Chifukwa Chake Tiyenera Kudziwa Dzina la Mulungu
“ALIYENSE amene amaitanira padzina la Yehova adzapulumutsidwa.” (Aroma 10:13, NW) Mwamawu amenewa mtumwi Paulo anagogomezera mmene kuliri kofunika kwa ife kudziwa dzina la Mulungu. Mawu ake akutibwezera kufunso lathu loyambirira lakuti: Kodi nchifukwa ninji Yesu anaika ‘kuyeretsedwa,’ kapena ‘kupatulidwa,’ kwa dzina la Mulungu pachiyambi penipeni pa Pemphero lake Lachitsanzo, patsogolo pankhani zina zambiri zofunika kwambiri motero? Kumvetsetsa mfundoyi, ife tifunikira kuzindikira bwinopo pang’ono tanthauzo la mawu aakulu awiri.
Choyamba, kodi mawu akuti ‘kuyeretsa,’ kapena ‘kupatula,’ amatanthauzanji kwenikweni? Kwenikweni iwo amatanthauza kuti: “kuyeretsa.” Koma kodi dzina la Mulungu siliri loyera kale? Ndithudi iro liri lotero. Pamene tipatula dzina la Mulungu, sitimalipangitsa kukhala loyera kwambiri koposa mmene liliri. M’malo mwake timalizindikira kukhala loyera, loikidwa padera, lolemekezedwa koposa. Pamene tipempherera dzina la Mulungu kupatulidwa, tikuyang’anira m’tsogolo kunthawi pamene chilengedwe chonse chidzalilemekeza monga loyera.
Chachiwiri, kodi kwenikweni nchiyani chimene chiri tanthauzo la liwulo “dzina”? Tawona kuti Mulungu ali ndi dzina, Yehova, ndi kuti dzina lakelo limawonekera nthawi zikwi zambiri m’Baibulo. Takambitsirananso, ponena za kufunika kwa kubwezeretsa dzinalo m’malo ake oyenerera m’malembo Abaibulo. Ngati dzinalo siliri mmenemo, kodi ndimotani mmene mawu a wamasalmo angakwaniritsidwire akuti: “Iwo akudziwa dzina lanu adzakhulupirira inu; pakuti, inu Yehova, simunawasiya iwo akufuna inu.”—Salmo 9:10.
Koma kodi ‘kudziwa dzina la Mulungu’ kumaphatikizapo chidziwitso chokha cha m’mutu chakuti dzina la Mulungu m’Chihebri ndilo YHWH, kapena m’Chichewa, Yehova? Ayi, kumatanthauza zoposa zimenezo. Pamene Mose anali Paphiri la Sinai, “Yehova anatsika mumtambo, naimapo pamodzi ndi iye [Mose] nafuula dzina la Yehova.” Kodi kulengezedwa kwadzina la Yehova kumeneku kunaphatikizapo chiyani? Kulongosoledwa kwa mikhalidwe yake iyi: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekeleza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.” (Eksodo 34:5, 6) Kachiwirinso, mwamsanga imfa yake isanachitike, Mose anati kwa Aisrayeli: “Ndidzalalikira dzina la Yehova.” Kodi nchiyani chimene chinatsatira? Kutchulidwa kwa ina ya mikhalidwe Yake yaikulu, ndiyeno kupendedwa kwa zimene Mulungu anali atakwaniritsa kulinga kwa Israyeli kaamba ka dzina Lake. (Deuteronomo 32:3-43) Chifukwa chake, kudziwa dzina la Mulungu kumatanthauza kuphunzira chimene dzinalo limaimira ndi kulambira Mulungu mwini dzinalo.
Popeza kuti Yehova wagwirizanitsa dzina lake ndi mikhalidwe yake, zifuno ndi machitidwe, tingathe kuwona chifukwa chake Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu nloyera. (Levitiko 22:32) Iro liri laulemerero, lalikulu, lochititsa mantha ndi lapamwambamwamba. (Salmo 8:1; 99:3; 148:13) Inde, dzina la Mulungu nloposalebulo wamba. Iro limaimira iye monga munthu. Iro silinali kokha dzina lakanthawi loti ligwiritsiridwe ntchito kwanthawi yochepa ndiyeno kulowedwa m’malo ndi maina aulemu onga akuti “Ambuye.” Yehova iye mwiniyo anati kwa Mose: “Yehova, . . . ndidzina langa nthawi yosatha, ichi ndichikumbukiro changa m’mibadwo mibadwo.”—Eksodo 3:15.
Ngakhale ayese motani, munthu sadzachotsa konse dzina la Mulungu padziko lapansi. “Pakuti kuyambira kotulukira dzuwa kufikira kolowera kwake dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu; ndipo m’malo monse adzaperekera dzina langa chofukiza ndi chopereka chowona; pakuti dzina langa lidzakhala lalikuru mwa amitundu, ati Yehova wamakamu.”—Malaki 1:11; Eksodo 9:16; Ezekieli 36:23.
Chifukwa cha ichi, kupatulidwa kwa dzina la Mulungu nkofunika kwambiri koposa nkhani ina iriyonse. Zifuno za Mulungu zonse nzogwirizanitsidwa nalo. Ndithudi, mavuto amtundu wa anthu anayamba pamene kwanthawi yoyamba Satana anachitira mwano dzina la Yehova mwa kumtcha Iye wabodza, ndi wosayenerera kulamulira fuko laumunthu. (Genesis 3:1-6; Yohane 8:44) Kokha pamene dzina la Mulungu lilemekezedwa bwino lomwe kuti mtundu wa anthu udzasangalala ndi chimasuko chotheratu kuchokera kuziyambukiro zowononga za bodza la Satana. Ndicho chifukwa chake Akristu amapempherera mwaphamphu kwambiri kaamba ka kupatulidwa kwa dzina la Mulungu. Komanso, palinso zinthu zimene iwo angachite kuliyeretsa.
Kodi Ndimotani Mmene Tingayeretserere Dzina la Mulungu?
Njira imodzi ndiyo kulankhula kwa ena ponena za Yehova ndi kusonya ku Ufumu wake kudzera mwa Yesu Kristu monga chiyembekezo chokha cha anthu. (Chivumbulutso 12:10) Ochuluka akuchita ichi, m’kukwaniritsidwa kwamakono kwa mawu aulosi a Yesaya awa: “Tsiku lomwelo mudzati, Muyamikire Yehova, bukitsani dzina lake, mulalikire machitidwe ake mwa mitundu ya anthu, munene kuti dzina lake lakwezedwa. Muimbire Yehova; pakuti wachita zaulemerero’ chidziwike ichi m’dziko lonse.”—Yesaya 12:4, 5.
Njira ina ndiyo kumvera malamulo a Mulungu ndi malangizo. Yehova anauza mtundu wa Israyeli kuti: “Muwasunge malamulo anga, ndi kuwachita; ine ndine Yehova. Musamaipsa dzina langa loyera; koma ndikhale woyera pakati pa ana a Israyeli; ine ndine Yehova wakukupatulani.”—Levitiko 22:31, 32.
Kodi ndimotani mmene kusunga Chilamulo kwa Aisrayeli kunapatulira dzina lake? Chilamulo chinaperekedwa kwa Aisrayeli pamaziko a dzina lake. (Eksodo 20:2-17) Chifukwa chake, pamene iwo anasunga Chilamulo, iwo anali kusonyeza ulemu woyenerera ndi kulemekezedwa kwa dzinalo. Ndiponso, dzina la Yehova linali pa mtundu wa Aisrayeli. (Deuteronomo 28:10; 2 Mbiri 7:14) Pamene iwo anachita moyenerera, izi zinawabweretsera chiyanjo chake, monga momwedi mwana amene amachita modzisungira bwino amabweretserera ulemu kwa atate wake.
Kumbali ina, pamene Aisrayeli analephera kusunga Chilamulo cha Mulungu, iwo anachitira mwano dzina lake. Chotero, machimo onga kuperekera nsembe mafano,kulumbira monama, kutsendereza osauka ndi kuchita dama lachigololo zalongosoledwa m’Baibulo kukhala ‘kuchitira mwano dzina la Mulungu.’—Levitiko 18:21; 19:12; Yeremiya 34:16; Ezekieli 43:7.
Mofananamo, Akristu apatsidwa lamulo m’dzina la Mulungu. (Yohane 8:28) Ndipo, iwonso, ali ogwirizanitsidwa ndi ‘anthu a dzina la Yehova.’ (Machitidwe 15:14) Chifukwa chake, Mkristu amene amapemphera mowona mtima kuti “Dzina lanu liyeretsedwe” adzapatula dzinalo m’moyo wa iyemwini mwa kumvera malamulo onse a Mulungu. (1 Yohane 5:3) Zimenezi zikaphatikizaponso malamulo operekedwa ndi Mwana wa Mulungu, Yesu, amene nthawi zonse analemekeza Atate wake.—Yohane 13:31, 34; Mateyu 24:14; 28:19, 20.
Usiku wa imfa yake isanachitike, Yesu anagogomezera kufunika kwa dzina la Mulungu kwa Akristu. Atanena kwa Atate wake kuti: “Ndinazindikiritsa iwo dzina lanu, ndipo ndidzalizindikiritsa,” iye akupitirizabe kulongosola kuti, “kuti chikondi chimene munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndi ine mwa iwo.” (Yohane 17:26) Kuphunzira kwa ophunzirawo dzina la Mulungu kunaphatikizapo kufika pa kuzindikira kwawo iwo eni chikondi cha Mulungu. Yesu anali atachititsa kukhala kotheka kwa iwo kuzolowerana ndi Mulungu monga Atate wawo wachikondi.—Yohane 17:3.
Mmene Limakuyambukirirani
Pamsonkhano wa m’zaka zazana loyamba wa atumwi ndi akulu Achikristu m’Yerusalem, wophunzira Yakobo anati: “Sumioni wabwereza kuti poyamba Mulungu anayang’anira amitundu, kuti atenge mwa iwo anthu a dzina lake.” Kodi inu mungadziwikitsidwe ndi awo amene Mulungu amawatenga kukhala “anthu a dzina lake” ngati mulephera kugwiritsira ntchito kapena kunyamula dzinalo?—Machitidwe 15:14.
Ngakhale kuli kwakuti ambiri ali okaikira kugwiritsira ntchito dzina la Yehova, ndi kuti otembenuza Baibulo ambiri amalisiya m’matembenuzidwe awo, mamiliyoni ambiri aanthu kuzungulira dziko avomereza mwachimwemwe mwayi wa kunyamula dzina la Mulungu, kuligwiritsira ntchito osati kokha m’kulambira komanso m’kalankhulidwe kawo katsiku ndi tsiku, ndi kulilengeza kwa ena. Ngati munthu wina akanalankhula nanu za Mulungu Wabaibulo nagwiritsira ntchito dzina lakuti Yehova, kodi ndikagulu kachipembedzo kati kamene inu mukanamgwirizanitsa nako? Pali kagulu kamodzi kokha m’dziko kamene kamagwiritsira ntchito dzina la Mulungu nthawi zonse m’kulambira kwawo, monga momwedi olambira ake am’nthawi zakale anachitira. Iwo ndiwo Mboni za Yehova.
Dzina lozikidwa pa Baibulo lakuti Mboni za Yehova limadziwikitsa Akristu amenewa kukhala ‘anthu a dzina la Mulungu.’ Iwo amanyadirira kunyamula dzinalo, chifukwa chakuti ndilo limene Yehova Mulungu iyemwiniyo anapereka kwa alambiri owona. Pa Yesaya 43:10, timawerenga kuti: “Ndinu mboni zanga, ati Yehova, ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha.” Kodi ndani amene Mulungu anali kulankhula za iye panopa? Talingalirani ena a mavesi oyambirira.
M’vesi 5 kufikira 7 la mutu umodzimodziwo, Yesaya akuti: “Usawope; pakuti ine ndiri ndi iwe; ndidzatenga mbewu zako kuchokera kum’mawa, ndi kusonkhanitsa iwe kuchokera kumadzulo. Ine ndidzati ndi kumpoto, Pereka; ndi kummwera, Usaletse; bwera nawo ana anga aamuna kuchokera kutali, ndi ana anga aakazi kuchokera kumalekezero a dziko lapansi; yense wotchedwa dzina langa, amene ndinamlenga chifukwa cha ulemerero wanga; ndinamuumba iye; inde, ndinampanga iye.” M’tsiku lathu, mavesi amenewo amasonya kwa anthu enieniwo a Mulunguamene wawasonkhanitsa m’mitundu yonse kumtamanda ndi kukhala mboni zake. Chotero dzina la Mulungu silimamdziwikitsa kokha iye komanso limathandiza kudziwikitsa atumiki ake owona padziko lapansi lerolino.
Madalitso a Kudziwa Dzina la Mulungu
Yehova amatetezera awo okonda dzina lake. Wamasalmo anati: “Popeza andikondadi ndidzampulumutsa; ndidzamkweza m’mwamba, popeza adziwa dzina langa.” (Salmo 91:14) Iye amawakumbukiranso iwo: “Pamenepo iwo akuwopa Yehova analankhula wina ndi mnzake; ndipo Yehova anawatchela khutu namva, ndi bukhu lachikumbutso linalembedwa pamaso pake, la kwa iwo akuwopa Yehova, nakumbukira dzina lake.”—Malaki 3:16.
Chotero, mapindu ochokera m’kudziwa ndi kukonda dzina la Mulungu sali olekezera kumoyo uno wokha. Kwa anthu omvera Yehova walonjeza moyo wosatha m’chimwemwe padziko lapansi Laparadaiso. Davide anauziridwa kulemba kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa: koma iwo akuyembekeza Yehova iwowa adzalandira dziko lapansi. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:9, 11.
Kodi zimenezi zidzatheka motani? Yesu anapereka yankho. m’Pemphero Lachitsanzo limodzimodzilo kumene anatiphunzitsa kupemphera kuti, “Dzina lanu liyeretsedwe,” iye anawonjezera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Inde, Ufumu wa Mulungu kudzera mwa Yesu Kristu udzapatula dzina la Mulungu ndi kubweretsanso mikhalidwe yabwino kudziko lapansili. Udzachotsa kuipa ndi kuchotsa nkhondo, upandu, njala, utenda ndi imfa.—Salmo 46:8, 9; Yesaya 11:9; 25:6; 33:24; Chivumbulutso 21:3, 4.
Mungakhoze kusangalala ndi moyo wosatha pansi pa Ufumu umenewu. Motani? Mwa kudziwa Mulungu. “Ichi chitanthauza moyo wosatha, kuchilandira kwawo chidziwitso cha inu, Mulungu wowona yekha, ndi cha uyo amene munamtuma, Yesu Kristu.” (Yohane 17:3, NW) Mboni za Yehova zidzakondwera kukuthandizani kulandira chidziwitso chopatsa moyo chimenecho.—Machitidwe 8:29-31.
Kukuyembekezeredwa kuti chidziwitso cha m’kabukhu kano chakukhutiritsani kuti Mlengi ali ndi dzina la iye mwini limene liri lofunika kwambiri kwa iye. Iro liyenera kukhalanso lamtengo wapatali kwambiri kwa inu. Muzindikiretu kufunika kwa kudziwa ndi kugwiritsira ntchito dzinalo, makamaka m’kulambira.
Ndipo mutsimikizetu kunena monga momwe mneneri Mika adanenera molimba mtima zaka mazana ambiri zapitazo kuti: “Mitundu yonse ya anthu idzayenda, wonse m’dzina la mulungu wake, ndipo ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu kunthawi yomka muyaya.”—Mika 4:5.
[Mawu Otsindika patsamba 28]
‘Kudziwa dzina la Mulungu’ kumatanthauza zambiri koposa kukhala ndi chidziwitso cham’mutu cha chenicheni chakuti dzina lake ndilo Yehova
[Mawu Otsindika patsamba 30]
Dzina la Yehova liri ‘laulemerero, lalikuru, lochititsa mantha ndi lapamwamba koposa.’ Zifuno zonse za Mulungu nzogwirizanitsidwa ndi dzina lake
[Bokosi patsamba 29]
M’nkhani ya mu Anglican Theological Review (October 1959), Dr. Walter Lowrie anagogomezera kufunika kwa kudziwa dzina la Mulungu. Iye analemba kuti: “M’maunansi aumunthu nkofunika kwambiri kudziwa dzina lenileni la munthu, dzina laumwini, la munthu amene timakonda, amene timalankhula naye, kapena ngakhale pamene tiri pafupi kulankhula naye. Zimenezo ziridi choncho ndi unansi wa munthu kwa Mulungu. Munthu amene sadziwa Mulungu ndi dzina sakumdziwadi iye monga munthu, ndipo alibe kuzolowerana kwakukambitsirana naye (chimene chiri tanthauzo lapemphero), ndipo sangakhoze kumkonda, ngati iye amangomdziwa kokha kukhala mphamvu yopanda umunthi.”