Nyimbo 98
Kumenyera Nkhondo Chikhulupiliro
(Yuda 3)
1. Yesu ananeneratu,
Zoipa zachuluka.
Chikondi cha ochuluka;
Chakhala chozirala.
Chotero tilimbikire
Chikhulupilirocho
Cholandiridwa ndi mpingo
Wachikristu wakale.
2. Tisalole Satanayo
Kutifo’ketsa ife;
Koma tiime zolimba,
Mwantchito ndi pemphero.
Mwa kumenyabe nkhondoyo,
Sitidzawopa anthu,
Tidzalimbikitsanabe
Kuti tipiliretu.
3. Menyerani nkhondo zedi
Chikhulupilirocho.
Khalani mboni zolimba
Kufikira mapeto.
Mwa kuyeretsedwa kwa Ya
Kuipa kudzathadi,
Tidzawomboledwa ndithu
Mwa Teokrase wake.