Nyimbo 5
Chilengedwe Chonse, Tamandani Yehova!
1. Chilengedwe, tamani Ya;
Mdalitse dzina lake.
Tsiku lonse angelonso
Amtamanda mokondwa.
2. Dzuŵa mwezi ndi nyenyezi
Zidziŵitsa Mulungu.
Zimamvera malamulo; Sizidzachoka konse.
3. Dziko limtamanda iye.
‘Nkhosazo’ zikusankha.
Kutumikira Mulungu Mumabwalo mokondwa.
4. Khamu lalikulu lidze
Kukachisi wa M’lungu.
Tiyenera kumlambira. Yekhayo ngwokwezeka.