Nyimbo 104
Nyimbo kwa Wammwambamwambayo
1. Tiimbire Yehovayo;
Chitamandocho ndichake.
Mokondwa tiimbira Ya,
Tilengeza za mphamvu yake.
(Korasi)
2. Kondwa lipenga lilira:
Ufumu wa Ya wabadwa.
Khalidwe kwa Mpulumutsi,
Lisonye chiphunzitso chake.
(Korasi)
3. Tiri m’nthaŵi “zotsiriza”;
Tetezera kulambira.
Mulungu ngwachilakiko;
Tipereka thamo kwa iye.
(KORASi)
Yehova alamula;
Apeza chilakiko.
Ndi Mwanayo, Wofunika,
Ufumuwo wadza.