Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • bw mutu 7 tsamba 97-111
  • Alendo ndi Okhala Akanthawi a Khalidwe Labwino Kwambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Alendo ndi Okhala Akanthawi a Khalidwe Labwino Kwambiri
  • Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ‘THAWANI ZILAKOLAKO ZA THUPI’
  • KHALIDWE LABWINO LINGATHANDIZE ENA KULANDIRA KULAMBIRA KOWONA
  • ZIFUKWA ZOSABWEZERERA
  • NJIRA YOPINDULITSA
  • Pitirizani Kukhala Monga “Anthu Osakhalitsa M’dzikoli”
    Nsanja ya Olonda—2012
  • “Mayendedwe Anu mwa Amitundu Akhale Okoma”
    Nsanja ya Olonda—2002
  • Ndife “Osakhalitsa” M’dziko Loipali
    Nsanja ya Olonda—2011
  • Khalani ndi Moyo Moyembekezera Kukwaniritsidwa kwa Lonjezo
    Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
Onani Zambiri
Kusankha Njira Yabwino Koposa ya Moyo
bw mutu 7 tsamba 97-111

Mutu 7

Alendo ndi Okhala Akanthawi a Khalidwe Labwino Kwambiri

1, 2. Kodi ndi motani m’mene alendo amaonedwera, ndipo chifukwa ninji?

MUNTHU amene mwapadera amaoneka kukhala wosiyana kwambiri ndi anthu a m’chitanganya m’chimene iye amakhala kawirikawiri amamkaikira ndi kumdabwa. Khalidwe lake lingakhale likupendedwa mosamalitsa koposa la anthu okhala m’deralo. Momvetsa chisoni, anthu ena angafikire pa kuipidwa maganizo ndi pfuko lonse lathunthu, mtundu kapena pfuko chifukwa cha khalidwe loipa la mlendo mmodzi yekha amene ali m’chitaganya chao. Ngakhale maboma amapanga malamulo ndi maweruzo amene amagwira ntchito kwa alendo okha. Ngati khalidwe la mlendo likulingaliridwa kukhala losayenera, iye angathamangitsidwe.

2 Kodi nchifukwa ninji zonsezi ziri zofunika kwambiri kwa Mkristu? Kodi ndi motani mmene ziyenera kuyambikirira mkhalidwe wake wa moyo?

3. (a) Kodi nchifukwa ninji Akristu oona ali “alendo” m’dziko lino? (b) Kodi ndi motani m’mene osakhulupirira amawaonera, ndipo chifukwa ninji?

3 M’dziko lino, Akristu oona ali “alendo ndi okhala akanthawi,” popeza kuti iwo akuyembekezera malo okhala okhalitsa monga mbali ya “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” zopangidwa ndi Mulungu. (1 Petro 2:11; 2 Petro 3:13) Chifukwa chakuti ophunzira enieni a Yesu Kristu amayesayesa kuganiza ndi kuchita mogwirizana ndi Malemba Oyera, osakhulupirira, kapena awo amene amagonyengezera kukhala akutsatira Chrikristu, angawanyoze monga ngati kuti iwo anali “alendo” osafunika. Koma lingaliro la dziko kulinga kwa Mkristu siliyenera kumpangitsa kulinga kuchita manyazi. Mwa lingaliro la Mulungu, mkhalidwe wake wa kukhala mlendo uli uja wa ulemu. Chifukwa cha chimenecho, Mkristu adzafuna kuchita zonse zimene angathe kudzisungira iye mwini m’njira imene simapatsa ali yense chifukwa choyenera chomtonzera.

4, 5. (a) M’zaka za zana loyamba C.E., kodi nchifukwa ninji mtumwi Petro analankhula za Akristu kukhala “alendo a chibalaliko”? (b) Kodi ndi motani m’mene Yehova Mulungu amawaonera?

4 Polembera okhulupirira anzake, mtumwi Petro anasonyeza kaimidwe kao kolemekezeka monga “alendo ndi okhala akanthawi.” Pachiyambiyambi pomwe pa kalata yake yoyamba, ife timawerenga kuti:

“Petro, mtumwi wa Yesu Kristu, kwa osankhidwa akukhala alendo a chibalaliko a ku Ponto, Galatiya, Kapadokiya, Asiya, ndi Bituniya, monga mwa kudziwiratu kwa Mulungu Atate, m’chiyeretso cha Mzimu, chochitira chimvero ndi kuwaza kwa mwazi wa Yesu Kristu.”—1 Petro 1:1, 2.

5 Kalelo m’zaka za zana loyamba C.E., okhulupirira anadzipeza atabalalitsidwira ku malo osiyanasiyana ndi kukhala pakati pa anthu ochuluka kwambiri osakhala Akristu. Kawirikawiri iwo anali kunyozedwa mosayenera ndi anansi awo. Chotero kuyenera kukhala kunali kulimbikitsa kwa iwo kuwerenga kapena kumva m’mene Yehova anawaonera monga momwe zinalongosoledwera m’kalata ya Petro. Iwo anali kwenikweni ‘osankhidwa’ opatulidwa a Mulungu. Wam’mwambamwambayo anali atawapanga kukhala chuma chake, anthu ake. Kalekale mpingo Wachikristu usanakhaleko wopangidwa ndi Ayuda ndi osakhala Ayuda, Wamphamvuyonse anadziwiratu kuti potsirizira pake pakakhala kagulu koteroko ka atumiki ake obalalikira ku mbali zosiyanasiyana za dziko lapansi. Kupyolera mwa kugwira ntchito kwa mzimu wa Mulungu pa iwo, iwo anapatulidwa kapena kusankhidwira kugwiritsiridwa ntchito mopatulika. Cholinga cha machititdwe a Yehova ndi iwo chinali chakuti iwo akhale ana ake omvera, omachita chifuniro chake. Kuzindikira kwao kugwiritsiridwa ntchito kwao kotereku ndi Mfumu ya M’chilengedwe Chonse ndithudi kuyenera kukhala kutawasonkhezera kwambiri, kukumawachititsa kufuna kukhala ndi moyo mogwirizana ndi chifuno cholemekezeka ku chimene Mulungu anawaika.

6. (a) Kodi ndi motani m’mene Akristu anapezera kaimidwe kawo koyera pamaso pa Mulungu? (b) Kodi nchiyani chimene chingaphatikizidwe ‘m’kukhala kwawo owazidwa ndi mwazi wa Yesu Kristu”?

6 Ndithudi, sichinali chifukwa cha kuyenerera kwa iwo eni kuti okhulupirirawo anafikira kukhala osankhidwa, anthu opatulidwa. Monga anthu, iwo anali ochimwa ndipo anayenera kuyeretsedwa, ndipo chotero mtumwi Petro ananena za iwo kukhala ‘owazidwa ndi mwazi wa Yesu Kristu.’ Zimenezi zikutikumbutsa za njira yoyeretsera ya Mwiisrayeli amene mwamwambo anakhala wodetsedwa, pakati pa zinthu zina, mwa kukhudza mtembo wa munthu. Kuti akhale woyera kachiwirinso, munthuyo anayernera kuwazidwa madzi oyeretsa. (Numeri 19:1-22) Mofananamo, mapindu otetezera machimo a nsembe ya Kristu anali atagwiritsiridwa ntchito kwa Akristu, akumawatheketsa kukhala ndi chikumbu mtima choyera pamaso pa Mulungu ndi kukhala ndi ufulu wa kulankhula m’kumfikira m’pemphero. (Ahebri 9:13, 14; 10:19-22) Ndiponso, pamene Aisrayeli analowetsedwa mu unansi wa pangano ndi Yehova, Mose anawaza anthu mwazi wa nyama zophedwera nsembe. (Eskodo 24:3-8) Chotero, mawu onena za ‘kuwazidwa ndi mwazi wa Yesu Kristu’ angakumbutsenso chenicheni chakuti okhulupirira amenewa anali atalowetsedwa m’pangano latsopano lochitiridwa unkhoswe ndi Yesu Kristu ndi kupangitsidwa kukhala logwira ntchito ndi mwazi wake wokhetsedwa ndi kuti tsopano iwo anali kukhala ndi phande m’mapindu a pangano limeneli.

7. Kodi mkhalidwe wathu wa kukhala “alendo” umafunanji kwa ife?

7 Mofanana ndi okhulupirira a m’zaka za zana loyamba C.E., ophunzira odzipereka a Yesu Kristu lero lino ali ndi kaimidwe kolemekezeka pamaso pa Yehova Mulungu. M’dziko lino iwo ayenera kudzisungira iwo eni monga “alendo” a khalidwe labwino ndi “okhala akanthawi.” Atapanda kutero, amadzetsa chitonzo pa Yehova Mulungu ndi mpingo wa anthu ake. Chifukwa cha chimenecho, onse afunikira kukumbukira chilangizo cha mtumwi Petro: “Okondedwa, ndi kudandaulirani ngati alendo ndi ogonera mudzikanize zilakolako za thupi zimene zichita nkhondo pa moyo.”—1 Petro 2:11.

8. Kodi ife sitiyenera kudzikola mosayenera kugwirizanitsidwa mosayenera ndi chiyani, ndipo chifukwa ninji?

8 Chifukwa cha kukhala ‘alendo ndi okhala akanthawi’ m’dongosolo la zinthu limene likupitali, sitingathe kudzilola ife eni kugwirizanitsidwa mosayenera ndi chiri chonse chopanga dongosolo limene liripo pa tsopano lino lopangidwa ndi anthuli. Palibe zigwirizano za pa dziko lapansi, zisoni, zisangalalo kapena chuma zimene ziri zachikhalire. Nthawi ndi zochitika zodzidzimutsa zimagwera anthu onse ndipo zingathe kusintha mikhalidwe ya munthu mwadzidzidzi ndi mokulira kwambiri. (Mlaliki 9:11) Chotero, muli nzeru yeniyeni m’kulabadira uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Iwo akukhala nawo akazi akhale monga ngati alibe; ndi iwo akulira, monga ngati salira, ndi iwo akukondwera, monga ngati sakondwera; ndi iwo akugula monga ngati alibe kanthu; ndi iwo akuchita nalo dziko lapansi, monga ngati osachititsa; pakuti maonekedwe a dziko iri apita.” (1 Akorinto 7:29-31) Kwa ife kumwerekera kotheratu m’zisoni kapena zisangalalo zimene ziri zipatso za mikhalidwe ndi maunansi zomasintha nthawi zonsezi kungachite mosemphana ndi kuyandikira kwathu pafupi kwambiri kwa Wam’mwambamwambayo ndi Mwana wake, ndi kutayikiridwa koopsa kwa ife eni.

9, 10. (a) Kodi nchiyani chimene chiri kanthu ponena za m’mene anthu audziko amalingalirira chuma? (b) Kodi nchifukwa ninji lingaliro lathu lonena za chuma liyenera kukhala losiyana ndi lija la osakhulupirira?

9 Mkhalidwe wa unyinji wa mtundu wa anthu umasonyeza moonekera bwino chifukwa chake sitiyenera kuyesa ‘kugwiritsira ntchito dziko mokwanira,’ Anthu mwachisawawa ali kaya osazindikira malonjezo a Mulungu a “miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano” kapena alibe chikhulupiriro chenicheni m’dongosolo latsopano lirinkudza lolungama limenelo. Chotero alibe kanthu kena kusiyapo moyo wawo wa tsopano lino pa kamene iwo angasumikepo maganizo. Iwo alibe chiyembekezo champhamvu ponena za mtsogolo. Ndicho chifukwa chake iwo ali odzipereka kotheratu ku kuganiza za zosowa zao za tsiku ndi tsiku ndipo amafuna kupeza zochuluka monga momwe angathere kuchokera ku dziko. (Mateyu 6:31, 32) Maso awo amayeretsedwa ndi chiyembekezo cha kupeza zobvala zabwino, zingwinjiri ndi ndolo zonyezimira, zokometsera za mtengo wapatali, mipando yokongola kapena nyumba zabwino kopambana. Iwo angayembekezere ndi kufunafuna kuchititsa ena kaso mwa njira ya chuma chakuthupi.—1 Yohane 2:15-17.

10 Mosiyana, Mkristu, amazindikira kuti mtsogolo mwamuyaya muli patsogolo pake. Kukakhala kupusa kwa iye kukhala womwerekera kwambiri ndi zochitika za moyo kwakuti iye alibiretu nthawi yoperekedwa kwa Mlengi pa amene mtsogolo mwake mumadalira. Izi sizikutanthauza kuti atumiki oona a Mulungu sangasangalale moyenera ndi zochuluka za zinthu zabwino kwambiri zimene ndalama zingathe kugula. Koma ngakhale zosangalatsa zabwino ndi chuma chakuthupi chopindulitsa siziyenera kukhala posumikapo maganizo pa moyo wathu, sizidzatero ngati timadziona kwenikweni kukhala “okhala a kanthawi” m’dongosolo liripoli. Pamene sitikukhala omwazamwaza kapena osasamala ndi chuma chathu, ife moyenerera timachiwerengera kwambiri monga momwe amachitira anthu odalirika amene amangobwereketsa chipinda chokhala ndi zonse, zipangizo, ziwiya kapena zinthu zina zimene iwo angafune. Anthu oterowo amasamalira zimenezi bwino lomwe koma samaikapo mtima wao monga ngati kuti chinali chuma chachikhalire. Moyo wathu uyenera kusonyeza kuti timazindikira kuti palibe chiri chonse m’dongosolo liripoli chimene chimapereka chitsimikiziro cha kukhalitsa, kuti ife tiri “alendo” ndi “okhala a kanthawi” chabe, tikupita patsogolo kumka ku dongosolo latsopano lolonjezedwa lopangidwa ndi Mulungu.

‘THAWANI ZILAKOLAKO ZA THUPI’

11. Kodi nchiyani chimene chikaphatikizidwa m’zilakolako za thupi zimene ife tiyenera kuzipewa?

11 Komabe, kuti njira yathu ya moyo ikhale yopambana monga Akristu, zochuluka kwambiri zikufunidwa kwa ife koposa kuzindikira chabe kuti, ponena za moyo wathu pa tsopano lino m’dziko lino, mikhalidwe yathu iri yokhoza kugweredwa ndi kusintha kwamwadzidzidzi. Tifunikiranso kulingalira mwamphamvu chidandauliro cha Baibulo cha ‘kuthawa zilakolako za thupi.’ Zimenezi ziri zikhumbo kapena zilakolako m’ziwalo za thupi la munthu. Kalata ya mtumwi Paulo kwa Agalatiya imabvumbula machimo amene zikhumbo zolakwa zimenezi zimawasonkhezera. Atatha kusonyeza kuti munthu amene akutsogozedwa ndi mzimu wa Mulungu samachita ‘chikhumbo chiri chonse cha thupi,’ mtumwiyo akundandalika ntchito za thupi-”dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere.”—Agalatiya 5:16, 19-21.

12, 13. (a) Kodi ndi motani m’mene zilakolako za thupi’ zimamenyanira ndi moyo’? (b) Kodi nchiyani chimene tiyenera kuchita kuti tisungebe kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu?

12 Chifukwa cha uchimo wa cholowa, timakhala ndi zitsenderezo zamphamvu za kulowetsedwa m’ntchito za thupi, ‘kukwaniritsa zilakolako za thupi,’ Zikhumbo zoipazo ziri ngati gulu lankhondo loukira limene likufunafuna kulamulira pa moyo wonse, munthu yense wathunthu, kumchititsa kugonjera ku kuchita zikhumbo zochimwa. Mtumwi Wachikristu Paulo anali wozindikira bwino kwambiri za nkhondo imene ingakhalepo mwakutero m’kati mwa munthuyo. Ponena za chochitika cha iye mwini, iye analemba kuti: “Ndidziwa kuti mwa ine, ndiko kuti, m’thupi langa, mulibe chabwino chikhalamo; pakuti kufuna kulimo mwa ine, koma kukhoza kuchita chimene chiri chabwino mulibe. Pakuti chabwino chimene ndikufuna kuchita, sindichichita, koma choipa chimene sindichifuna ndicho chimene ndimachitchita.” (Aroma 7:18, 19, NW) Nkhondo imeneyi inakupangitsa kukhala kofunika kwa Paulo ‘kupumpuntha thupi lake ndi kuliyesa kapolo, kuti atatha kulalikira ena, iye asakhale wosabvomerezedwa mwa njira ina.’ —1 Akorinto 9:27, NW.

13 Mofananamo, chikhumbo chathu cha kusunga kaimidwe kabwino pamaso pa Mulungu ndi kulandira dalitso lake chidzatisonkhezera kupanga kuyesetsa mwamphamvu kotero kuti zikhumbo zolakwa ziri zonse zikuletsedwa. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kupangitsa nkhondoyo kukhala yobvuta kwambiri kupyolera mwa kumwerekera m’zosangalatsa, zowerenga, mayanjano ndi mikhalidwe zimene ziri zotsimikizirika kusonkhezera ndi kukulitsa chitsenderezo ku zikhoterero zathu zochimwa? Chofunikanso kwambiri, tifunikira kutenga masitepe otsimikizirika kudzitetezera ife eni. Kuli bwino kukumbukira kuti sitingathe kupambana m’nyonga yathu ya ife eni koma tifunikira chilimbikitso cha abale athu odzipereka ndi chithandizo cha mzimu wa Mulungu. Mtumwi Paulo anafulumiza Timoteo “kulondola chilungamo, chikhulupiriro, chikondi, mtendere, limodzi ndi awo amene amaitanira pa Ambuye ndi mtima woyera.” (2 Timoteo 2:22, NW) Ngati zimenezi ndizo zimene tikuchita, pamenepo, mwa chithandizo cha mzimu woyera, tingathe kupambana m’kuletsa zikhumbo zolakwa kupeza chipambano pa ife. Motero, kukaniza kwathu zilakolako za thupi mwa kuchititsa maganizo athu kusumikidwa pa chimene chiri choona, cholungama, choyera, chokondedwa, choyenera ndi chotamandika kudzatitetezera ku kukhala osabvomerezedwa ndi Mulungu. (Afilipi 4:8, 9) Pambuyo pa kuyesayesa kuthandiza ena kupambana, ife enife sitidzakhala olephera.

KHALIDWE LABWINO LINGATHANDIZE ENA KULANDIRA KULAMBIRA KOWONA

14. Kodi ndi motani m’mene ena angapindulire mwa kutiona ‘tikupewa zilakolako za thupi’?

14 ‘Kuthawa kwathu zilakolako za thupi’ kumatsagana ndi phindu lina labwino kopambana. Mtumwi Petro analemba kuti: “Sungani khalidwe lanu labwino pakati pa amitundu, kuti, m’chinthu chimene iwo akunenerani ngati ochita zoipa, chifukwa cha ntchito zanu zabwino zimene iwo ali mboni zowona ndi maso akalemekeze Mulungu m’tsiku la kuyang’anira kwake.”—1 Petro 2:12, NW.

15. Kodi Akristu ananamiziridwa m’njira yotani m’zaka za zana loyamba C.E.?

15 M’zaka za zana loyamba, Akristu kawirikawiri anali kumvedwa molakwa, kusonyezedwa kukhala “ochita zoipa.” Chitsanzo chinali zisulizo zonga ngati zotsatirapozi: “Anthu awa avuta kwambiri mudzi wathu, . . . ndipo alalikira miyambo imene siiloleka ife kuilandira, kapena kuichita, ndife Aroma.” (Machitidwe 16:20, 21) ‘Anthu awa asanduliza dziko lokhalamo anthu.’ ‘Iwo achita zokana malamulo a Kaisara; akumanena kuti pali mfumu yina, Yesu.’ (Machitidwe 17:6,7, NW) Mtumwi Paulo anasulizidwa za kukhala “mliri, ndi woutsa mapanduko kwa Ayuda onse m’dziko lonse lokhalamo anthu.” (Machitidwe 24:5) Akulu akulu a mwa Ayuda okhala m’Roma anauza Paulo kuti: “Pakuti za mpatuko uwu, tidziwa kuti aunenera ponse ponse.”—Machitidwe 28:22.

16. (a) Kodi chitetezo chabwino kopambana cha Akristu oona ku kunamiziridwa nchiyani? (b) Kodi ndi motani m’mene zimenezi zingathandizire otsutsa?

16 Chinjirizo labwino kopambana lolimbanira ndi kuneneredwa monama koteroko ndiro khalidwe labwino. Pamene Akristu adzitsimikizira iwo eni kukhala osunga lamulo, akhoma misonkho mokhulupirika, asonyeza kufunitsitsa kuchita ‘ntchito iri yonse yabwino,’ ndipo pa ntchito zao za iwo eni ali ogwira ntchito mwakhama, oona mtima m’machitidwe ao, ndipo amasonyeza kudera nkhawa kwenikweni ndi thanzi la anthu anzawo-zinenezo zonenedwa motsutsana nawo zimasonyezedwa kukhala zonama. (Tito 2:2-3:2) Ngakhale anthu amene abwereza chidziwitso chojeda ponena za Akristu angathandizidwe motero kuona kulakwika kwa njira yao ndi kusonkhezeredwa kubvomereza kulambira kowona. Pamenepo, pa nthawi ya kuyang’anira kwa chiweruzo kwa Mulungu, oneneza monama apapita oterowo a Akristu angakhale pakati pa awo amene akulemekeza kapena kutamanda Wammwambamwamba.

17. Polingalira chiyambukiro chabwino cha khalidwe labwino pa openyerera, kodi nchiyani chimene tiyenera kuchilingalira mwamphamvu?

17 Chenicheni chakuti kukhala ndi moyo wolungama kwa Mkristu kungathe kukhala mphamvu yaikulu kwambiri ya chabwino chiyenera kutipangitsa kuganizira mwamphamvu ponena za njira imene ife timachitira ndi ena ndi ukulu umene tikusonyeza nawo chikondwerero mwa anansi athu. Ndithudi sitimafuna kudzichititsa kusaona zosowa za anthu okhala pafupi nafe. Ndi zoonadi, kukhala kwathu okoma mtima, ofunitsitsa kuthandiza ndi anansi odekha siziri “njira yochitira zinthu” chabe. Ndiwo maziko a kukhala kwathu Akristu. Mu Ulaliki wake wa Paphiri, Yesu Kristu analangiza kuti: “Zinthu ziri zonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero.” (Mateyu 7:12) Malemba amatifulumiza kuti: “Monga tiri nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.” (Agalatiya 6:10) “Ngati nkutheka monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) “Nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.”—1 Atesalonika 5:15.

18, 19 Mogwirizana ndi 1 Petro 3:8, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chowona ponena za makhalidwe ndi machitidwe athu monga Akristu?

18 Mwachionekere, kukhala Mkristu kumaphatikizamo zoposa kungochita zofunika zazikulu zoterozo monga ngati kufika pa misonkhano limodzi ndi okhulupirira anzathu ndi kuuza ena zoona za Baibulo. (Mateyu 28:19, 20; Ahebri 10:24, 25) Tikulamulidwanso kutsanzira Mwana wa Mulungu m’mikhalidwe yathu ndi machitidwe, m’chimene ife tiri monga anthu, anthu ali yense payekhapayekha. Mtumwi Petro analemba kuti: “Chotsalira, khalani nonse a mtima umodzi, ochitirana chifundo, okondana ndi abale, achisoni, odzichepetsa.” (1 Petro 3:8) Kukhala a “mtima umodzi,” kumafunikira kuti “mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.” (1 Akorinto 1:10) Kuganiza kwathu kuyenera makamaka kugwirizana ndi kwa Yesu Kristu amene anasonyeza chikondi chake mwa kupereka moyo wake kaamba ka ife. (Yohane 13:34, 35; 15:12, 13) Pamene kuli kwakuti ophunzira a Yesu Kristu ali ndi “mtima umodzi,” monga momwe kukuonekerera mwa chikondi chao ndi umodzi pa dziko lonse, mafunso amene ife ali yense payekha tiyenera kuyankha ndiwo: “Kodi ine moona mtima ndikuthandizira mzimu umenewu wa umodzi ndi chikondi? Motani, ndipo ku mlingo wotani?’

19 Ngati ife timakonda kwenikweni abale athu auzimu, tidzakhala okoma mtima ndi okhululukira. Chobvuta chitakambitsiridwa ndipo chothetsera nachibvomerezedwa, sitizapitirizabe kusunga nkhani kukhosi ndi kupewa dala ziwalo zina za mpingo Wachikristu zimene zinathandizira kupanga bvutolo. Mogwirizana ndi uphungu wa Petrowo, tifunikira kuchenjerera kuti tisagwere m’kukhala ouma mtima, aukali ndi kunyada kumene kuli kofala m’dziko. Ena ayenera kukhala okhoza kuona kuti tiri ndi ‘kumvera chifundo ena’ kapena kumvera chisoni awo amene akubvutika, kuti ife tiri ndi chikondi chosangalala kapena chikondano kwa abala athu auzimu, kuti ife tiri “omvera chisoni mwachikondi” kapena oyedzamira ku kusonyeza kumvera chisoni, ndi kuti tiribe lingaliro la kudzikweza koma tiri “odzichepetsa m’maganizo,” ofunitsita kutumikira ena.—Yerekezerani ndi Mateyu 18:21-35; 1 Atesalonika 2:7-12; 5:14.

20. Kodi kulabadira uphungu wa 1 Petro 3:9 kumafunanji kwa ife?

20 Ndiponso, sitiyenera kulekezera kusonyeza kwathu kumvera chifundo, kumvera chisoni ndi kukoma mtima kwa okhulupirira anzathu okha. (Luka 6: 27-36) Mtumwi Petro anapitirizabe kufulumiza Akristu ‘kusabwezera choipa ndi choipa kapena kutukwana ndi kutukwana, koma, mosemphana, kudalitsa.’ (1 Petro 3:9) Zimenezi sizikutanthauza kuti tidzatamanda anthu amene atibvulaza ndi kutitukwana kapena kuwachitira zosonyeza chikondi zochuluka. Koma tidzachita zabwino kopambana ndi kukhala ndi mtendere wa maganizo waukulu kopambana ndi chimwemwe ngati tipitirizabe kukhala okoma mtima ndi olingalira m’machitidwe athu ndi iwo, tikumayembekezera kuti iwo angathe kusintha njira zao ndi kukhala olandira madalitso a Mulungu.

ZIFUKWA ZOSABWEZERERA

21. Kodi ndi motani m’mene chitsanzo cha Yehova chingatithandizire m’kusabwezera?

21 Chenicheni chakuti Yehova Mulungu mwachifundo watikhululukira machimo athu pa maziko a nsembe ya Yesu chiyenera kutisonkhezera kuchitira ngakhale adani athu mu mkhalidwe wokoma mtima, womvera chisoni. Yesu Kristu anati: “Ngati simukhululukira anthu zolakwa zawo, ngakhale Atate wanu wakumwamba sadzakukhululukirani zolakwa zanu.” (Mateyu 6:15, NW) Chotero, kulandira kwathu madalitso osatha kuchokera kwa Mulungu kumayambukiridwa ndi kufunitsitsa kwathu kudalitsa ena. Yehova Mulungu amatilola kukumana ndi kuchitiridwa mopanda kukoma mtima. Pakati pa zifukwa zochititsa chimenechi pali chija chakuti tikhale ndi mwai wa kusonyeza kuti ife tiri okhulukira ndi omvera chisoni kwa anthu anzathu. Mtumwi Petro anasonyeza lingaliro limeneli mwa kupitirizabe kunena kuti: “Kudzatsata ichi [cha kudalitsa awo amene amafuna kukubvulazani] mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.” (1 Petro 3:9) Uku sindiko kunena kuti Atate wathu wakumwamba amafuna kuti ena atibvulaze. Iye wangochita chabe kuti iye sanalowemo kuimitsa kubvutitsidwa kwathu ndi zobvuta za anthu ochimwa okhala m’dziko lochimwa. Ndipo kumeneku kumatilola kusonyeza kaya ngati tikufuna kukhala ngati iye kwenikweni—achifundo, omvera chisoni ndi okhululukira.

22. Kodi Salmo 34:12-16 limapereka chilimbikitso chotani ponena za kupewa mzimu wa kubwezera?

22 Popitirizabe chilimbikitso chake cha kusabwezera m’mawu kapena m’zochita, Petro akugwira mawu Salmo 34:12-16 ndipo akulemba kuti:

“Pakuti, iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola. Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lawo; koma nkhope ya Ambuye iri pa ochita zoipa.”—1 Petro 3:10-12.

23, 24. (a) Kodi kumatanthauzanji kwa ife “kukonda moyo” ndi kufuna “kuona masiku abwino”? (b) Kodi ndi motani m’mene timapindulira mwa kusonyeza kukonda moyo?

23 Mawu a Petro amenewa akugogomezera kuti kuchitira anthu onse mokoma mtima ndiyodi njira yokha yoyenera yokhalira ndi moyo, njira yabwino kopambana yokhalira ndi moyo. Munthu amene ‘amakonda moyo,’ akumauyamikira monga mphatso yochokera kwa Mulungu, ndi amene amafuna “kuona masiku abwino”—masiku amene amampatsa lingaliro la chifuno ndi tanthauzo m’kukhala ndi moyo- amasonyeza zimenezi mwa kupititsa patsogolo chimwemwe cha anthu anzake. Iye amalamulira lirime lake, osaligwiritsira ntchito kunyozetsa, kutukwana, kunyenga kapena kukwangwanutsa ena. Chikhumbo chake ndicho kupewa kuipa konse ndi kuchita chimene chiri chabwino mwa lingaliro la Mulungu. Monga munthu amene akufunafuna ndi kulondola mtendere, iye sadzakhala woputa ena kapena wandeu koma adzapanga kuyesayesa kwamphamvu kupititsa patsogolo maunansi abwino ndi ena ndi pakati pa ena.—Aroma 14:19.

24 Munthu amene amasonyeza kukonda kwake moyo nwa kuthandiza ena kusangalala ndi chimwemwe ndi mtendere anadzipangitsa iye mwini kukhala munthu wabwino kuyenda naye. Ena amasonyeza mwa mawu ao ndi zochita kuti iwo amamlingalira kukhala wofunika, wofunidwa ndi woyamikiridwa. Chifukwa cha chimemecho, moyo wake sudzakhala konse wopanda pake kapena wopanda tanthauzo.—Miyambo 11:17, 25.

25. Kodi nchifukwa ninji tingakhale otsimikizira ponena za chisamaliro cha chikondi cha Mulungu ndi chithandizo?

25 Ngakhale kuli kwakuti kukoma mtima kwake sikungalandiridwe nthawi zonse mwachiyamiko, munthu woteroyo amatsimikiziridwa za chisamaliro chachikondi cha Yehova Mulungu. Popeza kuti maso a Wammwambamwambayo ali pa olungama ndipo makutu ake nthawi zonse ali acheru kuwamva, iye amadziwa zimene ziri kwenikweni zosowa zawo ndipo angayankhe mwansanga kukwaniritsa zimenezi. Iye adzawachititsadi kuona “masiku abwino,” pakuti kudzipereka kwaumulungu kumene iwo amasonyeza “kuli ndi lonjezo la moyo tsopano ndi uja umene ulinkudza.” (1 Timoteo 4:8, NW) Ku mbali ina, awo amene amachita chimene chiri choipa—amene samagwira ntchito kaamba ka mtendere ndi chimwemwe cha ena—sangayembekezere kusonyezedwa chibvomerezo cha Mulungu. “Nkhope” ya Mulungu iri yotsutsana nawo limodzi ndi chiweruzo chachitsutso, pakuti palibe chiri chonse chimakhala chosaonedwa ndi iye.

NJIRA YOPINDULITSA

26. Malinga ndi kunena kwa mawu a Petro, kodi ndani amene angafune kutiona tikubwerera ku machitachita oipa a dziko?

26 Kukumbukira nthawi zonse mapindu amene amachokera m’khalidwe labwino kudzatithandiza kukaniza zitsenderezo za kulowetsedwa m’machitachita oipa a dziko. Mtumwi Petro akutipatsa chilimbikitso champhamvu kulinga ku zimenezi, pamene akunena kuti:

“Nthawi yaiptayi idatifikira kuchita chifuno cha amitundu, poyendayenda ife m’kukhumba zonyansa, zilakolako, maledzero, madyerero, mamwaimwa, ndi kupembedza mafano kosaloleka; m’menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nawo kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano; amenewo adzamwerengera Iye wokhala wokonzeka kuweruza amoyo ndi akufa. Pakuti chifukwa cha ichi walalikidwa Uthenga Wabwino kwa iwonso adafawo, kut akaweruzidwe monga mwa anthu m’thupi, koma akakhale ndi moyo monga mwa Mulungu mumzimu.”—1 Petro 4:3-6.

27. Kodi nchifukwa ninji sitiyenera konse kufuna kubwerera ku dziko loipa?

27 Nthawi imene Mkristu angakhale ataonongera m’kukhutiritsa zikhumbo zake zochimwa ndi zilakolako pamene anali wosadziwa chifuniro cha Mulungu ndi chifuno ndithudi iyenera kukhala yokwanira kwa iye osafunanso konse kubwerera ku moyo wosonyezedwa ndi kupambanitsa ndi kupanda kudziletsa kwa makhalidwe. Sitimafuna konse kuiwala m’mene moyo wa kudzikhuritsa uliri wopanda pake ndi wopanda tanthauzo, ndi manyazi amene amatsagana nawo. (Aroma 6:21) Zosangalatsa zonyansa, zoipa, kubvina konyansa ndi kopenga, nyimbo zodzutsa chilakolako, zimene zakhala zochuka kwambiri m’dziko, ziyenera kutichititsa kuipidwa, osati kutikopa. Pamene kuli kwakuti sikungakhale kosabvuta kuneneredwa mwano ndi atsamwali apapitapo chifukwa chakuti timapewa zinthu zoterozo, ife ndithudi tiribe kanthu kali konse kokapindula mwa kugwirizana nawo m’mapwando ao openga ndi njira yao ya moyo yosadziletsayo. Koma timataya zochuluka mwa kutengera mkhalidwe wa dziko. Onse ochita chimene chiri choipa ayenera kudziyankhira pa mlandu chifukwa cha zoipa zawo pamaso pa Yesu Kristu, munthu amene Yehova Mulungu wamuika kuweruza amoyo ndi akufa. (2 Timoteo 4:1) Chifukwa chakuti chiweruzo chimenechi chiri chotsimikizirika, “mbiri yabwino” inalengezedwa kwa “akufa,” ndiko kuti, kwa akufa mwauzimu amene anafunikira kulapa, kutembenuka ndi kukhala amoyo mwa lingaliro la Mulungu mwa kugwiritsiridwa ntchito kwa mapindu otetezera machimo a nsembe ya Kristu kwa iwo.

28. (a) Kod nchifukwa ninji Akristu ‘angalingaliridwe monga mwa thupi mwa lingaliro la anthu”? (b) Kodi nchifukwa ninji kulingaliridwa koteroko sikuyenera kutibvutitsa maganizo?

28 Awo amene alapa amakhaladi a mtengo wapatali m’maso mwa Yehova Mulungu, ndipo iye amafuna kuti iwo asangalale ndi kukhala ndi moyo kwa chimwemwe kwamuyaya. Komabe, anthu a dziko lino, samazindikira kaimidwe kabwino kamene Akristu ali nako ndi Mlengi. Anthu audziko oterowo amaona ophunzira a Kristu monga momwe amaonera anthu ena ndi kuwalingalira “monga mwa thupi,” mwa kaonekedwe kakunja. Komabe, chenicheni chakuti kutilingalira kwao kuli kosayenera sikuyenera kutibvutitsa maganizo. Chimene chiri kanthu kwenikweni ndicho kaya ngati Yehova Mulungu akutilingalira kukhala ‘amoyo monga mumzimu,’ ndiko kuti, kukhala ndi miyoyo yauzimu. Zidzakhala choncho ngati moyo wathu upitirizabe kukhale wogwirizana ndi malamulo a Wammwambamwambayo.

29. Kodi ndi zifukwa zabwino zotani zimene tiri nazo zosungira khalidwe labwino?

29 Tiridi ndi chifukwa chabwino chosungira khalidwe labwino monga “alendo ndi okhala akanthawi” m’dongosolo liripoli. Wammwambamwambayo amakulamula. Chitsanzo cha iye mwini cha kuchita nafe mokoma mtima, kuchita mwachifundo ndi ife chimafuna kuti ife tikhale olingalira bwino, omvera chisoni ndi okhululukira m’machitidwe athu ndi ena. Khalidwe lathu loyamikirikalo limasonyeza bwino Mulungu wathu ndipo lingathandize ena kukhala atumiki ake. Kokha mwa kusunga khalidwe labwino tingathe kupitirizabe kukhale ndi dalitso la Yehova ndipo potsirizira pake kulandira moyo wamuyaya m’malo okhala achikhalire. Palibe njira ina iri yonse ya moyo imene iri yopindulitsa kwambiri pa tsopano lino ndi imene iri ndi lonjezo labwino kwambiri loterolo kaamba ka mtsogolo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena