Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • pe mutu 6 tsamba 57-68
  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?
  • Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • ADAKHALAKO KALE
  • MOYO WAKE PADZIKO LAPANSI
  • CHIFUKWA CHAKE ANADZA KUDZIKO LAPANSI
  • ANAPEREKA MOYO WAKE DIPO
  • CHIFUKWA CHAKE YESU ANACHITA ZOZIZWITSA
  • WOLAMULIRA WA UFUMU WA MULUNGU
  • Yesu Kristu, kupyolera mwa Amene Mulungu Adzawadalitsa Anthu
    Coonadi Cimene Cimatsogolera ku Moyo Wamuyaya
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso Yamtengo Wapatali Imene Mulungu Anatipatsa
    Zimene Baibulo Limaphunzitsa
  • Kodi Yesu Kristu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Dipo la Yesu Ndi Mphatso ya Mulungu Yamtengo Wapatali Kuposa Zonse
    Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni?
Onani Zambiri
Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi
pe mutu 6 tsamba 57-68

Mutu 6

Yesu Kristu—Kodi Anatumidwa ndi Mulungu?

1, 2. (a) Kodi pali umboni wotani wakuti Yesu Kristu anali munthu weniweni? (b) Kodi ndimafunso otani amene akufunsidwa ponena za Yesu?

PAFUPIFUPI munthu aliyense lerolino wamva za Yesu Kristu. Chiyambukiro chake pa mbiri chakhala chokulirapo koposa chija cha munthu wina aliyense. Ndithudi, kalenda yeniyeniyo yogwiritsiridwa ntchito m’mbali zochuluka za dziko lapansi yazikidwa pa chaka chimene iye akuganiziridwa kukhala atabadwa! Monga momwe The World Book Encyclopedia imanenera: “Madeti a chaka chimenecho chisanafike akulembedwa kukhala B.C., kapena Kristu asanafike. Madeti a pambuyo pa chaka chimenecho amalembedwa kukhala A.D., kapena anno Domini (m’chaka cha Ambuye wathu).”

2 Motero Yesu sanali munthu wopeka. Iye anakhalakodi monga munthu padziko lapansi. “M’nthawi zakale ngakhale adani a Chikristu sanakayikire [kukhalapo kwenikweni] kwa Yesu,” ikutero Encyclopædia Britannica. Motero kodi Yesu anali yani kwenikweni? Kodi iye anatumidwadi ndi Mulungu? Kodi nchifukwa ninji iye ali wotchuka kwambiri?

ADAKHALAKO KALE

3. (a) Malinga ndi mawu a mngelo, kodi Maliya akabala mwana wayani? (b) Kodi kunali kothekera motani kuti namwali Maliya abale Yesu?

3 Mosafanana ndi munthu wina aliyense, Yesu anaberekedwa ndi namwali. Dzina lake linali Maliya. Mngelo ponena za mwana wake anati: “Ameneyu adzakhala wamkulu ndipo adzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu.” (Luka 1:28-33, NW; Mateyu 1:20-25) Koma kodi ndimotani mmene mkazi amene sadakhale pamalo amodzi ndi mwamuna angakhalire ndi mwana? Kunali mwa njira ya mzimu wa Mulungu. Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake wauzimu woyera wamphamvu kuchokera kumwamba kumka kumimba ya namwali Maliya. Chinali chozizwitsa! Ndithudi Iye amene adalenga mkazi woyamba wokhala ndi kukhoza kodabwitsa kwa kubala ana anatha kuchititsa mkazi kukhala ndi mwana popanda atate waumunthu. Baibulo limafotokozakuti: “Pamene malire okwanira a nthawi anafika, Mulungu anatumiza Mwana wake, amene anafikira kukhala wochokera mwa mkazi.”—Agalatiya 4:4, NW.

4. (a) Kodi ndimoyo wotani umene Yesu anali nawo asanabadwe monga mwana? (b) Kodi Yesu ananenanji chosonyeza kuti adakhalako kale kumwamba?

4 Motero asanabadwe padziko lapansi monga munthu Yesu adali kumwamba monga munthu wauzimu wamphamvu. Iye anali ndi thupi lauzimu losawoneka kwa munthu, longa limene Mulungu ali nalo. (Yohane 4:24) Yesu mwiniyo kawirikawiri anatchula malo apamwamba amene iye anali nawo kumwamba. Pa nthawi ina anapemphera kuti: “Atate, ndilemekezeni pambali panu ndi ulemerero umene ndinali nawo pambali panu dziko lapansi lisanakhale.” (Yohane 17:5, NW) Iyenso anati kwa omumvetsera: “Inu ndinu ochokera pansi; Ine ndine wochokera kumwamba.” “Nanga bwanji ngati mukawona Mwana wa munthu alikukwera kumene anali kale lomwe?” “Asanayambe kukhala Abrahamu ndipo Ine ndiripo.”—Yohane 8:23; 6:62; 8:58; 3:13; 6:51.

5. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu adatchedwa “Mawu,” “Wobadwa woyamba” ndi “wobadwa yekha”? (b) Kodi ndintchito yotani imene Yesu adachita ndi Mulungu?

5 Asanadze kudziko lapansi Yesu anatchedwa Mawu a Mulungu. Dzina laulemu limeneli limasonyeza kuti iye anatumikira kumwamba monga amene analankhulira Mulungu. Iye amatchedwanso “Wobadwa woyamba” wa Mulungu, kudzanso Mwana wake “wobadwa yekha.” (Yohane 1:14; 3:16; Ahebri 1:6) Zimenezi zikutanthauza kuti iye anayambirira kulengedwa ana auzimu ena onse a Mulungu, ndi kuti iye ndiye yekha amene analengedwa ndi Mulungu molunjika. Baibulo limafotokoza kuti Mwana “wobadwa woyamba” ameneyuanali limodzi ndi Yehova m’kulenga zinthu zina zonse. (Akolose 1:15, 16) Motero pamene Mulungu anati, “Tipange munthu m’chifanizo chathu,” iye anali kulankhula ndi Mwana ameneyu. Inde, weniweniyo amene pambuyo pake anadza kudziko lapansi ndipo anabadwa mwa mkazi adakhala ndi phande m’kulengedwa kwa zinthu zonse! Iye anakhalako kale kumwamba ndi Atate wake kwa chiwerengero cha zaka chosadziwika!—Genesis 1:26; Miyambo 8:22, 30; Yohane 1:3.

MOYO WAKE PADZIKO LAPANSI

6. (a) Kodi ndizochitika zotani zimene zinachitika kubadwa kwa Yesu kutayandikira ndi pambuyo pake? (b) Kodi Yesu anabadwira kuti ndipo anakulira kuti?

6 Maliya adali atatomeredwa ndi Yosefe. Koma pamene iye anamva kuti mkaziyo anali ndi pakati iye anakhulupirira kuti adachita chigololo ndi mwamuna wina, ndipo chifukwa cha chimenecho iye sanali kudzamkwatira. Komabe, pamene Yehova anamuuza kuti kunali mwa njira ya mzimu Wake woyera chakuti mwanayo anakhaliridwa ndi pakati, Yosefe anatenga Maliya kukhala mkazi wake. (Mateyu 1:18-20, 24, 25) Pambuyo pake, pamene iwo anali kucheza mumzinda wa Betelehemu, Yesu anabadwa. (Luka 2:1-7; Mika 5:2) Pamene Yesu anali chikhalirebe khanda, Mfumu Herode anayesa kumupha. Koma Yehova anachenjeza Yosefe kotero kuti iye anatenga banja lake nathawira ku Igupto. Mfumu Herode atamwalira, Yosefe ndi Maliya anabwerera limodzi ndi Yesu kumzinda wa Nazarete m’Galileya. Iye anakulira muno.—Mateyu 2:13-15, 19-23.

7. (a) Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Yesu anali wa usinkhu wa zaka 12? (b) Kodi ndintchito yotani imene Yesu anaphunzira kuchita pamene anali kukula?

7 Pamene Yesu anali wa usinkhu wa zaka 12 anapita ndi banja lake ku Yerusalemu kukakhala paphwando lapadera lotchedwa Paskha. Pamene anali komweko iye anatha masiku atatu m’kachisi akumvetsera aphunzitsi ndi kuwafunsa mafunso. Anthu onse amene anamumvetsera anadabwa ndi kuchuluka kwa zimene anadziwa. (Luka 2:41-52) Pamene Yesu anakula m’Nazarete, iye anaphunzira kukhala kalipenta. Iye mosakayikira anaphunzitsidwa kuchita ntchito imeneyi ndi atate wake womlera, Yosefe, amenenso anali kalipenta.—Marko 6:3; Mateyu 13:55.

8. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Yesu anali wa usinkhu wa zaka 30?

8 Pa usinkhu wa zaka 30 kusintha kwakukulu kunachitika m’moyo wa Yesu. Iye anapita kwa Yohane Mbatizi napempha kubatizidwa, kuti anyikidwe kotheratu pansi pa madzi a Mtsinje wa Yordano. Baibulo limasimba kuti: “Yesu, pamene anabatizidwa, pomwepo anatuluka m’madzi: ndipo wonani, miyamba inamtsegukira Iye, ndipo anapenya mzimuwa Mulungu wakutsika ngati nkhunda nudza nutera pa Iye; ndipo wonani, mawu akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:16, 17) Simukadakhala chikayikiro m’maganizo mwa Yohane chakuti Yesu adatumidwa ndi Mulungu.

9. (a) Kodi ndiliti pamene Yesu, kwenikweni, anakhala Kristu, ndipo kodi nchifukwa ninji pa nthawi imeneyo? (b) Mwa ubatizo wake, kodi Yesu anali kudzipereka kuchitanji?

9 Mwa kutsanulira mzimu Wake woyera pa Yesu, Yehova anali kumdzoza kapena kumuika kukhala mfumu ya ufumu Wake ulinkudza. Pokhala atadzozedwa motero ndi mzimu, Yesu anakhala “Mesiya,” kapena “Kristu,” mawu amene m’chinenero Chachihebri ndi Chigiriki amatanthauza “Wodzozedwa.” Chifukwa cha chimenecho, iye anakhala, kunena zowona, Yesu Kristu, kapena Yesu Wodzozedwa. Motero mtumwi wake Petro anatchula “Yesu wa ku Nazarete, kuti Mulungu anamdzoza iye ndi mzimu woyera ndi mphamvu.” (Machitidwe 10:38) Ndiponso, mwa ubatizo wake m’madzi, Yesu anali kudzipereka kwa Mulungu kuti achite ntchito imene Mulungu adzamtumizira kudziko lapansi kuti achite. Kodi nchito yofunika imeneyo inali yotani?

CHIFUKWA CHAKE ANADZA KUDZIKO LAPANSI

10. Kodi ndichowonadi chotani chimene Yesu anadzera kudziko lapansi kudzasimba?

10 Pofotokoza chifukwa chake adadza kudziko lapansi, Yesu anauza kazembe Wachiroma Pontiyo Pilato kuti: “Ndabadwira ichi, ndipo ndalowera [chifuno] ichi m’dziko lapansi, kuti ndiyenera kuchitira umboni chowonadi.” (Yohane 18:37, NW) Koma kodi ndi chowonadi chenicheni chotani chimene Yesu anatumidwa kudziko lapansi kudzalengeza? Choyamba, chowonadi chonena za Atate wake wakumwamba. Iye anaphunzitsa omtsatira kupemphera kuti dzina la Atate wake “liyeretsedwe,” kapena liyesedwe loyera. (Mateyu 6:9) Ndipo iye anapemphera kuti: “Ndaliwonetsera dzina lanu kwa anthu amene mwandipatsa.” (Yohane 17:6) Ndiponso, iye anati: “Ndiyenera kulengeza mbiri yabwino ya ufumu wa Mulungu, chifukwa chakuti ndinatumizidwira zimenezi.”—Luka 4:43, NW.

11. (a) Kodi nchifukwa ninji Yesu analingalira ntchito yake kukhala yofunika kwambiri? (b) Kodi nchiyani chimene Yesu sanaleke konse kuchita? Motero kodi nchiyani chimene ife tiyenera kuchita?

11 Kodi ntchito yolengeza dzina la Atate wake ndi ufumu imeneyi inali yofunika motani kwa Yesu? Iye anati kwa ophunzira ake: “Chakudya changa ndicho kuti ndichite chifuniro cha Iye amene anandituma Ine, ndi kutsiriza ntchito yake.” (Yohane 4:34) Kodi nchifukwa ninji Yesu analingalirantchito ya Mulungu kukhala yofunika ngati chakudya? Chinali chifukwa chakuti Ufumuwo ndiwo njira mwa imene Mulungu adzakwaniritsa zifuno zake zabwino kwambiri kwa anthu. Ndiwo ufumu umenewu umene udzachotsa kuipa konse ndipo udzachotsera dzina la Yehova chitonzo chimene chadzetsedwa pa ilo. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 21:3, 4) Motero Yesu sanaleke kulengeza dzina la Mulungu ndi ufumu. (Mateyu 4:17; Luka 8:1; Yohane 17:26; Ahebri 2:12) Iye analankhula chowonadi nthawi zonse, kaya chinali chokondweretsa kapena ayi. Iye motero anapereka chitsanzo chimene ife tiyenera kutsatira ngati tikufuna kukondweretsa Mulungu.—1 Petro 2:21.

12. Kodi Yesu anadza kudziko lapansi kaamba ka chifukwa china chofunika chotani?

12 Komabe, kuti apangitse kukhala kothekera kwa ife kupeza moyo wosatha mkati mwa ulamuliro wa ufumu wa Mulungu, Yesu anafunikira kutsanula mwazi wake wamoyo mu imfa. Monga momwe atumwi awiri a Yesu ananenera kuti: “Talengezedwa kukhala olungama tsopano ndi mwazi wake.” “Mwazi wa Yesu Mwana [wa Mulungu] utichotsera uchimo wonse.” (Aroma 5:9; 1 Yohane 1:7, NW) Motero chifukwa chachikulu chimene Yesu anadzera kudziko lapansi chinali kudzatifera. Iye anati: “Mwana wa munthu sanadza kutumikiridwa koma kutumikira, ndi kupereka moyo [kapena, umoyo] wake dipo la anthu ambiri.” (Mateyu 20:28) Koma kodi kumatanthauzanji kuti Kristu anapereka moyo wake “dipo”? Kodi nchifukwa ninji kutsanulidwa kwa mwazi wamoyo wake mu imfa kunali kofunika kaamba ka chipulumutso chathu?

ANAPEREKA MOYO WAKE DIPO

13. (a) Kodi dipo chiyani? (b) Kodi ndimtengo wadipo wotani umene Yesu analipira kutimasula ku uchimo ndi imfa?

13 Liwulo “dipo” kawirikawiri limagwiritsiridwa ntchito pamene pali kufwamba. Wachifwamba atagwira munthu, iye anganene kuti iye adzabwezera munthuyo ngati kuchuluka kwakutikwakuti kwa ndalama kutalipiridwa monga dipo. Motero dipo ndiko kanthu kena kamene kamapereka chipulumutso kwa munthu wogwidwa. Ndiko kanthu kena kamene kamalipiridwa kotero kuti iye sakutaya moyo wake. Moyo waumunthu wangwiro wa Yesu unaperekedwa kuti upeze chimasuko cha anthu ku ukapolo ku uchimo ndi imfa. (1 Petro 1:18, 19; Aefeso 1:7) Kodi nchifukwa ninji chimasuko choterocho chinafunika?

14. Kodi nchifukwa ninji dipo loperekedwa ndi Yesu linafunika?

14 Zimenezi zinali chifukwa chakuti Adamu, gogo wa tonsefe, adapandukira Mulungu. Kachitidwe kake kakusayeruzika motero kanampangakukhala wochimwa, popeza kuti Baibulo limafotokoza kuti “tchimo ndilo kusayeruzika.” (1 Yohane 3:4; 5:17) Chifukwa cha chimenecho, iye sanali woyenerera kulandira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha. (Aroma 6:23) Chotero Adamu anadzitayira moyo waumunthu wangwiro padziko lapansi laparadaiso. Iye anatayiranso ana ake onse amene akabala chiyembekezo chabwino kwambiri chimenechi. Mungafunse kuti, ‘Koma kodi nchifukwa ninji, ana ake onse anafunikira kufa, popeza kuti anali Adamu amene anachimwa?’

15. Popeza kuti anali Adamu amene anachimwa, kodi nchifukwa ninji ana ake anafunikira kuvutika ndi kufa?

15 Zimenezi nchifukwa chakuti Adamu, pamene anakhala wochimwa, anapitirizira uchimo ndi imfa kwa ana ake, kuphatikizapo anthu onse okhala ndi moyo tsopano. (Yobu 14:4; Aroma 5:12) “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu,” Baibulo limatero. (Aroma 3:23; 1 Mafumu 8:46) Ngakhale Davide wopembedzayo anati: “Ndinabadwa m’mphulupulu: ndipo amayi wanga anandilandira m’zoipa.” (Salmo 51:5) Chifukwa cha chimenecho, anthu akhala akufa chifukwa cha uchimo umene unalandiridwa kuchokera kwa Adamu. Pamenepa. Kodi kunali kothekera motani kuti nsembe ya moyo wa Yesu imasule anthu onse ku ukapolo ku uchimo ndi imfa?

16. (a) M’kupereka dipo, kodi ndimotani mmene Mulungu anasonyezera kulemekeza lamulo lake lakuti ‘moyo uyenera kusinthanitsidwa ndi moyo’? (b) Kodi nchifukwa ninji Yesu anali munthu yekha amene akanatha kulipira dipo?

16 Njira yalamulo m’chilamulo cha Mulungu kwa mtundu wa Israyeli ikulowetsedwamo. Imafotokoka kuti ‘moyo uyenera kusinthana ndi moyo.’ (Eksodo 21:23; Deuteronomo 19:21) Mwa kusamvera kwake munthu wangwiroyo Adamu anadzitayira ndi ana ake onse moyo wangwiro padziko lapansi laparadaiso. Yesu Kristu anapereka moyo wangwiro wa iye mwini kuwombola chimene Adamu anataya. Inde, Yesu “anadzipereka dipo lolinganira kwa onse.” (1 Timoteo 2:5, 6, NW) Chifukwa chakuti iye anali munthu wangwiro, monga momwedi Adamu adaliri, Yesu akutchedwa “Adamu wotsiriza.” (1 Akorinto 15:45) Palibe munthu wina koposa Yesu akadapereka dipo. Zimenezi ziri chifukwa chakuti Yesu ndiye munthu yekha amene anakhalako chiyambire amene anali wolingana ndi Adamu monga mwana waumunthu wangwiro wa Mulungu.—Salmo 49:7; Luka 1:32; 3:38.

17. Kodi ndiliti pamene dipo linalipiridwa kwa Mulungu?

17 Yesu anafa pa usinkhu wa zaka 33 1⁄2. Koma pa tsiku lachitatu pambuyo pa imfa yake anaukitsidwa. Masiku makumi anai pambuyo pake iye anabwerera kumwamba. (Machitidwe 1:3, 9-11) Kumeneko, monga munthu wauzimu kachiwirinso, anawonekera “pamaso pa Mulunguchifukwa cha ife,” atanyamula mtengo wa nsembe yake yadipo. (Ahebri 9:12, 24) Panthawi imeneyo dipo linalipiridwa kwa Mulungu kumwamba. Chipulumutso tsopano chinali chopezeka kwa anthu. Koma kodi ndiliti pamene mapindu ake adzapezedwa?

18. (a) Kodi ndimotani mmene tingapindulire ndi dipo ngakhale tsopano? (b) Kodi nchiyani chimene dipo likutheketsa mtsogolo?

18 Ngakhale tsopano nsembe yadipo ya Yesu ingatipindulitse. Motani? Mwa kusonyeza chikhulupiriro mu iyo tingakhale ndi kaimidwe koyera pamaso pa Mulungu ndi kulowa m’chisamaliro chake chachikondi ndi chokoma mtima. (Chivumbulutso 7:9, 10, 13-15) Ambirife tingakhale titachita machimo owopsa tisanaphunzire za Mulungu. Ndipo ngakhale tsopano timapanga zolakwa, nthawi zina zazikulu kwambiri. Koma tingafunefune chikhululukiro kwa Mulungu momasuka pa maziko a dipo, ndi chidaliro chakuti iye adzatimva. (1 Yohane 2:1, 2; 1 Akorinto 6:9-11) Ndiponso, m’masiku alinkudza, dipo lidzatitsegulira njira yolandirira mphatso ya Mulungu ya moyo wosatha m’dziko lake latsopano lolungama. (2 Petro 3:13) Panthawi imeneyo onse amene akusonyeza chikhulupiriro m’dipo adazamasulidwa kotheratu kuukapolo kuuchimo ndi imfa. Iwo angayembekezere moyo kosatha muungwiro!

19. (a) Kodi ndichiyambukiro chotani chimene kuperekedwa kwa dipo kuli nacho pa inu? (b) Kodi mtumwi Paulo ananena kuti tiyenera kusonyeza motani kuyamikira kwathu dipo?

19 Kodi mukulingalira motani pakumva za dipo? Kodi silikusangalatsa mtima wanu kulinga kwa Yehova Mulungu kudziwa kuti iye amakusamalirani kwambiri chakuti iye anapereka Mwana wake wokondedwa chifukwa cha inu? (Yohane 3:16; 1 Yohane 4:9, 10) Koma, ganiziraninso, chikondi cha Kristu. Iye mofuunitsitsa anadza kudziko lapansi kudzatifera. Kodi sitiyenera kukhala othokoza? Mtumwi Paulo anafotokoza mmene tiyenera kusonyezera kuyamikira kwathu pamene anafotokoza mmene tiyenera kosonyezera kuyamikira kwathu pamene anati: “Adafera onse, kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa Iye amene adawafera iwo, nauka.” (2 Akorinto 5:14, 15) Kodi mudzasonyeza kuyamikira kwanu mwa kugwiritsira ntchito moyo wanu kutumikira Mulungu ndi Mwana wake wakumwamba Yesu Kristu?

CHIFUKWA CHAKE YESU ANACHITA ZOZIZWITSA

20. Kodi tikuphuziranji ponena za Yesu mwa kuchiritsa kwake wakhate?

20 Yesu akudziwika kwambiri ndi zozizwitsa zimene anachita. Iye anali ndi chifundo kwa anthu amene anali m’vuto, ndipo anali wofunitsitsa kugwiritsira ntchito mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu kuwathandiza. Mwa chitsanzo, munthu wina wanthenda yowopsa yakhate anadza kwa iye nati: “Ngati mufuna mukhoza kundikonza.” Yesu “anagwidwa chifundo, natansa dzanja namkhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa.” Ndipo munthu wodwalayo anachiritsidwa! —Marko 1:40-42.

21. Kodi ndimotani mmene Yesu anathandizira makamu?

21 Lingalirani chochitika china Chabaibulo, ndipo yerekezerani lingaliro lachifundo la Yesu kwa anthu ofotokozedwawo: “Ndipo makamu ambiri a anthu anadza kwa Iye, ali nawo opunduka miyendo, akhungu, osalankhula, opunduka ziwalo, ndi ena ambiri, nawakhazika pansi pa mapazi ake: ndipo Iye anawachiritsa; kotero kuti khamulo linazizwa, pakupenya osalankhula nalankhula, opunduka ziwalo nachira, ndi opunduka miyendo nayenda, ndi akhungu napenya, ndipo iwo analemekeza Mulungu wa Israyeli.”—Mateyu 15:30, 31.

22. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Yesu anasamaladi ponena za anthu amene iye anathandiza?

22 Chakuti Yesu anasamaladi ponena za anthu ovutika amenewa ndipo anafunadi kuwathandiza kungawonedwe ndi zimene iye kenako anauza ophunzira ake. Iye anati: “Mtima wanga uchitira chifundo khamu la anthuwa, pakuti ali chikhalire ndi Ine masiku atatu, ndipo alibekanthu kakudya, ndipo sindifuna kuwauza iwo amuke osadya, kuti angaziye panjira.” Motero Yesu, ndi mikate isanu ndi iwiri yokha ndi tinsomba towerengeka, anadyetsa mozizwitsa “amuna zikwi zinai kuwaleka akazi ndi ana.”—Mateyu 15:32-38.

23. Kodi nchiyani chimene chinasonkhezera Yesu kuukitsa mwana wamwamuna womwalira wa mkazi wamasiye?

23 Pa nthawi ina Yesu anakumana ndi mpingo wamaliro umene unalinkutuluka mumzinda wa Nayini. Baibulo likuifotokoza, kuti: “Anthu analikunyamula munthu wakufa, mwana wamwamuna mmodzi yekha, amake ndiye mkazi wamasiye. . . . Ndipo pamene Ambuye anamuwona, anagwidwa ndi chifundo chifukwa cha iye.” Iye anamva chifundo kwambiri ndi chisoni chake. Motero, polankhula ndi mtembowo, Yesu analamula kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka!” Ndipo zozizwitsa kwambiri! “Wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula. Ndipo anampereka kwa amake.” Taganizirani mmene amayi amenewo ayenera kukhala atamvera! Kodi inu mukanamva bwanji? Mbiri yonena za chochitika chapadera chimenechi inafalikira konsekonse. Nzosadabwitsa kuti Yesu ngodziwika kwambiri.—Luka 7:11-17.

24. Kodi zozizwitsa za Yesu zinasonyezanji ponena za mtsogolo?

24 Komabe zozizwitsa zimene Yesu anachita zinali za phindu losakhalitsa chabe. Anthu amene iye anachiritsa anayambanso kudwala. Ndipo awo amene iye anaukitsa anamwaliranso. Koma zozizwitsa za Yesu zinatsimikizira kuti iye anatumidwa ndi Mulungu, kuti iye analidi Mwana wa Mulungu. Ndipo izo zinatsimikizira kuti, ndi mphamvu ya Mulungu, mavuto onse aanthu angathetsedwe. Inde, izo zinasonyeza mochepera zimene zidzachitika padziko lapansi mu ufumu wa Mulungu. Pa nthawi imeneyo anjala adzadyetsedwa, odwala adzachiritsidwa, ndipo ngakhale akufa adzaukitsidwa! Ndipo kudwala, imfa kapena mavuto ena alionse sizidzachititsanso chisoni. Ha, limenelo lidzakhala dalitso lotani nanga!—Chivumbulutso 21:3, 4; Mateyu 11:4, 5.

WOLAMULIRA WA UFUMU WA MULUNGU

25. Kodi moyo wa Yesu ungagawidwe m’mbali zitatu zotani?

25 Moyo wa Mwana wa Mulungu uli ndi mbali zitatu. Yoyamba, pali chiwerengero chosadziwika cha zaka zimene iye anatha limodzi ndi Atate wake kumwamba asanakhale munthu. Yachiwiri, zaka 33 1⁄2 zimene iye anatha padziko lapansi pambuyo pa kubadwa kwake. Ndipo tsopano pali moyo wake iye atabwereranso kumwamba monga munthu wauzimu. Kodi ndimalo antchito otani amene iye wakhala nawo kumwamba chiukitsidwire?

26. Mwa kukhulupirika kwake padziko lapansi, Kodi Yesu anasonyeza kukhala woyenerera kukhala chiyani?

26 Mwachiwonekere, Yesu anayenera kukhala mfumu. Ngakhale mngelo analengeza kwa Maliya, kuti: “Iye adzachita ufumu . . . ku nthawi zonse; ndipo ufumu wake sudzatha.” (Luka 1:33) Mkati mwa uminisitala wake wapadziko lapansi analankhula nthawi zonse ponena za ufumu wa Mulungu. Iye anaphunzitsa omtsatira kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” Ndipo iye anawafulumiza kuti “koma muthange mwafuna ufumu wake.” (Mateyu 6:10, 33) Mwa kukhulupirika kwake padziko lapansi, Yesu anatsimikira kuti iye anali woyenerera kukhala mfumu ya ufumu wa Mulungu. Kodi iye anayamba kulamulira monga mfumu mwamsanga atabwerera kumwamba?

27. (a) Kodi Yesu anachitanji atabwerera kumwamba? (b) Kodi nchiyani chimene chinali chochita choyamba cha Yesu monga mfumu ya ufumu wa Mulungu?

27 Ayi, iye sanatero. Mtumwi Paulo akutchula Salmo 110:1, akumafotokoza kuti: “Iye [Yesu], mmene adapereka nsembe imodzi chifukwa cha machimo, anakhala padzanja lamanja la Mulungu chikhalire; kuyambira pomwepo alindirira, kufikira adani ake aikidwa akhale mpando ku mapazi ake.” (Ahebri 10:12, 13) Yesu anali kuyembekezera lamulo la Yehova, lakuti: “Chitani ufumu pakati pa adani anu.” (Salmo 110:2) Pamene nthawi imeneyo inafika, iye anayamba kuchotsa kumwamba Satana ndi angelo ake. Chotulukapo cha nkhondo imeneyo kumwamba chikufotokozedwa m’mawu awa: “Tsopano zafika chipulumutso, ndi mphamvu, ndi ufumu za Mulungu wathu, ndi ulamuliro wa Kristu wake; pakuti wagwetsedwa wonenera wa abale athu, wakuwanenera pamaso pa Mulungu wathu usana ndi usiku!” (Chivumbulutso 12:10) Monga momwe kwawonedwera m’mutu wina wammbuyomu wa bukhu lino, maumboni amasonyeza kuti nkhondo imeneyi kumwamba yachitika kale, ndipo Yesu Kristu akulamulira pakali pano pakati pa adani ake.

28. (a) Kodi nchiyani chimene Kristu adzachita posachedwapa? (b) Kodi tiyenera kuchitanji kuti tilandire tchinjirizo lake?

28 Posachedwapa kwambiri Yesu Kristu ndi angelo ake akumwamba adzachitapo kanthu kuchotsera dziko lapansi maboma onse adziko alipowa. (Danieli 2:44; Chivumbulutso 17:14) Baibulo limanena kuti iye ali ndi “lupanga lakuthwa, kuti akanthe nalo mitundu ya anthu; ndipo Iye adzawalamulira ndi ndodo yachitsulo.” (Chivumbulutso 19:11-16) Kuti titsimikizirike kukhala oyenerera tchinjirizo mkati mwa chiwonongeko chirinkudzachi, tiyenera kusonyeza chikhulupiriro mwa Yesu Kristu. (Yohane 3:36) Tiyenera kukhala ophunzira ake ndi kudzigonjetsera kwa iye monga Mfumu yathu yakumwamba. Kodi mudzatero?

[Chithunzi patsamba 58]

Yesu anasiya ntchito yake yaukalipenta kuti abatizidwe ndi kukhala wodzozedwa wa Yehova

[Chithunzi patsamba 63]

Yesu anali wolingana ndi munthu wangwiroyo Adamu

[Zithunzi patsamba 64]

Yesu anasonkhezeredwa ndi chifundo kuthandiza odwala ndi anjala

[Chithunzi patsamba 67]

Mwa kuukitsa akufa, Yesu anasonyeza zimene akachita pa mlingo wokulirapo kwambiri pamene ufumu wa Mulungu ulamulira

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena