Mutu 29
Kupangitsa Moyo Wabanja Kukhala Wabwino
1. (a) Kodi banja linayamba motani? (b) Kodi chifuno cha Mulungu ponena za banja chinali chotani?
PAMENE Yehova Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi woyambayo, iye anawagwirizanitsa pamodzi kuti abale ana. (Genesis 2:21-24; Mateyu 19:4-6) Chinali chifuno cha Mulungu kuti awiri okwatirana amenewa awonjezeke mwa kubala ana. Ndiyeno, pamene anawo akula, iwo anayenera kukwatirana ndi kupanga mabanja awoawo. Chinali chifuno cha Mulungu kuti, m’kupita kwa nthawi, mabanja achimwemwe akakhala m’mbali iriyonse ya dziko lapansi. Iwo akapanga dziko lapansi kukhala paradaiso wokongola kulikonse.—Genesis 1:28.
2, 3. (a) Kodi nchifukwa ninji Mulungu sangaimbidwe mlandu wa kulephera kwabanja? (b) Kodi musangalale ndi moyo wabanja wabwino kodi chofunika nchiyani?
2 Komabe, lerolino, mabanja akusweka, ndipo ambiri amene ali chikhalirebe limodzi sali okondwa. Motero munthu angafunse kuti: ‘Ngati banja linalengedwadi ndi Mulungu, kodi sitiyenera kuyembekezera zotulukapo zabwinopo?’ Komabe, Mulungu sangaimbidwe mlandu chifukwa cha kulephera kwabanja. Wopanga zinthu angapange chinthu china ndi kupereka malangizo onena za kuchigwiritsira kwake ntchito. Koma kodi chimakhala chifukwa cha wopanga zinthu ngati chinthucho chilephera pa chifukwa chakuti wogulayo sakutsatira malangizowo? Kutalitali. Chinthucho, ngakhale ngati chiri cha mkhalidwe wabwino kwambiri, chidzalephera chifukwa chakuti sichikugwiritsiridwa ntchito moyenera. Ziri choncho ndi banja.
3 Yehova Mulungu wapereka malangizo m’Baibulo onena za kukhala ndi moyo kwabanja. Koma ngati malangizo amenewa anyalanyazidwa, pamenepo bwanji? Ngakhale kuli kwakuti kakonzedwe kabanja nkangwiro, kangasweke. Pamenepo ziwalo zabanja sizidzakhala zokondwa. Ndiponso, ngati zitsogozo za m’Baibulo zitsatiridwa, kumeneku kudzapangitsa banja loyenda bwino ndi lokondwa. Chifukwa cha chimenecho, nkofunika kwambiri kuti, tikuzindikira mmenedi Mulungu analengera ziwalo zosiyanasina za banja, ndi malo antchito amene iye analinganiza kuti iwo akhale.
MMENE MULUNGU ANALENGERA MWAMUNA NDI MKAZI
4. (a) Kodi pali kusiyana kotani pakati pa amuna ndi akazi? (b) Kodi nchifukwa ninji Mulungu analenga kusiyana koteroko?
4 Aliyense angawone kuti Yehova sanalenge amuna ndi akazi mofanana. Nzowona kuti m’njira zambiri iwo ngofanana. Koma pali kusiyana kwachiwonekere m’kawonekedwe kawo kathupi ndi kaumbidwe kamtundu. Ndiponso, ali ndi mikhalidwe yamalingaliro yosiyana. Kodi nchifukwa ninji kusiyanako? Mulungu anawalenga motero kuti athandize aliyense kuti akwaniritse malo antchito osiyana. Mulungu atalenga mwamuna, Mulungu anati: “Sikuli bwino kuti munthu kuti apitirizebe kukhala yekha. Ndidzampangira womthandiza, monga womkwaniritsa.”—Genesis 2:18, NW.
5. (a) Kodi mkazi anapangidwa kukhala “wokwaniritsa” kwa mwamuna motani? (b) Kodi ukwati woyamba unachitikira kuti? (c) Kodi nchifukwa ninji ukwati ungakhale kakonzedwe kosangalatsadi?
5 Chokwaniritsa ndicho kanthu kena kamene kamalingana kapena kamayenda bwino ndi kanthu kenanso, kakumachipangitsa kukwanira. Mulungu analenga mkazi monga cholingana chokhutiritsa cha mwamuna kuti chimthandize m’kukwaniritsa malangizo operekedwa ndi Mulungu a kudzaza ndi anthu ndi kusamalira dziko lapansi. Motero atalenga mkazi kuchokera ku mbali ina ya mwamuna, Mulungu anapanga ukwati woyamba m’munda wa Edene momwemo mwa ‘kumtengera kwa mwamuna.’ (Genesis 2:22; 1 Akorinto 11:8, 9) Ukwati ungakhale kakonzedwe kosangalatsa chifukwa chakuti mwanuna ndi mkazi aliyense analengedwa ali ndi chosowa chimene wina ali ndi kukhoza kwa kukwaniritsa. Mikhalidwe yawo yosiyana imakwaniritsana. Pamene mwamuna ndi mkazi azindikirana ndi kudziwana ndi kugwirizana mogwirizana ndi ntchito zawo zogawiridwa, iwo aliyense payenkha amachita mbali yawo m’kumanga banja losangalala.
NTCHITO YA MWAMUNA
6. (a) Kodi ndani amene anapangidwa kukhala mutu wa banja? (b) Kodi nchifukwa ninji zimenezi ziri zoyenera ndi zopindulitsa?
6 Ukwati kapena banja limafuna utsogoleri. Mwanuna analengedwa ndi mlingo wokulirapo wa mikhalidwe ndi nyonga zofunika kupereka utsogoleri woterowo. Kaamba ka chifukwa chimenechi Baibulo limati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi, monganso Kristu ndiye mutu wa Eklesia.” (Aefeso 5:23) Kumeneku nkoyenera, pakuti palibe utsogoleri pamakhala vuto ndi chisokonezo. Kuti banja likhale lopanda umutu kukakhala ngati kuyesa kuyendetsa galimoto lopanda chowongolerera. Kapena, ngati mkazi akanati apikisane ndi umutu woterowo, kukakhala ngati kukhala ndi oyendetsa awiri m’galimoto, aliyense wokhala ndi chowongolerera choyendetsera gudumu lina lapatsogolo.
7. (a) Kodi nchifukwa ninji akazi ena samakonda lingaliro la umutu wa mwamuna? (b) Kodi aliyense ali ndi mutu, ndipo kodi nchifukwa ninji kakonzedwe ka Mulungu ka umutu kali kanzeru?
7 Komabe, akazi ambiri samakondwera ndi lingaliro lakuti mwamuna ayenera kukhala mutu wa banja. Chifukwa chimodzi chachikulu cha zimenezi nchakuti amuna ambiri sanatsatire malangizo a Mulungu onena za kuchita kwake umutu woyenera. Mosasamala kanthu za zimenezo, nchinthu chozindikirika kuti kuti gulu lirilonse ligwire ntchito bwino lomwe munthu wina amafunikira kupereka chitsogozo ndi kupanga zosankha zotsirizira. Motero Baibulo mwanzeru limati: “Mutu wa munthu yense ndiye Kristu; ndi mutu wa mkazi ndiye mwamuna; ndipo mutu wa Kristu ndiye Mulungu.” (1 Akorinto 11:3) M’kakonzedwe ka Mulungu, Mulungu ndiye amene alibe mutu. Wina aliyense, kuphatikizapo Yesu Kristu, kudzanso amuna ndi akazi, afunikira kulandira chitsogozo ndi kugonjera ku zosankha za ena.
8. (a) Kodi amuna akuyembekezeredwa kutsatira chitsanzo cha yani m’kusonyeza umutu? (b) Kodi amuna ayenera kuphunzira maphunziro otani m’chitsanzo chimenecho?
8 Zimenezi zikutanthauza kuti kuti akwaniritse ntchito yawo monga amuna okwatira, amuna ayenera kulandira umutu wa Kristu. Ndiponso, iwo ayenera kutsatira chitsanzo chake mwa kusonyeza umutu pa akazi awo monga momwe iye amachitira pa mpingo wake wa atsatiri. Kodi ndimotani mmene Kristu anachitira ndi atsatiri ake apadziko lapansi? Nthawi zonse kunali m’njira yokoma mtima ndi yolingalira. Iye sanali wankhanza kapena wamtima wapachala, ngakhale pamene iwo anali osafulumira kulandira chitsogozo chake. (Marko 9:33-37; 10:35-45; Luka 22:24-27; Yohane 13:4-15) Kunena zowona, iye mofunitsitsa anapereka moyo wake kaamba ka iwo. (1 Yohane 3:16) Mwamuna Wachikristu ayenera kuphunzira mosamalitsa chitsanzo cha Kristu, ndi kuchita kuyesetsa kwake konse kuchitsatira pochita ndi banja lake. Chifukwa cha chimenecho, iye sadzakhaal mutu wabanja wotsendereza, wodzikonda kapena wosalingalira.
9. (a) Kodi akazi ambiri amakhala ndi chidandaulo chotani? (b) Kodi amuna mwanzeru ayenera kukumbukira chiyani posonyeza umutu?
9 Kombabe, ku mbali ina, amuna ayenera kulingalira izi: Kodi mkazi wanu amadandaula kti inu kwenikweni simukuchita monga mutu wabanja? Kodi iye amanena kuti inu simukupereka chitsogozo m’banja, kulinganiza zochita zabanja ndi kusonyeza thayo la kupanga zosankha zotsiriza? Koma izi ndizo zimene Mulungu amafuna kwa inu, monga mwamuna, kuti muchite. Ndithudi, kukakhala kwanzeru kwa inu kukhala wolandira malingaliro ndi zofuna za ziwalo zina za banja ndi kulingalira malingaliro amenewa pamene mukusonyeza umutu. Monga mwamuna, inu mwachiwonekere muli ndi ntchito yovutirapo m’banja. Koma ngati mupanga kuyesayesa kowona mtuma kuikwaniritsa mosakayikira mkazi wanu adzawona kukhala woyedzamira kukupatsani chithandizo ndi chichirikizo.—Miyambo 13:10; 15:22.
KUKWANIRITSA NTCHITO YA MKAZI
10. (a) Kodi Baibulo limalimbikitsa akazi njira yotani? (b) Kodi nchiyani chimene chimachitika pamene akazi alephera kulabadira uphungu Wabaibulo?
10 Monga momwe Baibulo limanenera, mkazi analengedwa monga wothandiza kwa mwamuna wake. (Genesis 2:18) Mogwirizana ndi ntchito imeneyo, Baibulo limafulumiza kuti: “Akazitu akhale ogonjera kwa amuna awo.” (Aefeso 5:22, NW) Lerolino kuukira kwa akazi ndi mpikisano ndi amuna zakhala zofala. Koma pamene akazi akudziika patsogolo, akumayesa kutenga umutu, kachitidwe kawo nkosalephera kuchititsa vuto. Amuna ambiri, kunena zowona, amati: ‘Ngati iye akufuna kuyendetsa banja, mlekeni atero ndi kuliyendetsa.’
11. (a) Kodi mkazi angathandize mwamuna wake motani kutenga utsogoleri? (b) Ngati mkazi akwaniritsa ntchito yake yogawiridwa ndi Mulungu, kodi zimenezi nzosalephera kukhala ndi chiyambukiro chotani pa mwanuna wake?
11 Komabe, mungalingalire kuti mukukakamizidwa kutenga utsogoleri, popeza kuti mwamuna wanu sakutero. Koma kodi mungachite zambiri kumthandiza kusenza mathayo ake monga mutu wabanja? Kodi mumasonyeza kuti mumayang’ana kwa iye kaamba ka utsogoleri? Kodi mumapempha malingaliro ndi chitsogozo chake? Kodi mumapewa m’njira iri yonse kunyozetsa zimene amachita? Ngati inuyo mukuyesayesadi kukwaniritsa ntchito yanu yogawiridwa ndi Mulungu m’banja, mwamuna wanu mosakayikira adzayamba kuchita yake.—Akolose 3:18, 19.
12. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti akazi moyenerera angasonyeze malingaliro awo, ngakhale ngati amenewa sakugwirizana ndi a amuna awo?
12 Kumeneku sindiko kunena kuti mkazi sayenera kusonyeza malingaliro ake ngati iwo akusiyana ndi aja a mwamuna wake, ayi. Iye angakhale ndi lingaliro loyenera, ndipo banja likapindula ngati mwamuna wake akanamumvetsera. Mkazi wa Abrahamu Sara akuperekedwa monga chitsanzo kwa akazi Achikristu chifukwa cha kugonjera kwake kwa mwamuna wake. (1 Petro 3:1, 5, 6) Komabe iye anapereka chothetsera cha vuto labanja, ndipo pamene Abrahamu sanagwirizane naye Mulungu anamuuza kuti: “Umvere iwe mawu ake.” (Genesis 21:9-12) Ndithudi, pamene mwamuna apanga chosankha pa nkhani, mkazi ayenera kuchichirikiza ngati kuteroko sikudzamchititsa kuswa lamulo la Mulungu.—Machitidwe 5:29.
13. Kodi mkazi wabwino adzakhala akuchitanji, ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chiyambukiro pa banja lake?
13 M’kukwaniritsa moyenera ntchito yake, pali zambiri zimene mkazi anagachite m’kusamalira banja. Mwa chitsanzo, iye angakonze zakudya zopatsa thanzi, kusunga nyumba yaudongo ndi yosamalirika ndi kukhala ndi phande m’kuphunzitsa ana. Baibulo limafulumiza akazi okwatibwa “kukonda amuna awo, kukonda ana awo, kukhala olama m’maganizo, oyera, ogwira ntchito panyumba, abwino, odzogonjetsera kwa amuna a iwo okha, kotero kuti mawu a Mulungu sangachitiridwe mwano.” (Tito 2:4, 5, NW) Mkazi ndi amayi amene amakwaniritsa ntchito zimenezi adzapeza chikondi chosatha ndi ulemu wa banja lake.—Miyambo 31:10, 11, 26-28.
MALO A ANA M’BANJA
14. (a) Kodi malo oyenera a ana m’banja ngotani? (b) Kodi ana angaphunzirenji m’chitsanzo cha Yesu?
14 Yehova analangiza anthu awiri oyambawo kuti: “Mubalane, muchuluke.” (Genesis 1:28) Inde, Mulungu anawauza kuti abale ana. Ana anati akhale dalitso ku banjalo. (Salmo 127:3,-5) Popeza kuti iwo akudza pansi pa lamulo ndi malamulo a makolo awo, Baibulo limayerekezera malo a mwana ndi aja a kapolo. (Miyambo 1:8; 6:20-23; Agalatiya 4:1) Ngakhale Yesu anapitiriza kukhala wogonjera kwa makolo ake pamene anali mwana. (Luka 2:51) Zimenezi zikutanthauza kuti iye anawamvera, akumachita zimene iwo ananena. Ngati ana onse akanachita zimodzimodzi, kukanachititsadi chimwemwe chabanja.
15. Kodi nchifukwa ninji ana kawirikawiri amakhala chomvetsa chisoni chachikulu kwa makolo awo?
15 Komabe, koposa ndi kukhala dalitso ku banja, ana lerolino kawirikawiri amakhala magwero a chisoni chachikulu kwa makolo. Kodi nchifukwa ninji? Nchifukwa cha kulephera kwa ana, ndi makolo omwe, kugwiritsira ntchito m’miyoyo yawo malangizo a Baibulo onena za kukhala kwabanja. Kodi ena a malamulo ndi malangizo a Mulungu amenewa ndiotani? Tiyeni tipende owerengeka a iwo pamasamba otsatirapowo. Pamene tikutero, wonani ngati simukuvomereza kuti, mwa kuwagwiritsira ntchito, mungachititse chimwemwe m’banja lanu.
Kondani ndi Kulemekeza Mkazi Wanu
16. Kodi amuna akulamulidwa kuchitanji, ndipo kodi malamulo amenewa amachitidwa moyenerera motani?
16 Limodzi ndi nzeru yaumulungu, Baibulo limati: “Amuna azikonda akazi awo a iwo okha monga ngati matupi a iwo okha.” (Aefeso 5:28-30) Mobwerezabwereza, kudziwa zinthu kwatsimikizira kuti kuti akazi akhale okondwa iwo amafunikira kumva kuti iwo akukondedwa. Zimenezi zikutanthauza kuti mwamuna ayenera kupatsa mkazi wake chisamaliro chapadera, kuphatikizapo chikondi, kuzindikira ndi chitsimikiziritso. Iye afunikira ‘kupatsa ulemu,’ monga momwe Baibulo likunenera. Iye amachita zimenezi mwa kumlingalira m’zonse zimene iye amachita. M’njira imeneyi iye adzapeza ulemu wake. —1 Petro 3:7.
Lemekezani Mwamuna Wanu
17. Kodi akazi akulamulidwa kuchitanji, ndipo kodi iwo amachita zimenezi motani?
17 Nanga bwanji akazi? “Mkazi ayenera kukhala ndi ulemu waukulu kwa mwamuna wake,” Baibulo limatero. (Aefeso 5:33, NW) Kulephera kulabandira uphungu umenewu ndiko chifukwa chachikulu chimene amuna ena amaipidwira ndi akazi awo. Mkazi amasonyeza ulemu mwa kuchirikiza zosankha za mwamuna wake, ndi mwa kugwirizana naye ndimoyo wonse kukwaniritsa zolinga zabanja. Mwa kukwaniritsa ntchito yake yogawiridwa ndi Baibulo monga ‘wothandiza ndi wokwaniritsa’ kwa mwamuna wake, amapangitsa kukhala kwapafupi kwa mwamuna wake kumkonda.—Genesis 2:18.
Khalani Okhulupirika kwa Wina ndi Mnzake
18. Kodi nchifukwa ninji okwatirana ayenera kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake?
18 Baibulo limati: “Amuna ndi akazi ayenera kukhala okhulupirika kwa wina ndi mnzake.” Kwa mwamuna limati: “Khala wokondwa ndi mkazi wako ndipo peza chisangalalo chako ndi msungwana amene unakwatira . . . uperekerenji chikondi chako kwa mkazi wina? Ukonderenji kukongola kwa mkazi wa munthu wina?” (Ahebri 13:4; Miyambo 5:18-20, Today’s English Version) Inde, chigololo nchotsutsidwa ndi lamulo la Mulungu; chimachititsa vuto mu ukwati. “Anthu ochuluka amaganizira kuti chigololo chingakometse ukwati,” anatero wofufuza ukwati wina, koma iye ananenanso kuti chigololo nthawi zonse chimachititsa “mavuto enieni.” —Miyambo 6:27-29, 32.
Funafunani Chikondwerero cha Mnzanu
19.Kodi ndimotani mmene okwatirana angapezere chisangalalo chachikulu koposa m’kugonana?
19 Chimwemwe sichimadza pamene wina amafunafuna chikondwerero chakugonana kwakukulukulu kaamba ka iye mwini. M’malo mwake, chimapezedwa mwa kufunafunanso kukondweretsa mnzanu. Baibulo limati: “Mwamuna apereketu kwa mkazi wake mangawa ake; koma mkazinso achitetu chimodzimodzi kwa mwamuna wake.” (1 Akorinto 7:3, NW) Chigogomezero chiri pa kupereka, kupatsa. Ndipo mwa kupatsa, wopatsayo amalandiranso chikondwerero chenicheni. Kuli monga momwe Yesu Kristu ananenera kuti: “Muli chimwemwe chambiri m’kupatsa koposa ndi chimene chiri m’kulandira.”—Machitidwe 20:35, NW.
Dziperekeni kwa Ana Anu
20. Kodi nchifukwa ninji kuchita zinthu ndi ana anu kuli kofunika kwambiri?
20 Mwana wina wa pafupifupi usinku wa zaka zisanu ndi zitatu anati: “Atate wanga amagwira ntchito nthawi zonse. Iwo samakhala panyumba. Amandipatsa ndalama ndi zidole zambirimbiri, koma sindimawawona konse. Ndimawakonda ndipo ndikufuna ngati sakanamagwira ntchito nthawi zonse kotero ndikanatha kuwaona kwambiri.” Moyo wapabanja umakhala bwinopo kwambiri chotani nanga pamene makoko atsatira lamulo la Baibulo la kuphunzitsa ana awo ‘pamene akhala pansi m’nyumba yawo ndi pamene iwo agona pansi ndi pamene iwo adzuka’! Kudzipereka kwa ana anu, kutha nawo nthawi yabwino mokwanira, nkotsimikizirika kuchititsa chimwemwe chabanja.—Deuteronomo 11:19; Miyambo 22:6.
Perekani Chilango Chofunika
21. Kodi Baibulo limanenanji ponena za kupereka chilango kwa ana?
21 Atate wathu wakumwamba amapatsa makolo chitsanzo choyenera mwa kupatsa anthu ake chilangizo chowongolera, kapena chilango. Ana amafunukira chilango. (Ahebri 12:6; Miyambo 29:15) Pozindikira zimenezi, Baibulo limafulumiza kuti: “Atate, inu, . . . pitirizani kulera [ana anu] m’chilangizo ndi zosonkhezera maganizo za Yehova.” Kuperekedwa kwa chilango, ngakhale ngati kungaphatikizepo kupamantha kapena kuchotseredwa zoyenera, ndiko umboni wakuti makolo amakonda ana awo. Baibulo limati: “Iye wokonda [mwana wake wamwamuna] ndiye amene amamyambiza kumlanga.”—Aefeso 6:4; Miyambo 13:24; 23:13, 14, NW.
Ana—Kanizani Njira Zadziko
22. Kodi ana ali ndi thayo lanji, ndipo nchiyani chimene chikulowetsedwamo m’kulikwaniritsa?
22 Dziko limapanga kuyesayesa kwa kuchititsa ana kuswa malamulo a Mulungu. Ndiponso, monga momwe Baibulo limafotokozera, “utsiru umangidwa mumtima mwa mwana.” (Miyambo 22:15) Motero imakhala nkhondo kuchita chimene chiri chabwino. Komabe Baibulo limati: “Ana ndiyo ntchito yanu Yachikristu kumvera makolo anu, pakuti kumeneku ndiko chinthu choyenera kuchita.” Kudzapereka mphotho zazikulu. Motero, ana, khalani anzeru. Labadirani uphunguwo: “Kumbukirani Mlengi wanu pamene mudakali achichepere.” Kanizani ziyeso za kumeza mankhawala oledzeretsa, kuledzera, kuchita dama ndi kuchita zinthu zina zimene ziri zotsutsidwa ndi malamulo a Mulungu.—Aefeso 6:1-4; Mlaliki 12:1; Miyambo 1:10-19, Today’s English Version.
Phunzirani Baibulo Limodzi
23. Kodi mabanja adzakhala ndi mapindu otani mwa kuphunzira Baibulo limodzi?
23 Ngati chiwalo chimodzi cha banja chiphunzira ndi kugwiritsira ntchito ziphunzitso Zabaibulo, kudzachititsa chimwemwe chabanja. Koma ngati zonse zitero—mwamuna, mkazi ndi ana—limenelo lidzakhala banja lodala chotani nanga! Mudzakhala unansi wosangalatsa ndi weniweni, limodzi ndi kukambitsirana komasuka, pamene chiwalo chirichonse chabanja chiyesa kuthandiza zina kutumikira Yehova Mulungu. Motero chipangeni kukhala chizolowezi chabanja kuphunzira Baibulo limodzi!—Deuteronomo 6:4-9; Yohane 17:3.
KUTHETSA MAVUTO ABANJA BWINO LOMWE
24. Kodi nchifukwa ninji okwatirana ayenera kulolera zolakwa za wina ndi mnzake?
24 Ngakhale m’mabanja amene nthawi zonse amakhala okondwa, mudzakhala mavuto nthawi ndi nthawi. Zimenezi ziri chifukwa chakuti ife tonse ndife opanda ungwiro ndipo timachita zinthu zolakwa. “Ife tonse timakhumudwa nthawi zambiri,” limatero Baibulo. (Yakobo 3:2, NW) Motero okwatirana sayenera kufuna ungwiro kwa wina ndi mnzake. M’malo mwake, aliyense ayenera kulekerera zophophonya za wina. Chifukwa cha chimenecho, palibe aliyense wa okwatiranawo ayenera kuyembekezera ukwati wachimwemwe kotheratu, popeza kuti umenewu ngwosathekera kwa anthu opanda ungwiro kuupeza.
25. Kodi zovuta zaukwati ziyenera kuthetsedwa m’chikondi motani?
25 Ndithudi, mwamuna ndi mkazi adzafuna kuyesayesa kupewa zimene zimakhumudwitsa mnzake. Komabe mosasamala kanthu mmene iwo akuyesera mwamphamvu, iwo nthawi zina adzachita zinthu zimene zimakhumudwitsa wina. Pamenepa, kodi ndimotani, mmene zovuta ziyenera kuthetsedwera? Uphungu wa Baibulo ndiwo: “Chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo.” (1 Petro 4:8) Zimenezi zikutanthauza kuti okwatirana amene amasonyeza chikondi sadzapitiriza kufukula zolakwa zimene winayo wachita. Chikondi chimati, kwenikweni, ‘Inde, unapanga cholakwa. Koma momwemonso ine nthawi zina. Motero ndidzanyalanyaza zako, ndipo ungachite zomwezo kwa ine.’—Miyambo 10:12; 19:11.
26. Pamene vuto lina libuka, kodi chidzathandiza nchiyani m’kuthetsa nkhaniyo?
26 Pamene okwatirana ali ofunitsitsa kuvomereza zolakwa ndi kuyesa kuziwongola, makangano ambiri ndi zisoni zingapewedwe. Cholinga chawo chiyenera kukhala kuthetsa zovuta, osati kupambana makangano. Ngakhale ngati mnzanuyo ali wolakwa, pangitsani kukhala kosavuta kwambiri kuthetsa vutolo mwa kukhala wokoma mtima. Ngati mwalakwa, pemphani chikhululukiro modzichepetsa. Musakankhire mtsogolo, thetsani vutolo mofulumira. “Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.”—Aefeso 4:26.
27. Kodi nkutsatiridwa kwa uphungu Wabaibulo wotani kumene kudzathandiza okwatirana kuthetsa mavuto awo?
27 Makamaka ngati inu muli munthu wokwatira, mufunikira kutsatira lamulo la “kusamalira, osati mokondwera ndi zinthu zanu zokha, komanso mokondwera ndi zinthu zanu zokha, komanso mokondwera ndi zija za ena.” (Afilipi 2:4, NW) Mufunikira kumvera lamulo Labaibulo: “Dzivekeni chikondi chokoma mtima cha chisoni, kukoma mtima, kudzichepetsa maganizo, kudekha, ndi kuleza mtima. Pitirizanibe kupirirana ndi kukhululukirana mwaufulu ngati aliyense ali ndi chifukwa chidandaulira ndi wina. Monga momwedi Yehova mwaufulu anakukhululukirani, teroni inunso. Koma, kuphatikiza pa zinthu zonsezi, dzivekeni chikondi, pakuti ndicho chomangira changwiro cha chigwirizano.”—Akolose 3:12-14, NW.
28. (a) Kodi chisudzulo ndicho njira yothetsera mavuto aukwati? (b) Kodi nchiyani chimene Baibulo limanena kuti ndicho chokha cha chisudzulo chimene chimamasula munthu kukwatiranso?
28 Lerolino okwatirana ambiri samatsatira uphungu wa m’Mawu a Mulungu wowathandiza kuthetsa mavuto awo, ndipo iwo amafunafuna chisudzulo. Kodi Mulungu amavomereza chisudzulo monga njira yothetsera zovuta? Ayi, samavomereza. (Malaki 2:15, 16) Iye anafuna ukwati ukhale kakonzedwe ka moyo wonse. (Aroma 7:2) Baibulo limaloleza chifukwa chimodzi chokha chopezera chusudzulo chimene chimamasula munthu kukwatiranso, ndipo chimenecho ndicho chigololo. (Chigiriki, porneia, chisembwere choipitsitsa chakugonana) Ngati chigololo chichitidwa, pamenepo wopanda liwongoyo angasankhe kaya kupeza chisudzulo kapena ayi.—Mateyu 5:32.
29. (a) Ngati wokwatirana naye wanu sakugwirizana nanu m’kulambira Kwachikristu, kodi muyenera kuchitanji? (b) Kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo chothekera?
29 Bwanji ngati wokwatirana naye wakana kuphunzira Mawu a Mulungu limodzi nanu, kapena ngakhale kutsutsa ntchito yanu Yachikristu? Baibulo limakulimbikitsanibe kukhala ndi mnzanuyo ndi kusalingalira kulekana monga njira yapafupi yochokera m’mavuto anu. Chitani zimene inu panokha mungathe kuwongola mkhalidwewo m’nyumba mwanu mwa kugwiritsira ntchito zimene Baibulo limanena ponena za khalidwe lanu. M’kupita kwanthawi, chifukwa cha khalidwe lanu Lachikristu, mungapindule mnzanu. (1 Akorinto 7:10-16; 1 Petro 3:1, 2) Ndipo mudzakhala ndi dalitso lotani nanga ngati kudekha kwanu kwachikondi kufupidwa m’njira imeneyi!
30. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwambiri kwa makolo kupereka chitsanzo chabwino kwa ana awo?
30 Mavuto ambiri abanja lerolino amakhudza ana. Kodi nchiyani chimene chingachitidwe ngati zimenezi ziri choncho m’banja lanu? Choyambirira, monga makolo mufunikira kupereka chitsanzo chabwino. Zimenezi ziri chifukwa chakuti ana amayedzamira kwambiri kutsatira zimene muchita koposa zimene munena. Ndipo pamene zochita zanu zisiyana ndi mawu anu, ana amakhala ofulumira kuziwona. Motero, ngati mufuna kuti ana anu akhale ndi miyoyo yabwino ndi Yachikristu, inu eninu muyenera kupereka chitsanzo.—Aroma 2:21, 22.
31. (a) Kodi ana amafunikira chifukwa china chofunika chotani kaamba ka kumvera uphungu wa kholo lawo? (b) Kodi mungasonyeze bwanji mwana wanu nzeru ya kumvera lamulo la Mulungu limene limaletsa dama?
31 Ndiponso, mufunikira kukambitsirana ndi ana. Sikokwanira kungouza ana: ‘Sindifuna kuti muchite dama, chifukwa nloipa.’ Iwo afunikira kusonyezedwa kuti ndiye Mlengi wawo, Yehova Mulungu, amene akunena kuti zinthu zoterozo monga dama nzoipa. (Aefeso 5:3-5; 1 Atesalonika 4:3-7) Koma ngakhale zimenezi siziri zokwanira. Ana amafunanso kuthandizidwa kuwona chifukwa chake iwo ayenera kumvera malamulo a Mulungu, ndi mmene kumeneku kudzawapindulitsira. Mwa chitsanzo, mungasonyeze mwana wanu njira yodabwitsa imene khanda lamunthu limapangidwira mwa kugwirizana kwa ubwamuna wa mwamuna ndi dzira la mkazi, ndi kufunsa kuti: ‘Kodi suganiza kuti Iye amene anatheketsa chozizwitsa ichi cha kubadwa amadziwa kwambiri mmene anthu ayenera kugwiritsirira ntchito mphamvu zawo za kubala zopatsidwa ndi Mulungu?’ (Salmo 139:13-17) Kapena mungafunse kuti: ‘Kodi ukuganiza kuti Mlengi wathu Wamkulu akapanga lamulo la kutilanda chisangalalo m’moyo? M’malo mwake, kodi sitiyenera kukhala okondwa kwambiri ngati titamvera malamulo ake?’
32. (a) Kodi mkhalidwe wanu uyenera kukhala wotani ngati malingaliro a mwana sakugwirizana ndi a Mulungu? (b) Kodi mwana wanu angathandizidwe motani kuwona nzeru ya chimene Baibulo limanena?
32 Mafunso oterowo angayambitse mwana wanu kulingalira lamulo la Mulungu lolamulira kugwiritsiridwa ntchito kwa ziwalo zobalira. Landirani malingaliro ake. Ngati iwo sali chimene mukuwafuna kuti akhale, musakwiye. Yesani kuzindikira kuti mbadwo wa mwana wanu wapita patali kusiyana ndi ziphunzitso zolungama za m’Baibulo, ndiyeno yesani kumsonyeza chifukwa chake machitidwe oipa a mbadwo wake ali opusa. Mwina mwake mungasonyeze mwana wanu zitsanzo zenizeni za kumene chisembwere chachititsira ana apathengo, nthenda zopatsana mwa kugonana kapena mavuto ena. M’njira imeneyi iye akuthandizidwa kuwona ubwino ndi kuyenera kwa chimene Baibulo limanena.
33. Kodi nchifukwa ninji chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo cha kukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi chingatithandize kupangitsa moyo wabanja kukhala wabwino?
33 Makamaka chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo chakukhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi chingatithandize kupangitsa moyo wabanja kukhala wabwino. Kodi nchifukwa ninji choncho? Nchifukwa chakuti ngati tifunadi kukhala ndi moyo m’dongosolo latsopano la Mulungu, tidzayesa zolimba kukhala ndi moyo tsopano monga momwe tikuyembekezerera kukhala ndi moyo pa nthawi imeneyo. Zimenezi zikutanthauza kuti tidzatsatira mosamalitsa malangizo ndi chitsogozo cha Yehova Mulungu. Chifukwa cha chimenecho, Mulungu adzawonjezera chimwemwe chochuluka ku umuyaya wonse umene uli mtsogolo.—Miyambo 3:11-18.