Mutu 17
Paradaiso wa Chisangalalo kaamba ka Anthu Onse
1. (a) Kodi ndi motani m’mene wochita zoipa amene anafa pambali pa Yesu anayambira kusonyeza chikhulupiriro? (b) Kodi ndi chiyembekezo chotani chimene Yesu anapatsa wochita zoipa’yo, chikumagogomezera mkhalidwe wotani wa Mulungu? (2 Akorinto 1:3,4)
MALINGA ndi kunena kwa cholembedwa cha Luka, kukambitsirana kotsirizira kwa Yesu asanafe kunali ndi wochita zoipa wokhomeredwa pa mtengo pambali pake. Wochita zoipa amene’yu anadzudzula’di mbala inzake’yo kaamba ka kunenera mwano Yesu. Mwachionekere iye anayamba kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu.
“Ndipo iye anapitiriza kunena kuti: ‘Yesu, ndikumbukireni pamene mulowa mu ufumu wanu.’ Ndipo [Yesu] anati kwa iye: ‘Indetu ndinena ndi iwe lero lino, Udzakhala ndi ine m’Paradaiso.’” (Luka 23:39-43, NW)
Ha, ndi lonjezo lodabwitsa chotani nanga kwa munthu womafa! Chifundo cha Mulungu chikanatha kufutukulidwira ngakhale kwa mpandu woipa amene’yu, akumam’tonthoza ndi chiyembekezo cha moyo m’paradaiso wa ulemerero alinkudza’yo.
2. Fotokozani mwa fanizo m’mene chiyembekezo cha munthu chingakhalire cheni-cheni ponena za Paradaiso. (Ahebri 6:18)
2 Kukoma mtima ndi chifundo cha Mulungu zingathe’di kufutukulidwa kuti zilowetsemo anthu amene anali kutali kwambiri ndi kuchita chifuniro chake. Chotsatirapo’chi ndicho chitsanzo chamakono:
Kumadzulo kwa Japan, mnyamata wina anapatsidwa chilango cha kuphedwa kaamba ka kupha anthu awiri. M’kati mwa zaka za kuyembekezera kuphedwa, anamva za Baibulo ndi ‘mbiri yake yabwino,’ anaphunzira ndi kulandira uthenga wa Ufumu, ndipo anabatizidwa m’ndende. Olondera ndende anadabwa kuona mkhalidwe wake wauchinyama ukusintha kukhala wa chikondi, chisangalalo ndi mtendere. Iye anaphunzira mabukhu a akhungu ndipo anakopa mabukhu ambiri ophunzirira Baibulo kuti athandize anthu akhungu kunja kwa ndende m’phunziro lao. Iye analemba makalata ambiri kwa anthu akunja kwa ndende, kuwalimbikitsa iwo kukhala ndi chikhulupiriro Chachikristu. Pa m’mawa wa kuphedwa kwake, mmishonale anatsagana naye kumka ku makako. Mnyamata’yo anazindikira kuti iye tsopano ayenera kukwaniritsa chiweruzo cholungama, kupereka ‘moyo kaamba ka moyo,’ koma iye ananena mau ake kuti: ‘Lero lino ndikuona kukhala ndiri ndi chikhulupiriro champhamvu mwa Yehova, ndi mu nsembe ya dipo ndi chiyembekezo cha chiukiriro.’ Pambuyo pa kuwerenga lemba, nyimbo ndi pemphero, iye anayenda mwakachete-chete kumka kokaphedwa, nkhope yake inasonyeza bwino lomwe chiyembekezo champhamvu chimene chinali mu mtima mwake. Mau ake otsazikira anali akuti: ‘Kwa kanthawi ndidzagona, ndipo ngati chiri chifuniro cha Yehova ndidzaonana nanu nonse m’paradaiso.’
3. Kodi ndi chiyembekezo chodabwitsa chotani chimene chiripo kaamba ka akufa? (1 Akorinto 15:22)
3 Mofanana ndi wochita zoipa amene anafa limodzi ndi Yesu, mnyamata amene’yu anasonyeza chikhulupiriro m’chifundo ndi kukoma mtima kwachikondi kwa Mulungu. Kodi chikhulupiriro chotero’cho chiri ndi maziko abwino? Inde, pakuti Baibulo limalimbikitsa anthu onse “kukhala ndi chiyembekezo kwa Mulungu . . . chakuti kudzakhala chiukiriro cha olungama ndi osalungama omwe.” (Machitidwe 24:15, NW) Ha, ndi chiyembekezo chodabwitsa chotani nanga! Unyinji wa anthu akufa, abwino ndi oipa, uyenera kuukitsidwa ku manda, ndi kukhala ndi mwai wa kuyenerera moyo wosatha m’paradaiso wobwezeretsedwa’nso pa dziko lapansi. Koma paradaiso wa pa dziko lapansi amene’yu ayenera kukhala chabe chisonyezero cha paradaiso wabwino’di kopambana.
PARADAISO WAUZIMU WAULEMERERO
4. M’zaka za zana loyamba kodi ndi paradaiso wa m’tsogolo wotani pa nthawi’yo amene mtumwi Paulo anamuona m’masomphenya?
4 Mtumwi Paulo akulongosola kuti m’masomphenya “anakwatulidwa kunka ku Paradaiso, namva maneno osatheka kuneneka.” Kodi n’chiani chimene chiri “Paradaiso” amene’yu? Osati malo ena a kumwamba kwakuthupi, koma paradaiso wauzimu amene pa nthawi ina yam’tsogolo akadzetsa chisangalalo kwa anthu a Mulungu pano pa dziko lapansi. –2 Akorinto 12:1-4.
5. (a) Kodi ndi zochitika zotani zimene zinachititsa atumiki a Yehova kulowa m’paradaiso wauzimu? (b) Kodi ndi mikhalidwe yotani imene inafunga kumene’ko? (Yesaya 11:6-9)
5 Yehova anakhazikitsa paradaiso wauzimu amene’yu m’nthawi yake yokwanira. M’mbali yotsirizira ya zaka za zana la makumi awiri, ophunzira Baibulo oona mtima anazindikira kuti ambiri a machita-chita ndi ziphunzitso za machalichi a Chikristu cha Dziko zinachokera ku chipembedzo cha Babulo wakale, ndipo osati kuchokera m’Baibulo. Iwo anayamba kubvumbula ziphunzitso zonyenga monga ngati kusakhoza kufa kobadwa nako kwa moyo, chizunzo cha moto wa helo, ndi Utatu, ndi kubwezeretsa chiphunzitso cha Baibulo chonena za dipo la Yesu, chiukiriro ndi ufumu wa Mulungu. Kuyambira mu 1879, iwo mosalekeza afalitsa magazini a Nsanja ya Olonda monga ochirikizira choonadi cha Baibulo. Kwa zaka zoposa makumi atatu, pa maziko a kuwerengera nthawi kwa Baibulo, iwo anasonyeza m’tsogolo ku 1914 kukhala wapadera mu ulosi wa Baibulo. Ndipo pamene 1914 anafika, Nkhondo Yoyamba ya Dziko inaulika, yotsatiridwa ndi mabvuto ena, kusonyeza “chiyambi cha zowawa za sautso,” monga momwe’di Yesu ananeneratu. M’kati mwa nyengo imene’yo, atsogoleri achipembedzo a dziko anatonza ndipo anaunjika “udani” pa mboni zokhulupirika za Yehova, koma pofika 1919 amene’wa anamasuka kotheratu ku ukapolo wonse wa ufumu wa pa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga- “Babulo Wamkulu.” (Mateyu 24:3-9, NW; Chibvumbulutso 17:5) Iwo anapitirizabe pa “Njira ya Chiyero,” kulowa m’paradaiso wauzimu za amene mnereri’yo analemba kale-kale kuti:
“Ndipo oomboledwa a Yehova adzabwera, nadzafika . . . ndi kusekerera ndi kukondwa kosatha kudzakhala pa mitu yao; iwo adzakhala ndi kusekerera ndi kukondwa, ndipo chisoni ndi kuusa moyo kudzachoka.”–Yesaya 35:8-10.
6. (a) Kodi ndani amene choyamba akulowetsedwa m’paradaiso wauzimu amene’yu? (b) Kodi ndi kagulu kotani kamene kakuonekera kenako? (Yesaya 2:2-4)
6 Maulosi ali ndi zonena zochuluka ponena za maulemerero a paradaiso wauzimu amene’yu. Choyamba, otsalira a “kagulu ka nkhosa” ka Yesu ka atsatiri odzozedwa kalowetsedwa mu mkhalidwe wa paradaiso umene’wu. (Luka 12:32) Koma pambuyo pa kusimba kusankhidwa kwa Aisrayeli auzimu 144,000 amene’wa, Chibvumbulutso cha kwa Yohane chikulongosola ena amene ali ndi mwai wa kulowa m’paradaiso wokongola amene’yu kuti:
“Taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliwerenga, ochokera mwa mtundu uli wonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira ku mpando wachifumu [wa Yehova] ndi pamaso pa Mwanawankhosa [woperekedwa nsembe pa nthawi ina koma tsopano Yesu wolemekezedwa], atabvala zobvala zoyera.” (Chibvumbulutso 7:1-4, 9)
Pano pa dziko lapansi, “khamu lalikulu” likugwirizana ndi otsalira a “kagulu ka nkhosa” mu mkhalidwe wobvomerezeka m’paradaiso wauzimu.
7. Kodi paradaiso wauzimu wafutukuka mpaka pati? (Yesaya 60:22)
7 “Khamu lalikulu” likuonekera bwino kwambiri lero lino! Pamene otsalira’wo a “kagulu ka nkhosa” anatuluka mu zizunzo za Nkhondo Yoyamba ya Dziko, iwo anali zikwi zowerengeka chabe, okhala m’maiko owerengeka a Chikristu cha Dziko. Koma pa March 27, 1975, pamene Mboni za Yehova zinasonkhana m’mipingo yoposa 38,00 m’maiko 210 ndi zigawo za dziko lonse lapansi, kuchita phwando la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye kukumbukira imfa ya Yesu, chionkhetso cha osonkhana chinali anthu 4,925,643. Ndithudi, paradaiso wauzimu tsopano wafutukukira ku mbali za pa dziko lonse lapansi!
ONANI PARADAISO WA PA DZIKO LAPANSI!
8. Kodi paradaiso wa pa dziko lapansi adzasonyeza chiani? (Chibvumbulutso 21:2, 3)
8 Monga momwe’di chingalawa ndi okweramo ake zinapulumukira chigumula cha m’nthawi ya Nowa, momwemo paradaiso wauzimu ndi awo okhalamo adzapulumuka “chisautso chachikulu” ndi kulowa m’dziko lapansi lopanda kuipitsa. Ha, ndi maulemerero otani nanga amene adzayamba kuoneka pa dziko lapansi! “Khamu lalikulu” lopulumuka’lo lidzakhala ndi ntchito yochita mu ‘kugonjetsa dziko lapansi’ ndi kulisandutsa malo okhala okongola amene akusonyeza kukongola konse kwa paradaiso wauzimu za amene Yesaya analemba kuti:
“Chipululu ndi malo ouma adzakondwa; ndipo dziko loti se lidzasangalala ndi kuphuka ngati duwa. Lidzaphuka mochuluka ndi kusangalala, ngakhale kukondwa ndi kuyimba; . . . anthu’wo adzaona ulemerero wa Yehova, ukulu wake wa Mulungu wathu.” (Yesaya 35:1, 2)
Kukongola kokhazika mtima pansi kwa paradaiso wa pa dziko lonse lapansi kudzakweza’di Mlengi wamkulu wa kumwamba ndi dziko lapansi!
9. Kodi ndi mtundu wotani wa ufumu umene udzachititdwa pa paradaiso, ndipo kupyolera mwa yani? (Salmo 72)12)
9 M’dziko lapansi la paradaiso limene’lo, mau a anthu nawo’nso adzalowa’mo m’kutamanda Yehova ndi kukweza ufumu wake:
“Adzanenera ulemero wa ufumu wanu, adzalankhulira mphamvu yanu; kudziwitsa ana a anthu zamphamvu zake, ndi ulemerero waukulu wa ufumu wake.” (Salmo 145:10-13)
Kumbukirani, payenera kukhala ufumu wa zaka chikwi, wochititdwa ndi Yehova kupyolera mwa Mwana wake, Kristu Yesu, kaamba ka kudalitsidwa kwa mafuko onse ndi magulu a mitundu ya anthu. Udzakhala ulamuliro wa mtendere. Maprogramu onse oyambidwa kaamba ka kukonza anthu adzachitidwa mpaka kupambana. Umbombo ndi kuipa zidzalowedwa m’malo ndi kupanda dyera ndi chikondi. Olamulira sadzasamalira’nso olemera okha ndi kupondereza osauka ndi osowa, pakuti mneneri wa Mulungu akunena kuti: “Taonani mfumu idzalamulira m’chilungamo, ndi akalonga [pa dziko lapansi pano] adzalamulira m’chiweruzo.” (Yesaya 32:1) Pansi pa ulamuliro wa dziko limodzi, amene’yo adzakhala paradaiso’di!
10. (a) Kodi ndani amene “adzaukitsidwa” m’paradaiso? (Chibvumbulutso 20:12, 13) (b) Kodi ndi motani m’mene makonzedwe onse a Yehova kaambaka moyo akuchitiridwira chitunzi-thunzi? (Ezekieli 47:1, 9)
10 Ha, ndi kosangalatsa chotani nanga kudziwa kuti akufa ‘adzakhala’nso ndi moyo’kudzakhala nawo m’paradaiso amene’yo! (Yohane 11:25) Chaputala chotsirizira cha Chibvumbulutso chimalongosola kaamba ka ife ukulu wonse wa makonzedwe a Yehova amene iye akupanga kupyolera mwa Yesu Kristu operekera moyo kwa amene’wa ndi ena onse a anthu a pa nthawi imene’yo. Ali monga “mtsinje wa madzi a moyo, wonyezimira ngati krustalo, otuluka ku mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.” Mtsinje wophiphiritsira umene’wu ukuyenda chotsika ndi khwalala la mzinda wakumwamba, “Yerusalemu Watsopano,” kumene Yesu wolemekezedwa’yo ndi “mafumu” anzake 144,000 amakhala.
“Ndi tsidya iri la mtsinje ndi tsidya lake lija panali mtengo wa moyo wakubala zipatso khumi ndi ziwiri, ndi kupatsa zipatso zake mwezi ndi mwezi; ndipo masamba a mtengo ndiwo akuchiritsa nao amitundu.” (Chibvumbulutso 22:1, 2)
Motero, anthu a pa dziko lapansi adzasangalala ndi kugwiritsiridwa ntchito kwa nsembe ya Kristu kochiritsa’ko kufafaniza machimo ao ndi kuwachiritsa matenda ao onse ndi kupanda ungwiro. Ponena za ulamuliro wa Ufumu wa Kristu kwalembedwa kuti:
“Ayenera kuchita ufumu kufikira [Mulungu] ataika adani onse pansi pa mapazi ake. Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:25, 26)
M’dziko lapansi la paradaiso, imfa yochititsidwa ndi uchimo wolandiridwa kuchokera kwa Adamu ‘sidzakhalako’nso.’-Chibvumbulutso 21:4.
MOYO M’PARADAISO WOPANDA IMFA
11. Kodi n’chifukwa ninji imfa yochititsidwa ndi matenda ndi ngozi idzachoka? (Yesaya 25:8; Yobu 33:25)
11 Zopweteka zochititsa imfa, zonga ngati kansala, nthenda ya mtima ndi ukalamba, zidzachoka chifukwa cha kugwiritsiridwa ntchito kwa nsembe yotetezera machimo ya Kristu. ‘Koma bwanji ponena za imfa yangozi?’ wina angafunse motero. Ngakhale imene’yi sidzaoneka, pakuti paradaiso wa pa dziko lapansi adzachititsidwa kufanana ndi wauzimu, kumene ‘chibvulazo’ ndi ‘kuipitsa’ ziri zosadziwika. (Yesaya 11:9) Mkhalidwe wauzimu wa munthu udzam’tetezera ku kuchita mwaukandifere. Munthu wangwiro sadzapanga’nso zoyerekezera zolakwa monga momwe chikhoma chimalumphira mosalakwa kuchokera pa thanthwe kumka pa thanthwe lina pa thelezi. Ndipo’nso, ponene za upandu wosaonedweratu, angelo a Mulungu mosakaikira adzapereka chitetezo chakuthupi, monga momwe’di iwo tsopano lino ‘alamulidwira’ kutetezera anthu a Mulungu m’malo ao a chisungiko chauzimu.—Salmo 91:11.
12. Kodi dziko lapansi lidzadzazidwa ku mlingo wotani? (Mateyu 22:30)
12 Munthu wina’nso angafunse kuti, ‘Ngati anthu safa, kodi dziko lapansi silidzakhala ndi anthu ochulukitsitsa?’ Eya, kale mu 1970 Gulu la Mitundu Yogwirizana la Chakudya ndi Malimidwe linayerekezera kuti dziko lapansi likatha kutulutsa chakudya chokwanira kaamba ka choposa nthawi makumi anai chiwerengero chake cha anthu cha lero lino! Kuli kokha chifukwa cha zolakwa za ulamuliro wa anthu kuti anthu akubvutika ndi njala tsopano. Dziko lapansi liri lokhoza kuchirikiza banja lalikulu kwambiri la anthu koposa m’mene likuchitira lero lino, ndi kuti amene’wo akaphatikizamo akufa onse oukitsidwa. Ndipo’nso, lamulo loyambirira la Mulungu kwa munthu linali ‘kudzaza dziko lapansi ndi kuligonjetsa,’ osati kulidzaza mopambanitsa kosakhoza kupezapo bwino. Pamene mupempha munthu wina kudzaza bekete, simumayembekezera mpope wa madzi kulola madzi kutuluka mpaka nyumba yonse itasefukira. Mofananamo, kungayembekezeredwe kuti Yehova adzaletsa kubalana pa dziko lapansi’li m’nthawi ndi m’njira yake, ndi popanda kumvetsa chisoni anthu angwiro.—Genesis 1:28.
13. Kodi n’chifukwa ninji moyo wosatha sudzakhala wotopetsa? (Salmo 145:16)
13 ‘Koma kodi moyo wosatha sudzakhala wotopetsa?’ wina angatero. Sudzakhala choncho konse! Ubongo pokhala utabwezeretsedwa ku ungwiro, ndi matupi ku nyonga yosatha ya pa unyamata, anthu adzakhala ndi chikondwerero cha kufufuza zodabwitsa zopanda mapeto za chilengedwe. Nthawi zonse padzakhala zinthu zatsopano zozitumba, njira zatsopano zopangira maluso, mwai wonena za kukhosi ndi kugawira anthu ena zisangalalo zonse za dziko lapansi lopangidwa kukhala lokongola kwambiri. Ndipo ‘tsiku la kupuma’ la Yehova litatha, kodi ndi zolengedwa zatsopano zotani zimene iye sangazitulutse kuti zisangalatse zolengedwa zake?
14. Kodi ndi kaamba ka chifukwa chapadera chotani moyo wamuyaya udzakhala chisangalalo chosalekeza? (Salmo 37:3, 4)
14 Koposa zonse, ndi kokondweretsa chotani nanga m’mene kudzakhalira kupitirizabe kumwa pa kasupe wa “nzeru ya mitundu mitundu ya Mulungu,” ndi kulandira mosalekeza chuma chochulaka cha chikondi ndi nzeru yake! (Aefeso 3:10) Yesu amene anasangalala ndi kukhala kwa nthawi yaitali asankhale munthu mogwirizana ndi Yehova, ponena za iye mwini anati, “Ndiri ndi moyo chifukwa cha Atate.” Monga banja lachimwemwe, lobwezeretsedwa pansi pa ulamuliro wa Mulungu, mabiliyoni ambiri a anthu, kuphatikizapo ngakhale ochita zoipa akale, nawo’nso ‘adzakhala ndi moyo’ chifukwa cha makonzedwe odabwitsa a Yehova. Kupitirizabe kwao ‘kulandira chidziwitso’ cha Iye kudzatanthauza kusangalala kwao ndi moyo wokwanira kwaumuyaya wonse ukudza’wo!—Yohane 6:57; 17:3.
[Chithunzi patsamba 151]
Yesu anapereka chiyambekezo cha paradaiso ngakhale kwa waupandu womafa
[Chithunzi patsamba 157]
Makonzedwe a Yehova a moyo wamuyaya ali ngati mtsinje wosangalatsa pakati pa mitengo ya zipatso yobala zipatso