Kodi Imfa N’chiyani?
15 Pamene munthu afa, amabwerera ku fumbi. Sadziŵanso kanthu kali konse.—Salmo 146:4
Anthu akufa sangalankhule nanu kapena kuchita kanthu kali konse.—Mlaliki 9:5, 10
16 Koma angelo ambiri anakhala oipa. Tsopano iwo amayerekezera kukhala anthu amene anamwalira. Iwo amafuna kutipangitsa kukhulupirira kuti sitifa kwenikweni.—Genesis 6:1, 2; Yuda 6
17 Chotero Yehova Mulungu safuna kuti ife tikhulupirire angelo oipawo, otchedwa ziwanda.—Eksodo 22:18; Deuteronomo 18:10, 11; 32:17
Iye safuna kuti ife tichite kuombeza maula, ufiti kapena kumangirira zithumwa.—Agalatiya 5:19-21