Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • su mutu 23 tsamba 175-182
  • “Chikusoŵani Chipiriro”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Chikusoŵani Chipiriro”
  • Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KODI AKRISTU AYENERA KUCHITA MOTANI?
  • ‘ODALA AWO AMENE AKUPITIRIZA KUPIRIRA’
  • Amapereka Mphoto kwa Onse Omwe Amamutumikira
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Ebedi-meleki Ndi Chitsanzo Chabwino pa Nkhani ya Kulimba Mtima Komanso Kukoma Mtima
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
  • Yehova Ndi Mulungu Woyamikira
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Yehova Adzaweruza Aliyense Malinga ndi Ntchito Zake
    Utumiki Komanso Moyo Wathu wa Chikhristu—Ndandanda ya Misonkhano—2017
Onani Zambiri
Kupulumuka Kuloŵa m’Dziko Lapansi Latsopano
su mutu 23 tsamba 175-182

Mutu 23

“Chikusoŵani Chipiriro”

AWO amene apanga Yehova chidaliro chawo ndianthu achimwemwe chenicheni koposa padziko lapansi lerolino. Iwo amadziŵa kumene uphungu wabwino koposa wonena za mmene angalakire mavuto a moyo ungapezedwe​—⁠m’Mawu enieni a Mulungu. Iwo samawopa pamene akuyang’ana mtsogolo, chifukwa chakuti amadziŵa chimene chiri chifuno cha Mulungu kaamba ka dziko lapansi. (Yeremiya 17:​7, 8; Salmo 46:​1, 2) Komabe, mtumwi Paulo analembera Akristu anzake kuti: “Chikusoŵani chipiriro, kuti pamene mwachita chifuniro cha Mulungu, mukalandire lonjezano.” (Ahebri 10:36) Kodi nchiyani chimene chimachititsa kufunika kumeneku kwa chipiriro?

2 Imfa ya iyemwini isanachitike, Yesu anachenjeza atumwi ake chimene chinali mtsogolo, kuti: “Mukadakhala a dziko lapansi, dziko lapansi likadakonda zake zalokha; koma popeza simuli a dziko lapansi, koma ine ndinakusankhani inu mwa dziko lapansi, chifukwa cha ichi likudani inu. Kumbukirani mawu amene ine ndinanena kwa inu, kapolo saali wamkulu kwa mbuye wake. Ngati anandilondalonda ine, adzakulondalondaninso; ngati anasunga mawu anga, adzasunga anunso. Koma izi zonse adzakuchitirani chifukwa cha dzina langa, chifukwa sadziŵa wondituma ine.” (Yohane 15:​19-21) Zimenezo zakhala zowona motani nanga!

3 Otsatira a Yesu ndiodedwa chifukwa chakuti akukhala mkati mwa dziko limene limakana chimene Chikristu chowona chimaimira. Kristu limatanthauza “wodzozedwa.” Yesu Kristu ndiye wodzozedwa ndi Yehova kukhala Mfumu yolamulira dziko lonse lapansi. Chotero pamene Yesu ananena kuti ophunzira ake akazunzidwa ‘chifukwa cha dzina lake,’ anatanthauza kuti chizunzocho chikakhala chifukwa cha kumamatira kwawo kwa iye monga Mfumu Yaumesiya ya Yehova, chifukwa cha kumvera kwawo Kristu koposa wolamulira aliyense wapadziko lapansi, chifukwa cha kumamatira kwawo mokhulupirika ku Ufumu wake ndi kusaphatikizidwa m’zochitika za maboma a anthu. Yesu anawonjezera kuti chitsutsocho chikakhala chifukwa chakuti ozunzawo “sadziŵa wondituma ine”​—⁠ndiko kuti, amakana kuvomereza Yehova Mulungu monga Wolamulira Wachilengedwe chonse. (Yerekezerani ndi Eksodo 5:⁠2.) Kodi ndani amene ali wosonkhezera wamkulu wa chizunzo chimenechi? Satana Mdyerekezi.​—⁠Chivumbulutso 2:⁠10.

4 Makamaka popeza kuti Satana anatulutsidwa kumwamba pambuyo pa kubadwa kwa Ufumu Waumesiya wa Yehova mu 1914, chitsenderezo pa Akristu owona chakula. Musachichepse. Pali nkhondo yotheratu kumbali ya Mdyerekezi ndi ziŵanda zake yomenyana ndi onse amene aimira mbali ya Ufumu wa Mulungu m’dzanja la Yesu Kristu. Ponena za imeneyi, Chivumbulutso 12:17 chimati: “Ndipo chinjoka [Satana Mdyerekezi] chinakwiya ndi mkazi [gulu longa mkazi lakumwamba la Mulungu], nichinachoka kumka kuchita nkhondo ndi otsala a mbewu yake [otsatira a Kristu odzozedwa ndi mzimu padziko lapansi], amene asunga malamaulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” “Nkhosa zina,” nazonso, zikudzipeza mkati mwa kuŵirima kwa nkhondoyo. Mwanjira zamachenjera, Satana amayesayesa kuwakopa kapena kuwakakamiza kusiya kumvera malamulo a Mulungu. Amafuna kuwafooketsa ndiyeno kuwononga kotheratu uzimu wawo. Cholinga chake ndicho kutontholetsa kulengezedwa kwa Yesu monga Mfumu Yaumesiya ya Yehova. Koma m’nkhondo yauzimu imeneyi atumiki okhulupirika a Mulungu akulakika.

KODI AKRISTU AYENERA KUCHITA MOTANI?

5 Akuluakulu a boma ambiri amazindikira kuti Mboni za Yehova ndizo anthu osunga malamulo ndi kuti izo zimapereka chisonkhezero chabwino m’chitaganya. Komabe, maboma a anthu onse ndiwo mbali ya dongosolo la dziko lazinthu la Satana. (1 Yohane 5:19; Chivumbulutso 13:⁠2) Chotero sikuyenera kudabwitsa pamene maboma ena amaletsa misonkhano ya awo amene amalambira Mulungu wowona kutseka mabukhu awo ofotokoza Baibulo, kukaniza kulalikira kwawo Ufumu wa Mulungu, inde, ngakhale kuwaika m’ndende ndi kuwamenya. Ngati inu mwini mukumana ndi chipsinjo chotero, kodi mudzachitanji?

6 Atumwi a Yesu Kristu anali olemekeza akuluakulu a boma. Pamene anazunzidwa, sanabwezere. Koma pamene analamulidwa kuleka kuchita zimene Mulungu analamula, anayankha mwamphamvu: “Tiyenera kumvera Mulungu monga wolamulira koposa anthu.” (Machitidwe 5:​29, NW; Aroma 12:19; 1 Petro 3:15) Ngakhale pamene miyoyo yawo inathupsidwa, kuwopa imfa sikunawachititse kugonjera. Iwo anadziŵa kuti anali kutumikira “Mulungu wa kuukitsa akufa.” (2 Akorinto 1:9; Ahebri 2:​14, 15) Ngakhale anazunzidwa, anali okondwa​—⁠okondwa chifukwa chakuti anadziŵa kuti anali kukondweretsa Mulungu, okondwa kukhala ndi mwaŵi wa kulemekeza nawo dzina lake ndi kutsimikizira kukhulupirika kwawo kwa Mfumu yake yodzozedwa. (Machitidwe 5:​41, 42; Mateyu 5:​11, 12) Kodi ndinu munthu wamtundu umenewo? Kodi mumadzigwirizanitsa poyera ndi awo amene akukumana ndi zinthu zoterozo? Ebedi-meleki anali munthu amene sanaleke mwamantha. Kodi iye anali yani?

7 Ebedi-meleki anali Mwitiyopiya wowopa Mulungu amene anakhala m’Yerusalemu mkati mwa nyengo yaifupi ndi kuwonongedwa kwake ndi Babulo. Analambedwa ntchito m’banja la Mfumu Zedekiya. Panthaŵiyo Yeremiya analinkutumikira monga mneneri wa Yehova mu Ufumu wa Yuda ndi mitundu yozungulira. Chifukwa chakuti anapereka uthenga wochenjeza wa Mulungu mosasiyirira, anakhala wozunzidwa kwambiri. Mosonkhezeredwa ndi akalonga ena mu Yerusalemu, anaponyedwadi m’chitsime kuti amire m’matope ndi kufa. Ngakhale kuli kwakuti Ebedi-meleki sanali Mwisrayeli, anazindikira Yeremiya kukhala Mneneri wa Yehova. Atamva zimene zinachitidwa, mwamsanga Ebedi-meleki anafunafuna mfumu pa chipata cha mzinda kuti achonderere Yeremiya. Akumachita mogwirizana ndi malangizo a mfumu, mofulumira anatenga amuna 30 kudzanso zingwe ndi nsanza. Anauza Yeremiya kuti ayike sanza m’khwapa mwake kuchepetsa kucheka kwa zingwe, ndiyeno anakoka mneneriyo kumtulutsa m’chitsime.​—⁠Yeremiya 38:​4-13.

8 Ebedi-meleki mwachiwonekere anavutika maganizo ndi zimene akalonga angamchitire chifukwa cha kukhala atalepheretsa chiŵembu chawo, koma nkhaŵayo inapambanidwa ndi kulemekeza kwake mneneri wa Yehova ndi chidaliro chake mwa Mulungu. Chifukwa cha chimenecho, Yehova anatsimikiziritsa Ebedi-meleki kupyolera mwa Yeremiya kuti: “Tawona, ndidzafikitsira mudzi uwu mawu anga kuusautsa, osauchitira zabwino, ndipo adzachitidwa pamaso pako tsiku lomwelo. Koma ndidzakupulumutsa tsiku lomwelo, ati Yehova: ndipo sudzaperekedwa m’manja a anthu amene uwopa. Pakuti ndidzakupulumutsatu ndipo suudzagwa ndi lupanga, koma udzakhala nawo moyo wako ngati chofunkha, pakuti wandikhulupirira ine, ati Yehova.”​—⁠Yeremiya 39:​16-18.

9 Lonjezo limenelo nlamtengo wapatali chotani nanga kwa atumiki a Yehova lerolino! Mofanana ndi Ebedi-meleki, “nkhosa zina” zimawona zoipa zochitidwira kagulu kamakono ka Yeremiya, otsalira odzozedwa, ndipo zoyesayesa zimapangidwa kuletsa kulalikidwa kwa uthenga wa Yehova. Izo sizimazengereza kuchita chirichonse chothekera kutetezera ndi kuchirikiza kagulu ka odzozedwa. Chifukwa cha chimenecho, moyenerera, lonjezo la Yehova kwa Ebedi-meleki limazilimbikitsa, likumalimbikitsa chidaliro chawo chakuti Mulungu sadzalola otsutsa kuwawononga koma kuti Iye adzawatetezera monga kagulu kupyola chiwonongeko chadziko chirinkudza kufikira mu “dziko lapansi latsopano” Lake lolungama.

10 Sionse amene akuyenda m’mapazi a Yesu Kristu amathupsidwa ndi kuikidwa m’ndende, koma onse amakumana ndi chizunzo m’njira zosiyanasiyana. (2 Timoteo 3:12) Zikwi zambiri za akazi Achikristu, ndi amuna, kwa zaka zambiri apirira mokhulupirika chitsutso chachikulu m’banja mwawo mwenimweni. Ana, nawowonso, chifukwa cha chikhumbo chawo cha kutumikira Yehova, akanidwa ndi makolo. (Mateyu 10:​36-38) Achichepere Achikristu angakumanenso ndi chizunzo kusukulu; achikulire, kumalo awo antchito. Onse a Mboni za Yehova amachilaŵa pamene akukhala ndi phande m’kulalikira poyera Ufumu wa Mulungu. Kwa onse otere, mawu a Yesu amagwira ntchito: “Mudzakhala nawo moyo wanu m’chipiriro.”​—⁠Luka 21:⁠19.

11 Kwa ambiri, pali mikhalidwe ina imene imawayesa. Iwo angakhale ndi utenda wowopsa, umene umachotsera moyo chochuluka cha chisangalalao chake. Kapena, mwinamwake amakumana ndi mikhalidwe ya zachuma yovuta kwambiri. Kungakhale kwakuti, nthaŵi zina, mawu olankhulidwa ndi mabwenzi apafupi ngoipa ndi opanda chifundo. Ponena za kholo Yobu, Satana anagwiritsira ntchito njira zonsezi moyesa kuswa umphumphu wake. Kodi tidzachita motani ngati tiloŵa m’mikhalidwe yofanana?​—⁠Yakobo 5:⁠11.

12 Ndiponso, bwanji ngati ife enife tipeza kulabadira kwabwino kochepa ku ziyesayesa zathu za kuchitira umboni zifuno za Yehova? Kumeneko, nakonso, kumafuna chipiriro. Kumbukirani, mkati mwa zaka zonse zimene Nowa analalikira chigumula chisanadze, mkazi wake yekha ndi ana aamuna ndi akazi awo anagwirizana naye m’kutumikira Yehova. Anthu ena onse “sanalabadire.” (Mateyu 24:​39, NW) Mofananamo, lerolino, unyinji ‘sumalabadira.’ Komabe, M’zigawo zina, kumene nthaŵi ina kunali kulabadira kochepa ku uthenga Waufumu, tsopano kuli kututidwa kwakukulu kwa olambira Mulungu wowona. Odala ndiwo awo amene anapirira zaka zamphwayi kapena chitsutso chotheratu ndi amene tsopano akukhala ndi mbali m’kusonkhanitsa kwakukulu kumeneku!

‘ODALA AWO AMENE AKUPITIRIZA KUPIRIRA’

13 Kuti tipeŵe kulephera chiyembekezo chabwino kwambiri cha moyo mu “dziko lapansi latsopano,” nkofunika kwambiri kusaiŵala nkhani yaikulu yoyang’anizana ndi anthu onse​—⁠nkhani ya ulamuliro wachilengedwe chonse. Kodi tiri kumbali ya Yehova kotheratu? Kodi timazindikira kotheratu kuti pali mbali ziŵiri zokha, kuti palibe malo apakati? Ngati titi tisakhale ophedwa m’nkhondoyi, tifunikira kuzindikira ponse paŵiri udani ndi chinyengo chomwe kuti ndizo njira zogwiritsiridwa ntchito ndi Satana kuswa umphumphu wathu, kutichititsa kuleka kumvera Mulungu, kutipatutsa pantchito yofunika yochitira umboni Ufumu Waumesiya.​—⁠1 Petro 5:​8, 9; Marko 4:​17-19.

14 Tiyeneranso kukulitsa chidaliro chotheratu pa Yehova. Kukakhala kopusa chotani nanga kuyesa mwa nyonga yathu yokha kupeŵa misampha yobisika ya mdani wauzimu! Koma ngati tidalira Yehova ndi mtima wathu wonse, ndiyeno pamene tiloŵa m’vuto ndi kuyanga’anizana ndi chiyeso tidzayandikira pafupi kwambiri kwa iye. (Aefeso 6:​10, 11; Miyambo 3:​5, 6) Yehova samatikakamiza kuloŵa m’njira yakutiyakuti. Iye sadzatichititsa kusemphana ndi chifuniro chathu. Koma ngati titembenukira ku Mawu ake kaamba ka chitsogozo, kupempha kwa iye nyonga ndi kukhala pafupi ndi gulu lake, adzatsogoza mapazi athu. Ndipo adzatilimbikitsa ndi umboni watsopano wa chikondi chake chosatha.​—⁠Aroma 8:​38, 39.

15 Mavuto ndi mayeso zimene mukumana nazo zidzakuyesani. Kodi ndani amene mumaika poyamba m’moyo wanu? Kunena kwa Satana nkwakuti tonsefe tiri odera nkhaŵa kwakukukulukulu ndi ife eni. Anthu ochuluka ngotero. Yesu Kristu anali wosiyana. Kodi ndinu wosiyana? Kodi mwaphunzira kuika kulemekezedwa kwa dzina la Yehova poyamba? Ngati ziri choncho, pamenepo, mmalo mwa kuzemba mikhalidwe imene imayesa chikhulupiriro chanu, mudzakhoza kuyang’anizana nayo maso ndi maso, mukumapemphera kwa Yehova kuti akupatseni nzeru kuti mugwiritsire ntchito imeneyi kumlemekeza. Chizunzo chimene mumakumana nacho chidzatulutsa chipiriro; chipiriro chifukwa cha kukonda kwanu Yehova chidzadzetsa chiyanjo chake. “Wodala munthu wa kupirira poyesedwa; pakuti pamene wavomerezeka, adzalandira korona wa moyo, amene Ambuye adalonjeza iwo akumkonda iye.”​—⁠Yakobo 1:​2-4, 12; Aroma 5:​3, 4.

16 Sikokwanira kungoyamba utumiki wa Yehova kapena kupirira kwa kanthaŵi. Tiri m’makani a liŵiro, ndipo mphotho imapita kwa awo amene amadutsa mzera wotsiriza. Odala adzakhala awo onse amene akuyesetsabe maso awo atasumikidwa zolimba pa mphotho pamene dongosolo lakaleli liphwanyika! Nziyembekezo zaulemerero zotani nanga zimene zikuwayembekezera panthaŵiyo.​—⁠Ahebri 12:​1-3; Mateyu 24:⁠13.

[Mafunso]

1. (a) Kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova ziridi anthu achimwemwe? (b) Kodi ndiuphungu wotani pa Ahebri 10:36 umene umagwira ntchito kwa tonsefe?

2. Kodi nchifukwa ninji ophunzira a Yesu akafunikira chipiriro?

3. (a) Kodi nchifukwa ninji kuli ‘chifukwa cha dzina la Yesu’ chimene ophunzira ake amazunzidwa? (b) Kodi ndim’lingaliro lotani ozunza “samadziŵa” Uyo amene anatuma Yesu? (c) Kodi ndani amene kwenikweni ali wochititsa chizunzocho?

4. (a) Kodi ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwa Chivumbulutso 12:17 kumakhudzira miyoyo yathu? (b) Kodi cholinga cha Satana nchiyani?

5. Kodi ndimachitidwe otani amene maboma atenga pa Mboni za Yehova?

6. (a) Kodi ndilingaliro lotani limene tiyenera kukhala nalo kwa akuluakulu a boma? (b) Koma kodi nchiyani chimene tikutsimikiza zolimba kuchita? (c) Ngakhalebe tikuzunzidwa, kodi tingapitirizebe motani kukhala achimwemwe?

7. (a) Kodi Ebedi-meleki anali yani, ndipo nchifukwa ninji iye ali wokondweretsa kwa ife lerolino? (b) Pamene anamva kuti Yeremiya anali ataponyedwa m’chitsime chamatope, kodi Ebedi-meleki anachitanji, ndipo chifukwa ninji?

8. Kodi ndilonjezo lotsimikizirika lotani limene anatumiza kwa Ebedi-meleki, ndipo nchifukwa ninji?

9. (a) Kodi ndimotani mmene “nkhosa zina” zakhalira ngati Ebedi-meleki? (b) Chotero, kodi lonjezo la Yehova kwa Ebedi-meleki limatanthauzanji kwa “nkhosa zina” lerolino?

10. Kodi ndim’mbali ziti za moyo m’zimene Akristu amakumana ndi chizunzo?

11. (a) Kodi ndimikhalidwe ina yotani imene imapereka chiyeso chachikulu kwa ambiri? (b) Kodi ndaninso amene anawona zinthu zimenezi, ndipo chifukwa ninji?

12. (a) Kodi nchifukwa ninji Nowa kwenikweni anafunikira chipiriro mu uminisitala wake? (b) Kodi ndimotani mmene mkhalidwewo wakhalira wofanana m’nthaŵi yathu?

13. (a) Kuti tipitirizebe kupirira, kodi tiyenera kusaiŵala chiyani? (b) Kodi tifunikira kuzindikiranji ponena za njira za Satana?

14. (a) Kodi ndiunansi wotani umene tiyenera kukulitsa, ndipo ndi yani? (b) Kodi iye adzatithandiza motani?

15. (a) Kodi ndani amene ayenera kudza poyamba m’miyoyo yathu? (b) Kodi tiyenera kuwona motani mikhalidwe imene imayesa chikhulupiriro chathu?

16. Kodi nchonulirapo chotani chimene tiyenera kukhala tikukalimira kuchifikira?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena