Mutu 9
Amuna Amene Angakuthandizeni Kuchita Bwino
1, 2. (a) Pamene takumana ndi nsautso, kodi nchiyani chimene timafuna kuchokera kwa ena? (b) Mu mpingo Wachikristu, kodi ndani kwenikweni amene angachipereke?
LIWU lolimbikitsa m’nthawi ya nsautso, dzanja lothandiza pamene bvuto likuopseza- ha, ndi dalitso lotani nanga m’mene zimenezi zingakhalire! Chifukwa chakuti pamakhala kubuka kwa zopinga kuchinga njira yathu pamene tikuyenda kumka ku chonulirapo chathu cha moyo wosatha, chithandizo choterocho chiridi chofunika kwambiri. Ndithudi liri dalitso kuti mu mpingo Wachikristu muli abale achikulire okhulupirika amena angathe kupereka chilimbikitso chochuluka ndi chitonthozo zofunikazo.
2 Baibulo limanena za “abusa” amena kukhala “mphatso za anthu” zimene Yesu Kristu wapereka kaamba ka kulimbikitsidwa kwa mpingo m’chikondi. (Aefeso 4:7-16) Chifukwa cha chimenecho, ngati pa nthawi iri yonse mutaona kuti inu mukufooka m’chikhulupiriro, muli obvutika maganizo, osokonezeka kapena ngakhale achisoni chifukwa cha zobvuta kapena ziyeso, muyenera kufikira akulu odziperekawo kuti akuthandizeni kuti muumirire ku chosankha chanu cha kukhalabe ophunzira obvomerezeka a Mwana wa Mulungu.
3. Kod ndi chilangizo chotani chimene chikuperekedwa kwa akulu pa 1 Petro 5:1-3?
3 Kupenda zimene mtumwi Petro analemba kwa akulu kumasonyeza bwino lomwe mmene izo zingakhalire chithandizo chopatsa nyonga kwa inu ndi chifukwa chake. Timawerenga kuti:
“Kwa akulu pakati panu ndikupereka chidandauliro ichi, pakuti ine nanenso ndine mkulu limodzi ndi iwo ndi mboni ya mabvuto a Kristu, wokhala ndi phande ngakhale wa ulemerero umene uyenera kubvumbulutsidwa: Wetani gulu la nkhosa la Mulungu limene liri m’manja mwanu, osati mokakamizika, koma mofunitsitsa; osati kaamba ka chikondi cha phindu losawona mtima, koma mwachangu; osati monga ochita umbuye pa awo amene ali cholowa cha Mulungu, koma okhala zitsanzo za gulu la nkhosalo.”—1 Petro 5:1-3, NW.
4. Kodi ndi motani kanenedwe ka Petro kakusonyezera kuti iye sanadzikweze pamwamba pa akulu amene iye anali kuwalembera kalatawo?
4 Tingathe kukhala osangalala kuti pali amuna Achikristu amene amafuna kuchita mogwirizana ndi uphungu wa mtumwi Petrowo. M’kupereka chithandizo chauzimu kwa ziwalo za mpingo, iwo amapereka chithandizocho mu mzimu wofanana ndi uja umene unasonyezedwa ndi mtumwiyo. Kukuonda Mulungu ndi abale awo kumawasonkhezera. Onani kuti Petro sanadzikweza yekha pa akulu amene iye anali kuwadandaulira kapena kuwalimbikitsa. Iye ananena za iye mwini kukhala “mkulu limodzi nawo,” ndiko kuti, monga ‘mkulu mnzawo.’ Mtumwiyo motero anadzitcha iye mwini mbale amene anali ndi kumvetsetsa komvera chisoni mkhalidwe wao monga akulu mu mpingo. Kaimidwe ka maganizo ka kumvera chisoni koteroko m’kuchita ndi okhulupirira anzake kamapangitsa mkulu kukhala dalitso lenileni kwa abale ake.
5. Kod ndi motani m’mene Petro analiri “mboni ya mabvuto a Kristu”?
5 Mawu a Petro akusonyezanso kuti iye anazindikira thayo lolemera limene linali litaikiziridwa pa iye. Iye anadzidziwikitsa iye mwini kukhala “mboni ya mabvuto a Kristu, wokhala ndi phande ngakhale wa ulemerero umene uyenera kubvumbulutsidwa.” Petro anadziwa mwachindunji za mmene Mwana wa Mulungu anatukwaniridwa, kumenyedwa ndipo potsirizira pake kukhomeredwa pa mtengo. Iye anali wopenyerera wachindunji ndipo anaona Yesu Kristu woukitsidwayo ndi kukwera kwake kumwamba. Ndipo m’kalata yake yachiwiri iye akunena kuti:
“Sitinatsata miyambi yachabe, pamene tinakudziwitsani mphamvu ndi maonekedwe a Ambuye wathu Yesu Kristu, koma tinapenya m’maso ukulu wake. Pakuti analandira kwa Mulungu Atate ulemu ndi ulemerero, pakumdzera Iye mawu otere ochokera ku ulemerero waukulu, Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene Ine ndikondwera naye; ndipo mawu awa ochokera Kumwamba tidawamva ife, pokhala pamodzi ndi Iye m’phiri lija.”—2 Petro 1:16-18; yerekezerani ndi Mateyu 16:28-17:9.
6. Kodi ndi motani m’mene akulu amene Petro anawalembera anali ndi chifukwa chabwino cholabadirira mawu ake?
6 Nidthudi, akulu amene Petro analunjikitsako chilimbikitso chake anali ndi chifukwa chabwino cholabadirira mawu a mkulu mnzawo amene anatha kunena za iye mwini kukhala ‘mboni ya kubvutika kwa Kristu ndi wokhala ndi phande mu ulemerero umene uyenera kubvumbulutsidwa.’ Sikokha kuti mtumwiyo anawosonkhezera mu mkhalidwe wodzichepetsa koma chitsanzo chake cha iye mwini chinali choyenera kuchitsanzira, pakuti, monga momwe cholembedwa cha Baibulo chimasonyezera, mokangalika ndipo nthawi zina mwa kukhala pa upandu kwaukulu kwa iye mwini, iye anadziwitsa ena zinthu zimene iye anaziona.—Machitidwe 2:22-38; 4:8-12, 19, 20; 5:29-32.
7, 8. (a) Kodi nchiyani chimene mkulu ayenera kuzindikira ponena za mwini wa gulu la nkhosa? (b) Kodi ndi motani m’mene kumeneku kuyenera kuyambukirira kuchitira kwake mpingo?
7 Kuti mkulu lero lino akhale ngati Petro, iye afunikira kuzindikira kuti ziwalo za mpingo, sizake, koma, mwini wake ndi Yehova Mulungu. Mtumwi Paulo nayenso anasonyeza chenicheni chofunikira chimenechi. Kwa akulu a mpingo wa Efeso, iye anati: “Dzipenyerereni nokha ndi gulu lonse la nkhosa, pakati pa limene mzimu woyera wakuikani oyang’anira, kuweta mpingo wa Mulungu, umene iye anaugula ndi mwazi wa Mwana wake wa iye yekha.”—Machitidwe 20:28, NW.
8 Pa mtengo waukulu kwambiri kwa iye mwini, Yehova Mulungu anagula ziwalo za mpingo Wachikristu kukhala chuma chake. Palibe mtendo wokhulirapo kwambiri umene ukanatha kuperekedwa woposa wa mwazi wa Mwana wake wosachimwa. Pamene akulu ali ndi lingaliro la Yehova la mtengo wa mpingo wokhala m’manja mwao, limawathandiza kukhala okangalika m’kuthandiza munthu ali yense kukhalabe chuma cholemekezeka cha Wam’mwambamwambayo. Iwo adzafunikira kuyankha kwa Mulungu kaamba ka kuchitira moipa kuli konse gulu la nkhosalo. Ndicho chifukwa chake akulu ayenera kuyesayesa kukhala ndi kuzindikira koyenera mtengo wa munthu ali yense mu mpingo. Kumeneku kungathe kutumikira monga choletsa champhamvu kukhala ndi lingaliro la kukhala wampamwamba kulinga ku gulu la nkhosa’lo ndi kulichitira mwaukali, mochita ufumu. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:29.) Munthu ali yense payekha, ziwalo za mpingo zimamangiridwa kwambiri ndi abale amene amawapatsa ulemu ndi kulemekezeka kumene kuli kowayenera. Kumapatsa onse lingaliro la chisungiko pamene akulu adzitsimikizira iwo eni kukhala “abusa” enieni, omafunafuna ubwino wauzimu ndi wakuthupi wa gulu lonse la nkhosa.
“OSATI MOKAKAMIZA, KOMA MOFUNITSITSA”
9, 10. (a) Kodi ndi motani m’mene mkulu akachitira kuweta kwake “mokakamiza” ? (b) Kodi nchiyani chimene chikasonyeza kuti iye akuweta mpingo “mofunitsitsa”?
9 Mu mkhalidwe uli wonse woperekedwa kumene chithandizo chikufunika, munthu amakuona kukhala kosabvuta kwambiri kufikira munthu wina amene sali kokha ndi kukhoza kupereka chithandizo komanso ali ndi chikhumbo cha kutero. Moyenerera, Petro anafulumiza kuti akulu achite ubusa, “osati mokakamiza, koma mofunitsitsa.” (1 Petro 5:2, NW) Kuti akhale “mbusa” wabwino mu mpingo, munthu afunikira kuchenjera kuti asachite ntchito yake mwa lingaliro la kungoichita monga thayo. Ngati kusamalira mpingo kukachitidwa mwankhokera yopanda chimwemwe, mkuluyo akakhala akungokwaniritsa gawo “mokakamiza.” Gulu la nkhosa lingaone zimenezi ndi kufumuka, osafuna kuonjezera akatundu olemera a mkuluyo ndi zobvuta zawo. Komabe, pamene mkulu amapeza chisangalalo m’kusamalira mathayo ake chifukwa chakuti iye amafunadi kuchita ntchitoyo, ziwalo za mpingo zidzachititsidwa kuyandikira pafupi kwa iye. Kufunitsitsa kutumikira koteroko kumachokera m’kukonda kwambiri Mulungu ndi mpingo wa anthu ake. Kuli umboni wakuti mkuluyo akukwaniritsa utumiki wake kulinga ku gulu la nkhosa ndi lingaliro loyenera.
10 Ndithudi, kulingalira bwino kukufunika ku mbali ya mkuluyo kotero kuti asadzilemeze ndi ntchito zolemera zochuluka koposa zimene iye moyenerera angathe kuzichita. M’kupita kwa zaka ndi kuchepachepa kwa thanzi, iye sangakhale wokhoza kuchita zochuluka monga m’zaka zoyambirira, kukumafunikiritsa kuti iye apemphe amuna ena okhoza bwino kumthandiza. Komabe, iye angapezebe chisangalalo chowona m’kukhala wofunitsitsa “mbusa” m’kati mwa malire a zofooka zake.
‘OSATI KAAMBA KA PHINDU LOSAONA MTIMA KOMA MWACHANGU’
11. Kodi nchifukwa ninji pali upandu wa kuweta mpingo “kaamba ka chikondi cha phindu losaona mtima”?
11 Kuphatikiza pa kusonyeza mzimu wa kufunititsa, mkulu afunikira kukhala ndi cholinga choyera, chopanda dyera ngati iye ati akhale wothandiza kwenikweni kwa abale. Mtumwi Petro akuchenjeza za kutumikira monga mbusa “kaamba ka chikondi cha phindu losaona mtima.” Kugwiritsira ntchito gawo la kuweta la munthuwe kupezera chuma chakuthupi, chitamando kapena ulamuliro kukakhala kuligwiritsira ntchito mosaona mtima. Zowonadi, Baibulo limalangiza kupereka ‘ulemu wowirikiza’ kwa amuna amene amagwira ntchito zolimba pa kuphunzitsa. (1 Timoteo 5:17, 18) Koma ‘ulemu wowirikiza’ woterowo nthawi zonse uyenera kudza wokha kuchokera ku ziwalo za mpingo, wosachita kusakidwa konse ndi mkulu kapena kuonedwa ngati kanthu kena kamene iye moyenera amakayembekezera kapena kukayenerera kuchokera kwa iwo. Kutchuka kungadze kwa mkulu, mwina mwake chifukwa chakuti mikhalidwe yake imamsiya ali womasuka kukhala ndi phande mokwanira m’ntchito ya Ufumu koposa ena, kapena chifukwa cha mikhalidwe ina yapadera. Pangabuke mosabvuta chiyeso cha kupindula ndi kutchuka kwakeko, kukumatsogolera ku kufuna kwake, ngakhale kupereka lingaliro, la zinthu zakuthupi zimene ena angakhale okhoza kupereka kwa iye. Kumeneku mwina mwake kungatsogolere ku kugwirizana kwake kwakukulukulu ndi anthu olemera kwambiri okha mu mpingomo, monyalanyaza ena. Iye angakhale wokhumba kutamandidwa koma amakhala wochita khufiri, kapena ngakhale wonyansidwa, ndi chisulizo choyenera kapena uphungu.
12, 13. Kodi ndi motani m’mene mtumwi Paulo anasonyezera kuti iye anatumikira abale ake “mofunitsitsa”?
12 Pamene kuli kwakuti zimenezi zingachitike kwa amuna owerengeka kwambiri mu mpingo Wachikristu lero lino, akulu sayenera kuchepetsa upanduwo. Ngakhale m’zisonyezero zochepa kwambiri, mkhalidwe wa kufunafuna mapindu a zinthu zakuthupi kupyolera mwa maunansi auzimu uyenera kukanizidwa. Mtumwi Wachikristu Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Kwa akulu a mpingo wa Efeso, iye anatha kunena kuti:
“Kumbukirani kuti kwa zaka zitatu, usiku ndi usana, sindinaleka kulangiza aliyense wa inu ndi misozi. . . . Sindinasilira siliva kapena golidi wa munthu ali yense kapena zobvala. Inu nokha mudziwa kuti manja awa anagwira ntchito kudzipezera zosowa zanga ndi za awo amene ali nane. Ndasonyeza kwa inu mu zinthu zonse kuti mwa kugwira ntchito motero muyenera kuthandiza awo amene ali ofooka, ndipo muyenera kukumbukira mawu a Ambuye Yesu, pamene iye mwini anati, “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa chimene chiri m’kulandira.” —Machitidwe 20:31-35, NW.
13 Mpingo umapindula kwambiri ndi anthu amene amagwira ntchito “mofunitsitsa” monga momwe anachitira Paulo. Iye anali wokondwa kutumikira abale ake, osayang’ana mokhumbira pa chiri chonse chimene iwo anali nacho ndi chimene iye akanapindula nacho. Chisangalalo chake chinachokera m’kupatsa mwaufulu iye mwini m’kulimbikitsa abale ake.
14. Kodi nchiyani chimene timaphunzira kuchokera mu 1 Atesalonika 2:5-8 ponena za chimene chikuphatikizidwa m’kuweta mpingo “mofuunitsitsa”?
14 M’mene iye ndi atsamwali ake anatumikirira mopanda chinyengo kukusonyezedwa moonekera bwino ndi mawu ake kwa Atesalonika:
“Pa nthawi iri yonse sitinadza kwa inu (monga momwe mudziwira) ndi mawu oshashalika kapena ndi mtima wokhumba phindu, Mulungu ndiye mboni! Ndiponso sitanili kufunafuna ulemu wochokera kwa anthu, ayi, kaya kuchokera kwa inu kapena kuchokera kwa ena, ngakhale kuli kwakuti tikanatha kukhala katundu wotayitsa ndalama monga atumwi a Kristu. M’malo mwake, tinakhala odekha pakati panu, monga pamene amai oyamwitsa asamalira ana ake a iye mwini. Motero, pokhala ndi chikondi chokoma mtima kwa inu, tinakondwera kwambiri kupereka kwa inu, osati mbiri yabwino ya Mulungu yokha, komanso miyoyo yathu ya ife eni, chifukwa chakuti munakhala okondedwa kwa ife.” (1 Atesalonika 2:5-8, NW)
Inde, m’malo mwa kufunafuna phindu la munthu mwini kuchokera kwa ziwalo za mpingo, Paulo anachita monga momwe amachitira mai woyamwitsa amene amakonda kwambiri ana ake ndipo amaika zabwino zawo patsogolo pa zake za iye mwini. —Yerekezerani ndi Yohane 10:11-13.
15. Kodi akulu ayenera kufuna kuweta mpingo mu mkhalidwe wotani?
15 Kuphatikiza pa kusonkhezeredwa moyenera ndi kudera nkhawa ndi gulu la nkhosa, mkulu afunikira kukumbukira kufunika kwa kusamalira mpingo mu mkhalidwe woyenera. Mtumwi Petro analangiza akulu “kusachita umbuye pa awo amene ali cholowa cha Mulungu koma kuti iwo akhale zitsanzo za gulu la nkhosalo.’ (1 Petro 5:3, NW) Mogwirizana ndi chilangizo chimenechi, akulu sakadzikweza pamwamba pa abale awo. Kumeneku kukakhala kosemphana ndi zilangizo zimene Yesu anapatsa atsatiri ake:
“Musatchedwa Rabi; pakuti Mphunzitsi wanu ali mmodzi, ndipo inu nonse muli abale. Ndipo inu musatchule wina atate wanu pansi pano, pakuti alipo mmodzi ndiye Atate wa Kumwamba. Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Kristu. Koma wamkulu kopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu.” (Mateyu 23:8-11)
Chotero, m’malo mwa kupereka malamulo monga mbuye, kapena kuyesa kuyendetsa miyoyo ya ziwalo za mpingo, mkulu ali munthu amene modzichepetsa amatumikira abale ake. Mwa chitsanzo chake, iye amalimbikitsa gulu la nkhosa kukhala ngati Kristu.—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:9-12.
16. Kodi nchifukwa ninji akulu okhulupirika angathe kufikiridwa mwachidaliro?
16 Pamene akulu iwo eniwo apereka chitsanzo chabwino m’kukhala ndi moyo Kwachikristu ndi ntchito, iwo angachite zochuluka kuthandiza okhulupirira anzawo potsirizira pake kupezedwa ali obvomerezedwa ndi Yehova Mulungu. Ndiponso, Yesu Kristu, “mbusa wamkulu” pansi pa amene iwo akutumikira, adzafupa abusa onse ang’ono okhulupirika pa nthawi ya kubvumbuluka kwake kwaulemerero monga “Mfumu ya mafumu ndi Mbuye wa ambuye.” (Chibvumbulutso 19:16; 1 Timoteo 6:15) Monga momwe mtumwi Petro analembera: “Pamene mbusa wamkulu waonetsedwa, mudzalandira mphotho yosatha ya ulemerero. (1 Petro 5:4, NW) Zowonadi, amuna amene amatumikira abale awo kaamba ka chifukwa choyenera, ndi cholinga choyenera ndi mu mkhalidwe wolongosoka, ali othandiza kwenikweni ku mpingo, kukumachititsa kupeza kwao chimwemwe chachikulu m’njira yao ya moyo Yachikristu. (2 Akorinto 1:24) Musakaikire kupeza chithandizo cha akulu okhulupirika pali ponse pamene chiri chofunika.