Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gh mutu 20 tsamba 174-182
  • Njira ya Moyo Imene Imatsogolera ku Chimwemwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Njira ya Moyo Imene Imatsogolera ku Chimwemwe
  • Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘MUPEWE MAFANO’
  • ‘MUPEWE MWAZI’
  • ‘MUPEWE DAMA’
  • KUKHALA AKAPOLO A MULUNGU WACHIKONDI
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Kodi Mumalemekeza Moyo Ngati Mmene Mulungu Amachitira?
    Kodi Mungatani Kuti ‘Mulungu Apitirize Kukukondani’?
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Mungatani Kuti Mulungu Azikukondani?
Onani Zambiri
Mbiri Yabwino Yokusangalatsani
gh mutu 20 tsamba 174-182

Mutu 20

Njira ya Moyo Imene Imatsogolera ku Chimwemwe

1. (a) Kodi n’chifukwa ninji anthu ambiri-mbiri lero lino ali opanda chimwemwe? (Mlaliki 2:11, 18) (b) Kodi n’chiani chimene chikadzetsa chimwemwe cheni-cheni ku miyoyo yathu?

ANTHU ambiri amatenga lingaliro lakuti “Tidye timwe pakuti mawa timwalira.” Komabe, mtumwi Paulo akutichenjeza kuti tisakhale ndi “mayanjano” ndi anthu otero’wo. (1 Akorinto 15:32, 33) Ku mbali ina, pali anthu ena amene amayesa kufikira chonulirapo china chopindulitsa m’moyo, koma nthawi zonse amakumana ndi chochitika chodzidzimutsa chakuti chiri chonse chidzafupikitsidwa pambuyo pa zaka zochepa makumi asanu ndi awiri kapena makumi asanu ndi atatu. Ha, ndi kodabwitsa chotani nanga m’mene kukakhalira kulondola chifuno chopindulitsa m’moyo m’kati mwa zaka mazana ambiri, ndipo ngakhale zikwi zambiri! Kodi zimene’zo zikatipatsa chimwemwe cheni-cheni? Ndithudi zikatipatsa!

2. Kodi n’chifukwa ninji kuli koyenera kulingalira kuti Mulungu amatifuna kusangalala ndi moyo wamuyaya? (Salmo 133:1, 3)

2 Ndipo​—chisangalalo choonjezereka​—onjezereka!-ndicho chimene’di Mulungu akulinganizira anthu. “Waika zamuyaya m’mitima yao,” ndipo zimene’zi sakanazichita ngati miyoyo yao ikanadulidwa popanda mwai wa kufufuza m’njira yokhutiritsa “ntchito Mulungu wazipanga.” (Mlaliki 3:11) Inde, muyaya wa moyo wachifuno ndi wachimwemwe uli patsogolo kaamba ka awo amene adzakhala ndi mwai wa kukhala ndi moyo m’paradaiso wa pa dziko lapansi wa Mulungu.

3. (a) Kodi ndi njira ya moyo yotsimikizira yotani imene Yesu anaiyamikira? (Luka 6:31, 36) (b) Kodi ndi motani m’mene Yesu analongosolera malamulo akulu awiri? (Deuteronomo 6:5; Levitiko 19:18)

3 Pamene tikuphunzira za njira yomka ku moyo, tiyenera kufika pa kuona zinthu motsimikizira, ndi mwachidaliro. Pangakhale kuyenera m’mau ena otsu tsa, monga ngati aja a Confucius: “Musachitire ena zimene simukafuna kuti iwo akuchitireni.” Koma ndi opindulitsa kopambana chotani nanga m’mene aliri mau otsimikizira a Yesu a Lamulo la Makhalidwe Abwino: “Chifukwa chake zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inu’nso muwachitire iwo zotero”! (Mateyu 7:12) Ndipo posonyeza chimene chilamulo chonse cha Mose chinasonyeza’ko, Yesu akunena zochuluka koposa ndi njira ya moyo wopanda chochita:

“[Lamulo] la m’tsogolo ndiri, Mvera, Israyeli; Ambuye Mulungu wathu, Ambuye ndiye mmodzi; ndipo uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse. Lachiwiri ndi iri, Uzikonda mnzako monga udzikonda mwini. Palibe lamulo lina lakuposa awa.”​—Marko 12:29-31.

4. Kodi ndi lamulo “latsopano” lotani limene Yesu anapereka? (1 Yohane 3:16)

4 Ndithudi, zimene’zi zimafunikira moyo wokangalika ndi wokhala ndi tanthauzo, kusonyeza kuti timakonda Mulungu kweni-kweni ndi Mlengi wathu ndi kuti timasamalira’di anansi athu. Ponena za zimene’zi, Yesu anati’nso:

“Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inu’nso mukondane wina ndi mnzake. Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:34, 35)

Kodi lamulo limene’li liri “latsopano” m’njira yotani? M’chakuti likufuna mkhalidwe wapadera wa chikondi cha kudzipereka. Munthu wokhala ndi chikondi chimene’chi akafika mpaka ngakhale pa ‘kupereka moyo wake kaamba ka mabwenzi ake,’ monga momwe Yesu anachitira.​—Yohane 15:12, 13.

5. Kodi ndi motani m’mene mungakhalire ndi phande m’kukwanirtsa ulosi? (Marko 13:10)

5 Pozindikira kuti tsopano tikukhala ndi moyo pa “mapeto a dongosolo la zinthu,” Mboni za Yehova zimasonyeza’nso kukonda Mulungu ndi mnansi mwa kukhala ndi phande m’kukwaniritsidwa kwa ulosi waukulu wa Yesu wakuti “mbiri yabwino imene’yi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse.” (Mateyu 24:3, 14, NW) Inu’nso mungathe kukhala ndi phande, mwa kuuza anansi anu za chiyembekezo chabwino kwambiri cha ufumu wa Mulungu ndi ulamuliro wake pa dziko lapansi. Komabe, kukhala mboni ya Mulungu woona sikuli chabe nkhani ya kulankhula ndi ena zoona za Baibulo. Kuli’nso nkhani ya kukhalira moyo choonadi, kugwiritsira ntchito malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo m’njira yonse ya moyo wa munthu’yo.

6. (a) Kodi Mulungu amatifuna kukhala ndi moyo wa mtundu wotani? (Akolose 1:9, 10) (b) Chotero, kodi ndi uphungu wotani umene kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” kanapereka kwa Akristu osakhala Ayuda?

6 Zimene’zi sizikutanthauza kutsatira kwanu malamulo ochuluka kapena “mausachite.” Kukutanthauza kukhala kwanu ndi moyo wa masiku onse ndi wabwino, mukumadzipereka kaamba ka ena ndi kusonyeza kulemekeza uphungu woperekedwa ndi kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” ka Akristu odzozedwa kamene “mbuye,” Yesu, wakaika kupereka ‘chakudya chauzimu pa nthawi yoyenera.’ (Mateyu 24:45) M’zaka za zana loyamba, kagulu ka “kapolo” kamene’ka sikanapereka malamulo ochuluka kulamulira miyoyo ya Akristu osakhala Ayuda. Koma iwo anachula zinthu zingapo zoti azipewe, zimene zikuphatikizapo zotsatirapo’zi:

“Mzimu woyera ndi ife taona kuti n’kwabwino kusakuonjezerani katundu wina wolemera, koposa zinthu zoyenera’zi, kupitirizabe kupewa zinthu zoperekedwa nsembe kwa mafano ndi mwazi ndi zinthu zopotoledwa ndi dama. Ngati musunga zinthu zimene’zi mosamalitsa, mudzalemerera. Thanzi labwino kwa inu.” (Machitidwe 15:28, 29, NW)

Kodi n’chiani chimene chikulowetsedawamo mu “zinthu zoyenera’zi”?

‘MUPEWE MAFANO’

7. Kodi n’chifukwa ninji kuli kofunika kupewa kulambira mafano? (1 Akorinto 10:20, 21)

7 M’lachiwiri la Malamulo Khumi, Yehova Mulungu mwamphamvu analetsa kulambira mafano. Mtumwi Paulo naye’nso anapereka chilangizo chomvekera bwino, pa 1 Akorinto 10:14, kuti:

“Thawani kupembedza mafano.”

Koma kodi n’chifukwa ninji? Chifukwa chakuti umunthu wabwino kwambiri wa Mulungu wamoyo sungathe kuimiridwa konse ndi mafano opanda moyo opangidwa ndi mtengo, mwala kapena chitsulo. Amene’wa amaluluza Mulungu woona ndi wamoyo. Ofera chikhulupiriro a m’nthawi zoyambirira Zachikristu akanatha kudzipulumutsa ku kukhadzulidwa ndi zirombo m’mabwalo a masewera mwa kupereka kachidutswa chabe ka lubani pamaso pa chifano cha mfumu Yachiroma, koma iwo anakana kunyoza Mulungu motero. Mofananamo, awo amene amakhumba kukondweretsa Mulungu wamoyo lero lino ayenera kutenga kaimidwe kamphamvu kotsutsa kufukiza kubani pa maliro, ndi kupereka chakudya kapena chakumwa pa kaguwa kansembe ka banja kapena ka anthu onse, kudza’nso mitundu ina ya kulambira mafano.

‘MUPEWE MWAZI’

8. Kodi n’chifukwa ninji lamulo la ‘kupewa mwazi’ liri logwira ntchito pa anthu onse? (Machitidwe 15:19, 20)

8 Kuletsa kumene’ku kunapangidwa m’chilamulo cha Mose, ndipo ngakhale kale kwambiri pamene Yehova analamula Nowa, kholo la ife tonse kuti: “Mwazi-simuyenera kudya.” (Genesis 9:4, NW) Tiyenera kulemekeza mwazi monga wopatulika. Chifukwa, monga momwe chalongosoledwera pa Levitiko 17:14, n’chakuti “moyo [kapena, mphamu ya moyo] wa nyama zonse, ndiwo mwazi wake,’ ndipo moyo ndi wamtengo wapatali m’maso mwa Wopatsa Moyo, Yehova Mulungu. Chifukwa cha chimene’cho, Baibulo limasonyeza kuti tiyenera kupewa kudya nyama, monga ngati nkhuku zopotoledwa, zimene sizinakhetsedwa mwazi​—kaamba ka zifukwa zauzimu.

9. Kodi kukakhala koyenera kwa inu kulandira mwazi m’thupi, ndipo kodi kumene’ku kumakuikani pa ngozi iri yonse? (Machitidwe 21:25)

9 ‘Kupewa’ kumene’ku moyenerera kumaphatikizamo kusalowetsa kwathu mwazi wa munthu m’matupi athu mwa kuika mwazi m’thupi. Mwa njira imene’yi si kokha kuti timamvera lamulo la Mulungu, koma’nso chitetezo ku nthenda zopatsana monga ngati chindoko, malungo ndi kutupa kwa chiwindi, zimene zachititsa’di imfa kwa odwala ambiri olandira mwazi. Awo amene amafuna kulemekeza lamulo la Mulungu lonena za mwazi achita bwino kufuna-funa dokotala amene adzalemekeza kaimidwe kao kachikumbu mtima ndi kugwiritsira ntchito madzi oonjezera mwazi ngati patakhala kufunika. Pakhala zochitika za kamodzi-kamodzi pamene munthu amene mwachikumbu mtima anakana mwazi wafa, koma kusunga umphumphu ku lamulo la Mulungu kumatsimikiziritsa munthu wotero’yo chiukiriro m’paradaiso wa Mulungu.

‘MUPEWE DAMA’

10. Kodi n’chifukwa ninji tiyenera kukhalabe ndi lingaliro la Mulungu lonena za kugonana ndi ukwati? (2 Petro 2:9, 10, 14)

10 Chosankha cha kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wochenjera” ndipo’nso uphungu wa atumwi osiyana-siyana zikupangitsa kukhala koonekera bwino kuti tiyenera ‘kuthawa dama.’ (1 Akorinto 6:18) Koma ha, ndi losiyana motani nanga m’mene liriri lingaliro la dziko lero lino! Dama​—limene limaphatikizamo chigololo ndi machita-chita onse a kugonana kosakhala kwachibadwa, monga ngati kugonana kwa amuna okha-okha, kugonana kwa anthu ofanana ziwalo, kugonana ndi zinyama ndi kwina-tsopano kukuchitidwa mwaufulu pakati pa timagulu tambiri ta anthu. Lamulo la Mulungu limatitetezera ku zonse’zo. Mwa kukhala ndi lingaliro la Mulungu lonena za kugonana ndi ukwati, si kokha kuti tidzalemekeza Mlengi wathu Wamkulu, koma’nso kupewa kubvutika kwambiri ndi zisoni zambiri.

11. Kodi n’chiani chimene chidzatulukapo m’kusunga “zoyenera” zimene’zi? (2 Timoteo 1:13)

11 Ngati mukufuna kukondweretsa Mulungu, muyenera kusunga “zinthu zoyenera” zimene’zi, pakuti, mwauzimu, mwakuthupi ndi mwamalingaliro, zidzachititsa ‘thanzi labwino kwa inu!’

KUKHALA AKAPOLO A MULUNGU WACHIKONDI

12. Kodi chikondi cha Mulungu chiyenera kutisonkhezera kuchita chiani ndi miyoyo yathu? (Aroma 6:17, 18)

12 Ponena za “chikondi cha Mulungu,” mtumwi Yohane akunena kuti:

“Umo muli chikondi, sikuti ife tinakonda Mulungu, koma kuti Iye anatikonda ife, ndipo anatuma Mwana wake akhale chiombolo chifukwa cha machimo athu.” (1 Yohane 4:9, 10)

Kodi ndi motani m’mene mungayankhire chikondi cha Mulungu chimene’chi? Mungatero mwa kudzipatulira m’kudzipereka kwanu kwa Yehova, kukhala “kotero’ko, pamene iye anati:

13. Kodi n’chiani chimene chikufunika m’kupanga kudzipereka kwa Mulungu? (Ahebri 11:1, 6)

13 Mtumwi wina, Petro, anasonyeza chimene chikufunidwa m’kudzipereka kwa Mulungu kotero’ko, pamene iye anati:

“Lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu, kotero kuti zidze nyengo zakutsitsimutsa zochokera ku nkhope ya Ambuye.” (Machitidwe 3:19)

Muyenera kulapa mbali iri yonse imene munali nayo m’zisembwere, ndale za dziko ndi nkhondo za “dongosolo loipa la zinthu liripo’li.” (Agalatiya 1:3,4, NW) Muyenera kutembenuka, mukumayesa-yesa kubvala umunthu weni-weni Wachikristu, motsanzira Wopereka chitsanzo wathu, Yesu Kristu, ndi kupereka chichirikizo cha mtima wonse ku ulamuliro wa Yehova, monga momwe ukuimiridwira mu ufumu wa Kristu. Motero mumaleka kukhala “mbali ya dziko.”—Yohane 17:14-16.

14. Fotokozani mwa fanizo m’mene kuimira malamulo a khalidwe oyenera kungafupidwire. (Salmo 15:1-3)

14 Ena a atsamwali anu akale angakhale “odabwa ndi kunena mwamwano za inu,” chifukwa cha kusakhala’nso kwanu ndi phande mu ‘mkhalidwe wao wosadziletsa, . . . kulambira mafano ndi zina zopambanitsa.’ (1 Petro 4:3, 4) Komabe, chosankha chanu cha kukhala ndi moyo moona mtima ndi molungama pamaso pa Mulungu nthawi zonse chingatulutse mapindu osayembekezereka, monga m’chokumana nacho chotsatirapo’chi chosimbidwa ndi mmodzi wa Mboni za Yehova mu Philippines:

“Panali kuchotsedwa kwa ogulitsa ambiri a m’kampani yathu, chifukwa cha machita-chita a kusaona mtima. Chifukwa chakuti ndinatsatira malamulo a khalidwe labwino Achikristu ndinakhala wogulitsa yekha amene sanachotsedwe pa nthawi imene’yo. Posapita nthawi pambuyo pa chimene’chi ndinakwezedwera pa dipatimenti ina, kumene kunapezeka posapita nthawi kuti ambiri anali kulemba maoda onama kamba ka phindu la iwo eni. Kachiwiri’nso ndinali ine ndekha amene anasungabe ntchito yake, popeza anapeza kuti sindinalowetsedwe konse m’machita-chita a kusaona mtima. Kuchokera m’zochitika ziwiri zimene’zi ndinatsimikizira kuti kuona mtima ndi kukhulupirika ku malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo zimamasula munthu ku zisoni zazikulu zambiri ndipo zimatulutsa chitamando ku dzina la Mulungu.”

15. Kodi ndi liti pamene munthu ayenera kubatizidwa? (1 Petro 3:21; Mateyu 28:19, 20)

15 Kodi inu ndinu munthu amene akufuna kupanga moyo Wachikristu kukhala njira yanu ya moyo, limodzi ndi chiyembekezo cha moyo wosatha m’paradaiso wa pa dziko lapansi wa Mulungu? Pamenepo, pambuyo pa kulapa ndi kutembenuka, mungadzipereke m’pemphero kwa Yehova kuti mukhale “kapolo wake, pa maziko a chikhulupiriro chanu mu nsembe ya Yesu, ndiyeno kukusonyeza kudzipereka kumene’ku mwa kulandira ubatizo Wachikristu. Mwa kuchita zimene’zi, mudzakhala kapolo wosangalala wofanana ndi Atesalonika’wo amene mtumwi Paulo anawayamikira m’mau awa:

“M’malo monse chikhulupiriro chanu cha kwa Mulungu chidatuluka . . . munatembenukira kwa Mulungu posiyana nao mafano, kutumikira Mulungu weniweni wamoyo, ndi kulindirira Mwana wake achokere Kumwamba, amene anamuukitsa kwa akufa. Yesu, wotipulumutsa ife ku mkwiyo ulinkudza.”​—1 Atesalonika 1:8-10.

16. Kodi ndi chitsanzo chotani chimene chikusonyeza kuti kumvera Mulungu kumapfupidwa? (Machitidwe 5:29)

16 M’malo mwakuti akhale mboni zobatizidwa za Yehova, anthu anafunikira kupambana chitsutso chowawa, monga mu chitsanzo chotsatirapo’chi:

Mtsikana wina Wachichaina mu Taiwan anayamba kufika pa misonkhano limodzi ndi Mboni za Yehova ndi kulankhula ndi ena za ufumu wa Mulungu. Koma chitsutso cha banja chinakhala choipa kwambiri. Iye anamenyedwa nthawi zambiri-mbiri. Makolo ake analemba ganyu gulu la aupandu la pamalopo kupita ndi kukathupsya “apainiya” a Mboni amene anali kuphunzira ndi mtsikana’yo. Makalata ake anatengedwa ndipo Baibulo lake ndi mabukhu olongosola Baibulo anaonongedwa nthawi zambiri. Komabe, zoyesa-yesa zokoma mtima koma zamphamvu ku mbali ya mtsikana’yo pang’ono-pang’ono zinadzetsa ufulu woonjezereka. “Apainiya” a Mboni’wo anachoka m’tauni ya kwao’yo, koma pamene mtsikana’yo anasonyeza kuzindikira Kwachikristu ndi chikondi, mkhalidwe wa makolo ake unafewa ndipo iwo anam’lola kuyenda ulendo wa ora limodzi kupita kokha kumka ku tauni limene iye akafika pa misonkhano. Pambuyo pa zaka ziwiri za kuyesa-yesa kodekha iye anabatizidwa.

Chifukwa cha chitsimikiziro chake cha kumvera Mulungu ndi kupitirizabe kufikira ubatizo Wachikristu, mtsikana wachichepere amene’yu anali wokhoza kugwiritsa pa “moyo weni-weni wosatha.” Ha, ndi mphotho yotani nanga!​—1 Timoteo 6:12, 19.

17. (a) Kodi n’chifukwa ninji anthu obatizidwa chatsopano afunikira kupitirizabe kupanga kupita patsogolo? (Aefeso 4:14, 15) (b) Kodi n’chiani chimene chidzatulukapo m’kukhalabe kwathu m’chikondi cha Mulungu? (1 Yohane 4:16-19)

17 Ubatizo sindiwo mtundu wina wa “kumaliza maphunziro.” M’malo mwake, uli chiyambi cha unansi wachimwemwe kopambana ndi Yehova. Komabe, poyamba njira imene’yi ya moyo, inu mukali “mwana” m’choonadi ndipo muyenera kupitirizabe ‘kuyesa-yesa kufikira uchikulire.’ Pamene “mukutumikira Yehova” zisangalalo zanu zidzaonjezeka ndipo moyo wanu udzakhala watanthauzo moonjezereka-onjezereka ndi wokhutiritsa. (2 Timoteo 2:1; Ahebri 6:1, NW) Zoona, padzakhala ziyeso ndi zobvuta m’njira, koma mungathe kuyang’anizana ndi zimene’zi ndi chikhulupiriro cha mtima wonse chosonyezedwa ndi mtumwi Paulo:

“Ife tilakatu, mwa Iye amene anatikonda. Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chiri chonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chiri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 8:37-39)

Kukhalabe kwanu m’chikondi cha Mulungu kudzakhala chitetezo chanu.

[Chithunzi patsamba 177]

Mboni mwachikondi zimauza ena madalitso a Ufumu

[Chithunzi patsamba 181]

Ubatizo umayamba unansi wachimwemwe ndi Mulungu

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena