Nyimbo 17
“Mame” a Yehova Pakati pa Anthu Ambiri
1. Okongola ngati mame
Otsalira a Kristu.
Amamchititsatu kaso,
Posonkhana kwa iye.
2. Mkati mwa anthu ambiri,
Afanana ndi mame.
Atsitsimula ngofatsa.
Alondola mtendere.
3. Mabwenzi a otsalira
M’tsikuli Laufumu.
Nkhosa zina nzonga mame,
Zimatumikiranso.
4. Ambiri adzipereka,
Kumenyera Yehova.
Tikhaletu monga mame,
Polengeza Ufumu.