Kutaya Mimba
Tanthauzo: Kutaya mimba ndiko kuchotsa mluza kapena mwana wosabadwa amene kaŵirikaŵiri ali wosakhoza kukhala ndi moyo kunja kwa m’mimba. Kutaya mimba kapena kupita pachabe kwachibadwa kungachitike chifukwa cha kupanda ungwiro kwaumunthu kapena chifukwa cha ngozi. Kutaya mimba kwa dala kochitidwira kokha kupeŵa kubala mwana wosafunidwa ndiko kupha mwadala moyo waumunthu.
Kodi ndimotani mmene Magwero a moyo waumunthu ayenera kuyambukirira lingaliro lathu la nkhaniyi?
Mac. 17:28: “Mwa iye [Mulungu] tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda ndi kupeza mkhalidwe wathu.”
Sal. 36:9: “Chitsime cha moyo chiri ndi inu [Yehova Mulungu].”
Aroma 14:12: “Munthu aliyense wa ife adzadziŵerengera mlandu wake kwa Mulungu.”
Kodi Yehova amawona moyo wa mwana monga wamtengo wapatali ngakhale kuchiyambiyambi kwa kakulidweko pambuyo pa mimba?
Sal. 139:13-16, NW: “Inu [Yehova] munanditchinjiriza m’mimba mwa amayi. . . . Maso anu anawonadi mluza wa ine, ndipo ziŵalo zake zonse zinali zolembedwa m’bukhu lanu.”
Kodi Mulungu anayamba wanenapo kuti munthu akaimbidwa mlandu kaamba ka kuvulaza mwana wosabadwa?
Eks. 21:22, 23: “Akayambana amuna, nakakantha mkazi ali ndi pakati, kotero kuti abala, koma alibe kupwetekwa; alipe ndithu, monga momwe amtchulira mwamuna wa mkaziyo; apereke monga anena oweruza. Koma ngati kupweteka kukalipo, uzipereka moyo kulipa moyo.” (Matembenuzidwe ena amachititsa kuti kuwonekere ngati kuti m’chilamulo ichi kwa Israyeli nkhani yaikulu inali chimene chinachitikira kwa mayiyo, osati kwa mwana wosabadwayo. Komabe, Malembo oyambirira Achihebri, amanena za ngozi ya kupha kaya kwa mayiyo kapena mwana.)
Kodi kupha munthu dala pa chifukwa chosalolezedwa ndi Mulungu nkowopsa motani?
Gen. 9:6: “Amene akhetsa mwazi wa munthu, ndi munthunso mwazi wake udzakhetsedwa: chifukwa m’chifanizo cha Mulungu iye anampanga munthu.”
1 Yoh. 3:15: “Wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.”
Eks. 20:13: “Usaphe.”
Kodi lingaliro la dokotala lakuti kulola mimba kufikitsa nthaŵi yokwanira kukakhala kovulaza thanzi la mayiyo limalungamitsa kutaya mimba?
Nthaŵi zina malingaliro a madokotala ngolakwa. Kodi kukakhala kolungama kupha munthu mnzanu kuwopera kuti mungavulaze mnzake? Ngati panthaŵi ya kubadwa kwa mwana chosankha chiyenera kupangidwa pakati pa moyo wa mayi ndi uja wa mwana, kuli kwa anthu oloŵetsedwamowo kupanga chosankha chimenecho. Komabe, kupita patsogolo m’zamankhwala m’maiko ambiri kwachititsa mkhalidwe uwu kukhala wosawonekawoneka kwambiri.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Komatu ine ndiri ndi kuyenera kwa kupanga chosankha pankhani zimene zimayambukira thupi langa.’
Mungayankhe kuti: “Ndingathe kumvetsetsa mmene mukulingalirira. Kaŵirikaŵiri lerolino zoyenera zathu zimaponderezedwa ndi ena; unyinji sumadera nkhaŵa ndi zimene zimachitikira anthu ena. Koma Baibulo limapereka zitsogozo zimene zingatitetezere. Komabe, kuti tipeze mapindu, tiyeneranso kuvomereza mathayo.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Amayi ambiri asiyidwa ndi amuna amene ali atate a ana awo. Koma m’mabanja mmene onse aŵiri mwamuna ndi mkazi amakhala ndi moyo mwa miyezo ya Baibulo, mwamuna adzakondadi mkazi wake ndi ana ndipo mokhulupirika adzakhala nawo ndi kuwasamalira. (1 Tim. 5:8; Aef. 5:28-31)’ (2) ‘Ngati ife titi tilandire mwachindunji mtundu umenewu wachikondi ndi ulemu tifunikiranso kugwiritsira ntchito miyezo ya Baibulo m’maganizo athu kulinga ku ziŵalo zabanja lathu. Kodi ndimotani mmene Baibulo limanenera kuti tiyenera kuwona ana athu amene timabala? (Sal. 127:3; yerekezerani mosiyanitsa ndi Yesaya 49:15.)’