Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • go mutu 11 tsamba 175-183
  • Kupita kwa Dziko Logawanika

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kupita kwa Dziko Logawanika
  • Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “BABULO WAMKULU ATAONONGEDWA”
  • Kupha Babulo Wamkulu
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kuweruza Hule la Makhalidwe Oipa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • “Opani Mulungu Ndipo Mpatseni Ulemerero”
    Nsanja ya Olonda—1988
  • Kulimbana ndi Zilombo Ziwiri Zoopsa
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
Onani Zambiri
Boma Lathu la Dziko Likudza’lo—Ufumu wa Mulungu
go mutu 11 tsamba 175-183

Mutu 11

Kupita kwa Dziko Logawanika

1. Kodi “khamu lalikulu” likusangalala ndi kusintha kwa dziko koyandikira kotani?

IFE tsopano takuyandikira kwambiri ndi zaka zoposa mazana khumi ndi asanu ndi anai. Kuyandikira ku chiani? Ku kusintha kwa dziko kopindulitsa kuja kumene wolemba Baibulo wa m’zaka za zana loyamba C.E. anakulengeza, kuti: “Maonekedwe onse a dziko iri akupita.” (1 Akorinto 7:31, The New English Bible) “Khamu lalikulu” la anthu amene akudzikonzekeretsa kaamba ka” boma la dziko la Mulungu likudza’lo amasangalala kuti kupita kwa dziko logawanika’li kuli pafupi.—Chibvumbulutso 7:9,10.

2, 3. (a) Kodi nchiani chimene Mitundu Yogwirizana yalephera kuchitira dziko? (b) Kodi ndi motani m’mene Baibulo limalongosolera mophiphiritsira ufumu wachipembedzo wogawanitsa’wo?

2 Gulu la Mitundu Yogwirizana, ngakhale kuli kwakuti tsopano liri ndi zaka makumi atatu ndipo liri ndi mitundu yokhala ziwalo 150, lalephera kukonza mkhalidwe wa dziko wogawanika’wo. Lero lino nthumwi zambiri za U.N. zimazindikira kuti mphamvu yogawanitsa kopambana zonse ndiyo chipembedzo chaudziko. Kusiyana kwa chipembedzo n’kozika mizu kwambiri. Timagulu tachipembedzo tagawanitsa ngakhale magulu achipembedzo akulu. Chikristu cha Dziko chokha chagawika timagulu chikwi chimodzi kapena toposa. Mosasamala kanthu za kusiyana-siyana kwao, Mau a Mulungu amatisonkhanitsa tonse pamodzi kukhala ufumu umodzi wa dziko wa chipembedzo chonyenga. Amayerekezera ufumu wachipembedzo umene’wu ndi mkazi, kuti: “Mkazi’yo unamuona [mtumwi Yohane], ndiye mudzi waukulu, wakuchita ufumu pa mafumu a dziko.” (Chibvumbulutso 17:18) Tsopano, kodi ndani amene kweni-kweni ali “mkazi” amene’yu amene ali ngati mzinda wachifumu wochita ulamuliro pa olamulira a ndale za dziko? Mtumwi Yohane akutiuza, kuti:

3 “Pa mphumi pake padalembedwa dzina, chinsinsi: ‘Babulo Wamkulu, amai wa akazi achigololo ndi wa zinthu zonyansa za dziko lapansi.’ Ndipo ndinaona kuti mkazi amene’yo anali woledzera mwazi wa oyera mtima ndi mwazi wa mboni za Yesu.” (Chibvumbulutso 17:5, 6, NW) “Mkazi wachigololo wamkulu amene akhala pa madzi ambiri, amene mafumu a dziko lapansi anachita naye chigololo, pamene awo amene amakhala pa dziko lapansi anapangitsidwa kuledzera ndi vinyo wa chigololo chake.”—Chibvumbulutso 17:1, 2, NW.

4. Kodi ndi motani m’mene “chigololo” chake chayambukirira anthu wamba?

4 “Ufumu” umene Babulo Wamkulu wakhala nao pa mafumu a dziko lapansi wakhala uja wachigololo, njira ya “dama” lachipembedzo.” Anthu abvutika chifukwa cha kusanganiza kwake chipembedzo ndi ndale za dziko. Lakhala gawo lowawa kwa anthu wamba kumwa kuchokera m’manja mwake. Lawachititsa kudzandira monga ngati aledzera.

5. Kodi ndi m’njira yotani mkazi wachigololo amene’yu akukwerera “chirombo”? Chifukwa ninji?

5 “Mkazi wachigololo” wamkulu’yo wabala “akazi achigololo” ena ambiri achipembedzo ndipo wawapanga kukhala ziwalo za banja lake la pa dziko lonse. Lero lino Babulo Wamkulu amatamanda Mitundu Yogwirizana monga momwe iye anachitira papitapo ndi Chigwirizano cha Mitundu. Iye waika chidaliro chake mwa iyo m’malo mwa ufumu wa Mulungu Waumesiya, boma la dziko likudza’lo. Chotero iye waikwera. Kaamba ka chifuno cha kuchuka ndi kaamba ka phindu la iye yekha iye amadzilola kunyamulidwa nayo, motero kuchititsa ufumu wake wachipembedzo wogawanika’wo kugwirizana pamodzi mu mpangidwe wa “umodzi ngakhale mbali zake ziri zosiyana.” Koma chokwerapo chimene iye akukwerapo chiri choopsya. Sindiko popanda chifukwa kuti Baibulo limaphiphiritsira chokwerapo chake kukhala “chirombo” chofiiritsa chokhala ndi mitu isanu ndi wiri ndi nyanga khumi. Chirombo chimene’chi chiri ndi “maina amwano.” Chimene Babulo Wamkulu amacha chirombo chiri chonyansa kwa Mulungu.—Chibvumbulutso 17:3.

6. Kodi ndani amene tsopano akutuluka m’Babulo Wamkulu, ndipo chifukwa ninji?

6 Kodi ndi motani m’mene Mulungu adzabwezerera mwazi wosachimwa umene iye “waledzera” nawo? Mwa kulola gulu la “chirombo” kum’mtembenukira mwa udani pamene iye alola “chisautso chachikulu” kuyamba. Chionongeko chake chikutsatirapo. (Chibvumbulutso 17:15, 16; 19:1-3) Chifukwa cha chimene’cho tsopano, m’kati mwa “mapeto a dongosolo la zinthu” lino, Yehova Mulungu wachititsa mpfuu yofulumira kumvedwa pa dziko lonse kuti: “Tulukani m’menemo, anthu anga; kuti mungayanjane ndi machimo ake, ndi kuti mungalandireko ya miliri yake; pakuti machimo ake anaunjikizana kufikira m’Mwamba, ndipo Mulungu anakumbuka zosalangama zake.” (Chibvumbulutso 18:4, 5) Otsalira a “abale” auzimu a Kristu ndipo’nso “nkhosa” zimene zimapanga “khamu lalikulu” amvera lamulo la Mulungu ndipo atuluka. Chifukwa cha chimene’cho iwo sadzaonongeka limodzi naye mu “chisautso chachikulu.”

“BABULO WAMKULU ATAONONGEDWA”

7. Kodi “chirombo” chiri ndi cholinga cha kutumikira Mulung m’kumuononga?

7 Ufumu wa chipembedzo chonyenga utaonongedwa, sipadzakhala Chikristu cha Dziko choti chipitirizebe kucha gulu la Mitundu Yogwirizana kukhala “chisonyezero cha ndale za dziko cha Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.” Ziwalo za U.N. ndi mitundu ina imene siri ziwalo zake sizidzanganiza kuti zachitira Mulungu zabwino mwa kuononga mkazi wao wolemekezeka wapapitapo amene analedzera ndi mwazi wa “oyera” osachimwa ndi wa “mboni za Yesu.” Mitundu’yo sidzaononga “mkazi wachigololo” wachipembedzo’yo mwadala kubwezerera Mulungu ndi anthu ake ozunzidwa’wo. Iyo ikukuchita monga kachitidwe ka zipembedzo zonse, popanda cholinga cha kusiya chipembedzo choona, “mpangidwe wa kulambira umene uli woyera ndi wosadetsedwa mwa lingaliro la Mulungu ndi Atate,” monga momwe Yakobo 1:27, NW, amanenera. Pa tsopano lino loposa theka la ziwalo za U.N. zimene siziri za Chikristu cha Dziko zimakana kukhala kwake “chisonyezero cha ndale za dziko cha Ufumu wa Mulungu pa dziko lapansi.”

8. Chitatha kuononga Babulo Wamkulu, kodi “chirombo” chidzachitanji?

8 Chotero, pambuyo pa kuononga kwao Babulo Wamkulu (kuphatikizapo Chikristu cha Dziko), kodi n’chiani chimene mitundu youmirirabe kapena yogwirizana ndi U.N. idzachita? Chaputala chimodzi-modzi’cho chimene chimafotokoza gulu la “chirombo” kukhala lofanana ndi chirombo cha mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi chimatiuza kuti: ‘Imene’yi iri ndi chifuno chimodzi, ndipo chotero imapereka mphamvu yao ndi ulamuliro kwa chirombo. Imene’yi idzamenyana ndi Mwanawankhosa, koma, chifukwa chakuti iye ali Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, Mwanawankhosa adzawagonjetsa. Ndipo’nso, awo oitanidwa ndi osankhidwa ndi okhulupirika ndi iye adzatero.’ (Chibvumbulutso 17:13, 14, NW) Nkhondo imene’yi idzachitika pa nthawi imodzi-modzi ndi zija zimene zikufotokozedwa m’Chibvumbulutso 19:11-21. Yonse’yi ndiyo “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Harmagedo.—Chibvumbulutso 16:14, 16, NW.

9. Kodi n’chiani chimene chidzagwera “mafumu” okana Yehova ndi okana Kristu amene’wo?

9 M’njira yosonyeza imene’yi loto limene mmeneri Danieli analimasulira kwa Nebukadinezara mfumu ya Babulo wakale likukwaniritsidwa. Ufumu umene Mulungu wakumwamba akuukhazikitsa m’masiku a olamulira otsirizira a maboma a ndale za dziko alipo’wa “udzaphwanya ndi kutha maufumu onse’wa.” (Danieli 2:44, NW) Pamenepa padzakhala pachimake posafanana ndi pena pali ponse pa “nthawi ya masautso, siinakhale yotere kuyambira mtundu wa anthu kufikira nthawi yomwe ija.” (Danieli 12:1; Mateyu 24:21, 22; Marko 13:19, 20) Ponena za nthawi ya nkhondo ya m’chilengedwe chonse imene’yo kukunenedwa kwa Mtsogoleri Wankhondo Wamkulu wa Yehova, Yesu Kristu: “Yehova pa dzanja lamanja lako adzaphwanya mafumu tsiku la mkwiyo wake. Adzaweruza mwa amitundu, adzadzaza dziko ndi mitembo; adzaphwanya mitu m’maiko ambiri.” (Salmo 110:5,6) ‘Mutu’ wa ‘dziko liri lonse lokhala ndi anthu ambiri’ udzakhala utagona kwala pakati pa ‘malo odzaza mitembo.’ Kodi tingakaikire kuti “tsiku la mkwiyo wake” limene’li lidzakhala nthawi ya chipolowe kopambana?

10. Kodi ndi motani m’mene Petro amalongosolera kukhala laphokoso kwa “tsiku” la Yehova?

10 Mtumwi Petro akusonyeza phokoso la nthawi ya nsautso ya dziko yosafanana ndi ina iri yonse imene’yo m’kati mwa imene magulu okhazikitsidwa kwa nthawi yaitali a mtundu wa anthu akusungunuka monga ngati ndi moto wa ng’anjo ya nyuklea. Polembera osati kwa anthu audziko, koma kwa Akristu, amene angayembekezere kuona zinthu zimene’zi ndi kupulumuka, Petro akuti: “Komabe tsiku la Yehova lidzadza ngati mbala, m’limene miyamba idzachoka ndi phokoso loti fwaa, koma zinthu’zo pokhala zotentha kopambana, zidzasungunuka, ndipo dziko lapansi ndi ntchito zokhalamo zidzabvumbuluka. Popeza kuti zinthu zonse’zi ziyenera kusungunulidwa motero, kodi tiyenera kukhala anthu a mtundu wotani m’machitidwe a khalidwe lopatulika ndi ntchito za kudzipereka kwaumulungu, akuyembekezera ndi kukumbukirabe kwambiri kukhalapo kwa tsiku la Yehova, mwa limene miyamba pokhala pa moto idzasungunuka ndi zinthu pokhala zotentha kopambana zidzasungunuka! Koma pali miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ife tikuziyembekezera monga mwa lonjezano lake, ndipo m’zimene’zi mudzakhala chilungamo.”—2 Pet. 3:10-13, NW.

11. Kodi ndani amene adzakoleza moto wa “tsiku” limene’lo Pa nthawi yotani?

11 Kodi ndani amene adzasonkha moto wosakaza zonse umene’wo umene udzayeketsa zonse pa dziko lonse lapansi? Osati mitundu isanu ndi umodzi yokhala ndi zida za nyuklea mwa kuphulitsa maboma ao ounjikizana ndi mibvi yoponyera maboma m’ziukiro zodzidzimutsa pa wina ndi mnzake! Ai, koma Yehova Mulungu, Mlengi wa nyenyezi zonse zowala zokha m’milalang’amba yonse ya nyenyezi m’mlengalenga monse. Nthawi ya moto wonyeketsa idzakhala “tsiku la Yehova.” Ngakhale kuli kwakuti ofufuza Baibulofe tikudziwa kuti tikukhala ndi moyo mu “nthawi ya mapeto” yonenedweratu’yo, “mapeto a dongosolo la zinthu,” komabe tsiku la kuchotsedwa kwa maulamuliro aumunthu limene’lo lidzadza monga mbala. Maboma a ndale za dziko opangidwa ndi anthu, amene alamulira mtundu wa anthu mongofanana ndi miyamba yeni-yeni akulamulira dziko lapansi, adzakhala osakhoza kugwirizana pamodzi koma adzakhadzukana m’kumwazikana kwachipolowe. “Miyamba” yophiphiritsira imene’yi, monga momwe mtumwi Petro akunenera, “idzachoka ndi phokoso loti fwaa.” Phokoso la nthawi yaitali’lo, lofanana ndi lija la nthunzi yotulutsidwa ndi kutentha, lingaonjezeke kukhala kubangula pamene “miyamba” ya boma’yo ikuphwanyidwa kukhala mabwinja.

12. Kodi ndi m’lingaliro lotani “zinthu” zidzasungunuka pa “tsiku” limene’lo?

12 Kutentha kwa mkwiyo wa Mulungu kudzasonyezedwa mwamphamvu kwambiri pa dongosolo la zinthu lopanda umulungu lokhala pansi pa ulamuliro wa Satana, kwakuti lidzasungunulidwa, kunena kwake titero, likumataya kukhazikika ndi kugwirizana kwa m’kati. “Zinthu,” mzimu wokuta umene wazungulira dziko lapansi ndi umene umasonkhezera anthu okhala pa dziko lapansi onse, zidzataya kuzizira kuli konse kapena kukhazikika kumene linali nako. Mu mkwiyo wa moto wa tsiku la Yehova, mzimu wa zinthu umene’wo udzatentha mpaka kufika pa kuyera ndipo udzakolezera anthu kuchita machitidwe openga kuganiza kosokonezeka, kumenyana kwachiwawa ndi kwachipolowe pakati pa iwo eni kaamba ka kupulumuka kwa munthu mwini. Sudzachititsa’nso anthu kugwirizana pamodzi monga chitaganya chimodzi chogwirizana. Motero “zinthu” zophiphiritsira’zo zidzasungunuka, kunyeka!

13. Kodi ndi “dziko lapansi ndi ntchito zake” zotani zimene zikutanthauzidwa pano?

13 Chabwino, pamenepa, kodi “dziko lapansi” limene liyenera kuonongedwa lingatanthauze mpira wathu’wu? Ai, Iro limaphiphiritsira chitaganya cha anthu malinga ndi m’mene chikupitirizirabe pansi pa dongosolo lino la zinthu. Chitaganya cha anthu chiri ndi “ntchito” zambiri zodzisonyeza nazo chokha. Chiri ndi magulu ambiri a magulu masukulu ena ambiri, timagulu tambiri tachipembedzo ndi ambiri a ndale za dziko.

14. Kodi “dziko lapansi ndi ntchito ziri momwemo: zidzabvumbulidwa mu lingaliro lotani?

14 Kodi “kukhalapo kwa tsiku la Yehova” kudzasonyeza mpangidwe wonsewu wa chitaganya cha anthu ndi “ntchito” zake zadyera kukhala zotani? “Kukhalapo” kwa tsiku lamoto la chiweruzo chaumulungu limene’lo kudzachititsa zinthu zimene’zi kukhala poyera. Izo zidzabvumbulidwa mu mkhalidwe umene izo ziri kweni-kweni. Anthu adzachititsa zinthu zimene’zi kuonetsedwa kwa iwo kukhala zotsutsidwa ndi Mulungu wopanda dyera ndi wolungama. Monga momwe zinaliri m’masiku a Nowa chisanachitike chigumula cha pa dziko lonse lapansi, Yehova adzaona “kuti kuipa kwa anthu [kuli] kwakukulu pa dziko lapansi, ndipo’nso kuti ndingaliro zonse za maganizo [ziri] zoipabe zokha-zokha.” (Genesis 6:5) Chotero mogwirizana ndi kuona kwake zinthu za dziko lapansi, Yehova kachiwiri’nso adzafafaniza “anthu opanda umulungu,’ chitaganya chaumunthu chimene chimasonyezedwa ndi mau akuti “dziko lapansi.”—2 Petro 2:5; 3:7.

15. Kodi otsalira ndi “khamu lalikulu” adzakhala bwanji pa nthawi imene’yo?

15 Awo amene adzipanga ‘kusakhala mbali ya dziko.’ Ndiko kuti, otsalira a “abale” a Kristu auzimu ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” za Kristu, adzapezeka ali m’kati mwa “tsiku la Yehova” lamoto limene’li. Kodi iwo adzachitanji m’kati mwa “chisautso chachikulu” chimene’chi chimene sichidzabwerezedwa’nso? (Yohane 17:14, 16; 10:16) Iwo sadzakhala osungunulidwa limodzi ndi “miyamba” ya boma “zinthu” zosachedwa kunyeka’zo, ndi “dziko lapansi” la anthu oipa ndi “ntchito” zake zaudziko. Pansi pa “chihema” cha chitetezo cha Yehova, iwo adzapenya zinthu zodabwitsa kwambiri zimene zikuchitika ndipo sadzadabwitsidwa ndi kupita kwachiwawa kwa dziko logawanika’li, otsutsa ulamuliro wa Yehova.—Salmo 37:34.

16. Kodi amene’wa akukhala mboni zoona ndi maso za mtundu wotani za zochita za Mulungu?

16 Otetezeredwa mwaumulungu amene’wa sadzaopsyedwa ndi kupita kwa “miyamba” yakale imene’yi ndi “dziko lapansi” lakale. Iwo adzakondwera ndi kulemekezedwa kwa ulamuliro wa Yehova wa m’chilengedwe chonse kumene’ku. Iwo adzakhala mboni zoona ndi maso za “ntchito za Yehova, amene achita zopululutsa pa dziko lapansi.” Iwo adzazindikira kuti “aletsa nkhondo kumalekezero a dziko lapansi.” (Salmo 46:8, 9) Iwo adzayembekezera kukwaniritsidwa kwa kukhazikitsidwa kwa “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano,” zimene iwo aziyembekezera kwa nthawi yaitali mwachipiriro. Mokondwa iwo adzasangalala kuti potsirizira pake nthawi yafika kweni-kweni yakuti Yehova Mulungu akwaniritse lonjezo lake la “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.” ( 2 Petro 3:13) O tsopano chidzakhala chokumana nacho chosalongosoleka chotani nanga kwa iwo kupulumuka “chisautso chachikulu” ndi “nkhondo [yake] ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pa Harmagedo ndi kusungidwa amoyo kulowa m’dongosolo lake latsopano!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena