Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • my nkhani 81
  • Kudalira Thandizo la Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kudalira Thandizo la Mulungu
  • Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Anthu a Mulungu Atuluka m’Babulo
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Ezara
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mukhoza Kukhalabe Olimba Mtima pa Nthawi Yovuta
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Ukapolo M’babulo Mpaka pa Kumangidwa’nso kwa Malinga a Yerusalemu
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
Onani Zambiri
Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
my nkhani 81

NKHANI 81

Kudalira Thandizo la Mulungu

ANTHU ambirimbiri akuyenda ulendo wautali’wo wochokera ku Babulo kumka ku Yerusalemu. Koma pofika, Yerusalemu wangokhala bwinja lalikulu. Mulibe wokhalamo. Iwo ayenera kumanga chiri chonse kachiwiri’nso.

Chintu choyambirira chimene iwo akumanga ndicho guwa la nsembe. Awa ndi malo amene iwo angaperekerepo nsembe zopsyereza, kapena mphatso kwa Yehova. Miyezi yowerengeka pambuyo pake iwo akuyamba kumanga kachisi. Koma adani okhala m’maiko apafupipi sakufuna kuti Aisrayeli am’mange. Chotero Akuyesa kuwaopsyeza kuti aleke. Potsirizira pake, adani’wa akuchititsa mfumu yatsopano ya Perisiya kupanga lamulo loletsa ntchito yomanga’yo.

Zaka zambiri zikupitapo. Tsopano papita zaka 17 chibwerere Aisrayeli kuchokera ku Babulo. Yehova akutumiza mneneri wake Hagai ndi Zekariya kukauza anthu’wo kuyamba’nso kumanga. Anthu’wo akudalira m’thandizo la Mulungu, ndipo akumvera aneneri’wo. Iwo akuyamba kumanga’nso, ngakhale kuli kwakuti lamulo likunena kuti sayenera kukuchita.

Chotero mkulu wa Perisiya wochedwa Tatenayi akudza nafunsa Aisrayeli kuyenera kumene ali nako kwa kumanga kachisi. Iwo akumuuza kuti pamene iwo anali m’Babulo, Mfumu Koresi anawauza kuti: ‘Pitani, tsopano, ku Yerusalemu ndi kukamanga kachisi wa Yehova, Mulungu wanu.’

Tatenayi akutumiza kalata ku Babulo nafunsa ngati Koresi, amene tsopano ali wakufa, ananena’di zimene’zo. Posakhalitsa kalata ikudza kuchokera kwa mfumu yatsopano’yo. Ikunena kuti ananena’di. Ndipo chotero mfumu’yo ikulemba kuti: ‘Lolani Aisrayeli amange kachisi wa Mulungu wao. Ndipo ndikukulamulani kuwathandiza.’ M’kati mwa pafupi-fupi zaka zinai kachisi’yo watha, ndipo Aisrayeli ali achimwemwe kwambiri.

Zaka zina zambiri zukupitapo. Tsopano papita pafupi-fupi zaka 48 chiyambire pamene kachisi anamalizidwa. Anthu a m’Yerusalemu ali osauka, ndipo mzinda’wo ndi kachisi wa Mulungu sizikuoneka kukhala zokongola. Ku Babulo’ko Muisrayeli Ezara akumva za kufunikira kwa kukonza kachisi wa Mulungu. Chotero kodi mukudziwa chimene akuchita?

Ezara akumka kukaonana ndi Aritasasta, mfumu ya Perisiya, ndipo mfumu yabwino’yi ikupatsa Ezara mphatso zambiri zomka nazo ku Yerusalemu. Ezara akufunsa Aisrayeli okhala m’Babulo kum’thandiza kunyamula mphatso’zi kumka ku Yerusalemu. Anthu okwanira 6,000 akunena kuti adzamuka. Iwo ali ndi siliva wochuluka ndi golidi ndi zinthu zina za mtengo wapatali zomka nazo.

Ezara akubvutika maganizo, chifukwa chakuti muli anthu oipa m’njiramo. Anthu’wa angalande siliva ndi golidi wao, ndi kuwapha. Chotero Ezara akuitana anthu’wo, monga momwe mukuonera m’chinthunzi’chi. Ndiyeno akupemphera kwa Yehova kaamba ka chitetezo chake pa ulendo wao wobwerera ku Yerusalemu.

Yehova akuwatetezera. Ndipo pambuyo pa miyezi inai ya kuyenda, iwo akufika bwino lomwe ku Yerusalemu. Kodi zimene’zi sizikusonyeza kuti Yehova angatetezere awo amene amam’dalira kaamba ka chithandizo?

Ezara chaputala 2 mpaka 8.

Mafunso

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena