Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 1 tsamba 4-12
  • Kodi Planeti Dziko Lapansi Lidzakhala Chiyani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Planeti Dziko Lapansi Lidzakhala Chiyani?
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ZENIZENI ZIMENE SIZIYENERA KUNYALANYAZIDWA
  • KODI DZIKO LAPANSI LIDZAKHALA KWAUTALI WOTANI?
  • Kodi Dziko Lapansi Lidzathera m’Moto?
    Galamukani!—1997
  • Dziko Lapansi
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Dziko Lapansi Lidzawonongedwa?
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Dzikoli Lidzatha?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 1 tsamba 4-12

Mutu 1

Kodi Planeti Dziko Lapansi Lidzakhala Chiyani?

KODI mtsogolo mwakusungirani chiyani monga mmodzi wa anthu mabiliyoni ambiri okhala ndi moyo tsopano pa planetili Dziko Lapansi? Kodi mungakonde kuti ukhale moyo wamtendere ndi chisungiko, pakati pa anthu okondanadi? Zimenezo ndi zina zambiri zingakhale zanu. Koma sindimo mtsogolo mmene unyinji ukuyembekezera. Chifukwa ninji?

2 Chiwopsezo cha nkhondo ya nyukliya chayambitsa zikayikiro zazikulu ponena zakuti kaya padzakhala mtsogolo mulimonse kwa unyinji waukulu wa fuko la anthu. Pamene bomba la atomu linagwiritsiridwa ntchito m’nkhondo kwa nthaŵi yoyamba mu 1945, oposa 70 000 amuna, akazi ndi ana anaphedwa nthaŵi yomweyo. Zikwi zina zambiri zinafa imfa yomvetsa ululu mkati mwa masiku ndi zaka zotsatirapo. Koma lerolino bomba lenileni limodzi lankhondo liri ndi mphamvu ya kuphulika ya mabomba onse amene anaponyedwa mkati mwa Nkhondo Yadziko II. Pali zikwi makumi ambiri za zida zankhondo za nyukliya zolinganizidwira kugwiritsiridwa ntchito kwa mwamsanga. Ndiponso dziko likuwononga $2 000 000 000 patsiku kaamba ka mpikisano wa zida zankhondo umene umasiya anthu ambiri akuchita mantha.

3 Koma kodi bwanji ngati pangakhale kokha “nkhondo yanyukliya yaing’ono”? Zotulukapo zikakhalabe zowopsa. Mogwirizana ndi kunena kwa Carl Sagan, wasayansi wotchuka kwambiri, ngati mitundu ikanati igwiritsire ntchito ngakhale yochepa yake yanyukliya, “mposakayikiritsa kuti kutsungula kwathu kwa dziko lonse kukawonongedwa. . . . Ndipo pakuwonekera kukhala pali kuthekera kwenikweni kwa kusolotsedwa kwa anthu.” Anthu ambiri amayesa kuchotsa ziyembekezo zoterozo m’maganizo mwawo, koma kumeneko sikumachotsa ngoziyo. Chiŵerengero chokula mofulumira cha ena chapanga magulu a kupulumuka. Moyembekezera kuti ena adzapulumuka, amanga malo othaŵira m’madera akutali nawadzaza zakudya ndi mankhwala, ndiponso mfuti zothamangitsira oukira osafunikawo.

4 Kuwonjezera pankhondo yanyukliya, asayansi akuchenjeza za kuthekera kwa chiwonongeko chadziko chochokera m’njira imene malo akuwonongedwera. Kuipitsidwa kwa mpweya umene timapuma ndiko magwero a nkhaŵa yaikulu. Nkhalango zikuwonongedwa pamlingo wochititsa mantha; komabe zimenezi nzofunika ku kuzungulira kwa okosijeni yadziko lapansi, kuzungulira kwake kwa mvula ndi kusungitsa nthaka. Mwakupulukira ndi umbombo, malo achonde ofunika akuwonongedwa. Madzi akuipitsidwa, kaŵirikaŵiri ndi mankhwala akupha. Komabe zinthu zimenezi nzofunika kuchirikizira moyo wa anthu.

5 Inu mungalingalire kuti, chochititsa nkhaŵa mofulumira kwambiri, ndicho chenicheni chakuti upandu wachiwawa ukuchititsa anthu kukhala akaidi m’nyumba zawozawo. Chipolowe cha ndale zadziko ndi cha anthu chimachititsa moyo kukhala paupandu. Ulova wowanda ndi kuwonjezereka kwa kukwera mitengo zimachititsa umphaŵi ndi kugwiritsidwa mwala. Moyo wapanyumba wa ambiri ngwosakhuturitsa konse; kaŵirikaŵiri zomangira za chikondi zimene ziyenera kugwirizanitsa banja pamodzi zikusoŵeka. Kulikonse mkhalidwe wa anthu ngwakuti “Ine choyamba!”

6 Pamenepa, kodi nkuti, kumene munthu aliyense angapezeko maziko abwino oyembekezera kukhala ndi moyo wachisungiko? Ngati mtsogolo mwathu monga nzika za dziko lapansi munadalira kotheratu pa zimene anthu ndi mitundu amene akuchititsa mavuto ameneŵa ali ofunitsitsa ndi okhoza kuchita, mkhalidwewo ukakhaladi wopanda chiyembekezo. Koma kodi ziri choncho?

ZENIZENI ZIMENE SIZIYENERA KUNYALANYAZIDWA

7 M’zolinganiza zawo, anthu mwakaŵirikaŵiri samaphatikizamo Mlengi wa dziko lapansi ndi wa anthu. Koma kodi tingadziŵe motani chimene chiri chifuno Chake? Baibulo limatiuza. Bukhu limeneli limalongosola mobwerezabwereza kuti zimene zalembedwamo nzochokera kwa Mulungu, zouziridwa ndi Mulungu. Kodi kudzinenera kumeneku nkowona? Ngati kuli kowona, moyo wanu umadalira pa kuchita mogwirizana nalo. Chifukwa cha kufunika kwa nkhaniyi, tikukufulumizani kuti mupende Baibulolo nokha. Mudzapeza maulosi ake ochuluka kukhala apadera osonyeza chidziŵitso chatsatanetsatane chamtsogolo. Nzeru yake njosayerekezereka pamene ikufotokoza zinthu zimene ziri zofunika koposa ku chimwemwe chanu chosatha. Tiri ndi chidaliro chakuti, ngati mulingalira maumboni momomasuka maganizo, mudzazindikira kuti Baibulo likatha kokha kuchokera kumagwero auzimu, kwa Mulungu amene amakondadi anthu.a Baibulo liri ndi chidziŵitso chimene chiri chofunika ku kupulumuka kwathu panthaŵi yovuta ino m’mbiri ya anthu. Moyenerera, ndibukhu lofalitsidwa mofala koposa onse padziko lapansi.​—⁠Wonani 2 Petro 1:​20, 21; 3:​11-14; 2 Timoteo 3:​1-5, 14-17.

8 Vesi loyamba la Baibulo limalongosola chowonadi chofunika chakuti “Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.” (Genesis 1:⁠1)b Ngakhale anthu ena amasankha kusiya Mulungu kukhala wopanda dzina, Baibulo silimatero. Polongolosa Mlengi ndi dzina, Genesis 2:4 akutiuza kuti “Yehova Mulungu anapanga dziko lapansi ndi zakumwamba.” (Wonaninso Genesis 14:22; Eksodo 6:3; 20:11.) Mbali yaikulu ya Baibulo poyamba inalembedwa m’Chihebri, ndipo m’bukhu Labaibulo Lachihebri dzina lenileni la Mulungu limawonekera pafupifupi nthaŵi 7 000 monga dzina lopatulika la zilembo zinayi (יהוה). Omasulira ena amalitembenuza kukhala Yahweh, koma m’Chicheŵa mpangidwe wogwiritsiridwa ntchito mofala wa dzinalo ndiwo Yehova.

9 Dzinali silinapekedwe ndi anthu opembedza. Linasankhidwa ndi Mlengi mwiniyo. (Eksodo 3:​13-15; Yesaya 42:⁠8) Sidzina loti ligwiritsiridwe ntchito mosinthanitsa ndi Buddha, Brahma, Alla kapena Yesu. Moyenerera mneneri Mose anakumbutsa mtundu wakale wa Israyeli: “Dziŵani lerolino nimukumbukire m’mtima mwanu, kuti Yehova [Chihebri: יהוה] ndiye Mulungu, m’thambo lakumwamba ndi padziko lapansi palibe wina.” (Deuteronomo 4:39) Uyu ndiye Mulungu kwa amene Yesu Kristu anapemphera, Iye amene anamutcha “Mulungu wowona yekha.” Lerolino akulambiridwa ndi anthu ophunzitsidwa ochokera mu mtundu uliwonse padziko lapansi.​—⁠Yohane 17:3; Mateyu 4:​8-10; 26:39; Aroma 3:⁠29.

10 Chifukwa chakuti Yehova ndiye Mlengi wa dziko lapansi, planeti lonseli nlake, ndipo mtsogolo mwake muli m’manja mwake. (Deuteronomo 10:14; Salmo 89:11) Mavuto a anthu saali oposa mphamvu ya Mulungu ya kuŵathetsa. Chiyembekezo cha nkhondo yanyukliya chimachititsa anthu mantha. Koma kodi ndimalamulo ayani amene amalamulira machitidwe a nyukliya amene anachitika pamlingo wowopsa m’nyenyezi mabiliyoni osaŵerengeka? Kodi Mulungu alibe chidziŵitso ndi mphamvu zofunika kutetezera moyo pa planeti Dziko lapansi? Mofananamo, mavuto amene abuka chifukwa chakuti anthu ponse paŵiri mwaumbuli ndi mwadyera aipitsa malo awo okhala sadzalepheretsa chifuno cha Mulungu Wamphamvuyonse. Iye amene anali ndi nzeru ndi mphamvu zofunika kulengera dziko lapansi ndi mitundu yamoyo yochititsa chidwi pa ilo angazipatsenso chiyambi choyeretsedwa ngati chimenecho chiri chifuniro chake. (Yesaya 40:26; Salmo 104:24) Pamenepa, kodi nchiyani chimene, chiri chifuno cha Yehova mogwirizana ndi malo anthu okhala?

KODI DZIKO LAPANSI LIDZAKHALA KWAUTALI WOTANI?

11 Kodi chifuno cha Mulungu ndicho kuwononga dziko lapansi ndi zinthu zonse zamoyo pa ilo? Openda nyenyezi ena amanena kuti potsirizira pake dzuŵa lathu lidzakhala ndi kukula kwakukulu ndipo lidzakuta dziko lapansi. Pali ena amene amalingalira kuti, chifukwa cha mkhalidwe wa chilengedwe chowoneka weniweniwo, nthaŵi iyenera kudza pamene dzuŵa silidzaŵalanso ndipo dziko lapansi silidzachirikizanso moyo. Koma kodi iwo ngolondola? Kodi Mlengi amanenanji​—⁠Iye amene analenga dzuŵa ndi zinthu, Iye amene anayambitsa malamulo pa amene kukhalapo kwathu kumadalira?​—⁠Yobu 38:​1-6, 21; Salmo 146:​3-6.

12 Yehova anauzira Mfumu yanzeru Solomo kulemba za utali wa moyo wa munthu poyerekezeredwa ndi nyengo ya dziko lapansi lenilenilo. Pa Mlaliki 1:4 Solomo analemba mawu awa: “Mbadwo wina upita, mbadwo wina nufika; koma dziko lingokhalabe masiku onse.” Mbiri ya anthu imatsimikizira kunena zowona kwa ameneŵa. Ngakhale mbadwo umodzi wa anthu waloŵedwa m’malo ndi wina, dziko lapansi, mbulumbwa pamene imene tikukhala, limakhala chikhalire. Koma kwautali wotani? Mogwirizana ndi kumasulira kwenikweni kwa New World Translation of the Holy Scriptures, lidzakhala “kunthaŵi yosadziŵika.” Kodi zimenezo zikutanthauzanji?

13 Liwu Lachihebri lakuti ‘oh·lamʹ, lotembenuzidwa panopa “kunthaŵi yosadziŵika,” kwakukulukulu limatanthauza nyengo ya nthaŵi imene, mwa lingaliro la nthaŵi ino, iri yosadziŵika kapena yobisika koma ya nyengo yaitali. Imeneyo ingatanthauze kosatha. Kodi ikutero m’chochitika chino? Kapena kodi mawu ameneŵa amasonyeza kuti mwinamwake pa nthaŵi ina yamtsogolo mosadziŵika, yobisika kwa ife tsopano, dziko lapansi lidzatha? Zinthu zina zimene Baibulo limanena kuti zikapitiriza “kunthaŵi yosadziŵika” potsirizira pake zanadzathadi. (Yerekezerani ndi Numeri 25:13; Ahebri 7:12.) Koma Malemba amagwirizanitsanso ‘oh·lamʹ ndi chija chimene chiri chamuyaya​—⁠mwachitsanzo Mlengi mwiniyo. (Yerekezerani Salmo 90:2 ndi 1 Timoteo 1:17.) Ponena za chimene mawuwo amatanthauza ponena za dziko lapansi, sitikusiyidwa m’chikaikiro. Pa Salmo 104:5 tikuuzidwa: “Anakhazika dziko lapansi pamaziko ake, silidzagwedezeka kunthaŵi yonse.”c​—⁠Wonaninso Salmo 119:⁠90.

14 Chimene chidzakhala kosatha sindicho kokha mbulumbwa youma ndi yopanda kanthu. Pa Yeremiya 10:​10-12 (NW) tikuuzidwa: “Ndithudi Yehova ndiye Mulungu. . . . Ndiye Wopanga dziko lapansi ndi mphamvu yake, Iye wokhazikitsa zolimba dziko lobala ndi nzeru zake, ndi Amene mwa luntha lake anafunyulula thambo.” Wonani kuti sikokha kuti anapanga “dziko lapansi” komanso anakhazikitsa zolimba “dziko lobala.” Mmalo mwa mawu otsiriziraŵa, omasulira ambiri amatembenuza liwu Lachihebrilo te·velʹ kukhala kokha “dziko.” Komabe malinga ndi kunena kwa Old Testament Word Studies lolembedwa ndi William Wilson, te·velʹ limatanthauza “dziko lapansi, monga lachonde ndi lokhalidwa ndi anthu, mbulumbwa yokhalidwa, dziko.” Ponena za chifuno cha Yehova cha dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu ndi lachonde limeneli, Salmo 96:10 (NW) motsimikiziritsa limalengeza: “Yehova mwiniyo wakhala mfumu. Dziko lobala zipatso nalonso likhala lokhazikitsidwa zolimba kotero kuti silingagwedezedwe.”​—⁠Wonaninso Yesaya 45:⁠18.

15 Motero kuli mogwirizana ndi planeti Dziko lapansi pa limene tikukhala chakuti Yesu Kristu anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kwa Mulungu: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba, chomwecho pansi pano.”​—⁠Mateyu 6:​9, 10.

16 Chifuniro cha Yehova sichakuti dziko lapansi likhalidwe ndi anthu opanda ulemu kwa Mwiniwake ndi okhala ndi chikondi chochepa kwa wina ndi mnzake. Kalekale iye analonjeza kuti: “Ochita zoipa adzadulidwa; koma iwo akuyembekeza Yehova, iwoŵa adzalandira dziko lapansi. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:​9, 29) “Dziko lapansi lokhalidwa ndi anthu lirinkudzalo,” limene Baibulo limalankhula, lidzakhala ndi anthu owopa Mulungu ndi okonda mowonadi anthu anzawo. (Ahebri 2:5; yerekezerani ndi Luka 10:​25-28.) Masinthidwe ochitidwa pansi pa Ufumu wakumwamba wa Mulungu adzakhala aakulu kwambiri chakuti Baibulo limatchula “dziko lapansi latsopano”​—⁠osati mbulumbwa yosiyana, koma chitaganya chatsopano cha anthu chimene chidzakhala pakati pa mikhalidwe ya paradaiso imene Mlengi wa anthu analinganiza kuyambira panthaŵi imene anayamba chilengedwe chake chadziko lapansi.​—⁠Chivumbulutso 21:​1-5; Genesis 2:​7-9, 15.

17 Kwenikweni, kukhazikitsidwa kwa “dziko lapansi latsopano” limenelo, kudzatsatira chiwonongeko chachikulu​—⁠chija choposa chirichonse chimene anthu anawonapo. Kaamba ka ubwino wa dziko lapansi lenilenilo ndi onse amene akuyamikiradi Mlengi wake, iye ‘adzawononga iwo akuwononga dziko lapansi.’ (Chivumbulutso 11:​17, 18) Nthaŵi ya Mulungu yochita zimenezi yayandikira kwambiri! Pamene ikwanira, kodi inu mudzapezeka pakati pa opulumuka?​—⁠1 Yohane 2:17; Miyambo 2:​21, 22.

[Mawu a M’munsi]

a Wonani bukhu lakuti Is the Bible Really the Word of God?, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

b Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, malemba a Baibulo ogwidwa m’bukhu lino ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.

c Chifukwa cha chimenecho olemba mabukhu ena otanthauzira mawu amazindikira ‘oh·lamʹ monga momwe lagwiritsiridwira ntchito pa Mlaliki 1:4 kukhala likutanthauza “kosatha.” The New English Bible, Revised Standard Version, The Jerusalem Bible, The Bible in Living English, King James Version ndipo ena amatembenuza m’njira imeneyo.

[Mafunso]

1. Kodi ndimtsogolo mwamtundu wanji mmene mukuyembekezera, ndipo chifukwa ninji?

2, 3. Kodi ndimotani mmene chiwopsezo chankhondo yanyukliya chimasonkhezera mmene anthu ambiri amawonera mtsogolo?

4. Kodi nchifukwa ninji kuipitsidwa kwa malo okhala kumawonedwa kukhala chiwopsezo chachikulu?

5, 6. Kodi ndimikhalidwe ina yotani imene imalempheretsa anthu kuyembekezera moyo kukhala wotetezereka ndi wachimwemwe?

7. (a) Kodi ndiumboni wotani umene umasonyeza kuti Baibulo ndilo Mawu a Mulungu? (b) Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuti anthu adziŵe chimene Baibulo limanena?

8. Kodi ndidzina liti limene Baibulo limadziŵikitsa nalo Mlengi wa planeti Dziko Lapansi?

9. (a) Kodi dzina la Mulungu limenelo linayambitsidwa ndi yani? (b) Kodi dzina la Mulungu nlofunika motani kwa ife? (Yoweli 2:32; Mika 4:⁠5)

10. Kodi nchifukwa ninji chiwopsezo cha nkhondo yanyukliya ndi zivulazo zochitidwa ndi kuipitsidwa kwa malo ndi mpweya sizingalepheretse chifuno cha Mulungu cha dziko lapansi?

11. (a) Kodi nchiyani chimene asayansi ena amakhulupirira kuti potsirizira pake chidzachitikira dziko lapansi? (b) Kodi ndani amene amadziŵa zambiri za zinthu zimenezi koposa mmene iwo akuchitira, ndipo chifukwa ninji?

12. Kodi ndimotani mmene mawu a Mlaliki 1:4 atsimikizirira kukhala owona?

13. (a) Kodi chiyani chimene mawu akuti “nthaŵi yosadziŵika” angatanthauze? (b) Pamenepa, kodi tingakhale otsimikizira motani, kuti dziko lapansi lidzakhala kosatha?

14. Kodi timadziŵa bwanji kuti mbulumbwayi tsiku lina siidzakhala yapululu?

15. Kodi zenizeni zimenezi zimavomerezana motani ndi pemphero limene Yesu anaphunzitsa otsatira ake?

16. (a) Kodi ndimtundu wanji wa anthu umene udzakhala padziko lapansi panthaŵiyo? (b) Kodi “dziko lapansi latsopano” limene Baibulo limatchula nchiyani?

17. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kuphunzira zofuna za Mulungu za kupulumuka tsopano?

[Chithunzi chachikulu patsamba 5]

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena