Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • uw mutu 20 tsamba 154-160
  • Moyo ndi Mwazi—Kodi Mumachita Nazo Monga Zopatulika?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Moyo ndi Mwazi—Kodi Mumachita Nazo Monga Zopatulika?
  • Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Bwanji Ponena za Kugwiritsira Ntchito Mwazi?
  • Kodi Nkhaniyo Njowopsa Motani?
  • Kulemekeza Moyo ndi Mwazi Mwaumulungu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Muziona Moyo Ngati Mmene Mulungu Amauonera
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
  • Mafunso Ochokera kwa Oŵerenga
    Nsanja ya Olonda—2000
  • Onani Mphatso ya Moyo Wanu Kuti ndi Yamtengo Wapatali
    Nsanja ya Olonda—2004
Onani Zambiri
Ogwirizana m’Kulambiridwa kwa Mulungu Yekha Wowona
uw mutu 20 tsamba 154-160

Mutu 20

Moyo ndi Mwazi—Kodi Mumachita Nazo Monga Zopatulika?

1. (a) Kodi ndimotani mmene Mulungu amawonera moyo? (b) Kodi ndimotani mmene tingasonyezere kuti tikuyamikira mphatso ya Mulungu ya moyo?

SIKUYENERA kutidabwitsa kuti lingaliro la Mulungu la moyo liri losiyana kwambiri ndi lija ladziko. Kwa Mulungu, moyo wa munthu ngwopatulika. Kodi inu mumauwona motero? Timadalira pa Mulungu kotheratu, amene “apatsa zonse moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Mac. 17:25-28; Sal. 36:9) Ngati tikhala ndi lingaliro la Mulungu, tidzatetezera moyo wathu. Koma sitidzaswa lamulo la Mulungu m’kuyesayesa kupulumutsa moyo wathu wamakono. Timawona lonjezo la Mulungu la moyo wosatha kwa awo osonyeza chikhulupiriro m’Mwana wake kukhala lamtengo wapatali.—Mat. 16:25, 26; Yoh. 6:40; Yuda 21.

2. Kodi nkaimidwe ka maganizo kayani kulinga kumoyo kamene dziko limasonyeza, ndipo nkumtundu wanji wa kulingalira kumene nthawi zina izi zimatsogolerako?

2 Mosemphana, Yesu ananena kuti Satana Mdyerekezi, wolamulira wa dziko lino, “anali wambanda kuyambira pachiyambi.” (Yoh 8:44; 12:31) Kuyambira pachiyambi penipeni pa njira yake yachipanduko anabweretsa imfa kwa anthu. Mbiri yachiwawa yadziko imasonyeza mzimu wake. Koma Satana angakhozenso kupereka mawonekedwe owonekera kukhala osiyana. Chotero anthu amene asonkhezeredwa ndi kuganiza kwake amatsutsa kuti, pamene kuli kwakuti kungakhale bwino kukhala wopembedza, pamene moyo ukhala paupandu mukanapindulitsidwa mwa kulabadira uphungu wawo “waukatswiri” m’malo mwa kugwira mawu Baibulo. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:14, 15.) Pamene muyang’anizana ndi mkhalidwe wowonekera kukhala moyo kapena imfa, kodi ndinjira iti imene mtima wanu udzakhotererako? Ndithudi, chikhumbo chathu chiyenera kukhala kukondweretsa Yehova.

3. (a) Kodi nchifukwa ninji tiyenera makamaka kukondweretsedwa m’zimene Baibulo limanena ponena za mwazi? (b) Werengani Genesis 9:3-6 ndi Machitidwe 15:28, 29, ndiyeno yankhani mafunso ondandalikidwa pamwambapa ndi malemba awa.

3 Mawu a Mulungu amavumbula unansi wapafupi pakati pa moyo ndi mwazi, kumati: “Moyo [kapena mphamvu ya moyo] wa nyama ukhala m’mwazi.” Monga momwedi moyo uliri wopatulika, choteronso, Mulungu anachititsa mwazi kukhala wopatulika. Uli kanthu kena kamene kali kake, koti kagwiritsiridwe ntchito kokha mwa dongosolo limene avomereza. (Lev. 17:3, 4, 11; Deut. 12:23) Chotero timachita bwino kupenda mosamalitsa zimene amafuna kuti tichite ponena za mwazi.

Werengani Genesis 9:3-6

Kodi ndimachitachita otani m’dera lanu amene amakufunikiritsani kukhala maso kotero kuti musadye mwazi wa nyama?

Chifukwa cha chimene chanenedwa m’vesi 4 ponena za mwazi wa nyama, kodi mukanachita motani ponena za kumwa mwazi wa munthu (zimene zimachitika pa zochitika za masewera olimbana ndi zilombo ku Roma)?

Monga momwe kwasonyezedwera m’vesi 5 ndi 6, kodi nkwayani kumene kwakukulukulu tiyenera kudziwerengera mlandu wa kukhetsa mwazi wa munthu?

Werengani Machitidwe 15:28, 29

Kodi izi zikulongosola kuti zofunikazo zikagwira ntchito kokha m’nthawi yochepa? Kodi izi zikugwira ntchito kwa ife?

Kodi mwazi wa munthu sukuphatikizidwa mwa chinenero chogwiritsidwa ntchito pano?

Kodi lembali likusonyeza kuti zochitikazo sizingagwire ntchito ngati muli m’ngozi?

4. Monga momwe kwanenedwera pano, kodi nchochitika chotani chimene Malemba amasonyeza kuti munthu angafunikire kuchita kuti asakhale ndi mbali m’liwongo lamwazi?

4 Ponena za mwazi wa munthu, sitingayerekezere kuti kungoleka kokha kuchita mbanda kumatipewetsa liwongo lamwazi. Malemba amasonyeza kuti ngati tiri mbali ya gulu lirilonse limene liri ndi liwongo lamwazi pamaso pa Mulungu, tiyenera kuthetsa zigwirizano zathu ndi ilo ngati sitikufuna kugawana nawo m’machimo ake. (Chiv. 18:4, 24; Mika 4:3) Kachitidwe koteroko kamafunikira chisamaliro chofulumira.

5. Kodi ndimotani mmene changu mu uminisitala wakumunda chagwirizanitsidwira ndi kupanda liwongo lamwazi?

5 Ponena za atumiki a Mulungu amene wawatuma kuchenjeza chiwonongeko chirimkudza m’chisautso chachikulu, kukhala kwawo omasuka kuchokera ku liwongo lamwazi kumafunikiritsa kuti alengeze mokhulupirika uthenga umenewo. (Yerekezerani ndi Ezekieli 3:17-21.) Mtumwi Paulo anadziwona iyemwini monga wamangawa kwa anthu amtundu wonse chifukwa cha uminisitala wogawiridwa kwa iye. Anadziwona kukhala wopanda liwongo lamwazi wawo kokha pambuyo pa kuchitira umboni mosamalitsa kwa iwo za makonzedwe a Mulungu a chipulumutso. (Aroma 1:14, 15; Mac. 18:5, 6; 20:26, 27) Kodi changu chanu mu uminisitala wakumunda chimasonyeza kuzindikira kofananako za thayo limene liri pa Mboni za Yehova zonse?

6. Kodi nkugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa kutetezera ngozi ndi ulemu kaamba ka kupatulika kwa moyo?

6 Ngozi zochititsa imfa ziyeneranso kukhala zodetsa nkhawa kwambiri kwa ife. Pansi pa Chilamulo cha Mose anthu amene anachititsa imfa mwangozi ya anthu anzawo sanali kuwonedwa monga opanda liwongo. Zilango zinali kuperekedwa. (Eks. 21:29, 30; Deut. 22:8; Num. 35:22-25) Ngati tikumbukira lamulo lamakhalidwe abwino lophatikizidwa, tidzakhala osamala kupewa kuchitsa ngozi iriyonse ya kupha mwanjira imene tiyendetsera galimoto, mwa kuchita kwathu zaupandu mopusa kapena mwa kuloleza mikhalidwe yosatetezereka kupezeka m’nyumba yathu kapena kumalo athu a bizinesi. Kodi kaimidwe kanu ka maganizo ponena za zinthu izi kamasonyeza chiyamikiro chodzala cha kupatulika kwa moyo?

Bwanji Ponena za Kugwiritsira Ntchito Mwazi?

7. (a) Kodi kuika mwazi wa munthu mwa munthu wina nkogwirizana ndi kupatulika kwa mwazi? (b) Kodi nchifukwa ninji sikuli kwanzeru kulekezera lamulo la ‘kusala mwazi’ ku machitachita amene anali ofala m’zaka za zana loyamba?

7 Ngakhale kuli kwakuti chizolowezi ichi sichiri chatsopano, makamaka m’zaka za zana la-20 mwazi wagwiritsiridwa ntchito kwakukulukulu kuuika m’thupi, ncholinga cha kuchirikiza moyo. Ponse pawiri mwazi weniweni ndi nsanganizo za mbali zazikulu za mwazi zimagwiritsiridwa ntchito mwa dongosolo iri. Ndithudi, mankhwala a mtundu uwu samatsimikizira kuti wodwalayo sadzafa. Ndithudi, nthawi zina, imfa imatsatira monga chotulukapo chachindunji cha kugwiritsira ntchito mwazi. Koma chodetsadi nkhawa koposerapo nchakuti—kodi chofunika cha Baibulo chakuti ‘tisale mwazi’ chimagwira ntchito kumtundu umenewu wa mankhwala? Inde! Kulowetsa mwazi m’thupi lamunthu kuchokera ku cholengedwa china chirichonse, munthu kapena nyama, kumaswa lamulo la Mulungu. Kumasonyeza kunyozera kupatulika kwa mwazi. (Mac. 15:19, 20) Palibe maziko onenera kuti lamulo la ‘kusala mwazi’ lilekezere kumachitachita amene anali kuchitika m’zaka za zana loyamba zokha ndipo motero kuti asaphatikizepo maluso amakono a zamankhwala. Talingalirani nkhaniyi motere: Kodi ndani akananena kuti lamulo la Baibulo loletsa kupha mwambanda silinaphatikizepo kupha munthu mosaloledwa ndi lamulo ndi mfuti, popeza wonga sunatulukiridwe kufikira m’zaka za zana la-10? Ndipo kodi kukakhala kwanzeru kuumirira kuti chiletso chauchidakwa chinagwira ntchito kokha ku zakumwa zoledzeretsa zodziwika m’zaka za zana loyamba ndipo osati zakumwa zoledzeretsa zamakono? Kwa anthu amene amafunadi kukondweretsa Mulungu, uthenga woperekedwa ndi lamulo la ‘kusala mwazi’ nlomvekera bwino.

8. (a) Kodi mungadziwe bwanji kuti kaya mchitidwe wakutiwakuti wa mankhwala uli woyenerera kwa Mkristu? (b) Ngati dokotala anafuna kuchotsa wina wa mwazi wanu, kuusunga ndiyeno kuubwezera m’thupi lanu mkati mwa opaleshoni, kodi ndimalamulo a makhalidwe abwino Abaibulo ati amene angakuthandizeni kupanga chosankha chanzeru? (c) Kodi ndimotani mmene munthu angalingalirire mankhwala amene amafunikira kuti mwazi uyende kudzera m’chiwiya cha kunja kwa thupi?

8 Komabe, kucholowana kwa machitidwe ena a mankhwala kungadzutse mafunso. Kodi amenewa angayankhidwe motani? Choyamba, funsani dokotala wanu kaamba ka malongosoledwe omvekera bwino a mchitidwe wovomerezedwawo. Ndiyeno mwa pemphero upendeni mounikiridwa ndi malamulo a makhalidwe abwino a Baibulo. Dokotala angavomereze kuti mwazi wanu utengedwe ndi kusungidwa kudzagwiritsiridwa ntchito, ngati kudzafunika, mkati mwa opareshoni pambuyo pake. Kodi mukanavomereza? Kumbukirani kuti, mogwirizana ndi Chilamulo cha Mulungu choperekedwa kupyolera mwa Mose, mwazi wochotsedwa kuchokera m’cholengedwa unatsanuliridwa panthaka. (Deut. 12:24) Ife lerolino sitiri pansi pa lamulo Lachilamulo, koma uthenga wosasintha ngwakuti mwazi uli wopatulika ndipo, pamene uchotsedwa m’thupi lacholengedwa, uyenera kubwezeredwa kwa Mulungu mwa kuutsanulira pa choponda pamapazi ake, dziko lapansi. (Yerekezerani Mateyu 5:34, 35.) Chotero kodi ndimotani mmene kukanakhalira koyenerera kusunga mwazi wanu (ngakhale kwa nyengo yaifupi kwambiri) ndiyeno kuubwezera m’thupi lanu? Koma bwanji ngati dokotala akunena kuti, mkati mwa opareshoni kapena mkati mwa nthawi ina ya kupatsidwa kwanu mankhwala, mwazi ukayendetsedwa kudzera m’chiwiya china kunja kwa thupi lanu, ndiyeno, udzabwereranso mkati? Kodi mukavomereza? Ena alingalira kuti, mwa chikumbumtima choyera, akanalola zimenezo, malinga ngati chiwiyacho chinali ndi madzi osakhala mwazi. Awona chiwiya cha kunja chimenecho monga chowonjezera dongosolo lawo loyendamo mwazi. Ndithudi, mikhalidwe imasiyana, ndipo ndinu amene muyenera kupanga chosankha. Koma chosankha chanu chiyenera kukusiyani muli ndi chikumbumtima choyera pamaso pa Mulungu.—1 Pet. 3:16; 1 Tim. 1:19.

9. (a) Kutsimikizira ulemu kaamba ka chosankha chanu cha ‘kusala mwazi,’ kodi nkukonzekeratu kotani kumene kuyenera kuchitidwa? (b) Ngakhale m’chochitika cha ngozi, kodi ndi ndimotani mmene kukangana kosakondweretsa nthawi zina kungapewedwere? (c) Ngati dokotala kapena bwalo lamilandu linayesa kukakamiza kuti muikidwe mwazi, kodi mukanachita chiyani?

9 Kutsimikizira kuti dokotala wanu adzalemekeza chosankha chanu cha ‘kusala mwazi,’ lankhulani naye upandu wa zamankhwala uliwonse usanabuke. Ngati kuli kotheka kufufuza m’chipatala kaamba ka mankhwala, chitani mochenjera mwa pempho lolembedwa lakuti mwazi usagwiritsiridwe ntchito, ndiponso lankhulani za nkhaniyo inu mwini kwa dokotala amene adzasamalira matenda anu. Koma bwanji ngati pali ngozi yosayembekezeredwa? Kawirikawiri zochitika zosakondweretsa zingathe kupewedwa mwa kukhala ndi makambitsirano aulemu, anzeru ndi dokotala, mukumamlimbikitsa kugwiritsira ntchito maluso ake kuthandiza, koma molemekeza chikumbumtima chanu Chachikristu. (Miy. 15:1; 16:21, 23) Komabe, ngati mwinamwake dokotala wina wokhala ndi zolinga zabwino koma zolakwika aumirira kuti kukana mwazi kudzaika paupandu moyo wathu ndipo chotero ayesa kutikakamiza kugonjera, pamenepo chiyani? Chikhulupiriro m’kulungama kwa njira za Yehova chiyenera kutichititsa kuima nji. Kukhulupirika kwa Yehova kuyenera kutipangitsa kukana molimba mtima, chifukwa timasankha kumvera Mulungu koposa anthu.—Mac. 5:29; yerekezerani Yobu 2:4; Miyambo 27:11.

Kodi Nkhaniyo Njowopsa Motani?

10. Kodi nchifukwa ninji kunena kwakuti mwazi ngwofunika kupulumutsa moyo sikukanasintha lingaliro lathu lankhaniyo?

10 Kwa anthu amene sanadziwe kale Yehova, zigomeko zoyanja kuikidwa mwazi panthawi zina zingawonekere kusonyeza ulemu wapamwamba wa kupatulika kwa moyo. Koma sitikuiwala kuti unyinji wa opereka zigomeko m’njirayi umalekereranso kuwonongeka kwa moyo kupyolera mwa kutaya mimba. Yehova amadziwa zowonjezereka za moyo ndi mwazi koposa “katswiri” aliyense wa zamankhwala. Malamulo Ake onse atsimikizira kukhala kaamba ka phindu lathu, kutetezera moyo wathu wamakono ndi ziyembekezo zathu zamtsogolo. (Yes. 48:17; 1 Tim. 4:8) Kodi lamulo la ‘kusala mwazi’ liri ndi kusiyana kulikonse?

11. (a) Kodi ndinjira yokha iti imene Yehova analoleza Aisrayeli kugwiritsira ntchito mwazi? (b) Kodi nchifukwa ninji ichi chiri chofunika kwambiri kwa ife monga Akristu?

11 Kuopsa kwa nkhani ya kupatulika kwa mwazi kwagogomezeredwa ndi zimene Yehova ananena ponena za kugwiritsiridwa ntchito kumodzi kokha kwa mwazi. “Moyo wa nyama ukhala m’mwazi; ndipo ndakupatsani uwu paguwa lansembe, uchite chotetezera moyo wanu pakuti uchita chotetezera ndiwo mwazi, chifukwa cha moyo wake. Chifukwa chake ndinanena kwa ana a Aisrayeli, kuti: Asamadya mwazi mmodzi yense wa inu.” (Lev. 17:11, 12) Mwazi wonse wa nyama wotsanuliridwa paguwa lansembe la Yehova mogwirizana ndi chofunika chimenecho unaphiphiritsira mwazi wamtengo wapatali wa Yesu Kristu. (Aheb. 9:11, 12; 1 Pet. 1:18, 19) Chotero kupatulika kwa mwazi wa Yesu kwenikweniko kwagogomezeredwa ndi lamulo la Mulungu loletsa kugwiritsiridwa ntchito kulikonse kwa mwazi. Kuchokera mu izi kungawonedwe kuti kugwiritsira ntchito molakwa kulikonse kwa mwazi kumasonyeza kupanda ulemu kwakukulu kaamba ka makonzedwe a Yehova a chipulumutso kupyolera mwa Mwana wake.

12. Ngati ayang’anizana ndi imfa, kodi nchifukwa ninji Mkristu wowona samatembenukira ku kugwiritsira ntchito mwazi molakwa kulikonse m’kuyesayesa kukhala ndi moyo?

12 Poyang’anizana ndi mkhalidwe wa moyo kapena imfa, ha mmene kukanakhalira kusawona patali nanga kufulatira Mulungu! Ngakhale kuli kwakuti tikuyamikira mautumiki a madokotala a chikumbumtima chabwino, ife sitimachita mopanda chiyembekezo kuyesa kudzisunga kapena okondedwa athu tiri a moyo kwa masiku owerengeka kapena zaka mwa kuswa lamulo la Mulungu, monga ngati kuti moyo uno ndiwo wokha umene ulipo. Tiri ndi chikhulupiriro mumtengo wa mwazi wokhetsedwa wa Yesu ndi moyo wosatha umene umautheketsa. Ndi mtima wathu wonse tikhulupirira kuti atumiki okhulupirika a Mulungu—ngakhale awo amene amafa—adzafupidwa ndi moyo wamuyaya.—Yoh. 11:25; 1 Tim. 4:10.

Makambitsirano Openda

● Kodi nchiyani chimene chimapangitsa moyo ndi mwazi kukhala zopatulika? Kodi nchifukwa ninji dziko limaumirira kukhala ndi lingaliro losiyana?

● Ponena za nyama, kodi ndimotani mmene timasonyezera ulemu wa kupatulika kwa mwazi wake?

● Kodi ndim’njira zosiyanasiyana zotani m’zimene tonsefe timasonyezera kuti tikuchitira moyo wa munthu monga wopatulika? Kodi kutero kuli kofunika motani?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena