Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 4
  • Wapakati Koma Wosakwatiwa

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Wapakati Koma Wosakwatiwa
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Mariya Anakhala ndi Pakati Asanakwatiwe
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
  • “Ndinetu Kapolo wa Yehova!”
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • “Ndinetu Mdzakazi wa Yehova!”
    Nsanja ya Olonda—2008
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 4

Mutu 4

Wapakati Koma Wosakwatiwa

MARIYA ali m’mwezi wachitatu wa kukhala ndi pakati. Mudzakumbukira kuti anathera masiku ake oyambirira a mimba yake akuchezera Elizabeti, koma tsopano wabwerera kwawo ku Nazarete. Mwamsanga mkhalidwe wake udzawonekera kwa onse m’tawuni ya kwawo. Ndithudi, iye, ali mumkhalidwe wovuta!

Chimene chikupangitsa mkhalidwewo kukhala woipa ndicho chakuti Mariya ngwotomeredwa kudzakhala mkazi wa mmisiri wamatabwa Yosefe. Ndipo iye amadziŵa kuti, pansi pa lamulo la Mulungu kwa Israyeli, mkazi amene ali wotomeredwa kwa mwamuna wina koma amene alolera mwadala kugonana ndi mwamuna wina ayenera kuponyedwa miyala kufikira imfa. Kodi iye angafotokoze motani za mimba yake kwa Yosefe?

Popeza kuti Mariya wakhala kulibe kwa miyezi itatu, tiri otsimikizira kuti Yosefe ali wofunitsitsa kumuwona. Pamene akumana, mwachiwokere Mariya akumuuza nkhaniyo. Iye angafotokoze mwa njira imene angakhoze nayo kuti kuli kupyolera mwa mzimu woyera wa Mulungu kuti iye ali ndi pakati. Koma, monga mmene mungayerekezerere, chimenechi chiri chinthu chovuta kwambiri kuti Yosefe akhulupirire.

Yosefe amadziŵa mbiri yabwino imene Mariya ali nayo. Ndipo mwachiwonekere amamkonda kwambiri. Komabe, mosasamala kanthu za zimene angadzinenere, zikuwonekeradi kuti iye ali ndi pakati pa mwamuna wina. Ngakhale ziri choncho, Yosefe sakufuna kuti iye aponyedwe miyala mpaka imfa kapena kuchititsidwa manyazi poyera. Chotero akuganiza za kumsudzula mwamtseri. M’masiku amenewo, anthu otomerana anawonedwa monga okwatirana, ndipo chisudzulo chinafunikira kuthetsa chitomero.

Pambuyo pake Yosefe akali kuganiza nkhani imeneyi, akupita kukagona. Mngelo wa Yehova akuwoneka kwa iye m’loto ndipo akuti: “Usawope kudzitengera wekha Mariya mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chiri cha mzimu woyera. Ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo udzamutcha dzina lake Yesu, pakuti iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”

Pamene Yosefe adzuka, ngwoyamikira chotani nanga! Mosachedwa akuchita monga mmene mngelo anamuuzira. Akutengera Mariya kunyumba kwake. M’chenicheni, kachitidwe kameneka kapoyera kakutumikira monga dzoma laukwati, kukumapereka chidziŵitso chakuti Yosefe ndi Mariya ali okwatirana mwalamulo tsopano. Koma Yosefe sakudziŵa mkazi wake Mariya pamene ali ndi pakati pa Yesu.

Tawonani! Mariya ngwotopa ndi mwanayo, komabe Yosefe akumkweza pabulu. Kodi akupita kuti, ndipo nchifukwa ninji akupanga ulendo pamene Mariya ali pafupi kubala mwana? Luka 1:39-41, 56; Mateyu 1:18-25; Deuteronomo 22:23, 24.

▪ Kodi mkhalidwe wa maganizo wa Yosefe ngwotani pamene adziŵa za mimba ya Mariya ndipo chifukwa ninji?

▪ Kodi Yosefe angasudzule motani Mariya pamene ali osakwatirana?

▪ Kodi ndimchitidwe wapoyera wotani umene ukutumikira monga dzoma laukwati wa Yosefe ndi Mariya?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena