Nyimbo 160
Kuyenda Muumphumphu
1. Weruzeni Yehova Mulungu.
Ndidalira inu ndiyenda mu’mphumphu.
Ndipendeni ndi kundiyesatu;
Mundiyeretsetu ndidalitsidwedi.
(Korasi)
2. Sindikhala ndi anthu oipa.
Ndimadana ndi onyoza chowonadi.
Musachotse moyotu wangawu,
Ndi anthu ochimwa odzala chiwawa.
(Korasi)
3. Munyumbayo ndikonda kukhala.
Kulambira kwanuko kuli kwangwiro.
Ndidzayenda kuguwa lanulo,
Kukutamandani padzikolonseli.
(KORASi)
Koma ine Ndatsimikizira
Kuti ndidzayenda Mu’mphumphu kosatha!