Mutu 19
“Tamva Kuti Mulungu Ali ndi Inu”
“TIDZAMUKA nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” Ndizo zimene Baibulo lidaneneratu kuti anthu a m’mitundu yonse akanena m’nthaŵi yathu. (Zekariya 8:23) Ndipo kodi Mulungu ameneyu ndani amene ulosi wa Zekariya ukunena? Sitinasiyidwa m’chikaikiro. M’bukhu la Baibulo laling’ono kwambiri lino dzina lake lenileni limapezeka nthaŵi 135. Ndilo Yehova!
2 Iyemwiniyo anati ponena za dzina lake lenileni, Yehova: “Iri ndidzina langa nthaŵi yosatha, ichi ndichikumbukiro changa m’mibadwomibadwo.” (Eksodo 3:15) Kufunika kwa dzinalo kwasonyezedwa ndi chenicheni chakuti limapezeka pafupifupi nthaŵi 7 000 m’bukhu Labaibulo lathunthu Lachihebri—nthaŵi zochuluka kwambiri kuposa chiwonkhetso chophathikizidwa cha maina aulemu onga akuti Ambuye ndi Mulungu. Monga kudanenedweratu, mu “masiku otsiriza” ano dzinalo lafikira kukhala logwirizanitsidwa mwapadera ndi gulu limodzi la anthu.
“TIDZAMUKA NANU”
3 Ponena za zimenezi, mneneri Zekariya, panthaŵi ya kumangidwanso kwa kachisi wa Yehova m’Yerusalemu wakale, anauziridwa ndi Mulungu kulemba kuti: “Atero Yehova wamakamu: Kudzachitikanso kuti mitundu ya anthu, ndi okhalamo m’midzi yambiri adzifika, ndipo okhala m’mudzi umodzi adzamuka kumudzi wina, ndi kuti, Tiyeni msanga kukapepeza Yehova, ndi kufunafuna Yehova wa makamu; ndimuka inenso. Inde, mitundu yambiri ya anthu, ndi amitundu amaphamvu adzadza kufunafuna Yehova wa makamu m’Yerusalemu, ndi kupepeza Yehova. Atero Yehova wamakamu: Kudzachitika masiku awo amuna khumi adzagwira, ndiwo a manenedwe onse a amitundu, inde adzagwira mkawo wa munthu ali Myuda, ndi kuti, Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zekariya 8:20-23.
4 Kukwaniritsidwa kwakung’ono kumene ulosiwu unali nako mogwirizana ndi kachisi womangidwanso m’Yerusalemu, kuyambira m’nthaŵi ya Zerubabele, kunasonya mtsogolo ku kukwaniritsidwa kokulirapo kwambiri m’nthaŵi yathu. Mogwirizana ndi anthu ati? Ndithudi sikukakhala komveka kwa awo amene ‘akufunafuna Yehova’ kutembenukira kwa anthu amene mwamwambo amakanadi kutchula dzina la Mulungu, monga momwe amachitira Ayuda amene amamamatira ku kulambira kwawo kwamakolo. Ngakhale ku Dziko Lachikristu, limene limatsanzira mwambo Wachiyuda wa kupeŵa kugwiritsiridwa ntchito kwa dzina la Mulungu. Sikuli ku Yerusalemu wapadziko lapansi kumene anthu m’nthaŵi yathu akutembenukira kuti alambire Yehova. Monga momwe Yesu ananeneratu, Mulungu anasiya kachisi wake konko, ndipo anawonongedwa mu 70 C.E., wosadzamangidwanso kufikira nthaŵi ino. Zimenezi zimasonyeza kwa munthu wolingalira aliyense kuti Mulungu saali ndi Israyeli wosakhala Wachikristu.—Mateyu 23:37, 38; yerekezerani ndi 1 Mafumu 9:8, 9.
5 “Yerusalemu” amene lerolino amaimira Yehova walongosoledwa pa Ahebri 12:22 monga “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba.” Monga momwedi Yerusalemu wakale analiri chizindikiro chowoneka cha ulamuliro wa Yehova, “Yerusalemu wakumwamba” ndi Ufumu Waumesiya wa Mulungu mu umene Yesu Kristu anaikidwa pampando wachifumu pamapeto a Nthaŵi za Akunja mu 1914. (1 Mbiri 29:23; Luka 21:24) Boma limenelo liri ndi oimira padziko lapansi pano, awo amene mokhulupirika akulilengeza monga chiyembekezo chowona chokha cha anthu. Oyamba kulengeza kuti Ufumuwo unali utakhazikitsidwa mu 1914 anali otsalira a “kagulu ka nkhosa.” Amenewa ndiwo “Israyeli wa Mulungu,” kulankhula mwauzimu. Iwo ndiwo ‘Ayuda’ auzimu ponena za amene Zekariya analosera. (Luka 12:32; Agalatiya 6:16; Aroma 2:28, 29) Chiyambire 1931, chifukwa cha kukonda kwawo Mulungu ndi kuzindikira kwawo thayo lolengeza kuti Yehova ndiye Mulungu wowona ndi Wamphamvuyonse, iwo alandira dzinalo Mboni za Yehova.—Yesaya 43:10-12.
KODI AMADZIŴIKA BWANJI?
6 Chifukwa cha chenicheni chakuti Ayuda auzimu amenewa akwaniritsa mokhulupirika thayo lawo monga Mboni za Yehova, anthu owona mtima mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi athandizidwa “kufunafuna Yehova.” Afika pa kuzindikira kuti Yehova alidi ndi anthu amenewa amene ali ndi dzina lake. Kodi nchiyani chimene chimawatsimiziritsa zimenezi? Zinthu zambiri, pakati pa zimenezi pali zazikulu izi:
(1) Zikhulupiriro za Mboni za Yehova zonse nzozikidwa pa Baibulo—osati chabe pamalemba ochepekera koma Mawu a Mulungu athunthu. Mmalo mwa kuphunzitsa zinthu za m’mutu mwawo, Mboni za Yehova zimayankha mafunso mwa kusonyeza zimene Baibulo limanena. Zimalemekeza Yehova mwa kumlola kulankhula. (Yerekezerani ndi Yohane 7:16-18.)
(2) Baibulo limalongosola kuti Mulungu mwini akatenga m’mitundu “anthu a dzina lake.” (Machitidwe 15:14) Iwo eni akaitanira padzina lake ndipo akayesetsa kulilengeza m’dziko lonse lapansi. (Yesaya 12:4, 5) Mboni za Yehova ndiwo anthu amene agwirizana mwapadera ndi dzina lenileni la Mulungu, Yehova.
(3) Mboni za Yehova ziri ndi chakudya chauzimu chokhutiritsa chambiri. Zimene zimaphunzira m’Malemba ndi chiyambukiro chimene zimenezi ziri nacho pa lingaliro lawo ponena za moyo zimazipangitsa kukhala anthu achimwemwe, mosiyana ndi anthu ena onse. Izi ndizo zimene Yehova ananena kuti zikachitikira atumiki ake. (Yesaya 65:13, 14; yerekezerani ndi Mateyu 4:4.)
(4) Mboni za Yehova zimagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu kukhazikitsa muyezo wa khalidwe ndi kutsogoza zosankha zawo m’zochitika za moyo zatsiku ndi tsiku—m’mabanja awo, pantchito, m’masukulu, m’kusankha zosangulutsa, m’kuzindikira machitachita oti apeŵedwe, m’kudziŵa ntchito zofunika koposa m’zimene angakhalemo ndi phande. Yehova analonjeza kuti ‘iyemwini akalungamitsa njira’ za awo ochita zimenezi. (Miyambo 3:5, 6)
(5) Kuyang’aniridwa kwa mipingo ya Mboni za Yehova kwatsanzira kuja kwa mpingo wa Mulungu wa m’zaka za zana loyamba, mu umene akulu anali zitsanzo za gulu lankhosa ndi antchito anzawo a Ufumu wa Mulungu mmalo mwa kukhala kagulu kokwezeka ka atsogoleri achipembedzo. (1 Petro 5:2, 3; 2 Akorinto 1:24)
(6) Mboni za Yehova sizimaloŵa m’zochitika zandale za dziko koma zimachita ntchito imene Baibulo limalongosolera Akristu owona, ndiko kuti, kulalikira mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu m’dziko lonse kaamba ka umboni mapeto asanadze. (Mateyu 24:14; yerekezerani ndi Yohane 17:16; 18:36.)
(7) Mboni za Yehova zimakondanadi, monga momwe Yesu ananenera kuti ophunzira ake owona akatero. Mawonekedwe akhungu, magwero a fuko, mikhalidwe ya zachuma, mtundu, chinenero—palibe chirichonse cha zimenezi chimachititsa wina kunyoza mnzake. Mosasamala kanthu za kupanda ungwiro kwaumunthu, iwo onse ngogwirizanadi monga gulu laubale la m’mitundu yonse, ndipo kaamba ka zimenezi iwo amapereka thamo lonse kwa Mulungu. (Yohane 13:35; yerekezerani ndi Machitidwe 10:34, 35.)
(8) Mofanana ndi Akristu oyambirira, Mboni za Yehova m’nthaŵi zamakono zimapitirizabe kutumikira Mulungu mosasamala kanthu za chizunzo. Podalira Mulungu, sizimabwezera otsutsa. Monga momwe kunaliri kale, Mulungu wakhaladi ndi atumiki ake kuti awalanditse. (Yeremiya 1:8; Yesaya 54:17)
7 Izi ndizo zoŵerengeka chabe za chifukwa chake, monga momwe kunanenedweratu, “amuna khumi ndiwo a manenedwe onse a amitundu” akunenera ndi chitsimikizo chenicheni kwa otsalira a oloŵa nyumba a Ufumu kuti: “Tidzamuka nanu, pakuti tamva kuti Mulungu ali ndi inu.” (Zekariya 8:23) Malemba amagwiritsira ntchito “khumi” kuimira umphumphu ponena za zinthu za padziko lapansi, motero “amuna khumi” amenewa amaimira onse amene akulandira kulambira kowona tsopano mogwirizana ndi “abale” odzozedwa ndi mzimu a Kristu. Iwo sanangogwirizana ndi otsalira pamisonkhano yawo koma amazidziŵikitsa kukhala olambira Mulungu wawo, Yehova. Amapatulira miyoyo yawo kwa iye kupyolera mwa Yesu Kristu ndi kusonyeza kumeneku mwa ubatizo za m’madzi, motero kusonyeza kuti akufuna ‘kukhala ogwirizana ndi Yehova.’ Pamenepo mokondwera amaloŵa m’ntchito yochitidwa padziko lonse lapansi ndi mboni zake.—Zekariya 2:11; Yesaya 61:5, 6.
ZITSANZO ZOYENERA KUTSANZIRIDWA
8 Ena amene amatsanzira kachitidwe kameneka ngofanana ndi mfumu yaikazi ya ku Seba m’nthaŵi ya Solomo. Ali kutali ‘ankamva mbiri ya Solomo mogwirizana ndi dzina la Yehova,’ Iye anali asanalankhule ndi Solomo maso ndi maso ndipo anali asanafike ku kachisi wa Yehova m’Yerusalemu. Anali ndi zikaikiro kaya ngati zinali chonchodi zimene adamva. Koma anayesetsa kuti awone, kuyenda mwinamwake mamailo 1 400 (2 250 km) pangamila kuti atero. Iye anapeza mayankho a ‘mafunso ake onse ovutitsa maganizo’ nadzuma kuti: “Tawonani, anangondiuza dera lina lokha.” Sakanachitira mwina kusiyapo kunena kuti Yehova anakonda omlambira. (1 Mafumu 10:1-9) Ena amene anali otchuka m’dziko atsanzira chitsanzo chake lerolino, ndipo ambiri ochokera m’mikhalidwe yosaukirapo achita motero. Iwo amawona umboni wakuti Mboni za Yehova sizimayang’ana kwa munthu koma kwa Yesu Kristu, Solomo Wamkulu, monga Mfumu yawo. Mayankho amene amaperekedwa kuchokera m’Mawu a Mulungu amakhutiritsa maganizo ndi mitima yawo, ndipo amawona kukhala osonkhezereka kugwirizanitsa mawu awo m’kutamanda Yehova.—Yerekezerani ndi Luka 11:31.
9 Ena ali ngati Rahabi wa ku Yeriko, amene anali atakhutira ndi mbiri zolandiridwa zakuti Mulungu wa Israyeli anali “Mulungu wam’mwamba umo, ndi padziko lapansi.” (Yoswa 2:11) Pamene ozonda a ku Israyeli analoŵa m’dzikolo, iye anawalandira, nawabisa naika moyo wake pachiswe kuwatetezera. Anali ndi chikhulupiriro ndipo anapereka umboni wake mwa ntchito zake, akumagwirizana ndi anthu a Yehova. (Ahebri 11:31; Yakobo 2:25) Anatsatira mosamalitsa malangizo operekedwa a kupulumutsidwa kwake. Rahabi anasonyezanso kudera nkhaŵa kwachowonadi kaamba ka atate wake ndi amake, abale ake ndi alongo ake, akumatsegula njira yakuti iwo apulumuke ngati akamvera zofunika za kupulumuka. (Yoswa 2:12, 13, 18, 19) Chifukwa cha zimenezo iye ndi apabanja pake anapulumutsidwa pamene Yeriko ndi nzika zake zolambira Baala anafafanizidwa. (Yoswa 6:22, 23) Zimenezi ziri ndi tanthauzo lamphamvu m’nthaŵi yathu. Zimasonyeza kuti Yehova adzapulumutsa anthu amene ali ngati Rahabi. Kodi nchiyani chimene chimawasonyeza kukhala ngati iye? Amakhulupirira Yehova, amagwirizana ndi ziŵalo za Israyeli wauzimu, amatsatira mosamalitsa malangizo operekedwa kudzera m’ngalande imeneyi ndipo mwaphamphu amayesayesa kuthandiza ziŵalo zenizeni zabanja lawo ndi achibale ena kuwona nzeru ya kuchita mofanana.
10 Ndithudi, chikoka chenicheni, chimene chimakokera anthu a mitundu yonse m’kugwirizana ndi Mboni za Yehova, ndicho Yehova Mulungu mwiniyo. Mawu ake amawakondweretsa. Zipatso za mzimu wake m’miyoyo ya atumiki ake nzokondweretsa kwa iwo. Pamene afika pa kudziŵa bwino mikhalidwe yake ndi zochita zake ndi athu, iwo amakhumba nthaŵi pamene dzina la Mulungu lidzachotseredwa chitonzo chonse choikidwa pa ilo ndi Satana ndipo ndi anthu opanda chikhulupiriro. Iwo eni amayesayesa kuchita zinthu zawo m’njira imene idzakhala yokondweretsa kwa Mlengi wawo ndi imene idzasonkhezera ena kumlemekeza. (1 Petro 2:12) Ndimitima yawo yonse iwo amapemphera, monga momwe Yesu anaphunzitsira ophunzira ake kuti: “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (Mateyu 6:9, 10) Ndipo, mogwirizana ndi pemphero lawo, amapereka utumiki wopatulika kwa Mulungu mogwirizana kotheratu ndi awo amene amapereka umboni wachiwonekere wakuti iwo ali “anthu a dzina [la Yehova].”
[Mafunso]
1, 2. (a) Kodi nchiyani chimene Zekariya 8:23 amaneneratu kaamba ka nthaŵi yathu? (b) Kodi ndani amene ali Mulungu wotchulidwa panopa, ndipo kodi ndimotani mmene Baibulo limagogomezera dzina lake lenileni?
3. Monga momwe kudanenedweratu pa Zekariya 8:20-23, (a) kodi ndani amene akafunafuna Yehova? (b) ndipo mogwirizana ndi ayani?
4. Kodi nchifukwa ninji ulosi uwu sumagwira ntchito ku Chiyuda kapena Dziko Lachikristu?
5. Kodi ndimotani mmene Malemba amadziŵikitsira (a) “Yerusalemu” amene amaimira Yehova lerolino? (b) “mwamuna amene ali Myuda” ponena za amene Zekariya analosera?
6. (a) Kodi nchiyani chimene chakhutiritsa mamiliyoni ambiri a anthu ponena za amene ali anthu amene Mulungu ali nawo lerolino? (Lingalirani mfundo imodzi panthaŵi imodzi; ŵerengani malembawo.) (b) Kodi ndimfundo ziti zimene zakhala zogwira mtima kwa inu mwini?
7. (a) Kodi ndani amene ali “amuna khumi”? (b) Kodi ndimotani mmene amaperekera umboni wakuti Yehova wakhaladi Mulungu wawo?
8. (a) Kodi nchiyani chimene chinachititsa mfumu yaikazi ya ku Seba kupita ku Yerusalemu? (b) Kodi inachitanji pamene inafika, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani? (c) Kodi ndimotani mmene pakhalira anthu onga iye m’nthaŵi yathu? (Salmo 2:10-12)
9. (a) Kodi ndim’njira yotani imene mkhalidwe wa Rahabi unasiyanira ndi uja wa mfumu yaikazi ya ku Seba? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chapadera ponena za zochitika zotsogolera ku kupulumutsidwa kwa Rahabi ndi apabanja pake? (c) Kodi nchiyani chimene chimadziŵikitsa anthu amene ali ngati Rahabi lerolino?
10. (a) Monga momwe ulosi wa Zekariya umasonyezera, kodi nchiyani chimene chikukoka anthu kotero kuti akugwirizana ndi Mboni za Yehova? (b) Kodi ndimotani mmene tingasonyezere, m’lingaliro ndi machitidwe, kuti kukonda Yehova ndiko kumene kwadzazadi mitima yathu?