Mutu 24
Kodi Ife Tiri Pansi pa Malamulo Khumi?
1. Kodi Mose anapereka kwa anthu chilamulo chotani?
KODI YEHOVA Mulungu amatifuna kumvera malamulo otani? Kodi tiyenera kusunga chimene Baibulo limatcha “chilamulo cha Mose” kapena, nthawi zina, “Chilamulo”? (1 Mafumu 2:3; Tito 3:9) Chimenechinso chimatchedwa “chilamulo cha Yehova,” chifukwa chakuti iye ndiye Amene anachipereka. (1 Mbiri 16:40) Mose anangopitiriza Chilamulocho kwa anthu.
2. Kodi chilamulo chimenechi chapangika nchiyani?
2 Chilamulo cha Mose chiri ndi malamulo osiyanasiyana oposa 600, kapena timalamulo, kuphatikizapo 10 aakulu. Monga momwe Mose ananenera: “Iye [Yehova] anakulamulirani kuchita, ngakhale malamulo khumi; ndipo iye anawalemba pamapale awiri amiyala.” (Deuteronomo 4:13; Eksodo 31:18, King James Version) Koma kodi Yehova anapereka kwayani Chilamulocho, kuphatikizapo Malamulo Khumi? Kodi iye anachipereka kwa anthu onse? Kodi chifuno cha Chilamulocho chinali chotani?
KWA ISRAYELI KAAMBA KA CHIFUNO CHAPADERA
3. Kodi tikudziwa motani kuti Chilamulo chinaperekedwa kwa Israyeli yekha?
3 Chilamulocho sichinaperekedwe kwa anthu onse. Yehova anapanga pangano, kapena chivomerezano, ndi mbadwa za Yakobo, zimene zinakhala mtundu wa Israyeli. Yehova anapereka malamulo ake kwa mtundu umenewu wokha. Baibulo limamveketsa bwino zimenezi pa Deuteronomo 5:1-3 ndi Salmo 147:19, 20.
4. Kodi nchifukwa ninji Chilamulo chinaperekedwa kwa mtundu wa Israyeli?
4 Mtumwi Paulo anafunsa funso lakuti: “Pamenepa, kodi nchifukwa ninji, Chilamulo?” Inde, kodi Yehova anapereka chilamulo chake kwa Israyeli kaamba ka chifuno chotani? Paulo anayankha: “Kupangitsa zolakwa kuwoneka, kufikira itadza mbewu kwa amene lonjezolo lidaperekedwa . . . Chifukwa chake Chilamulo chakhala namkungwi [kapena, mphunzitsi] wathu wotsogoza kwa Kristu.” (Agalatiya 3:19-24, NW) Chifuno chapadera cha Chilamulo chinali kutetezera ndi kutsogoza mtundu wa Israyeli kotero kuti iwo akakhala okonzekera kulandira Kristu pamene anafika. Nsembe zambiri zofunidwa ndi Chilamulozo zinakumbutsa Aisrayeli kuti iwo anali ochimwa amene anafunikira Mpulumutsi.—Ahebri 10:1-4.
“KRISTU ALI CHIMALIZIRO CHA LAMULO”
5. Pamene Kristu anadza ndi kutifera, kodi nchiyani chimene chinachitikira Chilamulocho?
5 Ndithudi, Yesu Kristu, anali Mpulumutsi wolonjezedwa ameneyo, monga momwedi mngeloyo analengezera pa kubadwa kwake. (Luka 2:8-14) Motero pamene Kristu anadza ndi kupereka moyo wake wangwiro monga nsembe, kodi nchiyani chimene chinachitikira Chilamulo? Chinachotsedwa. “Sitikhalanso omvera namkungwi,” Paulo anatero. (Agalatiya 3:25) Kuchotsedwa kwa Chilamulo kunali chimasuko kwa Aisrayeli. Chidawavumbula monga ochimwa, pakuti iwo onse analephera kusunga Chilamulo chimenecho bwino lomwe. “Kristu anatiwombola ku temberero la chilamulo,” Paulo anatero. (Agalatiya 3:10-14) Motero Baibulo limanenanso kuti: “Kristu ali chimaliziro cha lamulo.”—Aroma 10:4; 6:14.
6. (a) Kodi pamene Chilamulocho chinatha chiyambukiro pa Aisrayeli ndi osakhala Aisrayeli chinali chotani, ndipo nchifukwa ninji? (b) Kodi Yehova anatenga kachitidwe kotani kulinga ku Chilamulo?
6 Chilamulo kwenikweni chinatumikira monga cholekanitsa kapena “khoma” pakati Aisrayeli ndi mitundu ina imene siinali pansi pake. Komabe, mwa nsembe ya moyo wake, Kristu “anathetsa . . . Chilamulo cha malamulo chokhala ndi malangizo, kuti akalenge anthu awiriwo [Mwisrayeli ndi wosakhala Mwisrayeli] mogwirizana ndi iyemwini kukhala munthu mmodzi watsopano.” (Aefeso 2:11-18, NW) Ponena za kachitidwe kamene Yehova Mulungu mwiniyo anatenga kulinga ndi chilamulo cha Mose, tikuwerenga kuti: “Anatikhululukira mokoma mtima zolakwa zanthu zonse nafafaniza cholembedwa chapamanja chotitsutsa, chimene chinali ndi malangizo [kuphatikizapo Malamulo Khumi] ndi amene anali otitsutsa [chifukwa cha kutsutsa Aisrayeli monga ochimwa]; ndipo Iye wachichotsa panjira mwa kuchikhomera pamtengo wophedwera.”(Akolose 2:13, 14, NW) Motero, Chilamulocho chinathetsedwa ndi nsembe yangwiro ya Kristu.
7, 8. Kodi nchiyani chimene chimatsimikizira kuti Chilamulo sichinagawike pawiri?
7 Komabe, anthu ena amanena kuti Chilamulo chikugawidwa kukhala mbali ziwiri: Malamulo Khumi, ndi ena a malamulowo. Ena a malamulowo, iwo amatero, ndiwo amene anatha, koma Malamulo Khumi alipobe. Komabe zimenezi sizowona. Mu Ulaliki wake wa pa PhiriYesu anagwira mawu kuchokera m’Malamulo Khumi kudzanso mbali zina za Chilamulo ndipo sanalekanitse pakati pawo. Motero Yesu anasonyeza kuti chilamulo cha Mose sichinagawike kukhala mbali ziwiri.—Mateyu 5:21-42.
8 Wonaninso, zimene mtumwi Paulo anauziridwa ndi Mulungu kulemba: “Tsopano tinamasulidwa kuchilamulo.” Kodi anali malamulo okha osati Malamulo Khumi amene Ayuda anamasulidwamo? Ayi, pakuti Paulo akupitiriza kunena kuti: “Koma ine sindikadazindikira uchimo, koma mwa lamulo ndimo; pakuti sindikazindikira chilakolako sichikadati chilamulo, Usasirire.” (Aroma 7:6, 7; Eksodo 20:17) Popeza kuti “Usasirire” ndilo lotsiriza la Malamulo Khumi, kuyenera kukhala kwakuti Aisrayeli anamasulidwanso ku Malamulo Khumi.
9. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti lamulo Lasabata lamlungu ndi mlungu linachotsedwanso?
9 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti lamulo la kusunga Sabata lamlungu ndi mlungu, limene liri lachinai la Malamulo Khumi, linachotsedwanso? Inde, zikutero. Chimene Baibulo limanena pa Agalatiya 4:8-11 ndi Akolose 2:16, 17 chimasonyeza kuti Akristu sali pansi pa chilamulo cha Mulungu choperekedwa kwa Aisrayeli, limodzi ndi chofunika chake cha kusunga Sabata lamlungu ndi mlungu ndi kusunga masiku ena apadera m’chaka. Chakuti kusunga Sabata lamlungu ndi mlungu sindiko chofunika Chachikristu kungawonedwenso mu Aroma 14:5.
MALAMULO AMENE AKUGWIRA NTCHITO KWA AKRISTU
10. (a) Kodi Akristu ali pansi pa malamulo otani? (b) Kodi ambiri a malamulo amenewa anatengedwa kuti, ndipo kodi nchifukwa ninji kuli koyenera kuti iwo anatengedwa m’menemo?
10 Kodi zimenezi zikutanthauza kuti, popeza kuti Akristu sali pansi pa Malamulo Khumi, iwo safunikira kusunga malamulo alionse? Kutalitali. Yesu anayambitsa “pangano latsopano,” lozikidwa pa nsembe yabwinopo ya moyo wake waumunthu wangwiro. Akristu akudza pansi pa pangano latsopano limeneli ndipo ali ogonjera ku malamulo Achikristu. (Ahebri 8:7-13; Luka 22:20) Ambiri a malamulo amenewa atengedwa m’chilamulo cha Mose. Zimenezi siziri zosayembekezeredwa kapena zodabwitsa. Chinthu chofananacho kawirikawiri chimachitika pamene boma latsopano litenga ulamuliro wa dziko. Mpambo wamalamulo wa boma lakale ungafafanizidwe ndi kulowedwa m’malo, koma mpambo wamalamulo watsopanowo ungasunge ambiri a malamulo a wakalewo. M’njira yofananayo, pangano Lachilamulo linatha, koma ambiri a malamulo ake akulu ndi zilangizo zinalowetsedwa m’Chikristu.
11. Kodi ndi malamulo kapena ziphunzitso zotani zoperekedwa kwa Akristu zimene ziri zofanana kwambiri ndi Malamulo Khumi?
11 Wonani mmene zimenezi ziriri choncho pamene mukuwerenga Malamulo Khumiwo pa tsamba 203, ndiyeno ayerekezereni ndi malamulo Achikristu ndi ziphunzitso zotsatirapozi: “Ndiye Yehova Mulungu wako amene uyenera kulambira.” (Mateyu 4:10, NW; 1 Akorinto 10:20-22) “Dzitetezereni ku mafano.” (1 Yohane 5:21, NW; 1Akorinto 10:14) “Atate wathu wakumwamba, dzina lanu liyeretsedwe [osati kuchitiridwa m’njira yosayenera].” (Mateyu 6:9, NW) “Ananu, mverani akukubalani.” (Aefeso 6:1, 2) Ndipo Baibulo limamveketsa bwino lomwe kuti mbanda, kuchita chigololo, kuba, kunama ndi kusirira zirinso zosemphana ndi malamulo a Akristu.—Chivumbulutso 21:8; 1 Yohane 3:15; Ahebri 13:4; 1 Atesalonika 4:3-7; Aefeso 4:25, 28; 1 Akorinto 6:9-11; Luka 12:15; Akolose 3:5.
12. Kodi njira ya lamulo Lasabata ikulowetsedwa motani m’kakonzedwe Kachikristu?
12 Angakhale Akristu sakulamulidwa kusunga Sabata lamlungu ndi mlungu, tikuphunzira kanthu kena m’kakonzedwe kameneko. Aisrayeli anapuma m’njira yeniyeni, koma Akristu ayenera kupuma m’njira yauzimu. Motani? Chifukwa cha chikhulupiriro ndi kumvera Akristu owona amaleka kuchita ntchito za iwo eni. Ntchito za iwo eni zimenezi zimaphatikizapo zoseyaseya za kukhazikitsa chilungamo cha iwo eni. (Ahebri 4:10) Mpumulo wauzimu umenewu umasungidwa osati tsiku limodzi lokha pamlungu koma kwamasiku onse asanu ndi awiri. Chofunika cha lamulo lenileni Lasabata cha kupatula tsiku limodzi kaamba ka zabwino zauzimu chinatetezera Aisrayeli ku kusagwiritsira ntchito nthawi yawo yonse mwadyera kufunafuna phindu lawo lakuthupi. Kugwiritsira ntchito njira imeneyi tsiku lirilonse m’njira yauzimu ndiko tchinjirizo lamphamvu kwambiridi ku kukondetsa zinthu zakuthupi.
13. (a) Kodi Akristu akufulumizidwa kukwaniritsa lamulo lotani, ndipo kodi iwo amalikwaniritsa motani? (b) Kodi Yesu anagogomezera lamulo lotani? (c) Kodi ndilamulo lotani limene liri maziko a chilamulo chonse cha Mose?
13 Motero Akristu akufulumizidwa ‘kukwaniritsa chilamulo cha Kristu,’ koposa ndi kusunga Malamulo Khumi. (Agalatiya 6:2) Yesu anapereka malamulo ambiri ndi zilangizo, ndipo mwa kuwamvera kwathu tikusunga kapena kukwaniritsa chilamulo chake. Makamaka, Yesu anagogomezera kufunika kwa chikondi. (Mateyu 22:36-40; Yohane 13:34, 35) Inde, kukonda ena ndiko lamulo Lachikristu. Ndiko maziko a chilamulo chonse cha Mose, monga momwe Baibulo likunenera: “Mawu amodzi akwaniritsa chilamulo chonse ndiwo: Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”—Agalatiya 5:13, 14; Aroma 13:8-10.
14. (a) Kodi padzapezeka ubwino wanji mwa kuphunzira ndi kugwiritsira kwathu ntchito zilangizo za chilamulo cha Mose? (b) Kodi chikondi chidzatisonkhezera kuchitanji?
14 Chilamulo choperekedwa mwa Mose, limodzi ndi Malamulo ake Khumi, chinali mpambo wa malamulo wolungama wochokera kwa Mulungu. Ndipo ngakhale kuli kwakuti sitiri pansi pa chilamulo chimenecho lerolino, zilangizo zaumulungu zokhala kutseri kwake ziri chikhalirebe za phindu lalikulu kwa ife. Mwa kuziphunzira ndi kuzigwiritsira ntchito tidzawonjezeka m’kuyamikira Wopereka malamulo wamkuluyo Yehova Mulungu. Koma makamaka tiyenera kuphunzira ndi kugwiritsira ntchito m’miyoyo yathu malamulo ndi ziphunzitso Zachikristu. Kukonda Yehova kudzatisonkhezera kumvera zonse zimene iye tsopano akufuna kwa ife.—1 Yohane 5:3.
[Bokosi patsamba 203]
MALAMULO KHUMI
1. “Ine ndine Yehova Mulungu wako . . . Usakhale nayo milungu yina koma Ine ndekha.
2. “Usadzipangire iwe wekha fano losema, kapena chifaniziro chirichonse cha zinthu za m’thambo la kumwamba, kapena za m’dziko lapansi, kapena za m’madzi a pansi pa dziko; usazipembedzere izo, usazitumikire izo . . .
3. “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe . . .
4. “Uzikumbukira tsiku la Sabata, likhale lopatulika. Masiku asanu ndi limodzi uzigwira, ndi kumaliza ntchito zako zonse; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usagwire ntchito iriyonse, kapena iwe wekha, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi . . .
5. “Uzilemekeza atate wako ndi amako; kuti achuluke masiku ako m’dziko limene Yehova Mulungu wako akupatsa iwe.
6. “Usaphe.
7. “Usachite chigololo.
8. “Usabe.
9. “Usamnamizire mzako.
10. “Usasirire [kukhumbira] nyumba yake ya mnzako, usasirire [kukhumbira] mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng’ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.”—Eksodo 20:2-17.
[Zithunzi pamasamba 204, 205]
Chilamulo chinatumikira monga khoma pakati pa Aisrayeli ndi anthu ena