Mutu 19
Chimene Chilamulo cha Mose Chimatanthauza kwa Inu
1. (a) Kodi nchiyani chimene chinasonyeza kuti, kuyambira mu 36 C.E., Akunja osadulidwa anali ovomerezeka kwa Yehova monga Akristu? (b) Kodi panali pankhani yanji pa imene Akristu ena oyambirira anali ndi maganizo amphamvu?
NKHANI yokanganirana kwambiri m’masiku a mtumwi Paulo inali yakuti kaya Akristu Achikunja anali ndi thayo lakuchita mogwirizana ndi zofunika za Chilamulo cha Mose. Nzowona kuti mu 36 C.E. mzimu woyera unatsanuliridwa pa Akunja osadulidwa. Koma Akristu ena okhala ndi ziyambi Zachiyuda analingalira mwamphamvu kuti ophunzira Achikunja ayenera kudulidwa ndi kuphunzitsidwa kusunga Chilamulo cha Mose. Kodi iko, kunalidi, kofunika kwa iwo kusunga Chilamulo chimenecho, kapena mwinamwake mbali yake? Pafupifupi 49 C.E. nkhaniyo inapititsidwa kubungwe lolamulira mu Yerusalemu.—Mac. 10:44-48; 15:1, 2, 5.
2. Kodi nchifukwa ninji nkhaniyi ikutikondweretsa?
2 Chotulukapo nchokondweretsa kwa ife. Chifukwa ninji? Osati kokha chifukwa chakuti panthawi zina timakomana ndi anthu amene amaumirira kunena kuti Akristu ayenera kuchita mogwirizana ndi zofunika zakutizakuti za Chilamulo, monga kusunga Sabata, komanso chifukwa chakuti Baibulo lenilenilo limanena kuti “Chilamulo chiri choyera, ndi chilangizo chake nchoyera, ndi cholungama, ndi chabwino.” (Aroma 7:12) Ngakhale kuli kwakuti chimatchedwa Chilamulo cha Mose chifukwa chakuti Mose anali mtetezi wa pangano Lachilamulo, kwenikweni magwero a Lamulo limenelo anali Yehova Mulungu.—Eks. 24:3, 8.
Kodi Nchifukwa Ninji Chilamulo?
3. Kodi nchifukwa ninji Chilamulo chinaperekedwa kwa Israyeli?
3 Mmene tikuwonera Chilamulo lerolino kumayambukiridwa ndi kuti kaya tikuzindikira chifukwa chimene Yehova anaperekera Chilamulo kwa Israyeli. Malemba amalongosola kuti: “Chinawonjezeka [kupangano la Abrahamu] chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera . . . momwemo chilamulo chidakhala namkungwi wathu wa kutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.” (Agal. 3:19, 24) Kodi ndimotani mmene Chilamulo chinachitira ichi?
4. (a) Kodi ndimotani mmene Chilamulo “chinadziwikitsira uchimo”? (b) Kodi ndimotani mmene chinatsogolereranso okhulupirira kwa Kristu?
4 Mwa kuyambitsa chitsanzo changwiro chophatikizapo mbali zosiyanasiyana zamoyo, chinasonyeza Ayuda kukhala ochimwa. Kunali kwachiwonekere kuti, mosasamala kanthu za zolinga zabwino ndi zoyesayesa zaphamphu, iwo sakanakhoza kukwaniritsa zofunika zake. Mogwiritsira ntchito Ayuda monga chitsanzo cha banja laumunthu lopanda ungwiro, Chilamulo chinasonyeza dziko lonse, kuphatikizapo aliyense wa ife, kukhala wochimwa, woyenerera chilango cha Mulungu. (Aroma 3:19, 20) Chotero chinagogomezera kufunika kwa mpulumutsi kaamba ka mtundu wa anthu, ndipo chinatsogolera okhulupirikawo kwa Yesu Kristu monga Mpulumutsi ameneyo. Mwanjira yotani? Chinamdziwikitsa kukhala munthu yekha amene anasunga Chilamulo mwaungwiro, chotero anali munthu yekha amene anali wopanda uchimo. Nsembe za nyama pansi pa Chilamulo zinali ndi mtengo wochepa chabe, koma monga munthu wangwiro, Yesu akanapereka moyo wake monga nsembe imene ikanachotsadi uchimo ndi kutsegula njira ya kumoyo wamuyaya kaamba ka onse osonyeza chikhulupiriro.—Yoh. 1:29; 3:16; 1 Pet. 1:18, 19.
5. Mogwiritsira ntchito malemba operekedwa, yankhani mafunso ophatikizidwa m’ndime iyi.
5 Ndi chiyambi chimenechi m’maganizo, kodi mukanayankha bwanji mafunso otsatirawa?
Kodi Chilamulo cha Mose chinayenera kukhala chogwira ntchito kwa anthu onse? (Sal. 147:19, 20; Eks. 31:12, 13)
Kodi Yehova anapereka chisonyezero chirichonse kwa Israyeli kuti tsiku lina pangano Lachilamulo likatha? (Yer. 31:31-33; Aheb. 8:13)
Kodi Malamulo Khumi, kuphatikizapo chofunika cha kusunga Sabata la mlungu ndi mlungu, akupitirizabe kugwira ntchito pambuyo Poti mbali zina za Chilamulo zinafafanizidwa? (Akol. 2:13, 14, 16; 2 Akor. 3:7-11 [monga momwe kwamveketsedwera ndi Eksodo 34:28-30]; Aroma 7:6, 7)
Kodi ndikupyolera mwa chiyani kuti Yehova anathetsa pangano Lachilamulo? (Akol. 2:13-17; Mat. 5:17, 18; Aroma 10:4)
6. Kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa ndi zigomeko zonena kuti Chilamulo cha Mose chikali kugwirabe ntchito?
6 Mothandizidwa ndi zimenezi, kodi nchiyani chimene chikutanthauzidwa mwa kupereka zigomeko zakuti Chilamulo cha Mose chikali kugwirabe ntchito? Kunena zowona, ichi chikuphatikizapo kukana chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. Kodi nchifukwa ninji izi ziri choncho? Chifukwa chakuti lingaliro lotero limakana chenicheni chakuti Yesu anakwaniritsa Chilamulo, mwa kutero kulambula njira yakuti Mulungu achithetse. Kwa anthu odzitcha Akristu, amene anasokeretsedwa ndi zigomeko zoyanja kusunga Chilamulo, kapena mbali yake, ina mtumwi Paulo analemba mwamphamvu kuti: “Mulibe kanthu ndi Kristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.”—Agal. 5:4; wonaninso Aroma 10:2-4.
7. (a) Kodi nchiyani chimene sichikuzindikiridwa bwino ndi awo otsutsa kuti mbali zina za Chilamulo zikupitirizabe? (b) Kodi ntchito Zachikristu nzofunika motani, ndipo kodi ndi unansi wanji umene izo ziri nawo m’kulandira kwathu mphatso ya moyo wamuyaya?
7 Awo amene amaumirira kuti mbali zina za Chilamulo zipitirizidwebe sakuzindikira kotheratu kuti kaimidwe ka chilungamo ndi Mulungu kamadalira, osati pantchito za munthuyo za Chilamulo, koma pachikhulupiriro cha munthuyo mu mtengo wansembe ya Yesu. (Agal. 3:11, 12) Amalingalira kuti munthuyo ayenera kudzitsimikizira iyemwini kukhala wolungama mwa ntchito zotero—chinthu chimene chiridi chosatheka kwa anthu ochimwa. Ndithudi, kuli kofunika, kuchita ntchito momvera malamulo a Mulungu ndi Kristu amene amagwira ntchito kwa Akristu. (Yak. 2:15-17; Mat. 28:19, 20) Izi ziri njira yosonyezera chikondi chathu ndi chikhulupiriro, ndipo kuzisowa kukanasonyeza kuti chikhulupiriro chathu chinali chakufa. Koma sitingakhoze kupeza chipulumutso mulimonse mmene tingagwirire ntchito zolimba. Palibe chipulumutso ku uchimo ndi imfa chingakhale chotheka popanda nsembe ya Yesu Kristu. Chotero moyo wamuyaya ndiwo mphatso yochokera kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu, chisonyezero chachisomo ndipo osati malipiro kaamba ka ntchito zathu.—Aef. 2:8, 9; Aroma 3:23, 24; 6:23.
8. Kodi nchiyani chimene bungwe lolamulira lam’zaka za zana loyamba linagamula ponena za nkhani yophatikizapo kugwira ntchito kwa Chilamulo cha Mose kwa Akristu Akunja?
8 Pamene nkhani yonena za kugwiritsidwa ntchito kwa Chilamulo cha Mose kwa Akristu Akunja inaperekedwa kubungwe lolamulira m’Yerusalemu m’zaka za zana loyamba, chosankha chawo chinali chogwirizana ndi zenizeni izi. Anavomereza kuti Yehova sanali kufunikiritsa okhulupirira Akunja kuchita ntchito momvera Chilamulo cha Mose mzimu woyera usanasanuliridwe pa iwo. Chosankha cha bungwe lolamulira limemelo chinandandalika “zinthu zofunika monga ziletso zina zimene zinali zogwirizana ndi Chilamulo, koma zimenezi zinazikidwa pa cholembedwa cha Baibulo chonena za zochitika zimene zinayambira Chilamulo. Chotero sikunali kukanikiza pa Akristu Akunja thayo la kugwirizana ndi Chilamulo cha Mose kapena mbali yake koma, m’malo mwake, panali kutsimikiziridwa kwa miyezo yovomerezedwa Mose asadakhale.—Mac. 15:28, 29; yerekezerani ndi Genesis 9:3, 4; 34:2-7; 35:2-5.
9. (a) Kodi Ayuda akali kufunsidwa ndi Mulungu kumvera Chilamulo cha Mose? (b) Kodi ndimakonzedwe apadera otani amene anapangidwa kaamba ka iwo ndi dongosolo m’limene Kristu anafera?
9 Pambuyo pa Pentekoste wa 33 C.E. Ayuda enieniwo sanafunikirenso kuchita mogwirizana ndi mpambo Wachilamulo cha Mose ndi Mulungu. Ndipo Ayuda amenewo amene anasonyeza chikhulupiriro anawona chifukwa chapadera chosangalalira ndi izi. Chifukwa ninji? Ngakhale kuli kwakuti Akunja analinso ochimwa ndipo chotero amafa, anali Ayuda okha amene oti nkutembereredwa ndi Mulungu chifukwa cha kukhala akuswa pangano la Chilamulo. Koma mwadongosolo la imfa ya Kristu—kupachikidwa pamtengo monga ngati kuti anali mpandu wotembereredwa—anatenga malo a Ayuda amenewo amene amkhulupirira ndi kupereka kumasulidwa kwawo ku chilango cholandiridwa monga chotulukapo cha kusamvera kwawo Chilamulo. (Agal. 3:10-13) Chotero anawapatsa chikhululukiro chimene sakanakhala nacho konse pansi pa Chilamulo cha Mose.—Mac. 13:38, 39.
10. Kodi kuchotsedwa kwa Chilamulo kunatsimikizirira m’njira yotani mfundo ya kulambira kogwirizanitsidwa?
10 Ndithudi, Chilamulo chinalekanitsa Ayuda ndi Akunja. Zofunika zimene sizinagwire ntchito kwa Akunja zinaikidwa pa Ayuda, ndipo Akunja osadulidwa anali kuletsedwa kugwirizana mokwanira ndi Ayuda m’kulambira kwawo. (Yerekezerani ndi Eksodo 12:48; Machitidwe 10:28.) Koma pamene Chilamulo chinatsiriza chifuno chake ndipo chinachotsedwa, kunali kotheka kwa Ayuda ndi Akunja osadulidwa kukhala ogwirizanitsidwa kupyolera mwa Kristu m’kulambiridwa kwa Mulungu mmodzi yekha wowona.—Aef. 2:11-18.
Kudziwa Chilamulo Kumatipindulitsa
11. Kodi ndimotani mmene chidziwitso cha Chilamulo chimatithandizira kuzindikira ziphunzitso za Kristu?
11 Ngakhale kuli kwakuti ife lerolino sitiri pansi pa Chilamulo, kuchidziwa kuli kopindulitsa kwambiri kwa aliyense wa ife. Mwanjira yotani? Kumbukirani, Yesu anabadwa mwa mayi Wachiyuda anakhala womvera Chilamulo cha Mose. Zinthu zina zimene anachita zingakhoze kuzindikiridwa mokwanira kokha pamaziko a chidziwitso cha zofunika za Chilamulo chimenecho. (Agal. 4:4; wonani Luka 22:7, 8.) Ndiponso anachitira uminisitala wake pakati pa anthu omvera Chilamulo. Chotero kawirikawiri ziphunzitso zake zinali zozikidwa pamikhalidwe yogwirizana ndi Chilamulo.—Yerekezerani ndi Mateyu 5:23, 24.
12. (a) Kodi ndikugwirizana kotani kumene Yesu anasonyeza pakati pa moyo wake ndi Chilamulo cha Mose? (b) Kodi ndimotani mmene mtumwi Paulo anasonyezera kufunika kwa kukhala ndi chidziwitso cha Chilamulo? (c) Kodi nchiyani chimene chingatuluke kuchokera m’kuzindikira kwathu tanthauzo lauzimu la zofunika zake?
12 Pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu anakumbutsa ophunzira ake kuti moyo wake monga munthu unali utakwaniritsa zinthu zolembedwa ponena za iye m’Chilamulo, mu Aneneri ndi m’Masalmo. (Luka 24:44) Ndiponso mtumwi Paulo anasonya kuzochitika zogwirizana ndi pangano la Chilamulo kukhala monga “chifaniziro ndi mthunzi wa zakumwambazo” ndipo ananena kuti ‘Chilamulo, pokhala nawo mthunzi wa zokoma zirimkudza.’ (Aheb. 8:4, 5; 10:1) Mfundo zolongosoka zodabwitsa zimene zikukwaniritsidwa mu unsembe wa Yesu Kristu ndi nsembe ya moyo wake waumunthu ziri m’Chilamulo cha Mose. Kuzindikira kwathu zimenezi kungakhoze kumveketsa tanthauzo lamakonzedwe amenewa kwa ife. Pakati pa zitsanzo zoloserazo pali chidziwitso chosonya kukakonzedwe ka kulambira Yehova movomerezeka lerolino pa kachisi wake wamkulu wauzimu. Pamene chidziwitso chathu cha zinthui zimenezi chikula, chiyamikiro chathu kaamba ka mpingo wa odzozedwa ndi mzimu ndi mbali yake pansi pa Yesu Kristu mogwirizana ndi kulambira kwathu nachonso chidzawonjezereka.
13. Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kusinkhasinkha pamalamulo a makhalidwe abwino kwambiriwo osonyezedwa m’Chilamulo?
13 Chilamulo cha Mose chiri mbali ya malemba ouziridwa ndi Mulungu, amene onse ali “opindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero.” (2 Tim. 3:16) Kufunafuna kwathu ndi kusinkhasinkha malamulo a makhalidwe abwino osatha pa amene Chilamulo chamangidwapo kungatithandize kukulitsa chikhumbo chathu chochokera pansi pa mtima cha kuchita zinthu zokondweretsa Mulungu. Ngati tizindikira mkhalidwe umene Chilamulo chinasonyako ndi kusonyeza mkhalidwe umenewo m’miyoyo yathu, ndikopindulitsa chotani nanga mmene kumeneko kudzakhalira!
14. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anafotokozera mwa fanizo kufunika kwa kuzindikira mkhalidwe umene zofunika za Chilamulo zinasonyeza? (b) Tchulani ena a malamulo a makhalidwe abwino kwambiri owonjezereka ophatikizidwa m’Chilamulo, monga momwe asonyezedwera patsamba 152. (c) Kodi ndimotani mmene kuzindikira zinthu izi kungatithandizire kukhala okondweretsa kwambiri kwa Mulungu?
14 Yesu anasonyeza mogwira mtima mu Ulaliki wake wa pa Phiri. Polankhula kwa anthu amene panthawiyo anali pansi pa Chilamulo, iye anasonyeza kuti, m’malo mwa kungopewa kuchita mbanda, iwo anafunikira kuchotsa chikhoterero chirichonse cha kusunga mkwiyo ndi kupewa kugwiritsira ntchito lirime lawo kululuza abale awo. M’malo mwa kukhala okhutira chifukwa chakuti sanachitepo chigololo konse, iwo sanayenera kuyang’ana mkazi mwachilakolako. Monga momwe zinaliri kwa iwo, nafenso tiyenera kuyesayesa kugwiritsira ntchito ziwalo zonse zathupi lathu mogwirizana ndi njira zolungama za Yehova. (Mat. 5:21, 22, 27-30; wonaninso Aroma 13:8-10.) Ngati tichita izi, tidzasonyeza kuti nafenso tikuzindikira tanthauzo la lamulo lalikulu koposa m’Chilamulo: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse.” (Mat. 22:36, 37) Ndithudi izi zidzatichititsa kuyandikira kwambiri kwa Yehova Mulungu. Ngakhale kuli kwakuti sitiri pansi pa mpambo Wacilamulo cha Mose, ife ndithudi tidzapindulitsidwa ndi chidziwitso cholongosoka cha malamulo a makhalidwe abwino pa amene chinazikidwapo ndi zitsanzo zolosera zimene chiri nazo.
Makambitsirano Openda
● Kodi nchifukwa ninji awo oumirira kumvera Chilamulo cha Mose akukanadi Kristu?
● Kodi ndimotani mmene chidziwitso cha Chilamulo chimatithandizira kuzindikira mbali ya Yesu m’chifuno cha Yehova?
● Ngakhale kuli kwakuti sitiri pansi pa Chilamulo, kodi ndizinthu zofunika zotani zimene tingazindikire kuchokera m’kuchiphunzira?
[Bokosi patsamba 152]
Zina za Ziphunzitso za Maziko m’Chilamulo cha Mose
Mathayo Kulinga kwa Mulungu
Lambirani Yehova yekha Eks. 20:3; 22:16
Kuchitira dzina lake mwaulemu Eks. 20:7; Lev. 24:16
Kondani ndi kumtumikira ndi mtima Deut. 6:5; 10:12; 30:16
wathunthu, moyo, nyonga
Opani kusam’mvera, muwopeni Deut. 5:29; 6:24
Mfikireni kokha mwa njira imene Lev. 1:1-5; Num. 16:
amavomereza 1-50; Deut. 12:5-14
Mpatseni zanu zabwino koposa; Eks. 23:19; 34:26
zinachokera kwa iye
Olambira ayenera kukhala audongo mwa Eks. 19:10, 11; 30:20
kuthupi
Zinthu zopatulika sizinayeneraEks. 20:8-10; 34:21;
kukankhidwira pambali kuchitira kuti Num. 15:32-36
tilondole zakuthupi
Machitachita Achipembedzo Oletsedwa
Kulambira mafano Eks. 20:4-6; Deut. 7:25
Chikhulupiriro cholowana Eks. 23:13; 34:12-15;
Kukhulupirira mizimu, nyanga, Eks. 22:18; Lev. 20:27;
kuombedza ula, kubwebweta, Deut. 18:10-12
matsenga, kutsirika
Mu Ukwati ndi Moyo wa Banja
Chigololo chinaletsedwa Eks. 20:14; Lev. 20:10
Osakwatirana ndi munthu wosatumikira Deut. 7:1-4
Yehova
Kugonana ndi wapachibale kunaletsedwa Lev. 18:6-16; 20:11
Pewani kugonana koluluzika Lev. 18:23; 20:13
Lemekezani moyo wa mwana wosabadwa Eks. 21:22, 23
Lemekezani makolo anu Deut. 21:18-21 Eks. 20:12; 21:15, 17;
Phunzitsani ana anu njira za Yehova Deut. 6:4-9; 11:18-21
Ntchito Zophatikizapo Anthu Ena
Wonani moyo wa munthu kukhala Eks. 20:13; Num. 35:
wopatulika 9-34
Kondani munthu mnzanu; pewani maudani Lev. 19:17, 18
Lemekezani okalamba Lev. 19:32
Sonyezani nkhawa yachikondi pa anthu Lev. 25:35-37; Deut. 15:
osauka, ana amasiye, akazi amasiye 7-11; 24:19-21
Osachitira nkhalwe agonthi ndi akhungu Lev. 19:14; Deut. 27:18
Khalani wowona mtima m’mabizinesi Lev. 19:35, 36; 25:14
Lemekezani chuma cha ena Eks. 20:15; 22:1, 6;
23:4; Deut. 22:1-3
Osasirira za ena Eks. 20:17
Ululani ochimwa tchimo lalikulu Lev. 5:1; Deut. 13:6-11
Nenani chowonadi; musachitire umboni Eks. 20:16; 23:1, 2
wonama
Osachita tsankhu chifukwa cha malo Eks. 23:3, 6; Lev. 19:15
apamwamba