Nyimbo 151
Tilalikire Mbiri Yabwino Imeneyi Yaufumu
1. Lalika Mbiri Yabwino ya Ufumu wa M’lungu.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Polalika mbiriyi tikhale olimba mtima.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Lalika mbiri pamakwalala ndi pamakomo;
Lalika mbiri yolembedwa kumitundu.
Lalika mwaluso, chifundo ndiponso mwachangu.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
2. Lalika madyererowo Yehova adzakonza.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Kuti lidzakhala phwando logaŵira ofatsa.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Lalika mbiri ya phwando la vinyo wosankhika,
Kuti onse anjala adzadye chakudya.
Kuti chipulumutso chikaŵalitsa pankhope.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
3. Lalika chisangalalo chomwe chidzakhalapo.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Okonda Mawu a M’lungu sakhala ndi chisoni.
Tilalike mbiri ya Ufumu!
Nenani pali thandizo kwa ochita chabwino,
Pali mtendere kwa odalira Mulungu.
Kutumikira Mulungu kuli kokondweretsa.
Tilalike mbiri ya Ufumu!