Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 22 tsamba 167-174
  • Musalakalake Zimene Zinasiyidwa m’Mbuyo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Musalakalake Zimene Zinasiyidwa m’Mbuyo!
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • “ZINALEMBEDWA KUTICHENJEZA”
  • “KUKALIMIRA MALO ABWINOPO”
  • Mtambo Waukulu Wotere wa Mboni!
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Mfundo Zazikulu za M’buku la Genesis—Chigawo Chachiŵiri
    Nsanja ya Olonda—2004
  • Kodi Muli ndi Chikhulupiriro Chonga cha Abrahamu?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Kumbukirani Mkazi wa Loti
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 22 tsamba 167-174

Mutu 22

Musalakalake Zimene Zinasiyidwa m’Mbuyo!

KUKWANIRITSIDWA kwa ulosi Wabaibulo kumasonyeza mosalakwa kuti lerolino tiri pakhomo penipeni pa dongosolo latsopano laulemerero la zinthu la Mulungu. Mwamsanga dziko loipa lidzatha, ndipo limodzi nalo kuwawa mtima, kugwiritsidwa mwala ndi chisoni zimene lachititsa. Dziko lapansi lidzasandulizidwa kukhala Paradaiso mu amene olambira Mulungu wowona akhala okhoza kukhala ndi moyo wangwiro waumunthu kosatha. Ponena za kutsimikizirika kwa malonjezo ake onena za zinthu zimenezi, Yehova anati kwa mtumwi Yohane: “Talemba; pakuti mawu awa ali okhulupirika ndi owona.” (Chivumbulutso 21:​1-5) Komabe, ngakhale ngati kungawonekere kukhala kwachilendo, anthu ena amene amadziŵa chowonadi ichi amabwerera kunjira ya moyo ya dziko limene Mulungu amati adzaliwononga. Nzachisoni motani nanga! Kodi iwo amachitiranji?

2 Pamene iwo ayamba akumva mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu ndi zimene udzachita, amazilandira mokondwa. Koma kulinso kofunika kufika ku uchikulire Wachikristu, kuzamitsa kuzindikira kwanu Mawu a Mulungu ndi kufunafuna njira zogwiritsira ntchito mokwanira m’moyo wanu. (Ahebri 6:​1, 11, 12) Ngati kusayamikira kuchititsa munthu aliyense kunyalanyaza kuchita zimenezi, iye sadzapitiriza kuwona mwaŵi wa kutumikira Mulungu kukhala wamtengo wapatali. Munthu wotero angakhale wosadekha kaamba ka madalitso akuthupi amene Mulungu walonjeza, pamene akulephera kuzindikira kufunikira kwake kwa kukula kwauzimu ndi kufunika kwa kukhala ndi phande mokwanira monga momwe kungathekere m’ntchito yolalikira ndi kupanga ophunzira imene Mulungu watipatsa kuti tichite tsopano. Kukhutiritsa zikhumbo za chuma chakuthupi ndi za zimene zimawonekera kukhala zokondweretsa kungayambe kutenga nthaŵi yake yowonjezerekawonjezereka. Osati zonse panthaŵi imodzi, koma pang’onopang’ono, iye amabwerera kudziko.​—⁠1 Timoteo 6:​9, 10.

3 Munthu anganene kuti amafuna kupulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano,” kukhala ndi moyo m’dziko limene muli chilungamo. Koma kodi kusankha kwake mabwenzi kumachirikiza zimene amenena? Ndithudi, tsiku ndi tsiku pali kuwonana kosapeŵeka ndi anthu amene samatumikira Yehova​—⁠kuntchito, kusukulu, pokagula zinthu, ngakhale panyumba. Koma m’nthaŵi zopuma kuntchito, patsogolo ndi pambuyo pa sukulu, pochitira telefoni kapena pokachezera mabwenzi, mkati mwa nthaŵi yosanguluka, kodi iye amasankha mabwenzi otani? Kodi kumapangadi kusiyana? Baibulo limachenjeza: “Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.” (1 Akorinto 15:33) Koma kodi nchiyani chimene chiri “mayanjano oipa?” Kodi pali kusiyana kulikonse kuti anthu ena samalambira Yehova, kuti amawonekera kuchita kokha zowonekera kukhala zolungama m’maso mwawo? Pa zimene taphunzira kale, tikudziŵa kuti anthu a mtundu umenewo sadzapulumuka kuloŵa mu “dziko lapansi latsopano.” Alionse amene amaluluza miyezo ya Yehova posankha mabwenzi mwamsanga adzadzipeza atabwerera m’dziko limene iwo nthaŵi ina analingalira kuti analinkulisiya mmbuyo. Koma zitsanzo zochenjeza zolembedwa m’Malemba zingatitetezere kunjira yotero ngati tizilabadira.​—⁠1 Akorinto 10:⁠11.

“ZINALEMBEDWA KUTICHENJEZA”

4 Pamene Yehova analanditsa Israyeli mu ukapolo mu Igupto, ha chinayenera kukhala chitsitsimulo chotani nanga kwa iwo! Chitsenderezo chankhalwe chimene anakumana nacho pambuyo pa imfa ya Yosefe chinapangitsa Igupto kuwonekera ngati ng’anjo yotentha imene anali ataponyedwamo. (Eksodo 1:​13, 14; Deuteronomo 4:20) Komano Yehova anabweretsa nkhonya khumi, kapena miliri, pa Igupto. Kusiyana pakati pa Mulungu wowona ndi milungu ya Igupto kunawonekera. Chotero, pamene Israyeli anachoka m’dziko, “ambiri osokonekeza” a osakhala Aisrayeli anapita nawo, monga momwedi lerolino “khamu lalikulu” limadzilekanitsira ndi dziko ndi kugwirizana ndi otsalira a Israyeli wauzimu. (Eksodo 12:38) Koma kodi nchiyani chimene chinachitika mu msasamo mwamsanga pambuyo pa kutuluka?

5 Wophunzira Wachikristu Stefano analongosola kuti: “Nabwerera mmbuyo m’mitima mwawo ku Aigupto.” Uku kunali miyezi yapang’ono chabe pambuyo pa kulanditsidwa kwawo. (Machitidwe 7:​39, 40) Kodi nchiyani chimene chinapereka umboni wake? Iwo anapanga mwana wang’ombe wagolide​—⁠chinthu chimene anazoloŵera mu Igupto​—⁠analengeza kuti anali kuchita “madyerero a Yehova.” Komatu anali kutsanzira Aigupto. (Eksodo 32:​1-6) Yehova anaipidwa nawo kwambiri. Khalidwe lawo linali lotsutsana mwachindunji ndi Chilamulo choperekedwa pa Phiri la Sinai. Zikwi zambiri zinataya miyoyo yawo. Kodi zinachitikiranji? Ngakhale kuli kwakuti anadziŵa malamulo a Yehova, mwachiwonekere iwo sanakulitse chiyamikiro cha mtima kaamba ka ameneŵa ndi chenicheni chakuti Mulungu wowona analidi kuwatsogolera.

6 Pamene anachoka mu Igupto, Israyeli ndi “anthu ambiri osanganikirana” omwe anamka nawo anadziŵa kuti chinali chinthu choyenera kuchita. Koma chaka chimodzi chitatha iwo anali asanaloŵebe m’Dziko Lolonjezedwa; anali asanakhalebe ndi nyumba mu “dziko loyenda mkaka ndi uchi.” Iwo onse anali ndi zakudya zokwanira zakuthupi, ndipo makamaka panali zakudya zambirimbiri zauzimu. Mtambo njo ndi moto zinapereka umboni wosalekeza wakuti Yehova anali kuwatsogolera. Pa Nyanja Yofiira ndi pa Phiri la Sinai iwo adawona umboni wowopsa wa mphamvu ya Yehova. Pangano Lachilamulo linawapatsa chakudya ndi chitsitsimulo chauzimu. Linaperekanso zochita zambiri kwa iwo mwachindunji, likumawasonyeza pamene iwo anafunikira kusintha khalidwe lawo, kuganiza kwawo, zolinga zawo, kotero kuti zimenezi zikakhale zokondweretsa kwa Yehova. Koma mmalo mwa kuyamikira zonse zimene Yehova anali kuwachitira, anayamba kulakalaka zinthu zakuthupi zimene anali nazo ku Igupto. Kulakalaka kwadyera kunachititsa chiwonongeko kwa ambiri.​—⁠Numeri 11:​4-6, 31-34.

7 Mwamsanga pambuyo pa zimenezi, Mose anatuma amuna kukazonda Dziko Lolonjezedwa. Pamene anabwerera iwo onse anavomerezana kuti linalidi “loyenda mkaka ndi uchi.” Koma azondi khumi anachita mantha ndi anthu akonko ndipo anawopsedwa ndi mizinda yawo ya malinga. Sanakhulupirire Yehova ndi mitima yawo yonse ndipo anachititsa mitima ya anthu kunthunthumira ndi mantha. Kachiŵirinso maganizo awo anabwerera ku Igupto, ndipo analankhula za makonzedwe akubwerera kumeneko. Chifukwa cha kusoŵa kwawo chikhulupiriro, mbadwo wonse wa usinkhu wa zaka 20 zakubadwa ndi wokulirapo potsirizira pake unafera m’chipululu, wosaloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.​—⁠Numeri 13:​27-33; 14:​1-4, 29.

8 Koposa zaka 400 zimenezi sanachitike, phunziro limodzimodzilo linagogomezeredwa m’mpangidwe wosiyana. Mwana wa mbale wa Abrahamu Loti analinkukhala m’Sodomu, mzinda woipa mwakhalidwe koma wolemera m’zinthu zakuthupi. Chisembwere chinali chachikulu kwambiri m’Sodomu ndi miraga yake chakuti Yehova anatsimikiza kuuwononga, wosadzamangidwanso. Angelo anatumidwa kukapulumutsa Loti ndi banja lake. Pamene Loti anachenjeza oyembekezeredwa kukhala apongozi ake, m’maso mwawo “anamuyesa wongoseka.” Koma sikunali kuseka. Mbandakucha angelowo anatulutsa mofulumira Loti ndi banja lake kunja kwa mzinda nawauza kuti athaŵe mosayang’ana mmbuyo. Miyoyo yawo inadalira pa kumvera. Loti ndi ana ake aŵiri aakazi anachita zimene anauzidwa ndipo anapulumuka. Koma mkazi wa Loti mwachiwonekere anali wankhokera kudzilekanitsa ndi zinthu zakuthupi zimene anazisiya mmbuyo. Potembenuka kuti ayang’ane mmbuyo, anataya moyo wake, nasandulika mwala wamchere. Kodi ife enife talabadira chimene zimenezo zimatanthauza? Kuti tisaphonye tanthauzolo, Yesu analiphatikiza m’chenjezo lonena za kufulumira kuthaŵa dongosolo lakale m’nthaŵi yathu. Kunali pochenjeza za kukhala odera nkhaŵa mopambanitsa ndi chuma chakuthupi chakuti iye mwachidule anati: “Kumbukirani mkazi wa Loti.” (Genesis 19:​12-26; Luka 17:​31, 32) Kodi nchiyani chimene chingatitetezere ku mbuna zimene zinakola Aisrayeli ndi mkazi wa Loti?

“KUKALIMIRA MALO ABWINOPO”

9 Kuti tipeŵe kusonkhezeredwa kuyang’ana mmbuyo, tifunikira kukulitsa chikhulupiriro chowonjezereka m’chimene chiri kutsogolo. Ahebri 11:1 (NW) amalongosola chikhulupiriro kukhala “chiyembekezo chotsimikiziridwa cha zinthu zoyembekezeredwa, chisonyezero chowonekera bwino cha zenizeni ngakhale sizinapenyedwe.” Ndicho chitsimikiziritso kapena lonjezo, ngati chikalata chaumwini wa chinthu mwalamulo, chakuti tidzalandira chimene Mulungu wolonjeza. Chikhulupiriro nchozikidwa paumboni wamphamvu, ndipo chifukwa cha chimenecho tiri ndi zifukwa zamphamvu zokhulupirira zimene sitinawone ndi maso athu enieni. Sindiko kunyengeka, kapena kufulumira kukhulupirira kokha chifukwa chakuti kanthu kena kakumvekera kukhala kabwino. Kuti tikhale ndi chikhulupiriro chenicheni tiyenera kufunitsitsa kudziŵa ife eni umboni umene uli maziko ake. Tifunikiranso kulingalira mosamalitsa mmene zimene tikuphunzira zikugwirizanira ndi miyoyo yathu ndi kukulitsa kuziyamikira kwenikweni kochokera mu mtima.

10 Abrahamu anali ndi chikhulupiriro choterocho. Chifukwa cha chimenecho, molamulidwa ndi Yehova Abrahamu anasiya mzinda wolemerera wa Uri mu Kaldayo nasamukira m’Kanani wakutali, dziko limene iye anali asanaliwone kale. Kumeneko anakhala monga mlendo, wosadzigwirizanitsa ndi maufumu alionse a mzinda kaamba ka chisungiko. “Anali kuyembekezera mzinda wokhala ndi maziko enieni [Ufumu Waumesiya wa Yehova], mmisiri ndi womanga wa mzinda umenewo ndiye Mulungu.” Ngati iye akanapitirizabe kulakalaka moyo wa m’Kaldayo, mosakaikira akanabwerera. Mmalo mwake, anali “kukalimira malo abwinopo, ndiko kuti, a kumwamba.” (Ahebri 11:​8-16, NW) Sikunali kwa zaka zochepa zokha, kapena ngakhale khumi kapena makumi aŵiri, zimene Abrahamu anakalimira “malo abwino” amenewo. Iye anapitirizabe kutero mpaka imfa yake zaka 100 kapena kuposa atachoka ku Uri. Iye sanangonena kuti anali ndi chikhulupiriro; anachisonyeza ndi ntchito zake. Chifukwa cha chimenecho mphoto yake njotsimikiziridwa. Chiyembekezo cha chiukiriro kwa iye nchotsimikizirika kwambiri chakuti, monga momwe Yesu ananenera, ‘kwa Mulungu, Abrahamu ngwamoyo.’​—⁠Luka 20:​37, 38; Yakobo 2:⁠18.

11 Koma bwanji ponena za mwana wa Abrahamu, Isake, ndi mwake wa Isake Yakobo? Iwo anali asanalaŵe m’khalidwe Wachikaldayo. Koma iwo sanawone chimenechi kukhala chifukwa chofufuzira chimene uwo unali. Pamene anamva kwa makolo awo malonjezo a Yehova anawalabadira. Anakulitsa chikhulupiriro ngati cha Abrahamu. Nawonso, anali “kukalimira malo abwinopo.” Mulungu sanachite nawo manyazi.​—⁠Ahebri 11:​9, 16, 20, 21; Genesis 26:​24, 25; 28:​20-22.

12 Kumbali ina, Esau mbale wa Yakobo sanayamikire zinthu zauzimu. Anakwatira akazi amene sanali olambira Yehova. Mmalo mwa kulemekeza zinthu zopatulika, anagulitsa kuyenera kwake kwa kubadwa ndi mbizi imodzi. (Genesis 25:​29-34; 26:​34, 35; Ahebri 12:​14-17) Iye anali munthu amene anafuna kukhutiritsidwa kuthupi kwatsopano. Mwana wamkazi wa Yakobo, Dina nayenso analoŵa m’vuto lalikulu. Chifukwa? Chifukwa chakuti anakonda kuzoloŵerana ndi “ana aakazi a dziko ilo” achikunja.​—⁠Genesis 34:​1, 2.

13 Ngati, mofanana ndi Abrahamu, Isake ndi Yakobo, inu mulidi “kukalimira malo abwinopo,” a moyo mu Ufumu Waumesiya wa Yehova, musadzilole kubwezeredwa m’dziko. Kumbukirani, dziko silimalonjeza mtsogolo mosatha. “Koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala kunthaŵi zonse.” Ndipo umenewo udzakhala moyo wokhutiritsa kwambiri motani nanga!​—⁠1 Yohane 2:⁠17.

[Mafunso]

1. (a) Kodi ndimadalitso otani amene ali patsogolo penipeni kaamba ka atumiki okhulupirika a Mulungu? (b) Komabe, kodi nchiyani chimene anthu ena achita?

2. (a) Kuti tipeŵe chotulukapo chotero, kodi nchiyani chimene munthu ayenera kuchita atatha choyamba kuphunzira chowonadi? (b) Ngati alephera kuchita zimenezi, kodi nchiyani chimene chingalamulire maganizo ake, ndipo limodzi ndi chotulukapo chotani?

3. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli kwaupandu kusankha anthu amene samalambira Yehova kukhala mabwenzi? (b) Kodi ndiliti pamene munthu angadzipeze mosavuta m’mayanjano omasuka ndi anthu otero?

4. (a) Kodi ndimoyo wanji umene Israyeli anali nawo mu Igupto Yosefe atafa? (b) Kodi nchifukwa ninji “unyinji wosanganikirana” unagwirizana ndi Israyeli pamene anawomboledwa mu Igupto? (c) Kodi chochitika cholosera chimenecho chakwaniritsidwa motani m’tsiku lathu?

5. (a) Mwamsanga atawomboledwa, kodi ndimotani mmene iwo ‘anabwererera ku Igupto’? (b) Kodi nchifukwa ninji zimenezi zinachitika?

6. (a) Kodi ndichakudya chotani chimene Yehova anawapatsa m’chipululu? (1 Akorinto 10:​3, 4) (b) Kodi nchifukwa ninji ena anayamba kulakalaka zimene anazoloŵera m’Igupto?

7. (a) Pamene azondi anabweretsa malipoti awo, kodi nchifukwa ninji anthu analankhula za kubwerera ku Igputo? (b) Kodi chotulukapo chake chinali chiyani? (Ahebri 3:​17, 19)

8. (a) Kuti Loti ndi banja lake apulumuke pamene Sodomu anawonongedwa, kodi anafunikira kuchitanji? (b) Kodi nchifukwa ninji mkazi wa Loti anasanduka mwala wamchere? (c) Kodi zimenezo ziri ndi uthenga wochenjeza wotani kwa ife?

9. Kodi chikhulupiriro nchiyani, ndipo kodi tingachikulitse motani?

10. (a) Kodi ndimotani mmene Abrahamu anaperekera umboni wa chikhulupiriro chake, ndipo kwautali wotani? (b) Kodi tikudziŵa motani kuti zimene anachita zinali zolungama?

11. Kodi ndimotani mmene Isake ndi Yakobo anasonyezera kuti, nawonso, anali ndi chikhulupiriro?

12. Kodi nchiyani chimene chinaloŵetsa Esau ndi Dina m’mavuto aakulu?

13. (a) Kodi moyo kwenikweni uli ngati chiyani kwa anthu amene ali mbali ya dziko lerolino? (b) Kodi nchiyani chimene chidzatitetezera kusabwezeretsedwamo?

[Chithunzi patsamba 172]

Kumbukirani mkazi wa Loti!

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena