Nyimbo 62
Achimwemwe, Ngachifundo!
1. Achimwemwe ngachifundo!
Okongola kwa Mulungu.
Anena kwa abwinowo
M’lungu akonda chifundo.
Pa Kalivali Mulungu
Anakonza dipo lathu.
Adziŵa kufo’ka kwathu,
Ndi kusonyeza chifundo.
2. Odala ndi achifundo;
Akhulukidwa machimo.
Apindula mwachifundo
Kristu pokhala pampando.
Agaŵana chifundochi
Polalikira ponsepo,
Pouza anthu: “Kondwani
Chifukwa Ufumu wadza.”
3. Achifundo asawope
Chiweruzo cha Mulungu;
Adzasonyeza chifundo
Onse okhala m’chifundo.
O tikhale achifundo
Kusonyeza mkhalidwewo
Mwa kuchita nawo mwaŵi
Kutsanzira M’lungu wathu.
(MWALIZANI)
Achimwemwe ngachifundo! Okongola kwa Mulungu.