Mutu 15
Kukhulupirira Malaulo Kungatsogolere ku Kupanda Chimwemwe
1. Kodi ndi liti pamene machita-chita oonekera ngati osabvulaza amakhala aupandu? (Yohane 8:31, 32)
KODI n’kopanda upandu kutsatira kukhulupirira malaulo? Anthu ena amaganiza choncho. Mwa chitsanzo, lingalirani, “milungu ya mwai isanu ndi iwiri: yooneka kukhala yosabvulaza ya miyambo ya Ajapana- yoitanitsidwa zaka mazana atatu zapita’zo kuchokera ku India. Imene’yi imanenedwa kukhala ikuimira maubwino asanu ndi awiri: moyo wautali, mwai, kuchuka, kunena zoona, ubwenzi, ulemu ndi ku khulukira. Ena a “maubwino” amene’wa angakhale abwino kwambiri mwa iwo okha, koma pamene iwo alowetsedwa m’mafano, ku amene anthu amayang’ana kaamba ka “mwai,” iwo amalowa m’chigawo cha malaulo.
2. Kodi ndi machita-chita okhulupirira malaulo otani amene mwawaona kwanu’ko, ndipo kodi amene’wa akhala opindulitsa?
2 Anthu okhulupirira malaulo pa dziko lonse amakhala ndi zitumwa “za mwai” zochuluka. M’maiko Achikatolika, a paulendo ena amakhalabe ndi mendulo zao za Christopher Woyera, ndipo Kum’mawa anthu ambiri amatenga “njirisi” zimene ziri ndi dzina la kachisi, kapena ulusi wa thonje wa “mwai” wozengenezedwa pa mkono. M’maiko a Kumadzulo, anthu ambiri amapewa “13 watsoka,” pamene m’Japan anthu okhulupirira malaulo amanyansidwa ndi “4,” chifukwa chakuti amachulidwa mofanana ndi “imfa.” M’maiko ambiri, malaulo a m’dzikomo amakhala ndi chiyambukiro champhamvu pa miyoyo ya anthu.
3. Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kuzindikira lingaliro la Yehova? (Mateyu 4:10)
3 Kodi ndi motani m’mene Mulungu wamoyo, Yehova, amaonera kukhulupirira malaulo kotero’ko? Ngati tikufuna kukhala achimwemwe kweni-kweni, kukakhala kotipindulitsa kukhala ndi lingaliro lofanana ndi limene iye ali nalo. Pamene Aisrayeli anagwa pa kulambira koyera kwa Yehova nalowa m’machitachita a kukhulupirira malaulo a anthu owazinga, mneneri wa Mulungu anawauza kuti:
“Inu amene mwasiya Yehova, amene mwaiwala phiri langa lopatulika, ndi kukonzera mlungu wamwai gome, ndi kudzazira mlungu waimfa zikho za vinyo wosanganiza; ndidzasankhiratu inu kulupanga.” (Yesaya 65:11, 12)
Awo amene analemekeza “mulungu wamwai” anaonongedwa!
4. Kodi n’chifukwa ninji Yehova mwamphamvu amatsutsa kukhulupirira malaulo? (Machitidwe 16:16-18; Deuteronomo 6:5, 14)
4 Kodi n’chifukwa ninji Yehova amatsutsa kwambiri machita-chita a kukhulupirira malaulo? Chiri chifukwa chakuti amachokera kwa Satana Mdierekezi ndi ziwanda zake, amene amagwiritsira ntchito zimene’zi kupatutsa ndi kuchititsa anthu kutalikirana ndi kulambira Mulungu “ndi mzimu ndi m’choonadi.” Ngati Satana akatha kuchititsa anthu kukhulupirira mu zitumwa “zamwai” kuchita ulauli ndi kukhulupirira malaulo kofala, iye akawasungabe m’manja mwake, kuwachititsa kusaona “mbiri yabwino” imene imachokera kwa Mulungu woona ndi wamoyo. Ponena za zimene’zi, Paulo anati:
“Ngati’nso Uthenga Wabwino wathu uphimbika, uphimbika mwa iwo akutayika; mwa amene mulungu wa nthawi yino ya pansi pano unachititsa khungu maganiza ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Kristu, amene ali chithunzi-thunzi cha Mulungu, chisawawalire.” (2 Akorinto 4:3, 4)
Satana akakonda kuchititsa anthu onse kutsatira kukhulupirira malaulo kwakhungu, m’malo mwa kupanga zosankha zoyenera zozikidwa pa “mbiri yabwino” ya m’Baibulo.
CHITETEZO KU CHIUKIRO CHA ZIWANDA
5. Kodi ndi motani m’mene tingapezere chitetezo ku mizimu yoipa?
5 Mu ina ya makalata ake, Paulo akumveketsa bwino lomwe kuti tiyenera kuima nji “motsutsana ndi makamu a mizimu yoipa,” ndi kuti tingathe kuchita zimene’zi mwa kubvala “zobvala zonse za zida za nkhondo zochokera kwa Mulungu,” zida za nkhondo zauzimu zimene ziri zosiyana kwambiri ndi zitumwa “zamwai” kapena machita-chita a kulambira mafano. Iye akutiuza kuti:
“Chifukwa chake, chirimikani, mutadzimangira m’chuuno mwanu ndi choonadi, ndipo mutakhala ndi chapachifuwa cha chilungamo, ndi kubveka mapazi anu kukonzekera mbiri yabwino ya mtendere. Koposa zinthu zonse, tengani chikopa chachikulu cha chikhulupiriro, chimene mudzakhala okhoza kuzimitsa nacho mibvi yonse yoyaka moto ya woipa’yo. Nipo’nso, landirani chisoti cha chipulumutso, ndi lupanga la mzimu, ndiko kuti, mau a Mulungu, pamene ndi mpangidwe uli wonse wa pemphero ndi pembedzero mukupitirizabe pemphero pa nthawi iri yonse mwa mzimu.” (Aefeso 6:11-18, NW)
Mwa kuphunzira choonadi, kukulitsa chilungamo ndi kulalikira “mbiri yabwino ya mtendere” kwa ena, tingathe kukhala ndi chikhulupiriro champhamvu chimene chidzatitetezera ku zuikiro zonse za ziwanda.
6. Kodi ndi motani m’mene anthu angadzimasulire ku ziwanda? (Yakobo 4:7, 8)
6 Komabe, pali ena amene alowa m’machita-chita auchiwanda, monga ngati kulankhula ndi mizimu, asanaphunzire “mbiri yabwino.” Anthu otero’wo angatofunikira kumenya nkhondo zolimba kuti amasuke kwa ziwanda. Mwa chitsanzo, panali munthu wina amene analandira uthenga tsiku ndi tsiku kuchokera kwa mzimu woipa, wom’kakamiza kuzipha. Wina anabvutitsidwa nthawi zonse ndi ziwanda-kufikira potsirizira pake anamasuka kotheratu ku mkhalidwe wake wakale. Anthu otero’wo achotsa ziwanda mwa kudzaza maganizo ao ndi ziphunzitso zabwino za Baibulo, akumapemphera kwa Yehova, ndipo ngakhale kuitana mopfuula dzina lake.
“Dzina la Yehova ndiro linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” – Miyambo 18:10.
7. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zingachititse bvuto? (b) Kodi n’chifukwa ninji okhulupirira atsopano mu Efeso anadalitsidwa ndi Mulungu?
7 Ali yense amene alowa m’chiukiro cha ziwanda akakhala wanzeru kudzichotsera iye mwini ndi banja lake zinthu ziri zonse zimene zingakhale ndi chigwirizano chiri chonse ndi kulankhula ndi mizimu. Mizimu yoipa yadziwika kukhala ikubwerera ku zinthu zotero’zo ndi kuputa wokhala nazo’yo mwa kum’pangitsa kudwala, kufooka kapena kukhala wamantha. Pamene Paulo analalikira mu Efeso, anadziwa kuti okhulupirira atsopano kumene’ko anatenga njira ya kachitidwe imene inadalitsidwa kwambiri ndi Yehova:
“Ambiri a iwo akuchita zamatsenga anasonkhanitsa mabukhu ao, nawatentha pamaso pa onse; . . . Chotero mau a Ambuye anachuluka mwamphamvu nalakika.”—Machitidwe 19:19, 20.
CHENJERANI NDI “KACHITIDWE KA KULANKHULA NDI MIZIMU”
8. (a) Kodi ndi mipangidwe ina yotani ya kulankhula ndi mizimu, imene Mulungu amaitsutsa? (b) Kodi n’chiani chimene chidzatulukapo kwa awo amene amalankhula ndi mizimu? (Chibvumbulutso 21:8)
8 Kodi Yehova amalingalira motani ponena za kuchita ulauli? Amene’wa akumveketsedwa bwino pa Deuteronomo 18:10-12, kumene iye akuwagwirizanitsa ndi kulankhula ndi mizimu:
“Asapezeke mwa inu munthu . . . wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa. Popeza ali yense wakuchita izi Yehova anyansidwa naye.”
Chifukwa cha chimene’cho, machita-chita auchiwanda onga ngati kuwerenga mipira ya galasi, kupenda mizera ya m’manja, kuipininga, kuombeza ndi matabwa a Ouija kapena ndi obwebweta zonse n’zonyansa m’maso mwa Yehova. Obwebweta amene amadzinenera kukhala akulankhula ndi “mizimu ya akufa” ali kweni-kweni kulankhula ndi mizimu yoipa imene imayerekezera kukhala anthu akufa. Mzimu woipa unayerekezera kukhala malemu mneneri Samueli m’kupereka uthenga kwa Mfumu yosakhulupirika Sauli, m’chochitika cholembedwa pa 1 Samueli 28:8-14. Pa Agalatiya 5:19-21, “kulankhula ndi mizimu” kukuikidwa pakati pa “ntchito za thupi” zimene zidzachititsa munthu kuchotsedwa mu ufumu wa Mulungu.
9. (a) Kodi n’chiani chimene chiri tanthauzo leni-leni la liu Lachigriki lakuti pharma’kia? (b) Kodi ndi machita-chita otani amene ali ndi chigwirizano ndi kulankhula ndi mizimu?
9 Kuli kokondweretsa kuti liu Lachigriki lotembenuzidwa pano kukhala “kulankhula ndi mizimu” ndiro phar-ma-ki’a, limene kweni-kweni limatanthauza “mankhwala.” Mu Expository Dictionary of New Testament Words ya Vine timawerenga kuti:
PHARMAKIA . . . kwakukulu-kulu limatanthauza kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala, mankhwala oledzeretsa, micheso; kenako, kupatsa mankhwala akupha; kenako, kuchita nyanga, . . . Onani’nso Chibv. 9:21; 18:23 . . . M’kuchita nyanga, kugwiritsiridwa ntchito kwa mankhwala oledzeretsa, kaya osapha kapena akupha, nthawi zonse kunali kutsagana ndi mau onenerera ndi kupempha mphamvu za kulankhula ndi mizimu, limodzi ndi kuperekedwa kwa zituma zosiyana-siyana, . . . kuti akhutiritse wofunsira’yo kuti pali magwero odabwitsa ndi mphamvu za wanyanga.”
Anthu lero lino amene amasuta mankhwala oledzeretsa monga ngati chamba, namgoneka, marijuana ndi anamgoneka ena akudzichititsa iwo eni kukhala osabvuta kugwidwa ndi ziwanda. Zimene’zi zikusonyezedwa m’chakuti ena amene “aledzera” mankhwala oledzeretsa amanena kuti iwo ‘akuyandikira Mulungu,” ‘akufutukula maganizo ao,’ ndi zina zotero. Ndipo’nso koti kugwirizanitsidwe ndi “kugwiritsira ntchito mankhwala oledzeretsa” ndiko kumwerekera ndi mtendza wa betel kapena fodya, machita-chita “oipa” amene amagodomalitsa maganizo ndi kufooketsa mphamvu za kupanga zosankha zoyenera, ndi zimene ziri zopanda chikondi cha mnansi. – 2 Akorinto 6:17-7:1.
MSAMPHA WA KUPENDA NYENYEZI
10. Kodi n’chiani chimene chiri magwero a kupenda nyenyezi? (2 Mbiri 33:5, 6)
10 M’zaka zaposachedwapa, unyinji wa anthu watembenukira ku kupenda nyenyezi kaamba ka chitsogozo. Ndipo’nso, mbiri imasimba kuti anthu ambiri ochuka-Hitler, Mussolini, Napoleon, Julius Caesar, Alexander the Great ndi ena-mokhulupirira malaulo atsatira “nyenyezi.” Kodi kupenda nyenyezi kwazikidwa pa chiani? Kupenda nyenyezi kumagawa mkwamba wa miyamba, zakuthambo, kukhala zigawo khumi ndi ziwiri za nyenyezi, kapena magulu a nyenyezi, chiri chonse cha izo chimene chinachulidwa kale-kale dzina la nyama yakuti-yakuti kapena munthu. Kukunenedwa kuti chigwirizano cha munthu ndi zakuthambo pa nthawi ya kubadwa chidzatsimikizira m’tsogolo mwake ndi mikhalidwe yake. Machati, kapena makhalidwe a nyenyezi, amalembedwa kusonyeza chimene “choikidwiratu” cha munthu, chabwino kapena choipa, chidzakhala tsiku ndi tsiku.
11. Kodi ndi motani m’mene sayansi imasonyezera kupenda nyenyezi kukhala kolakwa?
11 Koma kodi nyenyezi zimayambukira anthu pa nthawi ya kubadwa kwao? Malinga ndi kunena kwa asayansi, umunthu waukulu wa munthu umatsimikiziridwa, osati pa kubadwa, koma pa kutenga mimba–kuchiyambi-yambi kwa miyezi isanu ndi inai koposa zimene zasonyezedwa m’machati a kupenda nyenyezi. Komabe, nyenyezi ziri kutali kwambiri kosati m’kuyambukira munthu mwa mphamvu yokoka kapena kuunika, kaya pa kubadwa kapena pa kutenga mimba. Chokha chimene chingachokera kutali m’mlengalenga mwa njira ya kupenda nyenyezi chiri chisonkhezero cha ziwanda, ndiko kumene kupenda “nyenyezi” kungatsogolereko-ku kulamuliridwa ndi mizimu yoipa.
12. Kodi kupenda nyenyezi kunayambira kuti? (Yesaya 47:1, 12-14)
12 Kodi kupenda nyenyezi kunayambira kuti? The Encyclopedia Britannica (11th ed., Vol. II p. 796) imayankha kuti:
“Mbiri ya kupenda nyenyezi tsopano inayambira ku Babulo wakale, ndipo ndithudi ku mbali zoyambirira za mbiri ya Babulo . . . M’Babulo kudza’nso mu Asuri . . . kupenda nyenyezi kunapezeka m’dzoma laukumu monga imodzi ya njira ziwiri zazikulu zopezeka kwa ansembe . . . zotsimikizirira chifuniro ndi cholinga cha milungu, ina ikumakhala kupenda chiwindi cha nyama yoperekedwa nsembe [kaamba ka kuombezera maula].”
Chotero kupenda nyenyezi kunayambira ku malo amodzi-modzi’wo amene ufumu wonse wa chipembedzo chonyenga unayambira-m’Babulo wakale.
13. (a) Kodi ndi kaimidwe kotani kamene Mfumu yabwino Yosiya inatenga ponena za kachitidwe ka kupenda nyenyezi? (b) Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kuchotsa m’miyoyo yathu kukhulupirira malaulo? (Yobu 31:26-28)
13 Nanga, m’chiani chimene, chiyenera kukhala lingaliro lathu kulinga ku kupenda nyenyezi, kuchita ulauli, zitumwa za “mwai” ndi mipangidwe ina ya kukhulupirira malaulo? Ngati tikufuna kukondweretsa Mulungu, kaimidwe kathu kayenera kukhala kofanana ndi kaja kwa Mfumu yabwino Yosiya, amene ‘analetsa . . . iwo omwe ofukizira zonunkhira Baala, ndi dzuwa, ndi mwezi, ndi nthanda, ndi khamu lonse la kuthambo.’ (2 Mafumu 23:5) Ife’nso tiyenera kuchotsa kotheratu mitundu yonse ya kukhulupirira malaulo m’miyoyo yathu. Mwa kudalira m’njira iri yonse pa openda nyenyezi kapena alauli ena, si kokha kuti tidzakhala osakondweretsa kwa Mulungu wamoyo, koma koma tikatsogozedwa ku zosankha zolakwa kapena machita-chita, moonongetsa miyoyo yathu.
14. Kodi tiyenera kuika kuti chidaliro chathu, ndipo chifukwa ninji? (Salmo 25:8, 9)
14 Pamenepa, kodi n’kuti kumene tiyenera kuika chidaliro chathu cha m’tsogolo? Mfumu Solomo akutiuza kuti:
“Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; um’lemekeze m’njira zako zonse, ndipo iye adzaongola mayendedwe ako. Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova; nupatuke pazoipa.” (Miyambo 3:5-7)
Kupyolera mwa uphungu wanzeru woperekedwa m’Baibulo, Yehova amatimasula mu ukapolo ku kukhulupirira malaulo kopanda pake, ndipo amatipatsa chitsogozo chotsimikizirika chotsogolera ku moyo wachimwemwe kweni-kweni pansi pa ufumu wake wolungama.
[Chithunzi patsamba 133]
Kukhulupirira malaulo ogwirizanitsidwa ndi milungu “ya mwai,” zitumwa ndi kuchita ulauli n’zoopsya
[Chithunzi patsamba 138]
Kuchita ulauli si kobvomerezedwa ndi Mulungu
[Zithunzi patsamba 139]
Zakuthambo za openda nyenyezi zinayambira m’Babulo, kobadwira ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga