Nyimbo 185
Chiukiliro—Makonzedwe Achikondi a Mulungu
1. Chiukiliro chisonya
Chifundo cha M’lungu,
Chatsimikizidwa n’Kristu
M’chikondi cha M’lungu.
“Kagulu” kadzaukatu;
N’kukhala ndi moyo.
Popilira mpaka kufa,
Adzalamulira.
2. Moyo udzapatsidwanso
‘Kumtambo wa mboni.’
‘Chiukiliro chabwino’
Chalonjezedwatu.
Ngati “nkhosa zina” zifa
Zidzaukitsidwa
Kuchokera kumandako
Kudzatama M’lungu.
3. Onsewo okhala m’manda
Adzamvatu Yesu
Monga mbala yofa n’Yesu,
Adzakondwa m’moyo.
Potsiriza zaka chikwi,
Palitu chiyeso;
Amene adzapambana
Adzadalitsidwa.
4. O “otsalira” nonsenu
Ndi ‘nkhosa zinanu,’
Nenani akufa awo,
Adzawawonanso.
Chulukani muntchitozo
Mbuye walamula,
Poti mudziŵa imfayo
Singaletse mphotho.