Kodi Pali Chiyembekezo Chotani Kaamba ka Okondedwa Akufa?
“Atafa munthu, adzakhalanso ndi moyo kodi?” anafunsa motero mwamunayo Yobu kalekalelo. (Yobu 14:14) Mwinamwake inunso, mwadabwa ponena za zimenezi. Kodi mukanalingalira bwanji ngati munadziŵa kuti kugwirizanitsidwa ndi okondedwa anu kachiŵirinso kunali kotheka pompano padziko lapansi m’mikhalidwe yabwino koposa?
Eya, Baibulo limapanga lonjezo lakuti: “Akufa anu adzakhala ndi moyo; . . . adzauka.” Ndiponso Baibulo limati: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”—Yesaya 26:19; Salmo 37:29.
Kuti tikhale ndi chidaliro chenicheni m’malonjezo oterowo, tifunikira kuyankha ena a mafunso aakulu akuti: “Kodi nchifukwa ninji anthu amafa? Kodi akufa ali kuti? Ndipo tingatsimikizire motani kuti iwo angakhalenso ndi moyo?
Imfa, ndi Zimene Zimachitika Pamene Tifa
Baibulo limalongosola momvekera bwino kuti poyambirira Mulungu sanalinganize kuti anthu afe. Iye analenga anthu aŵiri oyambirira Adamu ndi Hava, nawayika m’paradaiso wa padziko lapansi wotchedwa Edene, ndipo anawalangiza kubala ana ndi kufutukulira malo awo okhala a Paradaiso amenewo padziko lonse lapansi. Iwo akafa kokha ngati sakamvera malangizo ake.—Genesis 1:28; 2:15-17.
Posoŵa chiyamikiro kaamba ka chifundo cha Mulungu, Adamu ndi Hava sanamvere ndipo anachititsidwa kulipirira chilango cholongosoledwa pasadakhale. “[Udzabwerera] kunthaka,” Mulungu anauza Adamu, “chifukwa kuti m’menemo unatengedwa. Chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.” (Genesis 3:19) Asanalengedwe Adamu kunalibe; anali fumbi. Ndipo kaamba ka kusamvera kwake, kapena uchimo, Adamu anaweruziridwa kubwerera kufumbi, kumkhalidwe wa kusakhalako.
Motero imfa ndiyo kusakhalako kwa moyo. Baibulo limasonyeza kusiyanako: “Mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha.” (Aroma 6:23) Posonyeza kuti imfa ndiwo mkhalidwe wa kusadziŵa kotheratu, Baibulo limati: “Pakuti amoyo adziŵa kuti tidzafa; koma akufa sadziŵa kanthu bii.” (Mlaliki 9:5) Pamene munthu afa, Baibulo limalongosola kuti: “Mpweya wake uchoka, abwerera kumka kunthaka yake; tsiku lomwelo zotsimikiza mtima zake zitayika.”—Salmo 146:3, 4.
Komabe, popeza kuli kwakuti ali Adamu ndi Hava okha amene sanamvere lamulolo m’Edene, kodi tonsefe timafa chifukwa ninji? Chiri chifukwa chakuti tonsefe tinabadwa pambuyo pa kusamvera kwa Adamu, ndipo chotero tonsefe tinalandira choloŵa cha uchimo ndi imfa kuchokera kwa iye. Monga momwe Baibulo limalongosolera kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi [Adamu], ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse.”—Aroma 5:12; Yobu 14:4.
Komabe wina angafunse kuti: ‘Kodi anthu sali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka pa imfa?’ Ambiri aphunzitsa zimenezi, ngakhale kunena kuti imfa ndiyo khomo loloŵera kumoyo wina. Koma lingaliro limenelo silimachokera m’Baibulo. Mmalo mwake, Mawu a Mulungu amaphunzitsa kuti inu ndinu moyowo, kuti moyo wanu kwenikweni ndinu, limodzi ndi mikhalidwe yanu yonse yakuthupi ndi maganizo. (Genesis 2:7; Yeremiya 2:34; Miyambo 2:10) Ndiponso, Baibulo limati: “Moyo wochimwawo ndiwo udzafa.” (Ezekieli 18:4) Palibe pamene Baibulo limaphunzitsa kuti munthu ali ndi moyo wosakhoza kufa umene umapulumuka pa imfa ya thupi.
Mmene Anthu Angakhalirenso ndi Moyo
Uchimo ndi imfa zitaloŵa m’dziko, Mulungu anaulula kuti chifuno chake chinali chakuti akufa abwezeretsedwe kumoyo kupyolera mwa chiukiriro. Motero Baibulo limalongosola kuti: ‘Abrahamu . . . [anazindikira] kuti Mulungu ngwokhoza kuukitsa [mwana wake Isake] kwa akufa.” (Ahebri 11:17-19) Chidaliro cha Abrahamu sichinaikidwe pachabe, chifukwa chakuti Baibulo limati ponena za Wamphamvuyonse: “Iye sakhala Mulungu wa akufa, koma wa amoyo: pakuti anthu onse akhala ndi moyo kwa iye.”—Luka 20:37, 38.
Inde, sikokha kuti Mulungu Wamphamvuyonse ali ndi mphamvu komanso ali ndi chikhumbo cha kuukitsa anthu amene iye wasankha. Yesu Kristu mwiniyo anati: “Musazizwe ndi ichi, kuti ikudza nthaŵi, imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira.”—Yohane 5:28, 29; Machitidwe 24:15.
Sipanapite nthaŵi yaitali atanena zimenezi, Yesu anakumana ndi dzoma la okaika maliro akutuluka m’mzinda Wachiisrayeli wa Naini. Mnyamata wakufayo anali mwana mmodzi yekha wa mkazi wa masiye. Powona chisoni chake chonkitsacho, Yesu anasonkhezeredwa ndi chifundo. Motero, akumalankhula kumtembo, iye analamula kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.” Ndipo mnyamatayo anakhala tsonga, ndipo Yesu anampereka kwa amake.—Luka 7:11-17.
Mofanana ndi chochitika cha mkazi wa masiye ameneyo, panalinso chisangalalo chachikulu pamene Yesu anapita kunyumba ya Yairo, mkulu wa Sunagoge wa Ayuda. Mwana wake wamkazi wa zaka 12 zakubadwa anali atamwalira. Koma pamene Yesu anafika kunyumba ya Yairo, anapita kwa mwana wakufayo nanena: “Buthu, tauka” Ndipo anauka!—Luka 8:40-56.
Pambuyo pake, bwenzi la Yesu Lazaro anamwalira. Pamene Yesu anafika kunyumba yake, Lazaro anali atafa kwa masiku anayi. Ngakhale kuli kwakuti anali ndi chisoni chachikulu, mlongo wake Marita anasonyeza chiyembekezo, akumati: “Ndidziŵa kuti adzauka m’kuuka tsiku lomaliza.” Koma Yesu anapita kumanda, nalamula kuti mwala uchotsedwe ndipo anaitana kuti: “Lazaro, tuluka.” Ndipo anatuluka!—Yohane 11:11-44.
Tsopano talingalirani za ichi: Kodi mkhalidwe wa Lazaro unali wotani mkati mwa masiku anayi amenewo amene anali wakufa? Lazaro sananene kanthu kalikonse konena za kukhala kumwamba kwaulemerero kapena helo wachizunzo, zimenedi iye akadanena ngati akanakhala kumeneko. Ayi, Lazaro anali wosadziŵa kanthu kotheratu mu imfa ndipo iye akanakhalabe wotero kufikira ‘kuuka kwa tsiku lomaliza,’ ngati Yesu sakanambwezeretsera kumoyo panthaŵiyo.
Ndizowona kuti zozizwitsa za Yesu zimenezi zinali kokha zopindulitsa kwakanthaŵi, popeza kuti awo amene adawaukitsa anamwaliranso. Komabe, iye anapereka umboni zaka 1 900 zapitazo kuti, mwa mphamvu ya Mulungu, akufa angakhozedi kukhalanso ndi moyo! Chotero mwa zozizwitsa zake Yesu anasonyeza pamlingo waung’ono zimene zidzachitika padziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu.
Pamene Wokondedwa Amwalira
Pamene mdaniyo imfa ikantha, chisoni chanu chingakhale chachikulu, ngakhale kuli kwakuti mungakhale ndi chiyembekezo cha chiukiriro. Abrahamu anali ndi chikhulupiriro chakuti mkazi wake adzaukanso, komabe timaŵerenga kuti: “Abrahamu anadza kumaliro a Sara, kuti amlire.” (Genesis 23:2) Ndipo bwanji ponena za Yesu? Pamene Lazaro anamwalira, iye “anadzuma mu mzimu, navutika mwini,” ndipo mwamsanga pambuyo pake, “analira.” (Yohane 11:33, 35) Chotero, pamene wokondedwa wanu amwalira, kulira sindiko kusonyeza chifooko.
Pamene mwana amwalira, kumakhala kovuta kwakukulukulu kwa amake. Motero Baibulo limavomereza chisoni chachikulu chimene amayi angakhale nacho. (2 Mafumu 4:27) Ndithudi, kumakhalanso kovuta kwa atate woferedwa. “Mwenzi nditakufera ine,” analira motero Mfumu Davide pamene mwana wake Abisalomu anafa.—2 Samueli 18:33.
Komabe, chifukwa chakuti muli ndi chidaliro m’chiukiriro, kumva kwanu chisoni sikudzakhala konkitsa. Monga momwe Baibulo limanenera, inu ‘simungalire monganso otsalawo, amene alibe chiyembekezo.’ (1 Atesalonika 4:13) Mmalo mwake, inu mudzayandikira kwa Mulungu m’pemphero, ndipo Baibulo limalonjeza kuti “iye adzakugwiriziza.”—Salmo 55:22.
Kusiyapo ngati kwasonyezedwa mwanjira ina, mawu onse a Baibulo ogwidwa muno ngochokera mu Revised Union Nyanja Version.