Mutu 3
Chiyembekezo Chokhala ndi Chitsimikiziritso Chotsimikizirika
1-3. (a) Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira chabe kukhalako kwa Mulungu sikuli kokwanira kuti ife tikhale ndi chibvomerezo cha Mulungu? (b) Malinga ndi kunena kwa Ahebri 11:6, kodi nchiyani chimene tiyenera kukhulupirira, ndipo kodi nchifukwa ninji chimenechi chiri chofunika?
ANTHU ambiri amanena kuti amakhulupirira kuti Mulungu aliko. Koma kukhala ndi moyo m’njira imene imapezetsa chibvomerezo cha Mulungu kumafuna zoposa zimenezo. Tifunikira kukhala okhutiritsidwa maganizo mwamphamvu kuti zimene zingadze kwa ife mwa njira ya nsautso ziri monga ngati palibe kanthu poyerekezera ndi madalitso akulu amene Mulungu Wamphamvuyonse adzapereka kwa atumiki ake.
2 Chifukwa cha ichi, kungotumikira Mlengi wathu mwa kuona kukhala athayo chifukwa cha kukhala kwake Wotipatsa Moyo sikulinso kokwanira. Lingaliro chabe la kuona kukhala wathayo siliri lamphamvu mokwanira kutipangitsa kukhalabe okhulupirika polingalira ziyeso zonse zimene tingakumane nazo-kuchitiridwa chipongwe mwa kumenyedwa ndi mwa mawu, kudwala, zogwiritsa mwala, mabvuto a chuma. Chikondi chokha champhamvu ndi chosasweka kwa Atate wathu wakumwamba chikatha kuchita zimenezo.
3 Kuti tikhale ndi chikondi cha mtundu umenewo kwa Mulungu, tiyenera kukhulupirira kuti iye mwini ndi wachikondi, wabwino, woolowa manja. Baibulo limasonyeza kuti chikhulupiriro choterocho chiri chofunika kotheratu kwa Akristu. Iro limati: “Iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti iye ali ndi kuti amakhala wopereka mphotho wa awo omfunafuna mwaphamphu.” (Ahebri 11:6, NW) Kuchepetsa kuli konse lonjezo la Mulungu la kudalitsa atumiki ake kumapotozadi kumdziwa kwathu. Kungatidodometse kuzindikira Yehova kukhala Mulungu amene amayamikira kwambiri ntchito zabwino kwambiri za anthu ake (Ahebri 6:10) Ndiponso, chikhulupiriro chathu champhamvu chakuti Wammwambamwambayo ali wopereka mphotho chimapanga mwa ife kulabadira koyamikira, chikumatisonkhezera kufuna kumkondweretsa.
‘OSUNGIDWA KAAMBA KA CHIPULUMUTSO’
4. Kodi ndi motani mmene Yehova Mulungu amatithandizira kupeza chipulumutso, ndipo chotero kodi nchiyani chimene tiyenera kukhala tikuchita?
4 Ndithudi, ife sitimapeza chipulumutso mwa utumiki wathu kwa Mulungu, monga ngati mwa kusunga khalidwe labwino ndi kuthandiza ena mwauzimu ndi mwakuthupi. Atate wathu wakumwamba iye mwini wapanga makonzedwe onse kaamba ka kupeza kwathu moyo wosatha, ndipo iye amatithandiza kuchita chifuniro chake ndi kulandira dalitso limenelo. Chifukwa cha chimenecho, chiyembekezo chathu chopatsidwa ndi Mulungucho, chimatilimbikitsa kudzigonjetsera kotheratu ku chitsogozo cha Mulungu. Chidaliro chotheratu mwa Yehova monga wopereka mphotho chimatitheketsa kupitirizabe kugwirizana naye m’kutipangitsa kukhala Akristu enieni, okula mokwanira. (Aefeso 4:13-15) Zoona, chigwirizano chokangalika choterocho ndi Mlengi wathu chimafuna kuti ife tiyesetse mwamphamvu kulamulira zizolowezi zathu zochimwa. Koma iye Ndiye amene, mwa njira ya mzimu wake woyera, amapangitsa kukula kwathu kwauzimu kukhala kothekera. Mawu otsatirapowa a mtumwi Petro mokondweretsa akugogomezera mbali ya Mulungu m’kulimbikitsa kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chatu:
“Wodalitsika Mulungu ndiye Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, Iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, mwa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire cholowa chosabvunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu, amene musungidwa ndi mphamvu ya Mulungu mwa chikhulupiriro, kufikira chipulumutso chokonzeka kukabvumbulutsidwa nthawi yotsiriza”—1 Petro 1:3-5.
5. Kodi nchifukwa ninji Akristu a m’zaka za zana loyamba anali ndi chifukwa chabwino chodalitsira Yehova?
5 Akristuwo kwa amene mawu amenewa analunjikitsidwako anali ndi chifukwa chabwino chodalitsira Yehova Mulungu, ndiponse cholankhulira zabwino ponena za iye kapena kumtamanda. Iwo anali atabalidwa kukhala ana a Wam’mwambamwambayo mwa kubadwa kwachiwiri, titero kunena kwake. (Yohane 1:12, 13; 3:5-8) “Kubadwa kwatsopano” kumeneku kunachitika kupyolera mwa kugwira ntchito kwa mzimu woyera kwa iwo. Sikunali monga chotulukapo cha kuyenerera kuli konse kwapadera kwa iwo kwakuti iwo anapangidwa kukhala ana a Mulungu. Kunali chifukwa cha chifundo cha Mulungu kapena kumvera chisoni kusonyezedwa mkukhala kwao okhululukidwa machimo ao. Pamene anakhala ana a Wamphamvuyonse, ophunzira a Yesu Kristu amenewa anapangidwanso kukhala olowa nyumba.
6.Kodi ndi ziti zimene ziri zina za mbali zimene zimapangitsa chiyembekezo Chachikristu kukhala “chamoyo”?
6 Monga olowa nyumba, iwo anali ndi chiyembekezo cha kulandira cholowa. Chiyembekezo chimenecho, monga momwe Petro akusonyezera, chiri “chiyembekezo chamoyo.” Chiri “chamoyo” m’njira yoposa imodzi. Mofanana ndi uthenga wa Mulungu kapena mawu, amene ali “amoyo ndi ochitachita, ” chiyembekezocho chiri chamoyo ndi champhamvu. (Ahebri 4:12) Kwakukulukulu, zimenezi ziri chifukwa chakuti chiri chiyembekezo choperekedwa ndi Mulungu wamoyo ndi wamuyaya, ndipo chazikikwa pa Mwana wake amene ‘sakufanso.’ Mwanayo ali ndi mphamvu ya moyo wosakhoza kuonongeka ndipo ali wokhoza kupulumutsa kotheratu awo omdalira. (Yeremiya 10:10; Habakuku 1:12; Ahebri 7:16, 25; 1 Petro 1:23) Yesu Kristu iye mwiniyo ndiye “mkate wamoyo” wotumizidwa ndi Mulungu ndipo “ngati munthu wina akadyako mkate umene, adzakhala ndi moyo kosatha.” (Yohane 6:50, 51, 57) Mwanayo amapereka “madzi amoyo” amene amakhala mwa awo owalandira “kasupe wa madzi otumphukira ku moyo wosatha.” (Yohane 4:10, 14) Nchimodzimodzinso, ndi “chiyembekezo chamoyo” choperekdwa monga chotulukapo cha “kubadwa kwatsopano” chiri chokhoza kutchitisa okhala nacho kupitirizabe mpaka kukafika kukukwaniritsidwa kwa mphotho yao ndi moyo wamuyaya.
7. Kodi ndi motani mmene “chiyembekezo chamoyo” chimayambukirira wokhala nacho wake?
7 Muli nyonga m’chiyembekezo chimenecho. Ndicho mphamvu yolimbikitsa, yopatsa nyonga m’moyo wa awo amene ali nacho. Chiyembekezo chimenechi chimayambukira moyo wao wathunthu, chimadzipangitsa kukhala choonekera bwino mwa njira imene iwo amagwiritsirira ntchito moyo wao. Mofanana ndi chikhulupiriro chenicheni, chiyembekezo choterocho sichingakhale chakufa, chopanda zipatso, chopanda ntchito zoti zisonyeze kuti chiripo. (Yakobo 2:14-26) Chiri chiyembekezo chokhala ndi mphamvu chimene chimatisonkhezera, ndipo timalimbikitsidwa, kuchirikizidwa ndi kupatsidwa nyonga ndi chitonthozo chake ndi kutsimikizirika kwake kosagwedezeka kwa kukwaniritsidwa.
8. Chifukwa chakuti chiri “chiyembekezo chamoyo,” kodi nchiyani chimene chinganenedwe ponena za kukwaniritsidwa kwake?
8 Pamenepa, mosiyana kwambiri ndi ziyembekezo za awo oika chidaliro chawo mwa anthu opanda ungwiro, omafa, chiyembekezo chimenechi sichiri chakufa chimene chidzagwiritsa mwala chifukwa cha kupanda maziko olimba. Sichingalephere kukwaniritsidwa. Lonjezo la Yehova losasinthika, limodzi ndi mphamvu yake yosayerekezereka yochikwaniritsa, zimatumikira monga maziko otsimikizirika a chiyembekezo Chachikristu.—Yerekezerani ndi Yesaya 55:10, 11; Ahebri 6:13-20.
9. Kodi nchiyani chimene chapangitsa “chiyembekezo chamoyo” chimenechi kukhala chothekera?
9 Mtumwi Petro akugwirizanitsa “chiyembekezo chamoyo” chimenechi ndi “kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu.” Pamene Mwana wa Mulungu anakhomeredwa pa mtengo ndipo ophunzira ake namuona akufa, chiyembekezo chao pa nthawi yomweyo chinafa limodzi naye. Koma pamene umboni wa kuuka kwake unawafika, chiyembekezo chao chinadzutsidwanso, chinakhala ndi moyo watsopano, ‘chinagwirira moto’ ndipo chinawasonkhezera kuchitira umboni. (Luka 24:13-34; Machitidwe 4:20) Chifukwa chakuti iye anaukitsidwira ku moyo wauzimu. Mwana wa Mulungu akanatha kupereka mtengo wa nsembe yake, mtengo woombola, kwa Atate. Yesu Kristu akanapanda kuukitsidwa, palibe ali yense amene akaomboledwa ku uchimo ndi imfa. (1 Akorinto 15:14-19) Pakanakhala popanda chiukiriro chakecho, sipakanakhalanso ‘chiyembekezo chamoyo.”
10. Kodi nchifukwa ninji Petro anatha kutchula cholowa kukhala ‘chosaola, chosadetsedwa ndi chosafota’?
10 Cholowa chabwino kwambiri chimene mtumwi Petro ndi okhulupirira anzake anachiyembekezera chiri “chosabvunda chosadetsa ndi chosafota.” Pokhala chosabvunda, sichingathe kuonongedwa kapena kusakazidwa m’njira iri yonse. Palibe kuipitsidwa kapena kudetsedwa kumene kukagwirizanitsidwa nacho, pakuti sichingathe kupezedwa kupyolera mwa kalinganizidwe kali konse kamachenjera, chinyengo kapena njira iri yonse yosagwirizana ndi lamulo. Cholowa chodabwitsa chimenecho sichidzaperekedwa m’manja mwa anthu opanda makhalidwe abwino. Ndiponse, mosafanana ndi maluwa okongola amene posapita nthawi amataya kukongola kwake ndi kuwala, kwaumuyaya wonse cholowacho sichidzafota konse m’kukhala kwake chabwino kwambiri ndi m’kukondweretsa.
11.Kodi nchifukwa ninji ‘cholowa’cho chiri chosungika ?
11 Malinga ndi kunena kwa mawu a Petro, cholowa cholonjezedwacho ‘chasungidwa mmwamba.’ Chiri chotsimikizirika kwa olowa m’nyumba anzake a Kristu. Kumwambako, icho chiri chotetezeredwa bwino kwambiri ndi chosungidwa bwino kopambana koposa m’sefa iri yonse ya m’banki, chifukwa chakuti miyamba yosaonekayo ndiyo malo ake okhala chikhalire a Mulungu wamuyaya, Yehova. (Salmo 103:19; 115:3, 16; Mateyu 5:11, 12) Ndiponso, mtumwi Petro anasonyeza kuti Wamphamvuyonse akawathandize kulandira cholowa chawo. Wammwambamwambayo mwa njira ya mzimu wake, akasonyeza “mphamvu” yake kwa iwo, akumawathandiza kukhalabe obvomerezeka pamaso pake, akumatetezera zabwino za moyo wao. Chifukwa cha chimenecho, “mu nthawi yotsiriza,” iwo sakagawana nawo m’chiweruzo chachitsutso choperekedwa pa opanda chikhulupiriro koma akapulmutsidwa kaamba ka moyo wosatha.
12. Kodi ndi motani m’mene Yehova Mulungu “adzatitetezerera” kaamba ka chipulumutso?
12 Mofanana ndi Akristu a m’zaka za zana loyamba, okhulupirira onse lero lino angathe kukhala ndi chidaliro chakuti Yehova Mulungu adzawatetezera kaamba ka chipulumutso. Mwa njira ya mzimu wake woyera, iye poyambirira anakupangitsa kukhala kothekera kwa ife kukhala ndi chikhulupiriro ndipo, mwa mzimu umodzimodziwo, iye adzapitirizabe kulimbikitsa chikhulupiriro chathu. Chikhulupiriro chimenechi chingatichititse kupyola mitundu yonse ya ziyeso mwachipambano. (1 Yohane 5:4) Kodi sitiri ndi zifukwa zabwino, panopo, zokhalira othokoza kaamba ka zimene Yehova Mulungu akupitirizabe kuchita kutithandiza kupeza moyo wosatha? Ndithudi, ndipo makamaka pamene tilingalira kuti zimenezi siziri chifukwa cha kuyenerera kwathu kuli konse koma chifukwa cha chifundo chachikulu cha Yehova.
IMFA SINGALETSE KUKWANIRITSIDWA KWA CHIYEMBEKEZO CHATHU
13. Kodi nchiyani chimene chimatsimikiziritsa kuti chiyembekezo chathu Chachikristu chakhazikika pa maziko olimba?
13 Ngakhale imfa singaletse kuona kwathu kukwaniritsidwa kwa chiyembekezo chathu Chachikristu. Zimene Atate wathu wakumwamba anachita mogwirizana ndi Mwana wake zimapereka chitsimikiziritso chotsimikizirika, chosalephera chakuti chiyembekezo chathu chazikidwa pa maziko amphamvu. Mtumwi Petro analemba kuti:
“Amene [Mwana wa Mulungu] anazindikiriratu lisanakhazikike dziko lapansi, koma anaonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi, chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.”—1 Petro 1:20, 21.
14. Kodi ndi motani mmene Yesu Kristu ‘anadziwidwiratu dziko lisanakhazikitsidwe’ ndi kuonetsedwa pa mapeto a nthawi”?
14 Adamu ndi Hava asanakhazikitse dziko la mtundu wa anthu mwa kubala ana, Yehova Mulungu anatsimikizira kuti Mwana wake wobadwa yekha akakhala munthu amene akaombola mtundu wa anthu ku ukapolo wa uchimo ndi imfa. (Yerekezerani ndi Genesis 3:15; 4:1, 2; Luka 11:49 –51.) Pa kudza kwa Mesiya, dongosolo la zinthu Lachiyuda, kuphatikizapo unsembe wake, nsembe ndi mautumiki a pa kachisi, linaolowa m’masiku make otsiriza. Kudza kwa Mesiya kunasonyeza kuyamba kwa nyengo yatsopano m’mbiri ya anthu. Chifukwa cha chimenecho, mtumwi Petro ananena za Kristu kukhala ‘akuonetsedwa pa chitsiriziro cha nthawi.’
15. Kodi nchifukwa ninji Petro ananena kuti Yesu Kristu anaonetsedwa “chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu”?
15 Koma kodi nchifukwa mtumwiyo ananena kuti mwana wa Mulungu anaonetsedwa “chifukwa cha inu amene mwa iye mukhulupirira Mulungu”? Yesu asanadze pa dziko lapansi pano, palibe ali yense akanatha kugwiritsira ntchito mwai wa ntchito ya kuombola imene iye akaichita. Kokha m’zaka za zana loyamba ndi pamene okhulupirira anayamba kutero. Mwa kusonyeza chikhulupiro mwa Kristu, okhulupirira amenewa analinso kukhulupirira Atateyo, Amene anatumiza Mwana ku dziko lapansi. (Yohane 17:21) Ndiponso, monga momwe Petro anafotokozera, zimene Yehova Mulungu anachitira Mwana wake –kumuukitsa ndi kumpatsa “ulemerero” mwa kum’kwezera ku dzanja lakelamanja—zimapereka chifukwa chabwino chokhulupirira ndi kuyembekezera mwa Wamphamvuyonse’yo. Kodi ziri choncho motani?
16. Kodi chiukiriro cha Yesu Kristu chiri chitsimikiziritso cha chiyani?
16 Monga momwedi kuliri kuti Wammwambamwambayo anaukitsa Mwana wake, iye angathenso kuukitsa ena a atumiki ake. Mwana wake, iye angathenso kuukitsa ena a atumiki ake. Popeza kuti Yesu Kristu anaukitsidwira ku moyo wosafa wakumwamba, ophunzira ake a m’zaka za zana loyamba akanatha kukhala otsimikizira kuti nawonso, akagawana naye mu ulemerero wakumwambawo. Kuukitsidwa kwa Mwana wa Mulungu kuli monga chitsimikiziritso chosasinthika chakuti anthu amene agona mu imfa adzaukitsidwira ku moyo.—1 Akorinto 15:12-22.
17. Kodi chiukiriro cha Yesu Kristu chiri chotsimikiziridwa bwino lomwe motani?
17 Ndicho chifukwa chake chenicheni cha chiukiriro cha Yesu chinafunikira kukhala chotsimikiziridwa bwino lomwe, ndipo chinatero. Panali ophunzira okwanira 500 amene anaona Mwana wa Mulungu woukitsidwayo. (1 Akorinto 15:6) Mboni zoona ndi maso zimenezi zinadziwa kuti adani a Mulungu angalande ufulu wao ndipo ngakhale kuwapha ngati iwo anapereka umboni wonena za chozizwitsa chachikulu chimenechi. Komabe, ophunzira okhulupirira a Yesu Kristu anachitira umboni chenicheni chimenechi molimba mtima kwambiri. (Yerekezerani ndi Machitidwe 4:1-3; 7:52-60.) Chikhulupiriro cholimba mtima choterocho chinali chothekera kokha chifukwa chakuti iwo anali ndi umboni wamphamvu wa kuukitsidwa kwake.
KUDZA KWA KRISTU MU ULEMERERO NKOTSIMIKIZIRIKA
18. Kodi nchiyani chimene mtumwi Petro akusonyeza ponena za “mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu”?
18 Monga momwe zinaliri ponena za kuukitsidwa kwa Mwana wake, Yehova Mulungu anatsimikizira kuona kuti umboni wowonekera bwino unaperekedwa ponena za kutsimikizirika kwa kudza kwa Kristu “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:30; Chibvumbulutso 1:7) Mtumwi Petro anati:
“Pakuti sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu otero ochokera ku ulemerero, waukulu. Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lopatulika lija.” (2 Petro 1:16-18)
Kodi Petro pano anali kunena za chochitika chiti?
19. Kodi ndi liti ndipo motani m’mene Petro, Yakobo ndi Yohane anakhalira mboni zoona ndi maso za kusandulika kwa Kristu?
19 Anali kunena za kusandulika kwa Ambuye Yesu Kristu. Nthawi ina pambuyo pa paskha wa 32 C.E., Mwana wa Mulungu anauza ophunzira ake kuti: “Indetu ndinena kwa inu kuti alipo ena a iwo aima pano sadzalawa ndithu imfa, kufikira adzaona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.” (Mateyu 16:28) Patapita masiku owerengeka, mawu a Yesu amenewo anakwaniritsidwa. Atatenga kutsagana naye atumwiwo Petro, Yakobo ndi Yohane, Mwana wa Mulungu anakwera pa phiri lalitari, mwina mwake la Herimoni. Ali pamwamba pa phiri limeneli, zotsatirapozi zinachitika: [Yesu] anasandulika pamaso pao; ndipo nkhope yake inawala monga dzuwa, ndipo zobvala zake zinakhala zoyera mbu ngati kuwala.” Motero atumwi atatuwo anatsimikiziridwa kuti kudza kwa Yesu mu mphamvu ya Ufumu kukakhaladi kwaulemerero. Pamenepo “mtambo wowala unaumbika ndipo munatuluka mawu, akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.” –Mateyu 17:1-5.
20. Kodi nchifukwa ninji kukhulupirira kubweranso kwa Yesu mu mphamvu ya Ufumu kuli ndi maziko amphamvu?
20 Chikhulupiriro m’kudza kwa Yesu mu mphamvu ya Ufumu, chotero, sichinazikidwe pa nthano zonama zopangidwa ndi anthu. Palibe machenjera kapena chinyengo chimene chinalowetsedwamo m’kuyesa kusonkhezera ena kulandira chikhulupiriro chakuti Mwana wa Mulungu akabweranso “ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” Petro, Yakobo ndi Yohane anaona Yesu Kristu akulemekezedwa pamaso pao penipenipo, ndipo iwo anamva mawu a Mulungu mwini akumveka kuchokera mu mtambo wowalawo kapena “ulemerero waukulu.” Mawu amenewa anabvomereza Yesu kukhala Mwana wokondedwa. Kubvomerezako ndi kaonekedwe konyezimira zimene zinaperekedwa kwa iye pa nthawi imeneyo zinalidi kuperekedwa kwa ulemu ndi ulemerero kwa Yesu. Chifukwa cha chibvumbulutso chabwino kwambiri chaumulungu chimenechi chochokera kwa Yehova. Petro moyenerera anatchula phiri kumene kunachitikira kusandulika kuja kukhala “phiri lopatulika.”
21. Kodi masomphenya a kusandulikawo ndi ofunika motani kwa ife?
21 Kodi kusandulika kumeneku kuyenera kukhala ndi tanthauzo lotani kwa okhulupirira? Petro akuyankha kuti: “Ndipo tiri nao mawu a chinenero okhazikika koposa; amene muchita bwino powasamalira, monga nyali younikira m’malo a mdima, kufikira kukacha, nikauka nthanda pa mtima yanu.” (2 Petro 1:19) Inde, masomphenya a kusandulika amamveketsa mawu olosera onena za kudza kwa Ambuye. Yesu Kristu mu mphamvu ya Ufumu. Masomphenya amenewa anapereka kuoneratu ulemerero wake wa ufumu. Ndithudi, kuphatikiza pa mphamvu, ukulu kapena ulemu. Chifukwa cha chimenecho, kusandulikako kumatumikiranso kutsimikizira kutsimikizirika kwa kudza kwa Yesu mu mphamvu.
22, 23. (a) Kodi ndi motani m’mene timasonyezera kuti ‘tikuchita bwino’ m’kumvetsera mawu aulosi? (b) Kodi ndi motani mmene mawu amenewo aliri ngati nyali?
22 Ife lero lino ‘tichita bwino’ kulabadira mawu a ulosi, pakuti palibe chiri chonse chimene chikakhala chofunika kwambiri ku zabwino za moyo wathu, chikakhala ndi mapindu akulu kapena okhalitsa kwambiri koposa chimenecho. Anthu motenthedwa maganizo anagwerenge nyuzi za dziko, kupenda zoneneratu kochitidwa ndi akatswiri a ndale za dziko a za chuma ndi a sayansi ndipo, potsirizira pake, nkupeza kuti sanafike pali ponse. Koma kuunika kowala kuchokera ku mawu a ulosi sikudzatitsogolera ku mseu wogoma kapena kutisiya pa zikwangwami zoloza miseu zosakoneza ndi zoombana ndi mphambano. Chotero mawu olosera amenewa ali oyenera kukhala ndi malo ofunika m’phunziro lathu ndi kusinkhasinkha. Tikakhala anzeru kudzichitisa ife eni kugwiritsira ntchito mwai wa kusonkhana ndi okhulupirira anzathu pamene “mawu’wo” akukambitsiridwa. Koma ‘kumvetsera kwathu’ kumalowetsamo zochuluka koposa kuwerenga mosamalitsa kapena kumvetsera mwaulemu. Kumatanthauza kuchitapo kanthu pa mawu oloserawo, kuwalola kusonkhezera khalidwe lathu, mmene timagwiritsirira ntchito nthawi yathu, nyonga ndi chuma. (Yerekezerani ndi Yakobo 1:22-27.) Inde, ife moyenerera timabvomereza kugwira ntchito kwenikweni kwa mawu olosera amenewo m’moyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndipo sitimangowaona monga kanthu kena kamene timakalingalira chabe mkati mwa nthawi ya kulambira kwa nthawi zonse.
23 Mogwirizana ndi kufulumiza kwa Petro, tiyenera kulola mawu oloserawo kutitumikira monga nyali yowala m’malo a mdima, omaunikira mitima yathu. Ngati ‘timvetsera’ mawuwo ndi kuwalola kutitsogoza m’zinthu zathu zonse za moyo, adzatiyendetsa bwino lomwe mpaka kukafika ku tsiku labwino kwambiri pamene “nthanda,” Ambuye Yesu Kristu, abvumbuluka mu ulemerero wake wonse waukulu. (Yerekezerani ndi Chibvumbulutso 22:16.) Kubvumbuluka kwa Mwana wa Mulungu kudzachititsa chionongeko kwa anthu opanda chikhulupiriro ndi kupereka madalitso abwino kwambiri kwa ophunzira ake odzipereka. (2 Atesalonika 1:6-10) Ndithudi chiyembekezo chimene chiri chogwirizanitsidwa ndi kukwaniritsidwa kwa mawu a ulosi chiyenera kutilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe kuti tipezedwe tiri obvomerezeka pamaso pa Ambuye wathu pa kubvumbuluka kwake.—Luka 21:34-36.
24. Kodi nchifukwa ninji tingakhale ndi chidaliro m’mawu onse olosera amene ali m’Baibulo?
24 Kunena zoona, mawu onse olosera amene ali Malemba Oyera afunikira kulingaliridwa molama maganizo ndi kuloledwa kutsogoza miyoyo yathu. Mkhalidwe weneweniwo wa mawu aulosi, mmene analembedwera, uyenera kutidzaza ndi chidaliro ponena za m’tsogolo Aneneri a Yehova sanaone mikhalidwe ina mu zochitika za anthu kukhala ya mtengo wapatali ndiyeno ndi kupanga zoneneratu mozika pa kumasulira kwa iwo eni zochitika zimenezi. Maulosi sanali malingaliro amene aneneri iwo eniwo anawafikira pambuyo pa kupenda kosamalira mikhalidwe imene inalipo pa nthawiyo. Ayi, aneneriwo anasonkhezeredwa maganizo ao ndi mzimu woyera ndipo anachitisidwa kufotokoza uthenga wa Mulungu. Mtumwi Petro akupitirizabe kuti: “Mudziwa ichi poyamba, kuti palibe ulosi wa malemba umene umachokera m’kutanthauzira kwa munthu mwini kuli konse. Pakuti ndi kale lonse ulosi sunadza mwa chifuniro cha munthu, koma anthu analankhula zochokera kwa Mulungu monga momwe mzimu woyera unawauzirira.” (2 Petro 1:20, 21, NW) Chifukwa chakuti ulosi woona sumachokera kwa anthu okhoza kulakwa koma umachokera kwa Mlengi wathu wa nzeru zonse, timadziwa kuti maulosi onse amene aikidwa m’Mawu a Mulungu adzakwaniritsidwa.
25. Kodi tinganenenji ponena za kutsimikizirika kwa chiyembekezo chathu Chachikristu?
25 Chiyembekezo Chachikristu chazikidwa pa unboni wamphamvu. Mboni zoona ndi maso zodalirika zimatsimikizira kuti anthu amene agona mu imfa adzaukitsidwira ku moyo ndi kuti Yesu Kristu adzasonyeza ulemerero wake ndi mphamvu. Limeneli lidzakhala tsiku labwino kwambiri pamene Ambuye wathu achitapo kanthu kulimbana ndi onse amene amakana kutumikira Mlengi ndi kulanditsa atsatiri ake okhulupirika ku kubvutika konse, akumadzetsa dongosolo latsopano lolungama lopanda matenda zopweteka ndi imfa.—Chibvumbulutso 21:4, 5.