Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 6
  • Mwana wa Lonjezo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mwana wa Lonjezo
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Mwana Amene Mulungu Analonjeza
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • ‘Anaganizira Tanthauzo la Mawu Onsewo Mumtima Mwake’
    Tsanzirani Chikhulupiriro Chawo
  • ‘Analingalira Mawuwo Mumtima Mwake’
    Nsanja ya Olonda—2008
  • Kodi Nkhani ya Mariya Imatiphunzitsa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 6

Mutu 6

Mwana wa Lonjezo

MMALO mwa kubwerera ku Nazarete, Yosefe ndi Mariya akutsalira ku Betelehemu. Ndipo pamene Yesu ali ndi masiku asanu ndi atatu, iwo akumdula, monga momwe Chilamulo cha Mulungu kwa Mose chimalamulilira. Kuli kwachiwonekerenso kuti ndimwambo wa kupatsa dzina mwana wamwamuna patsiku lachisanu ndi chitatu. Chotero akutchula mwana wawoyo dzina lakuti Yesu, monga momwe mngelo Gabrieli ananenera poyambapo.

Woposa mwezi umodzi ukupita, ndipo Yesu ali ndi masiku 40. Kodi makolo ake adzapita naye kuti tsopano? Ku kachisi ku Yerusalemu, amene ali makilomitala oŵerengeka chabe kuchokera kumene akukhala. Malinga ndi Chilamulo cha Mulungu kwa Mose, masiku 40 pambuyo pakubereka mwana wamwamuna, amayi afunikira kupereka nsembe yoyeretsa pa kachisi.

Zimenezo ndizo zimene Mariya akuchita. Monga chopereka chake, akubweretsa maunda aŵiri. Zimenezi zikuvumbula chinthu china ponena za mkhalidwe wa zachuma wa Yosefe ndi Mariya. Chilamulo cha Mose chimanena kuti mwana wa nkhosa, amene ali woŵerengeredwa mtengo kwambiri kuposa nkhunda, ayenera kuperekedwa. Koma ngati amayiwo sangakwanitse zimenezi, njiwa ziŵiri kapena maunda aŵiri akakhala okwanira.

M’kachisimo mwamuna wina wachikulire akuyangata Yesu m’manja mwake. Dzina lake ndiye Simeoni. Mulungu wavumbula kwa iye kuti sadzafa asanawone Kristu wolonjezedwa ndi Yehova kapena Mesiya. Pamene Simeoni afika kukachisi patsikuli, akutsogozedwa ndi mzimu woyera kukamwanako konyamulidwa ndi Yosefe ndi Mariya.

Pamene Simeoni ayangata Yesu akuyamika Mulungu, akumati: “Tsopano, Ambuye, monga mwa mawu anu aja, lolani ine, kapolo wanu, ndichoke mumtendere; chifukwa maso anga adawona chipulumutso chanu, chimene munakonza pamaso pa anthu onse, kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israyeli.”

Yosefe ndi Mariya akudabwa pamene akumva zimenezi. Pamenepo Simeoni akuwadalitsa ndipo akunena kwa Mariya kuti mwana wake wamwamunayo “uyu waikidwa akhale kugwa ndi kunyamuka kwa anthu ambiri mwa Israyeli” ndi kuti chisoni, monga lupanga lakuthwa, lidzapyoza moyo wake.

Pachochitikachi pali mneneri wachikazi wazaka 84 wotchedwa Anna. Kwenikweni, iye saphonya kufika pa kachisi. Paora lenileni limenelo iye akufika pafupi nayamba kuyamika Mulungu ndi kulankhula za Yesu kwa awo onse amene adzamva.

Yosefe ndi Mariya akondwa chotani nanga pazochitika zimenezi pakachisi! Ndithudi, zonsezi zikuwatsimikiziritsa kuti mwanayo ndiye Wolonjezedwa wa Mulungu. Luka 2:21-38; Levitiko 12:1-8.

▪ Kodi ndiliti pamene kunali kwachiwonekere kupatsa dzina khanda lalimuna Lachiisrayeli?

▪ Kodi nchiyani chinafunikira kwa mkazi Wachiisrayeli pamene mwana wake wamwamuna anali ndi masiku 40, ndipo kodi ndimotani mmene kukwaniritsidwa kwa chofunika chimenechi kumavumbulira mkhalidwe wazachuma wa Mariya?

▪ Kodi ndani amene akuzindikira amene anali Yesu pachochitika chimenechi, ndipo akusonyeza motani zimenezi?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena