Mutu 12
Kodi Mwadziŵikitsidwa kaamba ka Chiwonongeko kapena Chipulumutso?
MKHALIDWE wachipembedzo umene ulipo lerolino umatifunikiritsa kusonyeza zimenedi ziri m’mitima yathu. Kodi timakondadi Yehova ndi njira zake? Kodi tiri ngati Mwana wake, Yesu Kristu, kwa amene kunanenedwa kuti: “Mwakonda chilungamo, ndi kudana nacho choipa”? (Ahebri 1:9) Kodi tikufunitsitsa kusonyeza zimenezi poyera kotero kuti ena akudziŵa pamene tikuima? Cholembedwa cha Baibulo chonena za Yehu ndi Yehonadabu mwana wa Rekabu chimatithandiza kupenda lingaliro lathu.
2 M’zaka za zana lakhumi B.C.E., Yehu anadzozedwa kukhala mfumu pa ufumu wa mafuko khumi a Israyeli, umene unali ndi likulu lake ku Samariya. Analamulidwa kupha onse amene anali a m’nyumba yoipa ya Mfumu Ahabu, kuphatikizapo Yezebeli Mkazi wa mfumu, amene anachirikiza kulambiridwa kwa Baala mu Israyeli ndipo anayesayesa kuchotsa kulambiridwa kwa Yehova. Yehonadabu, Mkeni (chifukwa cha chimenecho, sanali Mwisrayeli), mosakaikira anadziŵa programu yakupha ya Yehu pamene anatuluka kukakomana ndi Yehu. Koma kodi kukonda Yehova kwa Yehonadabu kunali kwamphamvu motani? Kodi iye akadzidziŵikitsa poyera kukhala munthu amene anakhulupirira zolimba kuti Yehova yekha, Mulungu wowona, ayenera kulambiridwa?
“KODI MTIMA WAKO NGWOLUNGAMA NDI INE?”
3 Amuna aŵiriwa atapatsana moni. Yehu anapempha Yehonadabu kuti asonyeze poyera lingaliro lake. “Kodi mtima wako ngwolungama ndi ine,” anafunsa Yehu, “monga momwedi mtima wanga uliri ndi mtima wako?” Mosadodoma Yehonadabu anayankha kuti: “Momwemo.” “Ngati ngwotero, undithandizetu,” anayankha Yehu. Motero anakweza Yehonadabu m’galeta lake nati: “Tsagana nanetu ndi kuwonera kusalekerera kwanga opikisana ndi Yehova.” Yehonadabu sanadodome mwamantha.—2 Mafumu 10:15, 16, NW; wonaninso Deuteronomo 6:13-15.
4 Pofika m’Samariya, Yehu anachita kanthu kamene kanafunikiritsa onse amene analambira Baala kudzidziŵikitsa. Aneneri, ansembe ndi olambira Baala onse anaitanidwira ku nsembe yaikulu kunyumba ya Baala. Iwo anauzidwa kuti anthu alionse olephera kufika akawonongetsa miyoyo yawo. Yehu analangiza kuti zovala ziperekedwe kwa olambira onse a Baala kuti avale kotero kuti akadziŵike bwino lomwe. Alionse amene adadzitchanso kukhala olambira Yehova anachititsidwa kusonyeza amene iwo kwenikweni anamtumikira. Inawonekera kukhala nthaŵi yosangalatsa kwa Baala ndi kwa Satana Mdyerekezi, mulungu wonyenga amene kwenikweni Baala anaimira.
5 Amenewa sanali malo a olambira owona a Yehova. Kufufuza kunachitidwa kutsimikizira kuti olambira Baala okha analipo. Ndiyeno dzomalo linayamba. Panthaŵi imeneyi, kunja, amuna a Yehu okonzekera, ndipo pa kupereka kwake chizindikiro iwo anayamba kuchitapo kanthu. “Akantheni; asatuluke ndi mmodzi yense,” iye analamula. Wolambira Baala aliyense anaphedwa. Nyumba ya Baala inagwetsedwa. “Momwemo Yehu anawononga Baala m’Israyeli.” Yehonadabu anali pandunji pa Yehu kuwona zochitika zimenezo. (2 Mafumu 10:18-28) Kodi ndimotani mmene inuyo mukulingalirira ndi zimene zinachitika? Pamene kuli kwakuti palibe aliyense wa ife amene amakondwera ndi imfa ya ena, ngakhale ya anthu oipa, kodi tikuzindikira chifukwa chake kunali kofunikira ndi chifukwa chake zinalembedwa m’Baibulo kuti ife tiŵerenge lerolino?—Yerekezerani ndi Ezekieli 33:11.
6 Cholembedwacho sichikutilamulira kuwononga kaya nyumba za timagulu tachipembedzo kapena anthu odzipereka kukulambira konyenga. Yehova waika, osati mboni zake zamakono, koma Yesu Kristu wolemekezedwayo, monga Yehu Wamkulu, kupereka ziweruzo Zake zolungama. Mwakulola maulamuliro andale zadziko ogwirizana kusonyeza kuda kwawo Babulo Wamkulu, Mfumu yakumwamba idzachititsa kuwonongedwa kwa ulamuliro wadziko lonse wachipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 6:2; 17:16; 19:1, 2) Pamene anali padziko lapansi, Yesu anakana kuchita ngakhale kachitidwe kamodzi ka kulambira kamene kakanalemekeza Mdyerekezi. Iye anatsutsa kuikidwa pambali kwa Mawu a Yehova moyanja mwambo wa anthu ndi kugwiritsira ntchito kulambiridwa kwa Mulungu kaamba ka phindu landalama. Iye sanalekerere wopikisana ndi Yehova aliyense.—Luka 4:5-8; Mateyu 15:3-9; 21:12, 13.
7 Pamenepa, kodi nchifukwa ninji, Kristu, tsopano wolamulira pakati pa adani ake, akulola kulambira Baala kwamakono kukula mwachiwonekere? Kodi nchifukwa ninji iye mwachiwonekere akulola anthu kulemekeza mulungu wa dongosolo lino lazinthu osalangidwa mwa kukankhira pambali zofuna za Yehova? Kodi nchifukwa ninji amalekerera kuchita kwawo monga ngati kuti Mulungu sakutsutsa chigololo chawo, kulemekeza kwawo kakhalidwe kokondetsa zinthu zakuthupi, kuphatikizidwa kwawo m’zizoloŵezi za kulankhula ndi mizimu pamene akudzitcha kukhala Akristu, ndi kuphunzitsa kwawo ziphunzitso za Babulo monga ngati kuti zimenezi zinali mawu a Mulungu? Chochitika chakale chimasonyeza kuti zimenezi zikapereka chiyeso kwa anthu, kuwalola kusonyeza mowoneka amene akumlambira, ndipo motero kaya iwo akuyenerera chipulumutso kapena chiwonongeko.
8 Kodi mwasankha njira iti? Kodi mwaleka machitidwe onse amene angakudziŵikitseni monga wotsatira kulambira Baala kwamakono? Kodi mwadzilekanitsa ndi dziko ndi kuima monga wolambira wowona wa Yehova?—2 Akorinto 6:17.
9 Yehonadabu, pokhala wolambira Yehova wosakhala Mwisrayeli, anaphiphiritsira “nkhosa zina” zimene tsopano zikusonkhanitsidwa ndi chiyembekezo cha moyo wamuyaya padziko lapansi. Kodi mukusonyeza mzimu wa Yehonadabu? Kodi mukufunitsitsa kudzidziŵikitsa poyera ndi Yehu Wamkuluyo ndipo ndi otsatira ake odzozedwa padziko lapansi amene akulengeza “tsiku lakubwezera la Mulungu wathu” loyandikiralo? Kodi mukugaŵana nawo ntchito yofulumira imeneyo? (Yesaya 61:1, 2; Luka 9:26; Zekariya 8:23) Kodi mukupatsa Yehova kudzipereka kwanu kotheratu osalola chinthu chirichonse kukhala pamalo amene iye ayenera kukhala m’moyo wanu? (Mateyu 6:24; 1 Yohane 2:15-17) Kodi moyo wanu umasonyeza kuti unansi wanu ndi iye ndiwo chuma chanu chamtengo wapatali koposa, kuti kanthu kena kalikonse kamangidwa pa uwo?—Salmo 37:4; Miyambo 3:1-6.
KODI MULI NDI CHIZINDIKIRO?
10 Chikakhala cholakwa chachikulu kunena kuti ngati munthu ayesa kukhala ndi moyo “wabwino” ndipo ngati apeŵa zipembedzo zimene zikuchita zinthu zotsutsidwa mwachindunji m’Mawu a Mulungu, palibenso china chimene chikufunika kwa iye. Onse amene akuyembekezera kupulumuka kuloŵa “m’dziko lapansi latsopano” ayeneranso kudziŵikitsidwa mosalakwa monga olambira Yehova. (Chivumbulutso 14:6, 7; Salmo 37:34; Yoweli 2:32) Uthenga umenewu ukuperekedwa m’masomphenya operekedwa kwa mneneri Ezekieli Yerusalemu asanawonongedwe mu 607 B.C.E.
11 Ezekieli anamva Yehova akuitana awo osankhidwa kuwononga Yerusalemu wosakhulupirika ndi okhalamo ake. Iye anawona amuna asanu ndi mmodzi onyamula zida zokanthira, ndipo panalinso mwamuna mmodzi wovala bafuta, wokhala ndi cholembera cha inki cha mlembi m’chuuno mwake. Choyamba kwa mwamuna wovala bafuta ameneyu Yehova anati: “Pita pakati pa mudzi, pakati pa Yerusalemu, nulembe chizindikiro pamphumi zawo za anthu akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse zichitidwa pakati pake.” Ndiyeno kwa asanu ndi mmodzi enawo anati: “Pitani pakati pa mudzi kumtsata iye, ndi kukantha; maso anu asalekelere, musachite chifundo; iphanitu nkhalamba, mnyamata ndi namwali, makanda, ndi akazi; koma musayandikire munthu aliyense ali nacho chizindikiro, ndipo muyambe pamalo anga opatulika.” Ezekieli anawona m’masomphenyawo chiwonongeko chimene chinatsatira—chinali chachikulu kwambiri kotero kuti kunawonekera ngati kuti Israyeli yense amene anali chikhalirebe m’dzikolo anali kuwonongedwa. (Ezekieli 9:1-11) Kodi nchiyani chimene chinali njira yopulumukira? Chinali chizindikiro choikidwa pamphumi ya munthu ndi mwamuna wokhala ndi cholembera cha inki cha mlembi.
12 Anthu okha “akuusa moyo ndi kulira chifukwa cha zonyansa zonse” zochitidwa m’Yerusalemu ndiwo amene anaikidwa chizindikiro cha kupulumuka. Kodi “zinthu zonyansa” zimenezo zinali chiyani? Zisanu zandandalikidwa: (1) “Fano lansanje” pa chipata choloŵera m’bwalo lamkati la kachisi wa Yehova. Kaya linali ndi kawonekedwe kotani, chinthu chimenechi chinalinkupatsidwa kulambira kumene Aisrayeli anayenera kupatsa Yehova. (1 Mafumu 14:22-24) (2) Zozokotedwa za pakhoma za zokwaŵa ndi zirombo, pamaso pa zimene nsembe zofukiza zinalinkuperekeredwa mkati mwenimweni mwa kachisi. (3) Akazi olirira maliro imfa ya mulungu Tamuzi, limene linali dzina lina la Nimrode, wopandukira Yehova uja. (Genesis 10:9) (4) Amuna osonyeza chipongwe chachikulu mwa kufulatira kachisi wa Yehova ndi kugwadira dzuŵa. (Deuteronomo 4:15-19) (5) Monga chipongwe chotsirizira, anthu odzadza dziko ndi chiwawa kupatikizapo kusonyeza “nthambi,” mwinamwake chizindikiro champheto, kumphuno za Yehova. Kodi mungazindikire chifukwa chake Yehova ananyansidwa nawo?—Ezekieli 8:5-17.
13 Kodi ndimotani mmene inuyo mukulingalirira ku zizoloŵezi zamakono za Dziko Lachikristu zimene ziri zofanana ndi “zonyansa” zimenezi? (1) M’matchalitchi ake ambiri muli mafano amene anthu amagwadira kuwalambira, ngakhale kuli kwakuti Baibulo limatsutsa kutero. (1 Akorinto 10:14; yerekezerani ndi 2 Mafamu 17:40, 41.) (2) Limagwirizana ndi lingaliro la kuika kusinthika kwa munthu kuchokera ku zinyama mmalo mwa kulengedwa ndi Mulungu: ndiponso limaloŵa m’kusonyeza kulambira kwachangu pamaso pa zifaniziro za zinyama ndi mbalame zogwiritsiridwa ntchito monga zizindikiro za mitundu. (3) M’kulambira kwake limagwiritsira ntchito mtanda, umene kuchokera kalekale unali chizindikiro chachipembedzo cha Tamuzi, ndipo limaloŵa m’madzoma a kulirira awo amene afa m’nkhondo zokhetsa mwazi zimene zimasonyeza mzimu wa Nimrode. (Koma wonani Yohane 17:16, 17.) (4) Limafulatira chimene Mulungu amanena kupyolera mwa Mawu ake ndipo, mmalo mwake, limasankha “chidziŵitso” choperekedwa ndi sayansi yamakono ndi nthanthi ya anthu. (1 Timoteo 6:20, 21: yerekezerani ndi Yeremiya 2:13.) (5) Monga ngati kuti zimenezo zinali zosakwanira, limachirikiza chipanduko m’malo ena ndipo limakhala ndi lingaliro lokondwera ndi chigololo, uku likudzitcha kukhala likulankhula m’dzina la Mulungu. (2 Petro 2:1, 2) Anthu ena anawona malingaliro amenewa monga ngati aufulu. Iwo sangagwirizane ndi iwo onse, koma angagwirizane ndi ena kapena mwinamwake kusawatsutsa. Kodi mumalingalira motani ponena za zizoloŵezi zonyoza Mulungu zotero zimene zimabwevutsa anthu kwa Mlengi wa anthu?
14 Anthu ambiri agwiritsidwa mwala ndi matchalitchi ndipo samapitakonso. Iwo angakhumudwe kwambiri ndi chiwawa ndi kusawona mtima m’dziko. Koma zimenezo sizikutanthauza kwenikweni kuti iwo alembedwa chizindikiro cha kupulumuka. Ayenera kulembedwa chizindikiro ndi ‘mwamuna wokhala ndi cholembera cha mlembi.’ Maumboni amasonyeza kuti kagulu ka “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kakuchita ntchito yolemba chizindikiro imeneyo lerolino.—Mateyu 24:45-47.
15 Onse amene akufuna kulembedwa chizindikiro kuti akhale ali ndi chivomerezo cha Mulungu ayenera kuvomera chiphunzitso chimene Yehova amapereka kudzera mwa kagulu ka “kapolo” kameneko ndi kukhala olambira Yehova owona. Sayenera kukhala anthu amene amalemekeza Yehova ndi pakamwa pawo koma amenedi amakonda mikhalidwe yadziko. (Yesaya 29:13, 14; 1 Yohane 2:15) Ayenera kukonda Yehova ndi miyezo yake ndi kumva chisoni m’mtima, “kuusa moyo ndi kulira,” chifukwa cha ziphunzitso ndi zizoloŵezi zimene zimamnyoza. Palibe aliyense amene adzaika chizindikiro chenicheni cha inki pamphumi zawo. Koma pamene iwo ali ndi chizindikiro chophiphiritsira kudzakhala kwachiwonekere kwa onse kuti, monga Akristu odzipatulira, obatizidwa, avala “umunthu watsopano” wolongosoledwa pa Aefeso 4:24. Iwo ali ndi chikhulupiriro chamoyo. Poyera ndi mtseri amayesayesa kuchita zimene zidzalemekeza Yehova. Sianthu okha amene atuluka m’Chikristu cha Dziko koma onse, mosasamala kanthu za chiyambi, amene akuyembekezera kupulumuka kuloŵa “m’dziko lapansi latsopano” monga ogwirizana ndi kagulu ka odzozedwa ayenera kukhala ndi chizindikiro chimenechi.
16 Chatanthauzo mwapadera ndicho chenicheni chakuti akupha a Yehova anauzidwa kuti usinkhu, amuna kapena akazi, umbeta kapena ukwati sizinali chifukwa cha kulekerera wolakwira Yehova. Munthu wa muukwati ayenera payekha kukhala ndi chizindikiro chake kuti apulumutsidwe. Ngati makolo akaniza kuchititsa ana awo kulembedwa chizindikiro kapena ngati alephera kuŵalera kukhala atumiki a Yehova, ayenera kunyamula thayo la chimene chidzachitikira ana amenewo. Ngakhale kulikwakuti ana omvera a makolo opembedza amawonedwa kukhala ‘oyera’ ndi Yehova, opanduka samatero. (1 Akorinto 7:14; Salmo 102:28; Miyambo 20:11; 30:17) Ngati ana ali aakulu mokwanira kukhala Akristu obatizidwa koma safuna kufitsa zofunikazo, kaya iwo ngobatizidwa kapena ayi, usinkhu wawo sudzawachititsa kupulumutsidwa. Pamenepa, nkofunika chotani nanga, kuti munthu aliyense wa usinkhu wokhoza kudziyankhira kuti aikidwe chizindikiro mowonekera monga munthu wodzipatulira kwa Mulungu ndi kuchita chifuniro chake!
17 Yehova wasonyeza chifundo chachikulu kwa anthu mwa kutumiza mboni zake kuwachenjeza za chiwonongeko choyandikira ndi kusonya njira ya ku chisungiko. Koma iye amadziŵa bwino mbiri ya chipembedzo chonyenga ndi zipatso zovunda zimene icho chatulutsa. Pamene Babulo Wamkulu awonongedwa, palibe chifundo chidzasonyezedwa kwa aliyense amene aumirira kumamatira kwa iye. Kuti tipulumuke kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu, tiyenera kuyenda m’mapazi a Yesu Kristu monga olambira Yehova owona, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi.
[Mafunso]
1. Kodi ndimafunso otani amene phunziro lino likutilimbikitsa kusinkhasinkha?
2. Kodi Yehu ndi Yehonadabu anali ayani?
3. Kodi ndimotani mmene Yehonadabu anasonyezera poyera lingaliro lake ponena za kulambiridwa kwa Yehova?
4, 5. (a) Kodi ndimwanjira yotani imene Yehu anapangitsira olambira Baala kudzidziŵikitsa? (b) Kodi nkachitidwe kotani kamene kenako Yehu anatsatira, ndipo kodi Yehonadabu anali kuti? (c) Kodi mumalingalira motani chiwonongeko cha olambira Baala chimenecho?
6. (a) Kodi ndimotani mmene Babulo Wamkulu adzawonongedwera? (b) Pamene anali padziko lapansi, kodi Yesu anasonyeza motani kuti sanalekerere otsutsa Yehova?
7. (a) Kodi ena a maumboni amakono a kulambira Baala ndiotani? (b) Kodi nchifukwa ninji Kristu monga Mfumu walekerera zinthuzi?
8. Kodi ndimafunso amphamvu otani amene ife tifunikira kudzifunsa?
9. (a) Ngati ife tiri ofananadi ndi Yehonadabu, kodi tidzakhala tikuchitanji? (b) Kodi ndimotani mmene malemba otchulidwawo amagogomezerera kufunika kwa zinthuzi?
10. Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti olambira Yehova okha adzapulumuka?
11. (a) Longosolani masomphenya olembedwa pa Ezekieli 9:1-11. (b) Kodi njira yopulumukira inali chiyani?
12. (a) Kodi nchiyani chimene chiri zinthu zonyansa pa zimene olembedwa chizindikiro anali “kuusa moyo ndi kulira”? (b) Kodi nchifukwa ninji Yehova akayenera kunyansidwa ndi zinthu zotero?
13. (a) Potenga chimodzichimodzi, fotokozani machitidwe amakono amene ali ofanana ndi “zinthu zonyansa” zimenezo. (b) Kodi mumalingalira bwanji ponena za zizoloŵezi zimenezi?
14. Kodi nchifukwa ninji chenicheni chakuti munthu wagwiritsidwa mwala ndi matchalitchi sichimatanthauza kwenikweni kuti adzakhala wopulumuka?
15. (a) Kodi chizindikirocho nchiyani? (b) Kodi munthu amachipeza bwanji?
16. Kodi nchifukwa ninji masomphenya amenewa ali kwenikweni ofunika kwa ana ndi makolo awo?
17. Kodi taphunziranji panopa ponena za chifundo cha Yehova?
[Zithunzi patsamba 95]
Kodi inu mulidi ndi chizindikiro chofunika kaamba ka kupulumuka?