Mutu 20
‘Wochepa Asanduka Mtundu Wamphamvu’
AWO amene ali olambira Yehova akhala kwanthaŵi yaitali ochepa kwambiri poyerekezera ndi chiŵerengero cha anthu onse. Koma m’nthaŵi yathu chiŵerengero chawo chikuwonjezereka paliŵiro limene liri lokondweretsa kwa okonda chilungamo. Ponena za ukulu wa chiwonjezekocho, Yehova mwiniyo ananeneratu kuti: “Wamng’ono adzasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu. Ine Yehova ndidzafulumiza ichi m’nthaŵi yake!” (Yesaya 60:22) Monga momwe lembalo likufotokozera, Yehova mwiniyo akuchititsa zimenezi. Motani? Mwa kuchititsa kwake kukhalapo pakati pa atumiki ake mkhalidwe umene umawasiyanitsa kwambiri ndi magulu amitundu owazinga ndi umene umakoka mwamphamvu anthu owona mtima.
2 Zimenezi zinanenedweratu pa Yesaya 60:1, 2, pamene Yehova akulankhula ndi “mkazi” wake, gulu lake lopangika ndi zolengedwa zauzimu zokhulupirika kuphatikizapo ana obadwa ndi mzimu padziko lapansi, kuti: “Nyamuka, wala, pakuti kuunika kwako kwafika, ndi ulemerero wa Yehova wakutulukira. Pakuti tawona, mdima udzaphimba dziko lapansi, ndi mdima wa bii mitundu ya anthu, koma Yehova adzakutulukira, ndi ulemerero wake udzawoneka pa iwe.” Maziko a kusiyana kumeneku ndiwo kubadwa kwa Ufumu Waumesiya wokhala m’manja mwa Yesu Kristu mu 1914. Nthaŵi imeneyo inali pamene “ulemerero wa Yehova” unaŵala pa gulu lake lakumwamba, limene linabala Ufumuwo. Panali chifukwa cha kukondwera kwakukulu pakati pawo. (Chivumbulutso 12:1, 2, 5, 10-12) Ndipo padziko lapansi otsalira odzozedwa a oloŵa nyumba Aufumu analoŵa m’chisangalalo chimenecho. Kuyambira m’1919, iwo ‘anaŵala’ pamene anayamba kulengeza Ufumu wa Mulungu kwapadziko lonse lapansi kukhala chiyembekezo chenicheni ndi chimodzi chokha cha anthu.—1 Petro 2:9; Mateyu 5:14-16.
3 Mosiyana, m’1914 magulu amitundu a dziko, pomenya nkhondo kuti asungebe ufumu wawo, analoŵa m’nyengo ya chiwawa ndi kusasungika mu imene iwo sanatulukemo. Kusakhazikika chiyambire nthaŵi imeneyo kwachititsa ambiri kuzindikira kuti, mosasamala kanthu za “kupita patsogolo kwasayansi,” alibe mtsogolo mosungika momdalira. Ndithudi, ‘mdima ukuphimba dziko lapansi.’ Kodi chifukwa ninji sangathe kupeza njira yotulukira? Chifukwa chakuti mitundu yakana Yehova monga Mfumu. Kwenikweni, olamulira oŵerengeka amapereka utumiki wapakamwa kwa “Mulungu” amene dzina lake iwo samagwiritsira ntchito. Iwo ngotsimikiza kuchita zinthu okha, koma mavuto amene iwo akuyang’anizana nawo ngoposa mphamvu ya munthu kuwathetsa. (Yeremiya 8:9; Salmo 146:3-6) Dziko lamakono, limodzi ndi umbombo ndi kuipa kwake, laloŵa ‘masiku ake otsiriza.’ Palibe njira imene lingapeŵere chiwonongeko chimene chikuliyembekezera. Anthu okha amene akukhulupirira kotheratu Ufumu wa Mulungu angayang’ane mtsogolo ndi chidaliro. M’ziŵerengero zazikulu, anthu owona mtima akuzindikira zimenezi ndipo akugwirizana mwamphamvu ndi Mboni za Yehova, zimene sizimalankhula kokha za Ufumu koma zimayesetsa mwaphamphu kukhala mogwirizana ndi zimene zimalalikira.
‘WAMNG’ONO ASANDUKA CHIKWI’
4 Pamene Nkhondo Yoyamba Yadziko inatha, kusonkhanitsidwa kwa oloŵa nyumba Aufumu kunali kusanathebe. Panali chikhalirebe “ana amuna” ndi “ana aakazi” ena a Yerusalemu wakumwamba amene anafunikira kudzazitsa 144 000 onenedweratuwo amene akalamulira limodzi ndi Kristu kumwamba. Komabe, Yehova ananeneratu kutsirizidwa kwa ntchito imeneyo, kuti: “Tukula maso ako uwunguzewunguze ndi kuwona; iwo onse asonkhana pamodzi, adza kwa iwe; ana ako amuna adzachokera kutali, ndi ana ako aakazi adzaleredwa pambali.” (Yesaya 60:4) Chifukwa cha kulengeza Ufumu kochitidwa kuyambira ndi pambuyo pa 1919, ena zikwi zambiri anadzipatulira kwa Yehova, anabatizidwa ndipo anadzozedwa ndi mzimu woyera. Komabe, onse pamodzi, gulu lonse la oloŵa nyumba a Ufumu linanenedwa ndi Yesu kukhala chabe “kagulu kankhosa.” (Luka 12:32) Kuti akwaniritse zimene zinanenedweratu pa Yesaya 60:22, ndithudi kukakhala ena amene akasonkhanitsiridwa ku kulambira kowona. Ndithudi zakhala motero!
5 Iwo akutchulidwa pa Yesaya 55:5 m’njira iyi: “Tawona, iwe udzaitana mtundu umene sunaudziŵa, ndi mtundu umene sunakudziŵa udzakuthamangira, chifukwa cha Yehova Mulungu wako, ndi chifukwa cha Woyera wa Israyeli; pakuti iye wakukometsa.” Amenewa ndianthu ochokera kunja kwa Israyeli wauzimu. Iwo akuchokera m’mitundu yambiri koma iwo amakhala anthu ogwirizana, onse opereka chichirikizo chokhulupirika ku Ufumu wa Mulungu. Iwo ndiwo “mtundu” umene otsalira a Israyeli wauzimu ‘sanaudziŵe’ panthaŵi imeneyo mogwirizana ndi kumvetsetsa kwawo Malemba, ndiponso anthu amenewa kalero sanazindikire moyenera atumiki a Mulungu. Koma chifukwa cha kulalikidwa kwa mbiri yabwino, iwo amakokedwa chifukwa chakuti iwo amazindikira kuti Aisrayeli auzimu amenewa amalambira Mulungu wowona ndipo chifukwa chakuti iwo amawona mwa iwo kukongola kwauzimu kumene kungachokere kokha m’dalitso la Mulungu.
6 Mosasamala kanthu za zonse zimene Satana wachita kuletsa kulalikidwa kwa uthenga Waufumu ndi kupatutsira maganizo a anthu ku zinthu zina, kuunika kwa chowonadi kumapitiriza kufika ngakhale ku mbali zakutali za dziko lapansi. Chotulukapo chakhala monga momwe Mulungu kalekale ananenera molosera kwa “mkazi” wake kuti: Pamenepo udzawona ndi kuunikidwa, ndipo mtima wako udzanthuthumira ndi kukuzidwa; pakuti unyinji wa nyanja udzakutembenukira, chuma cha amitundu chidzafika kwa iwe. . . . Ndipo adzalalikira matamando a Yehova.” (Yesaya 60:5, 6) Inde, “khamu lalikulu” la anthu amene panthaŵi ina anali mbali ya “nyanja” ya anthu otalikirana ndi Mulungu, anthu amene miyoyo yawo inadetsedwa ndi “mdima wa bii” umene umaphimba mitundu, lagwirizana ndi Israyeli wauzimu. Mmaso mwa Mulungu, amenewa alidi chuma chochokera m’mitundu yonse.
7 Panthaŵi ya kumangidwanso kwa kachisi wa Yehova m’Yerusalemu, iye anachititsa mneneri wake Hagai kulengeza kuti: “Ndidzagwedeza amitundu onse, ndi zofunika za amitundu onse zidzafika, ndipo ndidzadzaza nyumba iyi ndi ulemerero, ati Yehova wamakamu.” (Hagai 2:7) Kusankhwinyidwa ndi kugwedezedwa kwa mitundu potsirizira pake kumafika ku chiwonongeko chawo, koma chimenecho chisanachitike “zofunika za amitundu onse” ziyenera kusonkhanitsidwa kuchokera pakati pawo ndi kuloŵetsedwa m’kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova, nyumba yake yolambirira ya m’chilengedwe chonse. Iwo adzapeza chisungiko munomo pamene dziko liwonongeka. Ndiwo olambira amoyo oterowo amene ali ofunika kwa Yehova. Chuma chawo chakuthupi sindicho chimene iye akufuna. (Mika 6:6-8) Chinthu cha phindu lalikulu koposa chimene iwo angapereke kwa Yehova ndicho kulambira kwawo kwa moyo wonse. Iwo amadza ndi zopereka za kudzipereka kwamtima ndi utumiki wachangu, iwo onse ‘akumalengeza matamando a Yehova.’ Ndichisangalalo chotani nanga chimene kuwonekera kwawo kwapereka kwa atumiki okhulupirika a Yehova kumwamba ndi padziko lapansi pomwe!
8 Kodi kudzakhala angati a olambira Yehova amenewa amene ali ndi chiyembekezo cha moyo padziko lapansi Laparadaiso? Baibulo silimapereka chiŵerengero. Chasiyidwa chiri chotsegukira anthu ambiri ochokera m’mitundu yonse amene adzalandira makonzedwe achikondi a Yehova. Komabe, chisonyezero cha chimene chigayembekezeredwe, chikupezeka m’Yesaya 60:8, chimene chimawafotokoza kukhala nkhunda “auluka ngati mtambo”—mtambo umene ukudetsadi dziko pansi pake. Chimenechi chikusonyeza kuyenda kwa chiŵerengero chachikulu cha anthu m’nthaŵi yaifupi. Limodzi ndi palapala wamkulu ameneyu wa olambira Yehova, kunanenedweratu, kuti “wamng’ono” wa Israyeli wauzimu ‘akasanduka chikwi, ndi wochepa adzasanduka mtundu wamphamvu,’ ndipo Yehova ananena kuti ‘akakufulumiza m’nthaŵi yake.’ (Yesaya 60:22) Kodi zimenezo zikuyenerana ndi zimene zachitikadi?
9 Pambuyo pa nkhondo yoyamba yadziko panali kokha zikwi zoŵerengeka za okhala ndi phande mwachangu m’kupereka umboni wapoyera wonena za Ufumuwo. Pofika 1935 iwo anakwanira osapitirira 60 000 padziko lonse lapansi. Mu 1941 chiŵerengero cha olengeza Ufumu chinapyola chandamale cha 100 000. Pofika 1953, panali oposa 500 000. Zaka khumi pambuyo pake anafika miliyoni. Pofika chiyambi 1984, anali 2 652 323. Pa avereji, iwo amapatulira oposa kwambiri maola miliyoni patsiku kukusonyeza ena chifukwa chake Ufumu wa Mulungu wokha umapereka chiyembekezo chenicheni cha mtsogolo. Poyerekezera chiŵerengero chimene, monga Mboni za Yehova, chimapereka umboni wakuti iwo ali nzika za Ufumu Waumesiya wa Yehova, nkwachiwonekere kuti mitundu yokwanira 60 ya dziko lerolino iri ndi ziŵerengero zawo za anthu zimene ziri zocheperapo m’kuchuluka koposa “mtundu” womawonjezerekawu. Komabe, “mtundu” wapadera umenewu, ulibe mbali m’ndale zadziko koma ngwodzipatulira kotheratu ku kutumikira Mulungu wowona.
10 Kodi amenewa ndiwo mapeto okwanira ku amene ulosi umenewu udzakwaniritsidwa? Zimene zachitika kale nzokwanira kuyenerana ndi kufotokoza kwa Baibulo. Ndipo nkodabwitsanso, pamene tilingalira mikhalidweyo, pansi pa imene ntchito imeneyi yachitidwira—zopinga zimene zalakidwa, umboni wa chitsogozo cha Mulungu kuti ipambane, kudzipereka kosonyezedwa ndi awo amene akuichita. Ozizwitsanso, ndiwo masinthidwe amene yachititsa m’miyoyo ya anthu. Koma kuwonjezeka kwa anthu oimira Yehova poyera sikukulekeka, ndiponso sikukuchepachepa. Mkati mwa zaka zaposachedwapa pakhala, pa avereji, oposa 10 000 mwezi uliwonse odzipereka kuti abatizidwe m’madzi, ndipo chiwonkhetsocho chakhala chikukwera chaka chirichonse. Onsewa, mwa kuchita chimene ubatizo wawo umaphiphiritsira, angakhale ndi chiyembekezo chotonthoza cha kupulumuka kuloŵa “m’dziko lapansi latsopano.”
11 Mamiliyoni a anthu amenewa saali chabe ophunzira Baibulo oima pawokha, aliyense akumatumikira Mulungu m’njira yakeyake. Iwo ndianthu amene mogonjera akukhala mbali ya gulu lowoneka la Yehova. Monga momwe tawonera, choyamba oloŵa nyumba Aufumu “anasonkhanitsidwa.” Tsopano ena ochokera m’mitundu, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wapadziko lapansi, ‘akudza kwa iwo.’ (Yesaya 60:4, 5) Akhala ogwirizana “m’gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi,” Yesu Kristu. (Yohane 10:16) Mtumwi Petro anafotokoza Akristu owona kukhala ‘gulu la abale’ lapadziko lonse, ndipo Paulo anawafulumiza kuti asadzilekanitse koma kuti ‘asonkhane pamodzi,’ ndipo makamaka pamene tsiku la kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu likuyandikira. (1 Petro 5:9; Ahebri 10:23-25) M’njira imeneyo iwo amalimbikitsidwa ndi kukonzekeretsedwa kukhala ndi phande m’chifuno chachikulu chimene gulu limeneli likukhalira. Ndipo kodi chimenecho nchiyani? Kulemekeza dzina la Yehova.—1 Petro 2:9; Yesaya 12:4, 5.
NTCHITO YOTI ICHITIDWE
12 Onse amene akugwirizana ndi gulu la Yehova posapita nthaŵi amazindikira kuti awo amene alimo ngogwira ntchito. Motsanzira Yesu Kristu iwo onse ngolalikira Ufumu wa Mulungu okangalika, umene uli njira mwa imene dzina la Yehova lidzayeretsedwa. Yesu mwiniyo anati: “Kundiyenera Ine ndilalikire Uthenga Wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumidzi inanso.” (Luka 4:43) Iye analankhula mwamphamvu ponena za kufunika kwakuti ena aumbe miyoyo yawo pa kuchitidwa kwa chifuniro cha Mulungu. Anaphunzitsa omtsatira kuchita ntchito imodzimodziyo imene iye analinkuchita. Ponena za nthaŵi mu imene ife tiri, iye ananeneratu kuti “mbiri yabwino imeneyi ya ufumu” ‘ikalalikidwa m’dziko lonse lapansi lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni ku mitundu yonse.’ (Mateyu 24:14, NW) Imeneyi ndintchito yofunika koposa imene aliyense wa ife angachite lerolino. Kodi nchifukwa ninji kuli choncho? Chifukwa chakuti mwa imeneyo timachirikiza ulamuliro woyenera wa Yehova Mulungu, pa umene thanzi la zolengedwa zonse limadalira. Mwa kukhala ndi phande ndi moyo wonse m’ntchito imeneyi, timasonyeza kuyamikira kwathu kukoma mtima kwapadera kwakukulu kwa Yehova. Timathandizanso anthu anzathu kugwiritsira ntchito njira yokha mwa imene kuli kothekera kwa iwo kupulumuka chisautso chachikulu choyandikiracho.—Yerekezerani ndi 1 Timoteo 4:15, 16.
13 Mikhalidwe imene iwo amapeza mkati mwa gulu la Yehova imakondweretsa mitima yawo. Monga momwe Yehova ananeneratu kudzera kwa Yesaya kuti: “Ndidzakuikira akapitawo a mtendere, ndi oyang’anira ntchito a chilungamo.” (Yesaya 60:17) Mtendere umene ulipo suli chabe wapakwamwa koma weniweni, chipatso cha mzimu woyera wa Mulungu. Zimenezi sizikutanthauza kuti munthu amapeza mtendere wotheratu chifukwa chokha chakuti iye amagwirizana ndi gulu. Iye mwini ayenera kuphunzira ‘kulondola zinthu zopangitsa mtendere ndi zinthu zimene ziri zolimbikitsana.’ (Aroma 14:19) Amafunikira kuphunzira kusonyeza nzeru yaumulungu m’kulimbana ndi zofooka za ena, kuti apereke umboni wa kuleza mtima ndi kudziletsa, kukhala wokhululukira kwa ena monga momwedi iye akufunira Mulungu kuti amkhululukire. Inde, iye ayeneranso ‘kupanga mtendere.’ (Yakobo 3:17, 18; Agalatiya 5:22, 23; Akolose 3:12-14) Iwo amene akutero amapeza chisangalalo chachikulu m’kukhala ndi mbali ya “mtundu wamphamvu” umene tsopano ukupangika ndi umene uli wodzipatulira ku utumiki wa Yehova, “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Ndizo ziŵalo za “mtundu” umenewu zimene zidzapulumutsidwa pamene Yehova apereka chiweruzo padziko lonse lapansi limene limagonjera Satana monga wolamulira wake.
[Mafunso]
1. (a) Ponena za ukulu wa chiwonjezeko cha olambira owona, kodi nchiyani chimene Yehova ananeneratu? (b) Kodi ndani akuchititsadi zimenezi, ndipo motani?
2. (a) Kodi Yesaya 60:1, 2 akulunjikitsidwa kwa yani? (b) Kodi ndim’njira yotani imene “ulemerero wa Yehova” unaŵalitsidwira pa iye? (c) Kodi ndimotani mmene otsalira ‘aunikiridwira’?
3. (a) Kodi nchifukwa ninji, makamaka chiyambire 1914, ‘mdima wakuta dziko lapansi’? (b) Kodi nchiyani chimene chiri chothetsera chokha chenicheni?
4. M’kukwaniritsidwa kwa Yesaya 60:4, kodi ndintchito yosonkhanitsa yotani imene inapatsidwa chisamaliro choyamba?
5. Kodi ndimotani mmene magwero a chiwonongeko chowonjezereka akhalira monga momwe anafotokozedwera pa Yesaya 55:5?
6. Kodi uthenga Waufumu ukufikitsidwa kuti, ndipo limodzi ndi zotulukapo zokondweretsa zotani?
7. Mwa njira imene chiwonjezeko chanenedweratu, kodi ndimotani mmene Yehova akusonyezera chimene chiri kwenikweni chamtengo wapatali m’maso mwake?
8. Kodi Baibulo limapereka zisonyezero zotani ponena za ukulu wa kusonkhanitsidwa kwa oloŵa nyumba apadziko lapansi oyembekezeredwa a Ufumuwo?
9. Kodi chiwonjezeko choterocho chachitika ku ukulu wotani chiyambire 1935?
10. (a) Kodi ndimikhalidwe yotani imene imapangitsa kuwonjezeka kumeneku kukhala kozizwitsa m’maso mwathu? (b) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti zambiri zidakali mtsogolo?
11. (a) Kodi ndimotani mmene Baibulo limasonyezera kuti mamiliyoni amenewa akukhala mbali ya gulu? (b) Kodi chifuno chachikulu cha gulu limeneli nchiyani?
12. (a) Kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera ntchito imene tosefe tiyenera kukhala tikuchita? (b) Kodi njofunika motani, ndipo kodi chifukwa ninji?
13. (a) Pa Yesaya 60:17, kodi ndimkhalidwe wotani umene unanenedweratu kaamba ka gulu la Yehova? (b) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tiulandire mokwanira? (c) Kodi nchiyembekezo chotani chimene chiri pamaso pa awo amene akutero?