake, n’kofunika kwambiri kuti tidzilekanitse kotheratu ndi chipembedzo chonyenga!—Chibvumtulutso 18:2-4
KULAMBIRA KUMENE MULUNGU AMAKUBVOMEREZA
9. Kodi n’chifukwa ninji olambira oona ayenera kusonkhana pamodzi? (Aefeso 4:15, 16)
9 Mtumwi Paulo akulongosola chimene olambira oona a Mulungu ayenera kukhala akuchita lero lino, m’mau awa:
“Tigwiritse chibvomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjeza’yo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muoma tsiku lirikuyandika.” (Ahebri 10:23-25)
Chotero, pamene tsiku’lo likuyandikira mofulumira kwmabiri lakuti Mulungu aononge Babulo Wamkulu ndi magulu ena onse osalungama, ndi kubwezeretsa pa dziko lapansi’li paradaiso waulemerero, awo amene amam’konda amasonkhana pamodzi, m’malo mwakuti aphunzire Mau a Mulungu ndi kulimbikitsana.
10. Kodi ndi motani m’mene umunthu wathu ukulowetsedweramo m’kulambira koona? (Akolose 3:9, 10, 12-14)
10 Komabe, kulambira koona kumalowetsamo zochuluka koposa kusonkhana ndi ena amene amakonda Mulungu. M’malo mwakuti tikhale olandirika kwa Mulungu, tiyenera kupatuka, osati kokha ku chipembedzo chonyenga, koma’nso ku njira yoipa ya dziko. Mtumwi Paulo akutilangiza kubvula “umunthu wakale,” limodzi ndi khalidwe lake losadziletsa, uchisi ndi umbombo. Ndipo’nso, iye akuti:
“Muyenera kupangidwa kukhala atsopano mwa mphamvu yosonkhezera maganizo anu, ndipo muyenera kubvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu m’chilungamo cheni-cheni ndi kukhulupirika.” (Aefeso 4:19-24, NW)
Chifukwa cha chimene’cho mkhalidwe wathu uyenera kukhala woyera mwamakhalidwe ndi wolimbikitsa mwauzimu kwa awo otizinga. Mokhulupirika kwa Mulungu, tiyenera kum’landira monga wolamulira wa miyoyo yathu.
11. Kodi ndi chitsanzo china chotani cha kulambira koona chimene Yesu anapereka? (Luka 8:1)
11 Yesu iye mwini anapereka chitsanzo cha kulambira koona m’njira ina yofunika. Mwamsanga atangotha kuyesedwa ndi Mdierekezi, iye anayamba ntchito yofotokozedwa pa Mateyu 4:17.
“Kuyambira pamenepo Yesu anayamba kulalikira, ndi kunena, Tembenukani mitima, pakuti Ufumu wa Kumwamba wayandikira.”
Zaka zina zitatu pambuyo pake, pa kuweruzidwa kwake pamaso pa Pilato, Yesu anatsimikizira kuti kuchitira kwake umboni choonadi chonena za ufumu wa Mulungu kunakhala mbali yofunika ya kulambira kwake pamene anali pa dziko lapansi. Iye anati:
“Ndinadzera ichi kudza ku dziko lapansi, kuti ndikachite umboni ndi choonadi. Yense wakukhala mwa choonadi amva mau anga.” (Yohane 18:37)
Kodi inu mwamvetsera mau ake? Pamenepo, inu’nso, mungasangalale ndi mwai wa kuchitira umboni choonadi chonena za ufumu wa Mulungu monga momwe anachitira Yesu.
12. Kodi ndi pemphero lachitsanzo lotani limene Yesu anatsiyira? (Yohane 14:13, 14; 15:16)
12 Mbali ina yofunika ya kulambira koona ndiyo pemphero, limene liyenera kuperekedwa kwa Yehova kupyolera m’dzina la Yesu, amene nsembe yake yoombola inatitsegulira njira yofikira kwa Mulungu. Baibulo limatsutsa pemphero lamwambo ndi lobwereza-bwereza. Yesu iye mwini anati:
“Popemphera musabwereze-bwereze chabe iai, monga amachita anthu akunja, chifukwa ayesa kuti adzamvedwa ndi kulankhula-lankhula kwao. Chifukwa chake inu musafanane nao: pakuti Atate wanu adziwa zomwe muzisowa, inu musanayambe kupempha Iye. Chifukwa chake pempherani inu chomwechi.”
Pamenepo Yesu anapereka pemphero lachitsanzo, osati kuti libwerezedwe-bwerezedwe monga mwambo limodzi ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa kolona kapena fano, koma kuti litumikire monga chitsogozo kwa ife. Iye ananena kuti choyamba ife moyenerera tikupemphera kuti dzina la Atate wathu wakumwamba, Yehova, liyeretsedwe, kuti ufumu wake udze ndi kuti chifuniro chake chichitidwe pa dziko lapansi monga momwe kuliri kumwamba. Kachiwiri, tingathe kupempha Mulungu kutipatsa zosowa zathu za tsiku ndi tsiku, kutikhulukira zolakwa zathu zauchimo, ndi kutithandiza kusunga umphumphu mosasamala kanthu za “woipa’yo,” Satana. (Mateyu 6:5-13) Mapemphero onse, kaya operekedwa mwam’tseri, m’banja lathu kapena mu msonkhano wa mpingo, liyenera kuperekedwa, osati mwa njira yamwambo yochita kulowezedwa, koma moona mtima lochokera mu mtima. Mapemphero athu ayenera kukhala opanda kotheratu machita-chita amwambo a chipembedzo Chachibabulo. ‘Koma kodi kukhulupirira malaulo n’kobvulaza?’ mungafunse motero. Tiyeni tione.
[Chithunzi patsamba 125]
Osati akachisi ndi tiakachisi, koma kulambira kokhala ndi mzimu ndiko kumene kuli kanthu kwa Mulungu
[Chithunzi patsamba 128]
Krisimasi si Wachikristu
[Chithunzi patsamba 131]
Olambira Yehova amasonkhana kudzaphunzira Mau a Mulungu ndi kuuza ena mbiri yabwino