Nyimbo 21
Tamandani Ufumu wa Yehova!
1. Akristunu tamandani
Ufumu wa Yehova,
Wokhazikitsidwa tsono
Ndi Mwana wake mmwamba.
Mikayeli agonjetsa
Satana ndi ziwanda.
Kristuyo adzatamanda
Mulungu m’dziko lonse.
2. Patsogolo “otsalira”
A “kagulu kankhosa”
Atamanda Ufumu wa
Mulungu wokwezedwa.
Oyembekezera dziko
Kukhala paradaiso
Thandizani “otsalira,”
Kulengeza Ufumu.
3. Tamani mosangalala!
Phunzitsani mwaluso;
Thandizani ofatsawo
Kukhala “’nthu abwino.”
Tamani Ufumu wake;
Bukitsani ubwino.
Udzadzetsa madalitso,
Ndi kulemekeza Ya.