Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • rs tsamba 157-tsamba 161
  • Kubadwanso

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kubadwanso
  • Kukambitsirana za m’Malemba
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ngati Wina Anena Kuti—
  • Kodi Kubadwanso Kumatanthauza Chiyani?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • Kumwamba
    Kukambitsirana za m’Malemba
  • Kodi Kubadwanso Ndiyo Njira Yopezera Chipulumutso?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • Kodi Ndani Amene Amabadwanso?
    Nsanja ya Olonda—1992
Onani Zambiri
Kukambitsirana za m’Malemba
rs tsamba 157-tsamba 161

Kubadwanso

Tanthauzo: Kubadwanso kumaphatikizapo kubatizidwa m’madzi (“kubadwa mwa madzi”) ndi kubadwa ndi mzimu wa Mulungu (“kubadwa ndi . . . mzimu”), chotero kukhala mwana wa Mulungu ndi chiyembekezo cha kukhala ndi phande mu Ufumu wa Mulungu. (Yoh. 3:3-5) Yesu anali ndi chokumana nacho ichi, monga momwe a 144 000 aliri amene ali oloŵa nyumba limodzi naye mu Ufumu wakumwamba.

Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kwa Akristu alionse “kubadwanso”?

Mulungu analinganiza kugwirizanitsa chiŵerengero chochepa cha anthu okhulupirika limodzi ndi Yesu Kristu mu Ufumu wa wakumwamba

Luka 12:32: “Musawopa, kagulu kankhosa inu; chifukwa Atate wanu akonda kukupatsani ufumu.”

Chiv. 14:1-3: “Ndinapenya, tawonani, Mwanawankhosayo [Yesu Kristu] ali kuimirira paphiri la Ziyoni, ndipo pamodzi ndi iye zikwi zana mphambu makumi anayi kudza anayi . . . ogulidwa kuchokera kudziko.” (Wonanitsamba 208, 209, pamutu wakuti “Kumwamba.”)

Anthu sangapite kumwamba ndi matupi anyama ndi mwazi

1 Akor. 15:50: “Ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kuloŵa ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichimaloŵa chisavundi.”

Yoh. 3:6: “Chobadwa m’thupi chikhala thupi, ndipo chobadwa mwa mzimu, chikhala mzimu.”

Anthu okha amene “abadwanso,” mwanjira iyi kukhala ana aamuna a Mulungu, angagaŵane mu Ufumu wakumwamba

Yoh. 1:12, 13: “Koma onse amene anamulandira iye [Kristu Yesu], kwa iwo anapatsa mphamvu ya kukhala ana a Mulungu, kwa iwotu, akukhulupirira dzina lake; amene sanabadwa ndi mwazi, kapena ndi chifuniro chathupi, kapena ndi chifuniro chamunthu, koma cha Mulungu.” (“Onse amene anamulandira iye” samatanthauza kuti anthu onse amene akhulupirira mwa Kristu. Tawonani amene akutchulidwa, monga kwasonyezedwa ndi vesi 11 [“ake amwini yekha,” Ayuda]. Mwaŵi umodzimodziwo waperekedwa kwa ena amtundu wa anthu, koma kokha ku “kagulu kankhosa.”)

Aroma 8:16, 17, NW: “Mzimu uwo wokha umachitira umboni ndi mzimu wathu kuti ife tiri ana a Mulungu. Pamenepa, ngati, tiri ana, tirinso oloŵa nyumba ogwirizana limodzi ndi Kristu, malinga ngati tivutika limodzi kuti tikalemekezedwenso limodzi.”

1 Pet. 1:3, 4: “Wodalitsidwa Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Kristu, iye amene, monga mwa chifundo chake chachikulu, anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo, pa kuuka kwa akufa kwa Yesu Kristu; kuti tilandire choloŵa chosavunda ndi chosadetsa ndi chosafota, chosungikira m’Mwamba inu.”

Kodi iwo adzachitanji kumwamba?

Chiv. 20:6: “Adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Kristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi iye zaka chikwizo.”

1 Akor. 6:2: “Kodi sumudziŵa kuti oyera mtima adzaweruza dziko?”

Kodi munthu amene saali “wobadwanso” angapulumutsidwe?

Chiv. 7:9, 10, 17: “Zitatha izi [mtumwi Yohane atatha kumva chiŵerengero cha awo amene “akabadwanso,” amene akapanga Israyeli wauzimu ndi amene akakhala ndi Kristu kumwamba; yerekezerani ndi Aroma 2:28, 29 ndi Agalatiya 3:26-29] ndinapenya, tawonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga, ochokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe, akuimirira kumpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala zovala zoyera, ndi makhwata akanjedza m’manja mwawo; ndipo afuula ndi mawu aakulu, nanena, Chipulumutso kwa Mulungu wathu wakukhala pampando wachifumu, ndi kwa Mwanawankhosa . . . Mwanawankhosa [Yesu Kristu], wa kukhala pakati pa mpando wachifumu adzawaweta, nadzawatsogolera kumadzi amoyo.”

Pambuyo pa kundandalika anthu achikhulupiriro a m’nyengo za Chikristu chisanakhale, Ahebri 11:39, 40 amati: “Iwo onse adachitidwa umboni mwachikhulupiriro, sanalandira lonjezanolo, popeza Mulungu adatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe amphumphu popanda ife.” (Kodi ndani amene panopa akutanthauzidwa mwakuti “ife”? Ahebri 3:1 amasonyeza kuti iwo ndiwo “olandirana nawo maitanidwe akumwamba.” Pamenepo, anthu okhulupirika okhala m’nthaŵi za Chikristu chisanakhale, ayenera kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wangwiro kwinakwake kosakhala m’mwamba.)

Sal. 37:29: “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala m’mwemo kosatha.”

Chiv. 21:3, 4, NW: “Tawonani! Chihema cha Mulungu chiri ndi anthu, ndipo iye adzakhala pamodzi ndi iwo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Ndipo Mulungu mwiniyo adzakhala limodzi nawo. Ndipo iye adzapukuta msozi uliwonse m’maso mwawo, ndipo sikudzakhalanso imfa, ngakhale kulira maliro ngakhale kufuula ngakhale kupweteka sizidzakhalakonso. Zinthu zoyambazo zapita.”

Kodi nkotheka kwa munthu kukhala ndi mzimu wa Mulungu ndipo komabe nakhala ‘wosabadwanso’?

Ponena za Yohane mbatizi, mngelo wa Yehova anati: “Adzadzazidwa ndi mzimu woyera, kuyambira asanabadwe.” (Luka 1:15) Ndipo pambuyo pake Yesu anati: “Sanauke wakubadwa mwa akazi munthu wamkulu woposa Yohane mbatizi; koma iye amene ali wochepa mu ufumu wakumwamba amkulira iye [Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti Yohane sadzakhala m’miyamba ndipo chotero panalibe chifukwa chakuti iye “abadwenso”]. Ndipo kuyambira masiku a Yohane mbatizi kufikira tsopano lino [pamene Yesu analankhula mawuwa] ufumu wakumwamba uli wokakamizidwa.”—Mat. 11:11, 12.

Mzimu wa Yehova “unagwira ntchito” pa Davide ndipo “unalankhula” mwa iye (1 Sam. 16:13; 2 Sam. 23:2), koma palibe paliponse pamene Baibulo limanena kuti iye “anabadwanso.” Panalibe kufunikira kwa iye “kubadwanso,” chifukwa chakuti, monga momwe Machitidwe 2:34 amanenera kuti: “Davide sanakwere kumwamba.”

Kodi nchiyani chimene lerolino chimadziŵikitsa anthu okhala ndi mzimu wa Mulungu?

Wonani tsamba 320, 321, pamutu waukulu wakuti “Mzimu.”

Ngati Wina Anena Kuti—

‘Ndinabadwanso’

Mungayankhe kuti: ‘Ndiko kuti tsiku lina mukuyembekezera kukakhala ndi Kristu kumwamba, kodi sichoncho? . . . Kodi munayamba mwadabwa chimene opita kumwamba adzachita kumeneko?’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Adzakhala mafumu ndi ansembe, kulamulira pamodzi ndi Kristu. (Chiv. 20:6; 5:9, 10) Yesu ananena kuti amenewa akakhala kokha “kagulu kankhosa.” (Luka 12:32)’ (2) ‘Ngati pali mafumu, payeneranso kukhala nzika zimene iwo adzalamulira. Kodi zimenezi zidzakhala ayani? . . . Nazi mfundo zina zimene ndinapeza kukhala zokondweretsa kwambiri pamene zinasonyezedwa kwa ine. (Sal. 37:11, 29; Miy. 2:21, 22)’

‘Kodi munabadwanso?’

Mungayankhe kuti: ‘Ndimawona kuti chimene anthu amatanthauza mwa kumati “kubadwanso” sichiri nthaŵi zonse chofanana. Kodi mungandiuze chimene kumatanthauza kwa inu?’

Kapena munganene kuti: ‘Mufuna kudziŵa kuti kaya ndinavomereza Yesu Kristu monga Mpulumutsi wanga ndi kulandira mzimu woyera, kodi sichoncho? Ndiloleni ndikutsimikizireni kuti yankho ndilo Inde; ngati sizinali zotero sindikanakhala ndikulankhula ndi inu za Yesu.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Koma pamene ndikuganiza za kukhala ndi mzimu woyera, ndimapeza kuti umboni wamzimu umenewu ukusoŵeka momvetsa chisoni mwa ambiri odzitcha kukhala Akristu. (Agal 5:22, 23)’ (2) ‘Kodi mukanasangalala kukhala ndi moyo padziko lapansi iri ngati aliyense anasonyeza mikhalidwe yaumulungu imeneyo? (Sal. 37:10, 11)’

Kuthekera kwina: ‘Ngati mwa mawuwo mutanthauza kuti, “Kodi ndinavomereza Kristu monga Mpulumutsi wanga?” yankholo ndilo Inde. Onse a Mboni za Yehova atero. Koma, kwa ife, kubadwanso kumaphatikizapo zowonjezereka kuposa zimenezo.’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: (1) ‘Pamene Yesu analankhula za kubadwanso ananena kuti kunali kofunika kuloŵa Ufumu wa Mulungu, boma lake lakumwamba. (Yoh. 3:5)’ (2) ‘Baibulo limasonyezanso kuti anthu ambiri amene amachita chifuniro cha Mulungu adzakhala ndi moyo pano padziko lapansi, monga nzika zachimwemwe za Ufumu umenewo. (Mat. 6:10; Sal. 37:29)’

Malingaliro owonjezereka: Awo amene ali a kagulu kakumwamba angayankhe kuti: ‘Inde, ndiri. Koma Baibulo limachenjeza tonsefe kusakhala ndi chidaliro chopambanitsa cha ife eni. Tifunikira kudzipenda kuti titsimikizire kuti tikuchitadi zimene Mulungu ndi Kristu akuyembekezera kwa ife. (1 Akor. 10:12)’ Ndiyeno mwinamwake wonjezerani kuti: ‘Kodi ndithayo lotani limene Yesu anaika pa ophunzira ake owona? (Mat. 28:19, 20; 1 Akor. 9:16)’

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena