Mutu 7
Yesu ndi Openda Nyenyezi
AMUNA ena angapo akudza kuchokera Kummaŵa. Iwo ndiwo openda nyenyezi—anthu amene amadzinenera kukhala odziwa kutanthauzira mkhalidwe wa nyenyezi. Pamene anali kwawo Kummaŵa, iwo anawona nyenyezi yatsopano, ndipo ayilondola kwa makilomitala mazana ambiri kufika ku Yerusalemu.
Pamene openda nyenyezi afika ku Yerusalemu, akufunsa kuti: “Ali kuti amene anabadwa Mfumu ya Ayuda? chifukwa tinawona nyenyezi yake kummaŵa, ndipo tinadzera kudzamlambira iye.”
Pamene Mfumu Herode amva zimenezi ku Yerusalemu, iye akukwiya kwambiri. Chotero akuitana akulu ansembe nawafunsa kumene Kristu adzabadwira. Pozika yankho lawo pa Malemba, iwo akuyankha kuti: “Ku Betelehemu.” Pamenepo, Herode akuchititsa openda nyenyezi kudza kwa iye nawauza kuti: “Yendani mufunitsitse za kamwanako; ndipo pamene mudzampeza, mundibwezere mawu, kuti inenso ndidzadze kudzamlambira iye.” Koma kwenikweni, Herode akufuna kupeza mwanayo kuti amuphe!
Atachoka, chinthu chodabwitsa chikuchitika. Nyenyezi imene adaiwona pamene anali Kummaŵa ikuyenda patsogolo pawo. Mwachiwonekere imeneyi sinyenyezi wamba, koma yaperekedwa mwapadera kuti iwatsogolere. Openda nyenyezi akuitsatirabe mpaka ikuima pamwamba pa nyumba imene Yosefe ndi Mariya akukhala.
Pamene openda nyenyezi aloŵa m’nyumbamo, akupeza Mariya ndi mwana wake wakhandayo, Yesu. Pamenepo onsewo akumgwadira. Ndipo akutulutsa mphatso zawo za golidi, zonunkhira, ndi mure. Pambuyo pake, pamene ali pafupi kubwerera ndi kuuza Herode za kumene kuli mwanayo, akuchenjezedwa ndi Mulungu m’kulota kuti asatero. Chotero iwo akubwerera kudziko lakwawo ndi njira ina.
Muganiza kuti ndani amene anapereka nyenyezi imene inayenda m’mlengalenga kutsogolera openda nyenyezi? Kumbukirani, nyenyeziyo sinawatsogolere mwachindunji kwa Yesu ku Betelehemu. Mmalomwake, inawatsogolera ku Yerusalemu kumene anakumana ndi Mfumu Herode, amene anafuna kupha Yesu. Ndipo akadaterodi ngati Mulungu sanaloŵerere ndi kuchenjeza openda nyenyeziwo kusakauza Herode kumene Yesu anali. Anali mdani wa Mulungu, Satana Mdyerekezi, amene anafuna kuti Yesu aphedwe, ndipo anagwiritsira ntchito nyenyezi imeneyo kuyesayesa kukwaniritsa chifuno chake. Mateyu 2:1-12; Mika 5:2.
▪ Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti nyenyezi imene openda nyenyezi anawona sinali nyenyezi wamba?
▪ Kodi Yesu ali kuti pamene openda nyenyezi ampeza?
▪ Kodi nchifukwa ninji timadziŵa kuti Satana ndiye anapereka nyenyezi kutsogolera openda nyenyeziwo?