Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • gt mutu 18
  • Yohane Achepa, Yesu Akula

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yohane Achepa, Yesu Akula
  • Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Nkhani Yofanana
  • Ntchito ya Yesu Inayamba Kuwonjezeka Kuposa ya Yohane
    Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo
  • Kodi Yohane Anasoŵa Chikhulupiliro?
    Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
  • Kodi Yohane Analibe Chikhulupiriro?
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Yohane M’batizi—Chitsanzo Chabwino pa Nkhani Yokhalabe Wosangalala
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2019
Onani Zambiri
Munthu Wamkulu Woposa Onse Amene Anakhalako
gt mutu 18

Mutu 18

Yohane Achepa, Yesu Akula

PAMBUYO pa Paskha m’ngululu ya 30 C.E., Yesu ndi ophunzira ake akuchoka m’Yerusalemu. Komabe, iwo sakubwerera kwawo ku Galileya koma akumka kudziko la Yudeya, kumene akuchita ubatizo. Yohane Mbatizi wakhala akuchita ntchito yofananayo kwa pafupifupi chaka chimodzi tsopano, ndipo iye adakali ndi ophunzira amene akuyanjana naye.

Kwenikweni, Yesu sakubatiza konse iye mwini, koma ophunzira ake akutero pansi pa chitsogozo chake. Ubatizo wawo uli ndi chizindikiro chofanana ndi chija chochitidwa ndi Yohane, ukumakhala chizindikiro cha kulapa kwa Myuda machimo pa chipangano cha Chilamulo cha Mulungu. Komabe, pambuyo pa chiukiriro chake, Yesu akulangiza ophunzira ake kuchita ubatizo umene uli ndi chizindikiro chosiyana. Ubatizo Wachikristu lerolino ndiwo chizindikiro cha kudzipatulira kwa munthu kutumikira Yehova Mulungu.

Komabe, pamfundo yoyambirirayi muuminisitala wa Yesu, onse aŵiri Yohane ndi iye, ngakhale kuti akugwira ntchito molekana, akuphunzitsa ndi kubatiza anthu olapa. Koma ophunzira a Yohane akuchita nsanje ndi kumdandaulira ponena za Yesu: “Rabi, . . . tawonani yemweyu abatiza, ndipo anthu onse alinkudza kwa iye.”

Mmalo mwa kukhala wansanje, Yohane akukondwera kuwona chipambano cha Yesu ndiponso iye akufuna kuti ophunzira ake akondwere. Iye akuwakumbutsa kuti: “Inu nokha mundichitira umboni kuti ndinati, Sindine Kristu, koma kuti ndiri wotumidwa mtsogolo mwake mwa iye.” Ndiyeno akugwiritsira ntchito chitsanzo china chabwino kwambiri: “Iye amene ali naye mkwatibwi ali mkwati, koma mnzake wa mkwatiyo, wakuimirira ndi kumvera iye, akondwera kwakukulu chifukwa cha mawu a mkwatiyo; chifukwa chake chimwemwe changa chimene chakwanira.”

Yohane, monga bwenzi la Mkwati, anasangalala kuchiyambiyambi miyezi isanu ndi umodzi pamene anadziŵikitsa ophunzira ake kwa Yesu. Ena a iwo anakhala ziŵalo zoyembekezeredwa za kagulu ka mkwatibwi wa Kristu kakumwamba koti kapangidwe ndi Akristu odzozedwa ndi mzimu. Yohane akufuna kuti ophunzira ake amene alipowo nawonso atsatire Yesu, popeza kuti chifuno chake ndicho cha kukonzekeretsa njira ya uminisitala wachipambano wa Kristu. Monga momwe Yohane Mbatiziyo akufotokozera kuti: “Iyeyo ayenera kukula koma ine ndiyenera ndichepe.”

Wophunzira wa Yesu watsopano Yohane, amene papitapo analinso wophunzira wa Yohane Mbatizi, akulemba za chiyambi cha Yesu ndi ntchito Yake yofunika pachipulumutso cha anthu, akumati: “Iye wochokera kumwamba ali woposa onse; . . . Atate akonda Mwana, nampatsa zinthu zonse m’dzanja lake. Iye amene akukhulupilira Mwanayo ali nawo moyo wosatha; koma iye amene sakhulupilira Mwanayo sadzawona moyo, koma mkwiyo wa Mulungu ukhala pa iye.”

Pasanapite nthaŵi yaitali Yohane Mbatizi atanena za kuchepa kwa ntchito yake, iye akugwidwa ndi Mfumu Herode. Herode watenga Herodiya, mkazi wa Filipo mbale wake, monga mkazi wake, ndipo pamene Yohane avumbula mwapoyera zochitika zakezo monga zosayenera, Herode akumuika m’ndende. Pamene Yesu amva za kumangidwa kwa Yohane, iye akuchoka m’Yudeya ndi atumwi ake kumka ku Galileya. Yohane 3:22–4:3; Machitidwe 19:4; Mateyu 28:19; 2 Akorinto 11:2; Marko 1:14; 6:17, 20.

▪ Kodi nchiyani chimene chiri tanthauzo la ubatizo wochitidwa motsogozedwa ndi Yesu chiukiliro chake chisanachitike? Ndi pambuyo pa chiukiliro chake?

▪ Kodi Yohane akusonyeza motani kuti kudandaula kwa atumwi ake kuli kosayenerera?

▪ Kodi Yohane waikidwiranji m’ndende?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena