Nyimbo 206
‘Kondwerani m’Chiyembekezo’
1. Tiyamikira Mulungu
Ka’mba ka chiyembekezo.
Chiritu ngati nangula;
Chithandiza kupilira.
Chirinso ngati chisoti,
Chiletsa mivi kupyoza;
Chitichotsera zoipa
Chilimbitsa m’chilungamo.
2. Tikondwa m’chiyembekezo
Akufawo adzauka
Kuchoka kumanda awo
Kudzapanga paradaiso!
Inde, kunthaŵi zosatha
Adzakhalabe padziko
Adzapezatu chimwemwe,
M’makonzedwe a Mulungu.
3. M’chiyembekezo cholimba,
Tisachitetu choipa,
Koma kuphunzira Mawu
A M’lungu ndi kupemphera.
Kuti enanso akondwe,
Mwa dyera tisabisire,
Koma tidziŵitse iwo,
Kuti aime kwa M’lungu.