Oyera Mtima
Tanthauzo: Mogwirizana ndi kunena kwa chiphunzitso cha Roma Katolika, oyera mtima ali awo amene anafa ndi amene tsopano ali ndi Kristu kumwamba amene avomerezedwa ndi Tchalitchi kaamba ka chiyero chapadera ndi chisomo. Chilengezo cha upo wa Tridentine chonena za chikhulupiriro chimafotokoza kuti oyera mtima akapemphedwa kukhala ankhoswe kwa Mulungu ndi kuti ponse paŵiri zotsalira za oyera mtima ndi zifanizo za oyera mtima ziyenera kulemekezedwa. Nazonso, zipembedzo zina, zimapempha chithandizo cha oyera mtima. Zipembedzo zina zimaphunzitsa kuti mamembala awo onse ali oyera mtima ndipo ngopanda uchimo. Baibulo limatchula oyera mtima nthaŵi zambiri. Limatchula kwa otsatira a Kristu odzozedwa ndi mzimu a 144 000 kukhala otero.
Kodi Baibulo limaphunzitsa kuti munthu ayenera kukhala atapeza ulemelero wakumwamba asanazindikiridwe kukhala woyera mtima?
Baibulo limatchuladi oyera mtima, amene ali kumwamba. Yehova akulankhulidwa kukhala “woyera mtima [Chigiriki haʹgi·on].” (1 Pet. 1:15, 16; wonani Levitiko 11:45.) Yesu Kristu akulongosoledwa kukhala “Woyera mtima [haʹgi·os] wa Mulungu” pamene anali padziko lapansi ndipo monga “woyera [haʹgi·os]” pamene anali kumwamba. (Marko 1:24; Chiv. 3:7, JB) Nawonso angelo ali “oyera.” (Mac. 10:22, JB) Liwu lamaziko limodzimodzilo m’Chigiriki choyambirira likugwiritsiridwa ntchito kuchiŵerengero chokulirapo cha anthu padziko lapansi.
Mac. 9:32, 36-41: “Kunali, pakupita Petro ponseponse, anatsikiranso kwa oyera mtima [ha·giʹous] akukhala ku Luda. M’Yopa munali wophunzira dzina lake Tabita [amene anamwalira] . . . [Petro] potembenukira kumtembo anati, Tabita, uka. Ndipo anatsegula maso ake; ndipo pakuwona Petro, anakhala tsonga. Ndipo Petro anamgwira dzanja, namnyamutsa; ndipo mmene adaitana oyera mtima ndi amasiye, anampereka iye wamoyo.” (Mwachiwonekere oyera mtima ameneŵa anali asanakwere konse kumwamba, ndiponso simunthu mmodzi yekha wapadera monga Petro amene anawonedwa monga woyera mtima.)
2 Akor. 1:1; 13:12, JB: “Kuchokera kwa Paulo, woikidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi wa Kristu Yesu ndi kuchokera kwa Timoteo mmodzi wa abale, kutchalitchi cha Mulungu ku Korinto ndi kwa oyera mtima [ha·giʹois] onse mu Akaya monse.” “Patsani moni mwa kupsopsonana kopatulika. Oyera mtima onse akukupatsani moni.” (Akristu oyambirira onse ameneŵa amene anayeretsedwa ndi mwazi wa Kristu napatulidwa kaamba ka utumiki wa Mulungu kukhala oloŵa nyumba anzake a Kristu oyembekezeredwa ananenedwa kukhala oyera mtima. Mwachiwonekere kuzindikiridwa kwawo monga oyera mtima sikunakankhiridwe mtsogolo kufikira pambuyo pa kufa kwawo.)
Kodi kuli kogwirizana ndi Malemba kupemphera kwa “oyera mtima” kuti iwo achite monga ankhoswe kwa Mulungu?
Yesu Kristu anati: “Pempherani inu chomwechi; Atate ŵathu wa Kumwamba, . . .” Chotero mapemphero ayenera kulunjikitsidwa kwa Atate. Yesu anatinso: “Ine ndine njira, ndi chowonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate koma mwa ine. Ngati mudzapempha kanthu m’dzina langa, ndidzachita.” (Mat. 6:9; Yoh. 14:6, 14) Motero Yesu anatsutsa lingaliro lakuti munthu aliyense angakhoze kutenga malo a kukhala nkhoswe. Mtumwi Paulo anawonjezera ponena za Kristu kuti: “Amene adafera, inde makamaka, ndiye amene adauka kwa akufa, amene akhalanso padzanja lamanja la Mulungu, amenenso atipempherera ife.” ‘Iye ali nawo moyo wosatha kuti apembedzere onse amene afika kwa Mulungu kupyolera mwa iye.’ (Aroma 8:34; Aheb. 7:25, NW) Ngati ife tifunadi kuti mapemphero athu amvedwe ndi Mulungu, kodi sikukakhala kwanzeru kuyandikira Mulungu mwa njira imene Mawu ake amalangizira? (Wonaninso tsamba 258, 259, pamutu wakuti “Mariya.”)
Aef. 6:18, 19: “Pochezera pamenepo chichezerere ndi kupembedzera oyera mtima onse, ndi ine ndemwe, kuti andipatse mawu m’kunditsegulira m’kamwa molimbika, kuti ndizindikiritse anthu chinsinsicho cha uthenga wabwino.” (Kanyenye wawonjezeredwa.) (Panopa chilimbikitso chaperekedwa kupembedzera oyera mtima, koma osati kwa iwo kapena kupyolera mwa iwo. New Catholic Encyclopedia, 1967, Vol. XI, p. 670, imavomereza kuti: “Kaŵirikaŵiri m’Chi[pangano] Cha[tsopano], pemphero lonse, lamtseri kudzanso loperekedwa poyera, limalunjikitsidwa kwa Mulungu Atate kudzera mwa Kristu.”)
Aroma 15:30: “Ndikudandaulirani, abale, mwa Ambuye wathu Yesu Kristu ndi chikondi cha Mzimu, kuti mudzalimbike pamodzi ndi ine m’mapemphero anu kwa Mulungu chifukwa cha ine.” (Mtumwi Paulo, amene iyemwini anali woyera mtima, anapempha Akristu anzake amene analinso oyera mtima kumpempherera. Koma tawonani kuti Paulo sanalunjikitse mapemphero ake kwa oyera mtima anzake amenewo, ndiponso mapemphero awo ompempherera sanaloŵe mmalo mwa unansi wapafupi umene Paulo mwiniyo anali nawo ndi Atate mwanjira ya pemphero. Yerekezerani ndi Aefeso 3:11, 12, 14.)
Kodi ndimotani mmene chizoloŵezi cha kulambira zinthu zakale ndi zifanizo za “oyera mtima” chiyenera kuwonedwera?
New Catholic Encyclopedia ikuvomereza kuti: “Motero kuli kopanda pake kufunafuna kulungamitsa mwambo mwa zotsalira m’Chipangano Chakale; ndiponso chisamaliro chachikulu sichikuperekedwa ku zotsala m’Chipangano Chatsopano. . . . [“bambo” wa Tchalitchi] Origen akuwonekera kukhala akulingalira chizoloŵezichi kukhala chizindikiro chachikunja cha kupereka ulemu ku zinthu zokhudzika.”—(1967), Vol. XII, pp. 234, 235.
Kuli kokondweretsa kuwona kuti Mulungu anaika maliro a Mose, ndipo palibe munthu amene anadziŵa kumene manda ake anali. (Deut. 34:5, 6) Koma Yuda 9 amatiuza kuti Mikayeli mngelo wamkulu anakangana ndi Mdyerekezi ponena za mtembo wa Mose. Chifukwa ninji? Chifuno cha Mulungu cha kuutaya mwanjira yakuti anthu sakadziŵa kumene akaupeza chinafotokozedwa momvekera bwino. Kodi Mdaniyo anafuna kutsogolera anthu kumtembowo kotero kuti ukaikidwe pa chiwonetsero ndipo mwinamwake kukhala chinthu cholambiridwa?
Ponena za kulambiridwa kwa mafano a “oyera mtima,” wonani nkhani yakuti “Zifanizo.”
Kodi nchifukwa ninji “oyera mtima” Achikatolika amasonyezedwa ndi kuunika kozungulira mutu?
New Catholic Encyclopedia imavomereza kuti: “Mkhalidwe wotchuka koposa, wogwiritsiridwa ntchito kwa oyera mtima onse, ndiwo nimbus (mtambo), kuunika kwa mpangidwe wozungulira mutu wa woyera mtima. Magwero ake ndiwo nyengo ya Chikristu isanafike, ndipo zitsanzo zikupezedwa m’zithunzi zojambulidwa Zachihelene zimene chiyambi chake chiri chachikunja; kuunika kozungulira mutu kunagwiritsiridwa ntchito, monga momwe kwatsimikiziridwa ndi zithunzi zojambulidwa ndi za pandalama, ndi anthu olambiridwa ndi milungu monga ngati Neptune, Jupiter, Bacchus, ndipo makamaka Apollo (mulungu wa dzuŵa).”—(1967), Vol. XII, p. 963.
The New Encyclopædia Britannica imati: “M’zithunzithunzi zojambulidwa Zachihelene ndi Zachiroma mulungu wa dzuŵa Helios ndi mafumu Achiroma kaŵirikaŵiri amawonekera atavala nduŵira yachifumu yambaliŵali. Chifukwa cha chiyambi chake chachikunja, mchitidwewo unapeŵedwa pakati pa zithunzithunzi zojambulidwa za Akristu oyambirira, koma mzera umodzi wozungulira wa nimbus unavomerezedwa ndi olamulira Achikristu kaamba ka malo antchito a lamulo. Kuyambira cha pakati pa zaka za zana la 4, Kristu anadziŵikanso ndi mpangidwe umenewu wachifumu . . . Kunali m’zaka za zana la 6 pamene kuunika kozungulira mutu kumeneku kunafikira kukhala chizoloŵezi kwa Namwali Mariya ndi oyera mtima ena.”—(1976), Micropædia, Vol. IV, p. 864.
Kodi kuli koyenera kusanganiza Chikristu ndi zizindikiro zachikunja?
“Kuunika ndi mdima siziyenderana. Kristu saali wogwirizana ndi Beliyari [Beliyali; Satana], ndiponso wokhulupirira alibe chirichonse cha kugaŵana ndi wosakhulupirira. Kachisi wa Mulungu sadyerana ndi mafano, ndipo ndiye amene ife tiri—kachisi wa Mulungu wamoyo. . . . Pamenepo chokani kwa iwo ndi kutalikirana nawo, ati Ambuye. Musagwire kanthu kodetsedwa, ndipo ine ndidzakulandirani ndi kukhala atate wanu, ndipo inu mudzakhala ana anga aamuna ndi ana anga aakazi, ati Ambuye Wamphamvuyonse.”—2 Akor. 6:14-18, JB.
Kodi ziŵalo zonse za gulu lachipembedzo zingakhale zoyera mtima ndipo motero nazikhala zopanda uchimo?
Zinalidi zowona kuti onse amene anapanga mpingo Wachikristu wa m’zaka za zana loyamba anali oyera mtima. (1 Akor. 14:33, 34; 2 Akor. 1:1; 13:13, RS, KJ) Iwo akufotokozedwa kukhala anthu amene analandira “chikhululukiro cha machimo” ndipo “anayeretsedwa” ndi Mulungu. (Mac. 26:18; 1 Akor. 1:2, RS, KJ) Komabe, iwo sananene kuti anali omasuka ku uchimo uliwonse. Iwo anabadwa monga mbadwa za Adamu wochimwa. Kaŵirikaŵiri choloŵa chimenechi chinakupangitsa kukhala kovuta kwa iwo kuchita cholungama, monga momwe mtumwi Paulo modzichepetsa anavomerezera. (Aroma 7:21-25) Ndipo mtumwi Yohane ananena mosabisa mawu kuti: “Tikati kuti tiribe uchimo, tidzinyenga tokha, ndipo mwa ife mulibe chowonadi.” (1 Yoh. 1:8) Chotero, kukhala woyera mtima m’lingaliro limene liwulo likugwiritsiridwa ntchito kwa otsatira owona a Kristu sikumatanthauza kuti iwo ngosakhoza kuchimwa m’thupi.
Ponena za kuti kaya Akristu owona onse lerolino ali oyera mtima okhala ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba pamaso pawo, wonani tsamba 206-209.
Ngati Wina Anena Kuti—
‘Kodi mumakhulupirira oyera mtima?’
Mungayankhe kuti: ‘Kodi mukulingalira ati?’ Ngati munthuyo atchula Mariya ndi/kapena atumwi, inu mwinamwake mungawonjezere kuti: (1) ‘Inde, iwo amatchulidwa m’Malemba Opatulika, ndipo ndimakhulupirira zimene zalembedwa mmenemo. Koma ndiri kwakukulukulu wokondwera ndi zimene akuchita tsopano ndi mmene zimatiyambukirira, kodi inu simuli wotero? . . . Ndapeza kanthu kena kokondweretsa kwambiri ponena za iwo muno m’Malemba Opatulika, ndipo ndingakonde kukagaŵana nanu. (Chiv. 5:9, 10)’ [Tamverani, ponena za zimene mungagwiritsire ntchito ngati funso lidzutsidwa ponena za mawu alembedwa m’lembalo: JB imati “kulamulira dziko.” CC imati “kulamulira padziko lapansi.” Kx imalongosola kuti “kulamulira monga mafumu padziko lapansi.” Koma NAB ndi Dy amati “kulamulira padziko lapansi.” Kaamba ka ndemanga za gramala ya Chigiriki, wonani tsamba 210, pamutu wakuti “Kumwamba.”] (2) ‘Kodi moyo udzakhala wotani mu ulamuliro wa boma lotero? (Chiv. 21:2-4)’
Kapena munganene kuti (ngati inu nthaŵi ina munali Mkatolika): ‘Kwa zaka zambiri ndinkakhala ndi phande m’mapwando a oyera mtima ndipo nthaŵi zonse ndinkapemphera kwa iwo. Komano ndinaŵerenga kanthu kena m’Malemba Opatulika kamene kanandichititsa kupendanso zimene ndinali kuchita. Chonde, imani ndikusonyezeni. (Wonani tsamba 332.)’