Mutu 8
Kuthaŵa Wolamulira Wankhalwe
YOSEFE akudzutsa Mariya kuti amuuze nkhani yofulumira kwambiri. Mngelo wa Yehova wangowonekera kumene kwa iye, akumati: “Tauka, nutenge kamwanako ndi amake, nuthaŵire ku Aigupto, nukakhale kumeneko kufikira ndidzakuuza iwe; pakuti Herode adzafuna kamwana kukawononga iko.”
Mwamsanga, atatuwo akuthaŵa. Ndipo izi zangochitika panthaŵi yake chifukwa chakuti Herode wadziŵa kuti openda nyenyezi amnyenga ndipo achoka m’dzikolo. Kumbukirani, kuti iwo anafunikira kubwezera mawu kwa iye pamene apeza Yesu. Herode wakwiya. Chotero m’kuyesayesa kupha Yesu, akupereka lamulo la kupha ana aamuna onse m’Betelehemu ndi milaga yake amene ali ndi zaka zakubadwa ziŵiri kapena kucheperapo. Iye akukhazika maziko a kuŵerengera msinkhu kumeneku pachidziŵitso chimene adapeza poyambirira kuchokera kwa openda nyenyezi amene adachokera Kummaŵa.
Kuphedwa kwa makanda achimuna onse ndiko kanthu kena kowopsa kukawona! Asilikali a Herode akuloŵa nyumba ndi nyumba. Ndipo pamene apeza khanda lachimuna, akuligwira kulichotsa m’manja mwa amake. Sitidziŵa kuchuluka kwa makanda amene iwo akupha, koma kulira kwakukulu ndi kuchema kwa anakubala kukukwaniritsa ulosi wa m’Baibulo wonenedwa ndi mneneri wa Mulungu Yeremiya.
Zidakali chomwecho, Yosefe ndi banja lake akufika mwachisungiko ku Aigupto, ndipo tsopano iwo akhala kumeneko. Koma usiku wina mngelo wa Yehova akuwonekeranso kwa Yosefe m’loto. “Tauka, nutenge kamwana ndi amake,” akutero mngeloyo, “nupite kudziko la Israyeli: chifukwa anafa uja wofuna moyo wake wa kamwanako.” Chotero m’kukwaniritsidwa kwa ulosi wina wa Baibulo umene umanena kuti Mwana wa Mulungu akaitanidwa kuchoka mu Aigupto, banjalo likubwerera kudziko lakwawo.
Mwachiwonekere Yosefe ali ncholinga cha kukhala ku Yudeya, kumene anali kukhala m’tauni ya Betelehemu asanathaŵire ku Aigupto. Koma amva kuti mwana woipa wa Herode Arikelao ndiye mfumu ya Yudeya, ndipo m’kulota kwina iye akuchenjezedwa ndi Yehova za upanduwo. Chotero Yosefe ndi banja lake akumka chakumpoto kukakhazikika m’tauni ya Nazarete m’Galileya. Kunoko m’chitanganya ichi, kutali ndi malo apakati a moyo wa kulambira Kwachiyuda, Yesu akukulirako. Mateyu 2:13-23; Yeremiya 31:15; Hoseya 11:1.
▪ Pamene openda nyenyezi sakubwerera, kodi ndichinthu chochititsa mantha chotani chimene Mfumu Herode akuchita, koma kodi Yesu akutchinjirizidwa motani?
▪ Pobwerera kuchokera ku Aigupto, kodi nchifukwa ninji Yosefe sakukakhalanso ku Betelehemu?
▪ Kodi ndimaulosi a Baibulo ati amene akukwaniritsidwa mkati mwa nyengo imeneyi?