Mutu 11
Yohane Akonza Njira
ZAKA khumi ndi zisanu ndi ziŵiri zapita kuyambira pamene Yesu anali mwana wa zaka 12 akumafunsa aphunzitsi m’kachisi. Iri nthaŵi ya ngululu ya chaka cha 29 C.E., ndipo kukuwonekera kuti, aliyense, akulankhula za Yohane mbale wina wa Yesu, amene akulalikira m’dziko lonselo mozungulira Mtsinje wa Yordano.
Yohane alidi munthu wochititsa chidwi, ponse paŵiri m’kawonekedwe ndi m’kalankhulidwe. Zovala zake ziri za ubweya wangamira, ndipo amavala lamba wachikopa m’chuuno mwake. Chakudya chake ndicho dzombe ndi uchi. Ndipo uthenga wake? “Tembenukani mitima; chifukwa ufumu wakumwamba wayandikira.”
Uthengawu ukuchititsa chidwi omvetsera ake. Ambiri akuzindikira kufunikira kwawo kulapa, ndiko kuti, kusintha mkhalidwe wawo ndi kukana njira yawo yapapitapo yamoyo kukhala yosafunika. Chotero kuchokera kugawo lonse lozungulira Yordano, ndipo ngakhale ku Yerusalemu, anthu akudza kwa Yohane m’ziŵerengero zazikulu, ndipo iye akuwabatiza, akumawamiza pansi pa madzi a Yordano. Chifukwa ninji?
Yohane akubatiza anthu kuchitira chizindikiro, kapena kuvomereza, kulapa kwawo kochokera pansi pa mtima kaamba ka kuchimwira pangano Lachilamulo cha Mulungu. Motero, pamene Afarisi ena ndi Asaduki adza ku Yordano, Yohane akuwatsutsa. “Obadwa a njoka inu,” iye akutero. “Wonetsani inu zipatso za kuyenera kutembenuka mtima: ndipo musamayesa kunena mwa inu nokha kuti, Atate wathu tiri naye Abrahamu; pakuti ndinena ndi inu kuti mwa miyala iyi Mulungu akhoza kuukitsira Abrahamu ana. Ndiponso tsopano lino nkhwangwa yaikidwa pa mizu ya mitengo: chifukwa chake mtengo uliwonse wosabala zipatso zabwino udulidwa nuponyedwa pamoto.”
Chifukwa cha chisamaliro chonse chimene Yohane akulandira, Ayuda akutumiza ansembe ndi Alevi kwa iye. Ameneŵa akufunsa kuti: ‘Kodi iwe ndiwe yani?’
‘Sindiri Kristu,’ Yohane akunena motero.
‘Nangano pamenepa?’ iwo akufunsa motero. ‘Kodi ndiwe Eliya?’
‘Sindiri,’ iye akuyankha motero.
‘Kodi ndiwe Mneneri?’
‘Ayi!’
Chotero iwo akuumirirabe kufunsa kuti: ‘Kodi ndiwe yani? kutsata kuti tikapereke yankho kwa awo amene anatituma. Kodi ukuti bwanji ponena za iwe mwini?’
Yohane akufotokoza kuti: “Ndine mawu a wofuula m’chipululu, Lungamitsani njira ya Mbuye, monga anati Yesaya mneneriyo.”
“Koma ubatiza bwanji,” iwo akufuna kudziŵa, “ngati siuli Kristu kapena Eliya, kapena Mneneriyo?”
“Ine ndibatiza ndi madzi,” iye akuyankha motero. “Pakati panu paimirira amene simumdziŵa, ndiye wakudza pambuyo panga.”
Yohane akukonza njira mwakuchititsa anthu kukhala ndi khalidwe labwino la mtima kulandira Mesiya, amene adzakhala Mfumu. Ponena za Ameneyu, Yohane akuti: “Ndiye wakudza pambuyo panga, amene sindiyenera kummasulira lamba la nsapato yake.” Kwenikweni, Yohane akunenadi kuti: “Wakudza pambuyo panga analipo ndisanabdwe ine; chifukwa anakhala woyamba wa ine.”
Motero, uthenga wa Yohane wakuti, “ufumu wakumwamba wayandikira,” ukutumikira monga chidziŵitso chapoyera chakuti uminisitala wa Mfumu yoikidwa ya Yehova, Yesu Kristu, uli pafupi kuyamba. Yohane 1:6-8, 15-28; Mateyu 3:1-12; Luka 3:1-18; Machitidwe 19:4.
▪ Kodi Yohane ndimunthu wamtundu wanji?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yohane akubatiza anthu?
▪ Kodi nchifukwa ninji Yohane anganene kuti Ufumu wayandikira?